< בראשית 9 >

ויברך אלהים את נח ואת בניו ויאמר להם פרו ורבו ומלאו את הארץ 1
Ndipo Mulungu anadalitsa Nowa ndi ana ake aamuna nati kwa iwo, “Berekanani ndipo muchulukane ndi kudzaza dziko lapansi.
ומוראכם וחתכם יהיה על כל חית הארץ ועל כל עוף השמים בכל אשר תרמש האדמה ובכל דגי הים בידכם נתנו 2
Nyama zonse za dziko lapansi, ndi mbalame zonse za mlengalenga, ndi chamoyo chilichonse chokwawa, ndiponso nsomba zonse za ku nyanja; zidzakuopani ndipo ndazipereka kuti muzilamulire.
כל רמש אשר הוא חי לכם יהיה לאכלה כירק עשב נתתי לכם את כל 3
Tsopano chamoyo chilichonse chidzakhala chakudya chanu. Monga momwe ndinakupatsirani ndiwo zamasamba, tsopano ndikupatsaninso nyama iliyonse.
אך בשר בנפשו דמו לא תאכלו 4
“Koma musamadye nyama imene ikanali ndi magazi oyenda.
ואך את דמכם לנפשתיכם אדרש מיד כל חיה אדרשנו ומיד האדם מיד איש אחיו--אדרש את נפש האדם 5
Aliyense wopha munthu adzaphedwa, nyama iliyonse yopha munthu idzaphedwa, munthu aliyense wopha munthu mnzake, adzaphedwa.
שפך דם האדם באדם דמו ישפך כי בצלם אלהים עשה את האדם 6
“Aliyense wopha munthu, adzaphedwanso ndi munthu; pakuti Mulungu analenga munthu mʼchifanizo chake.
ואתם פרו ורבו שרצו בארץ ורבו בה 7
Inu muberekane ndi kuchulukana kuti mudzaze dziko lonse lapansi ndi kuligonjetsa.”
ויאמר אלהים אל נח ואל בניו אתו לאמר 8
Mulungu anawuza Nowa ndi ana ake kuti,
ואני הנני מקים את בריתי אתכם ואת זרעכם אחריכם 9
“Tsopano Ine ndapangana ndi iwe ndi zidzukulu zako zamʼtsogolomo,
ואת כל נפש החיה אשר אתכם בעוף בבהמה ובכל חית הארץ אתכם מכל יצאי התבה לכל חית הארץ 10
pamodzi ndi zamoyo zonse, mbalame, ziweto ndi nyama zonse za kuthengo, ndi zonse zimene zinatuluka mʼchombo pamodzi ndi iwe.
והקמתי את בריתי אתכם ולא יכרת כל בשר עוד ממי המבול ולא יהיה עוד מבול לשחת הארץ 11
Pangano langa ndi ili: Ine ndilonjeza kuti sindidzawononganso zamoyo ndi madzi a chigumula. Chigumula sichidzawononganso dziko lapansi.”
ויאמר אלהים זאת אות הברית אשר אני נתן ביני וביניכם ובין כל נפש חיה אשר אתכם--לדרת עולם 12
Ndipo Mulungu anati, “Ine ndikupereka chizindikiro ichi cha pangano langa la pakati pa Ine ndi iwe, ana ako, zamoyo zonse, pamodzi ndi mibado ya mʼtsogolo.
את קשתי נתתי בענן והיתה לאות ברית ביני ובין הארץ 13
Ndayika utawaleza wanga mʼmitambo, ndipo chidzakhala chizindikiro cha pangano langa ndi dziko lapansi.
והיה בענני ענן על הארץ ונראתה הקשת בענן 14
Nthawi zonse pakakhala mitambo mu mlengalenga ndipo utawaleza uwoneka,
וזכרתי את בריתי אשר ביני וביניכם ובין כל נפש חיה בכל בשר ולא יהיה עוד המים למבול לשחת כל בשר 15
ndizikumbukira pangano langa pakati pa Ine ndi inu ndi zolengedwa zonse. Madzi sadzakhalanso chigumula chowononga dziko lapansi.
והיתה הקשת בענן וראיתיה לזכר ברית עולם בין אלהים ובין כל נפש חיה בכל בשר אשר על הארץ 16
Utawaleza ukamadzaoneka mʼmitambo, ndidzawuona ndi kukumbukira pangano losatha pakati pa Mulungu ndi zamoyo zonse pa dziko lapansi.”
ויאמר אלהים אל נח זאת אות הברית אשר הקמתי ביני ובין כל בשר אשר על הארץ 17
Choncho Mulungu anati kwa Nowa, “Ichi ndiye chizindikiro cha pangano limene ndalichita pakati pa Ine ndi zamoyo zonse pa dziko lapansi.”
ויהיו בני נח היצאים מן התבה--שם וחם ויפת וחם הוא אבי כנען 18
Ana aamuna a Nowa amene anatuluka mʼchombo muja anali Semu, Hamu ndi Yafeti. Hamu anali abambo ake a Kanaani.
שלשה אלה בני נח ומאלה נפצה כל הארץ 19
Ana aamuna a Nowa amenewa ndiwo anali makolo a anthu onse pa dziko lapansi.
ויחל נח איש האדמה ויטע כרם 20
Nowa anali munthu woyamba kulima munda wamphesa.
וישת מן היין וישכר ויתגל בתוך אהלה 21
Tsiku lina pamene Nowa anamwako vinyo wa zipatso za mʼmundawo analedzera ndipo anavula zovala zake zonse ndi kugona mu tenti yake ali maliseche.
וירא חם אבי כנען את ערות אביו ויגד לשני אחיו בחוץ 22
Hamu, abambo ake a Kanaani ataona kuti abambo ake ali maliseche anakawuza abale ake awiri aja omwe anali panja.
ויקח שם ויפת את השמלה וישימו על שכם שניהם וילכו אחרנית ויכסו את ערות אביהם ופניהם אחרנית וערות אביהם לא ראו 23
Koma Semu ndi Yafeti anatenga chofunda nachiyika pa mapewa awo; ndipo anayenda chamʼmbuyo naphimba umaliseche wa abambo awo. Anafulatira kuti asaone umaliseche wa abambo awo.
וייקץ נח מיינו וידע את אשר עשה לו בנו הקטן 24
Nowa atadzuka, kuledzera kutatha, ndikudziwa zimene mwana wake wamngʼono wamwamuna uja anamuchitira,
ויאמר ארור כנען עבד עבדים יהיה לאחיו 25
anati, “Atembereredwe Kanaani! Adzakhala kapolo wa pansi kwenikweni kwa abale ake.”
ויאמר ברוך יהוה אלהי שם ויהי כנען עבד למו 26
Anatinso, “Atamandike Yehova, Mulungu wa Semu! Kanaani akhale kapolo wa Semu.
יפת אלהים ליפת וישכן באהלי שם ויהי כנען עבד למו 27
Mulungu akulitse dziko la Yafeti; Yafeti alandire madalitso pamodzi ndi Semu, ndipo Kanaani akhale kapolo wawo.”
ויחי נח אחר המבול שלש מאות שנה וחמשים שנה 28
Chitatha chigumula, Nowa anakhala ndi moyo zaka 350.
ויהיו כל ימי נח תשע מאות שנה וחמשים שנה וימת 29
Anamwalira ali ndi zaka 950.

< בראשית 9 >