< בראשית 17 >
ויהי אברם בן תשעים שנה ותשע שנים וירא יהוה אל אברם ויאמר אליו אני אל שדי--התהלך לפני והיה תמים | 1 |
Pamene Abramu anali ndi zaka 99, Yehova anamuonekera nati, “Ine ndine Mulungu Wamphamvuzonse. Ukhale munthu wochita zolungama nthawi zonse.
ואתנה בריתי ביני ובינך וארבה אותך במאד מאד | 2 |
Ndipo Ine ndikulonjeza kuti ndidzakupatsa zidzukulu zambiri.”
ויפל אברם על פניו וידבר אתו אלהים לאמר | 3 |
Pomwepo Abramu anadziponya pansi ndipo Mulungu anati kwa iye,
אני הנה בריתי אתך והיית לאב המון גוים | 4 |
“Pangano langa ndi iwe ndi ili: Udzakhala kholo la mitundu yambiri ya anthu.
ולא יקרא עוד את שמך אברם והיה שמך אברהם כי אב המון גוים נתתיך | 5 |
Sudzatchedwanso Abramu; dzina lako lidzakhala Abrahamu, chifukwa ndakusandutsa kukhala kholo la mitundu yambiri ya anthu.
והפרתי אתך במאד מאד ונתתיך לגוים ומלכים ממך יצאו | 6 |
Ndidzakupatsa zidzukulu zambiri motero kuti mitundu yambiri ya anthu idzatuluka mwa iwe. Mafumunso adzatuluka mwa iwe.
והקמתי את בריתי ביני ובינך ובין זרעך אחריך לדרתם--לברית עולם להיות לך לאלהים ולזרעך אחריך | 7 |
Pangano langa ndi iwe pamodzi ndi zidzukulu za mibado ya mʼtsogolo lidzakhala la muyaya. Ndidzakhala Mulungu wako ndi Mulungu wa zidzukulu zako.
ונתתי לך ולזרעך אחריך את ארץ מגריך את כל ארץ כנען לאחזת עולם והייתי להם לאלהים | 8 |
Dziko lonse la Kanaani, limene iwe ukukhala tsopano, ndalipereka kwa iwe ndi kwa zidzukulu zako kuti likhale chuma chanu mpaka muyaya. Ndipo Ine ndidzakhala Mulungu wa zidzukulu zako.”
ויאמר אלהים אל אברהם ואתה את בריתי תשמר--אתה וזרעך אחריך לדרתם | 9 |
Kenaka Mulungu anati kwa Abrahamu, “Koma iwe pamodzi ndi zidzukulu zako zobwera pambuyo pako mʼmibado ya mʼtsogolomo, sungani pangano langali.
זאת בריתי אשר תשמרו ביני וביניכם ובין זרעך אחריך המול לכם כל זכר | 10 |
Iwe pamodzi ndi zidzukulu zako zobwera pambuyo pako muzisunga pangano ili loti mwamuna aliyense pakati panupa azichita mdulidwe.
ונמלתם את בשר ערלתכם והיה לאות ברית ביני וביניכם | 11 |
Kuyambira tsopano muzichita mdulidwe ndipo ichi chidzakhala chizindikiro cha pangano langa ndi iwe.
ובן שמנת ימים ימול לכם כל זכר--לדרתיכם יליד בית--ומקנת כסף מכל בן נכר אשר לא מזרעך הוא | 12 |
Kuyambira tsopano mpaka mibado ya mʼtsogolomo mwana wamwamuna aliyense pakati panu amene wakwana masiku asanu ndi atatu ayenera kuchita mdulidwe. Awa ndi ana obadwa mʼbanja lako, kapena akapolo ochita kugula ndi ndalama, mlendo osakhala wa mʼmbumba yako.
המול ימול יליד ביתך ומקנת כספך והיתה בריתי בבשרכם לברית עולם | 13 |
Achite mdulidwe ndithu mwana wamwamuna aliyense, mbadwa ngakhale kapolo wochita kugula ndi ndalama, ndipo ichi chidzakhala chizindikiro pa thupi lanu cha pangano langa lamuyaya.
וערל זכר אשר לא ימול את בשר ערלתו--ונכרתה הנפש ההוא מעמיה את בריתי הפר | 14 |
Mwamuna aliyense amene adzakhala wosachita mdulidwe adzachotsedwa pakati pa anthu ake chifukwa sanasunge pangano langa.”
ויאמר אלהים אל אברהם שרי אשתך לא תקרא את שמה שרי כי שרה שמה | 15 |
Mulungu anatinso kwa Abrahamu, “Sarai mkazi wako, sudzamutchanso Sarai; dzina lake lidzakhala Sara.
וברכתי אתה וגם נתתי ממנה לך בן וברכתיה והיתה לגוים מלכי עמים ממנה יהיו | 16 |
Ndidzamudalitsa ndipo adzakubalira mwana wamwamuna. Ndidzamudalitsa kuti akhale mayi wa mitundu ya anthu; mafumu a anthuwo adzachokera mwa iye.”
ויפל אברהם על פניו ויצחק ויאמר בלבו הלבן מאה שנה יולד ואם שרה הבת תשעים שנה תלד | 17 |
Abrahamu anadzigwetsa pansi pamaso pa Yehova, Iye anaseka nati, “Kodi munthu wa zaka 100 nʼkubala mwana? Kodi Sara adzabereka mwana pa msinkhu wa zaka makumi asanu ndi anayi?”
ויאמר אברהם אל האלהים לו ישמעאל יחיה לפניך | 18 |
Ndipo Abrahamu anati kwa Mulungu, “Bwanji mumudalitse Ismaeli.”
ויאמר אלהים אבל שרה אשתך ילדת לך בן וקראת את שמו יצחק והקמתי את בריתי אתו לברית עולם לזרעו אחריו | 19 |
Koma Mulungu anati, “Ayi, koma mkazi wako Sara adzakubalira mwana wamwamuna, ndipo udzamutcha Isake. Ndidzasunga pangano langa losatha ndi iyeyu komanso ndi zidzukulu zobwera pambuyo pake.
ולישמעאל שמעתיך--הנה ברכתי אתו והפריתי אתו והרביתי אתו במאד מאד שנים עשר נשיאם יוליד ונתתיו לגוי גדול | 20 |
Koma za Ismaeli, ndamva. Ndidzamudalitsadi, ndipo adzakhala ndi zidzukulu zambiri. Iye adzakhala kholo la mafumu khumi ndi awiri ndipo mwa iye mudzatuluka mtundu waukulu wa anthu.
ואת בריתי אקים את יצחק אשר תלד לך שרה למועד הזה בשנה האחרת | 21 |
Koma ndidzasunga pangano langali ndi Isake amene Sara adzakubalira pofika nthawi ngati ino chaka chamawa.”
ויכל לדבר אתו ויעל אלהים מעל אברהם | 22 |
Atatha kuyankhula, Mulungu anamuchokera Abrahamu.
ויקח אברהם את ישמעאל בנו ואת כל ילידי ביתו ואת כל מקנת כספו--כל זכר באנשי בית אברהם וימל את בשר ערלתם בעצם היום הזה כאשר דבר אתו אלהים | 23 |
Tsono Abrahamu anachita mdulidwe mwana wake Ismaeli ndi onse amene anali mʼbanja lake, mbadwa ngakhale kapolo ochita kugula ndi ndalama, monga mmene Mulungu analamulira.
ואברהם--בן תשעים ותשע שנה בהמלו בשר ערלתו | 24 |
Abrahamu anali ndi zaka 99 pamene anachita mdulidwe,
וישמעאל בנו בן שלש עשרה שנה בהמלו--את בשר ערלתו | 25 |
ndipo mwana wake Ismaeli anali ndi zaka khumi ndi zitatu;
בעצם היום הזה נמול אברהם וישמעאל בנו | 26 |
Onse, Abrahamu ndi mwana wake Ismaeli, anachita mdulidwe tsiku limodzi.
וכל אנשי ביתו יליד בית ומקנת כסף מאת בן נכר--נמלו אתו | 27 |
Aliyense wamwamuna wa pa banja pa Abrahamu, kuphatikizapo iwo amene anabadwira pa banja pomwepo kapena akapolo ogula ndi ndalama kwa alendo, anachita mdulidwe.