< בראשית 50 >

ויפל יוסף על פני אביו ויבך עליו וישק לו 1
Kenaka Yosefe anadzigwetsa pa nkhope ya abambo ake, nawapsompsona kwinaku akulira.
ויצו יוסף את עבדיו את הרפאים לחנט את אביו ויחנטו הרפאים את ישראל 2
Ndipo Yosefe analamula antchito ake a chipatala kuti akonze thupi la Israeli ndi mankhwala kuti lisawole. Kotero antchitowo anakonzadi thupilo.
וימלאו לו ארבעים יום כי כן ימלאו ימי החנטים ויבכו אתו מצרים שבעים יום 3
Antchito aja zinawatengera masiku 40 kuti akonze mtembo uja popeza ntchito ngati imeneyi inafunikira masiku monga amenewa. Ndipo Aigupto anamulira Yakobo kwa masiku makumi asanu ndi awiri.
ויעברו ימי בכיתו וידבר יוסף אל בית פרעה לאמר אם נא מצאתי חן בעיניכם--דברו נא באזני פרעה לאמר 4
Yosefe atatha kulira maliro a abambo ake, anayankhula kwa nduna za Farao nati, “Ngati mungandikomere mtima, chonde mundiyankhulire kwa Farao kumuwuza kuti,
אבי השביעני לאמר הנה אנכי מת--בקברי אשר כריתי לי בארץ כנען שמה תקברני ועתה אעלה נא ואקברה את אבי--ואשובה 5
‘Abambo anga anandilumbiritsa ndipo anati, ‘Ndatsala pangʼono kumwalira, ukandiyike mʼmanda amene ndinakumba ndekha mʼdziko la Kanaani.’ Tsono mundilole ndikayike abambo anga, ndipo ndikabweranso.’”
ויאמר פרעה עלה וקבר את אביך כאשר השביעך 6
Farao anati, “Pita ukayike abambo ako monga anakulumbiritsa kuti uchite.”
ויעל יוסף לקבר את אביו ויעלו אתו כל עבדי פרעה זקני ביתו וכל זקני ארץ מצרים 7
Kotero Yosefe anapita kukayika abambo ake. Nduna zonse za Farao, akuluakulu a bwalo lake ndi akuluakulu a ku Igupto, anapita naye pamodzi.
וכל בית יוסף ואחיו ובית אביו רק טפם וצאנם ובקרם--עזבו בארץ גשן 8
Anapitanso onse a pa banja la Yosefe ndi abale ake ndi onse amene anali a pa banja la abambo ake. Ana awo okha, nkhosa ndi ngʼombe zinatsala ku Goseni
ויעל עמו גם רכב גם פרשים ויהי המחנה כבד מאד 9
Asilikali okwera pa magaleta ndi asilikali a pa akavalo anapita nayenso pamodzi. Linali gulu lalikulu.
ויבאו עד גרן האטד אשר בעבר הירדן ויספדו שם מספד גדול וכבד מאד ויעש לאביו אבל שבעת ימים 10
Atafika pa Goreni ha-Atadi, pafupi ndi Yorodani, anachita mwambo waukulu wa maliro. Choncho Yosefe analira maliro a abambo ake masiku asanu ndi awiri.
וירא יושב הארץ הכנעני את האבל בגרן האטד ויאמרו אבל כבד זה למצרים על כן קרא שמה אבל מצרים אשר בעבר הירדן 11
Akanaani amene ankakhala ku Goreni ha-Atadi ataona mwambo wa maliro anati, “Aigupto ali ndi mwambo wa maliro a akulu.” Ndi chifukwa chake malo amenewo a pafupi ndi Yorodani amatchedwa Abeli-Mizraimu.
ויעשו בניו לו--כן כאשר צום 12
Choncho ana a Yakobo anachita monga momwe abambo awo anawalamula:
וישאו אתו בניו ארצה כנען ויקברו אתו במערת שדה המכפלה אשר קנה אברהם את השדה לאחזת קבר מאת עפרן החתי--על פני ממרא 13
Ndiye kuti ana a Yakobo anamunyamula kupita naye ku Kanaani kuti akamuyike mʼphanga limene lili mʼmunda wa Makipela pafupi ndi Mamre. Abrahamu anagula mundawo kwa Efroni Mhiti kuti pakhale manda.
וישב יוסף מצרימה הוא ואחיו וכל העלים אתו לקבר את אביו אחרי קברו את אביו 14
Atatha kuyika abambo ake, Yosefe anabwerera ku Igupto, pamodzi ndi abale ake ndi onse amene anapita nawo kukayika abambo ake.
ויראו אחי יוסף כי מת אביהם ויאמרו לו ישטמנו יוסף והשב ישיב לנו את כל הרעה אשר גמלנו אתו 15
Abale ake a Yosefe ataona kuti abambo awo amwalira, anati, “Nanga tidzatani ngati Yosefe anatisungira mangawa nafuna kutibwezera pa zoyipa zonse zimene tinamuchitira?”
ויצוו אל יוסף לאמר אביך צוה לפני מותו לאמר 16
Motero anatumiza mawu kwa Yosefe kuti, “Abambo anu anasiya malangizo asanafe nati:
כה תאמרו ליוסף אנא שא נא פשע אחיך וחטאתם כי רעה גמלוך ועתה שא נא לפשע עבדי אלהי אביך ויבך יוסף בדברם אליו 17
‘Zimene mudzayenera kunena kwa Yosefe ndi izi: Ndikukupempha kuti uwakhululukire abale ako cholakwa chawo ndi machimo awo, popeza anakuchitira zoyipa.’ Ndiye tsopano chonde tikhululukireni zolakwa zimene ife akapolo a Mulungu wa abambo anu tinachita.” Yosefe atangomva mawu amenewa anayamba kulira.
וילכו גם אחיו ויפלו לפניו ויאמרו הננו לך לעבדים 18
Kenaka abale ake anabwera nadzigwetsa pansi pamaso pake, nati, “Ife ndife akapolo anu.”
ויאמר אלהם יוסף אל תיראו כי התחת אלהים אני 19
Koma Yosefe anawawuza kuti, “Musachite mantha. Kodi ine ndalowa mʼmalo mwa Mulungu?
ואתם חשבתם עלי רעה אלהים חשבה לטבה למען עשה כיום הזה להחית עם רב 20
Inu munafuna kundichitira zoyipa, koma Mulungu anasandutsa zoyipazo kuti zikhale zabwino kuti zikwaniritsidwe zimene zikuchitika panozi, zopulumutsa miyoyo yambiri.
ועתה אל תיראו--אנכי אכלכל אתכם ואת טפכם וינחם אותם וידבר על לבם 21
Kotero, musachite mantha. Ine ndidzasamalira inu pamodzi ndi ana anu omwe.” Tsono iye anawalimbitsa mtima powayankhula moleza mtima.
וישב יוסף במצרים הוא ובית אביו ויחי יוסף מאה ועשר שנים 22
Yosefe anakhala mu Igupto pamodzi ndi banja lonse la abambo ake. Anakhala ndi moyo zaka 110
וירא יוסף לאפרים בני שלשים גם בני מכיר בן מנשה--ילדו על ברכי יוסף 23
ndipo anaona mʼbado wachitatu wa ana a Efereimu. Yosefe anatenganso ana a Makiri, mwana wa Manase kukhala ngati ana a mʼbanja lake.
ויאמר יוסף אל אחיו אנכי מת ואלהים פקד יפקד אתכם והעלה אתכם מן הארץ הזאת אל הארץ אשר נשבע לאברהם ליצחק וליעקב 24
Kenaka Yosefe anati kwa abale ake, “Ine ndatsala pangʼono kufa. Koma mosakayika Mulungu adzakuyangʼanirani nadzakutengani kukutulutsani mʼdziko lino kupita ku dziko limene Iye analonjeza kwa Abrahamu, Isake ndi Yakobo.”
וישבע יוסף את בני ישראל לאמר פקד יפקד אלהים אתכם והעלתם את עצמתי מזה 25
Ndipo Yosefe analumbiritsa ana a Israeli lumbiro nati, “Lonjezani kuti Mulungu akadzakusungani mudzanyamula mafupa anga kuwachotsa ku malo kuno.”
וימת יוסף בן מאה ועשר שנים ויחנטו אתו ויישם בארון במצרים 26
Choncho Yosefe anafa ali ndi zaka 110. Motero iwo atakonza thupi lake ndi mankhwala kuti lisawole, analiyika mʼbokosi ku Igupto.

< בראשית 50 >