< יחזקאל 29 >

בשנה העשרית בעשרי בשנים עשר לחדש--היה דבר יהוה אלי לאמר 1
Pa tsiku lakhumi ndi chiwiri la mwezi wakhumi, chaka chakhumi, Yehova anandiyankhula kuti:
בן אדם--שים פניך על פרעה מלך מצרים והנבא עליו ועל מצרים כלה 2
“Iwe mwana wa munthu, tembenukira kwa Farao, mfumu ya Igupto, ndipo unenere modzudzula mfumuyo pamodzi ndi dziko lake.
דבר ואמרת כה אמר אדני יהוה הנני עליך פרעה מלך מצרים התנים הגדול הרבץ בתוך יאריו אשר אמר לי יארי ואני עשיתני 3
Uyiwuze mfumuyo kuti, ‘Ine Ambuye Yehova ndikuti, “‘Ndine mdani wako, iwe Farao mfumu ya Igupto, iwe ngʼona yayikulu yogona pakati pa mitsinje yako. Umanena kuti, ‘Mtsinje wa Nailo ndi wanga; ndinadzipangira ndekha.’
ונתתי חחיים (חחים) בלחייך והדבקתי דגת יאריך בקשקשתיך והעליתיך מתוך יאריך ואת כל דגת יאריך בקשקשתיך תדבק 4
Koma ndidzakukola ndi mbedza mʼkamwa mwako ndipo nsomba za mʼmitsinje yako zidzakangamira ku mamba ako. Tsono ndidzakutulutsa mu mtsinje mwakomo pamodzi ndi nsomba zimene zakangamira ku mamba ako.
ונטשתיך המדברה אותך ואת כל דגת יאריך על פני השדה תפול לא תאסף ולא תקבץ--לחית הארץ ולעוף השמים נתתיך לאכלה 5
Ndidzakutaya ku chipululu, iwe pamodzi ndi nsomba zonse za mʼmitsinje yako. Udzagwera pamtetete kuthengo popanda munthu woti akutole kuti akayike maliro ako. Ndidzakusandutsa chakudya cha zirombo za pa dziko lapansi ndi mbalame za mlengalenga.
וידעו כל ישבי מצרים כי אני יהוה יען היותם משענת קנה לבית ישראל 6
Motero aliyense amene amakhala mu Igupto adzadziwa kuti Ine ndine Yehova. “‘Iwe unakhala ngati ndodo yabango ku Aisraeli.
בתפשם בך בכפך (בכף) תרוץ ובקעת להם כל כתף ובהשענם עליך תשבר והעמדת להם כל מתנים 7
Pamene anakugwira unathethekera mʼmanja mwawo ndi kucheka mapewa awo. Pamene anakutsamira, unathyoka ndipo misana yawo inagwedezeka.
לכן כה אמר אדני יהוה הנני מביא עליך חרב והכרתי ממך אדם ובהמה 8
“‘Nʼchifukwa chake Ine Ambuye Yehova ndikuti, ndikubweretsera lupanga kuti lidzaphe anthu pamodzi ndi nyama zomwe.
והיתה ארץ מצרים לשממה וחרבה וידעו כי אני יהוה יען אמר יאר לי ואני עשיתי 9
Dziko la Igupto lidzasanduka lopanda anthu. Pamenepo iwo adzadziwa kuti Ine ndine Yehova. “‘Popeza iwe unati, ‘Mtsinje wa Nailo ndi wanga; ndinawupanga ndine,’
לכן הנני אליך ואל יאריך ונתתי את ארץ מצרים לחרבות חרב שממה ממגדל סונה ועד גבול כוש 10
nʼchifukwa chake Ine ndikudana nawe pamodzi ndi mitsinje yakoyo, ndipo ndidzasandutsa dziko la Igupto bwinja kuyambira chipululu cha Migidoli mpaka ku mzinda wa Asiwani, kukafika ku malire a Kusi.
לא תעבר בה רגל אדם ורגל בהמה לא תעבר בה ולא תשב ארבעים שנה 11
Palibe phazi la munthu kapena la nyama limene lidzapondepo. Kudzakhala kopanda anthu kwa zaka makumi anayi.
ונתתי את ארץ מצרים שממה בתוך ארצות נשמות ועריה בתוך ערים מחרבות תהיין שממה ארבעים שנה והפצתי את מצרים בגוים וזריתים בארצות 12
Ndidzasandutsa dziko la Igupto kukhala chipululu ngati zipululu za mayiko ena. Kwa zaka makumi anayi mizinda yakenso idzakhala yopasuka pakati pa mizinda yopasuka. Ndipo ndidzathamangitsira Aigupto pakati pa mitundu ya anthu ndi kuwabalalitsira mʼmayiko.
כי כה אמר אדני יהוה מקץ ארבעים שנה אקבץ את מצרים מן העמים אשר נפצו שמה 13
“‘Komabe Ine Ambuye Yehova ndikuti: Pakutha pa zaka makumi anayi ndidzasonkhanitsa Aigupto onse kuchokera ku mayiko amene ndinawabalalitsirako.
ושבתי את שבות מצרים והשבתי אתם ארץ פתרוס על ארץ מכורתם והיו שם ממלכה שפלה 14
Ndidzachotsa Aiguptowo ku ukapolo ndipo ndidzawabwezera ku Patirosi kumene anachokera. Kumeneko iwo adzakhala ufumu wotsika.
מן הממלכות תהיה שפלה ולא תתנשא עוד על הגוים והמעטתים--לבלתי רדות בגוים 15
Udzakhala ufumu wotsika kwambiri kupambana maufumu ena onse ndipo sudzadzitukumula pakati pa mitundu ina. Ndidzawufowoketsa kwambiri kotero kuti sudzathanso kulamulira mitundu ya anthu.
ולא יהיה עוד לבית ישראל למבטח מזכיר עון בפנותם אחריהם וידעו כי אני אדני יהוה 16
Aisraeli sadzadaliranso Aigupto. Koma kuti chilango chawo chidzawakumbutsa tchimo lawo lija lofunafuna thandizo kuchokera ku Igupto. Pamenepo iwo adzadziwa kuti Ine ndine Ambuye Yehova.’”
ויהי בעשרים ושבע שנה בראשון באחד לחדש היה דבר יהוה אלי לאמר 17
Pa tsiku loyamba la mwezi woyamba, chaka cha 27, Yehova anandiyankhula kuti:
בן אדם נבוכדראצר מלך בבל העביד את חילו עבדה גדולה אל צר--כל ראש מקרח וכל כתף מרוטה ושכר לא היה לו ולחילו מצר על העבדה אשר עבד עליה 18
“Iwe mwana wa munthu, kale Nebukadinezara mfumu ya Babuloni inagwiritsa ntchito ankhondo ake kukathira nkhondo mzinda wa Turo, mpaka munthu aliyense anachita dazi chifukwa chosenza katundu, ndipo ananyuka pa phewa. Komabe ngakhale iyeyo, kapena gulu lake lankhondo sanaphulepo kanthu pa ntchito yonse imene anayigwira polimbana ndi mzindawo.
לכן כה אמר אדני יהוה הנני נתן לנבוכדראצר מלך בבל את ארץ מצרים ונשא המנה ושלל שללה ובזז בזה והיתה שכר לחילו 19
Nʼchifukwa chake Ine Ambuye Yehova ndikuti, Ine ndidzapereka Igupto kwa Nebukadinezara mfumu ya Babuloni, ndipo iyo idzatenga chuma chake ndi kuchifunkha ngati malipiro a gulu lake lankhondo.
פעלתו אשר עבד בה נתתי לו את ארץ מצרים אשר עשו לי נאם אדני יהוה 20
Ndamupatsa Nebukadinezara Igupto ngati mphotho ya kulimbika kwake chifukwa iyo ndi gulu lake lankhondo anandigwirira ntchito, akutero Ambuye Yehova.
ביום ההוא אצמיח קרן לבית ישראל ולך אתן פתחון פה בתוכם וידעו כי אני יהוה 21
“Pa nthawi imeneyo ndidzapereka mphamvu yatsopano pa Aisraeli, ndipo ndidzatsekula pakamwa pako, iwe, Ezekieli kuti uthe kuyankhula pakati pawo. Pamenepo iwo adzadziwa kuti Ine ndine Yehova.”

< יחזקאל 29 >