< יחזקאל 18 >
Yehova anandiyankhula nati:
מה לכם אתם משלים את המשל הזה על אדמת ישראל לאמר אבות יאכלו בסר ושני הבנים תקהינה | 2 |
“Kodi anthu inu mumatanthauza chiyani mukamabwerezabwereza kunena mwambi uwu wokhudza dziko la Israeli kuti: “‘Nkhuyu zodya akulu zimapota ndi ana omwe?’”
חי אני נאם אדני יהוה אם יהיה לכם עוד משל המשל הזה--בישראל | 3 |
“Ndithu pali Ine wamoyo, akutero Ambuye Yehova, simudzanenanso mwambi umenewu mu Israeli.
הן כל הנפשות לי הנה כנפש האב וכנפש הבן לי הנה הנפש החטאת היא תמות | 4 |
Pakuti moyo uliwonse ndi wanga. Moyo wa abambo ndi wanga, wamwananso ndi wanga. Munthu wochimwa ndi amene adzafe.
ואיש כי יהיה צדיק ועשה משפט וצדקה | 5 |
“Tiyerekeze kuti pali munthu wolungama amene amachita zolungama ndi zolondola.
אל ההרים לא אכל ועיניו לא נשא אל גלולי בית ישראל ואת אשת רעהו לא טמא ואל אשה נדה לא יקרב | 6 |
Iye sadyera nawo pa mapiri a chipembedzo kapena kupembedza mafano a Aisraeli. Iye sayipitsa mkazi wa mnzake kapena kugonana ndi mkazi pamene akusamba.
ואיש לא יונה--חבלתו חוב ישיב גזלה לא יגזל לחמו לרעב יתן ועירם יכסה בגד | 7 |
Iye sapondereza munthu wina aliyense, koma amabwezera wangongole nʼchigwiriro chake. Iye salanda zinthu za osauka, koma amapereka chakudya kwa anthu anjala, ndipo amapereka zovala kwa anthu ausiwa.
בנשך לא יתן ותרבית לא יקח--מעול ישיב ידו משפט אמת יעשה בין איש לאיש | 8 |
Iye sakongoletsa ndalama mwa katapira, kapena kulandira chiwongoladzanja chachikulu. Amadziletsa kuchita zoyipa ndipo sakondera poweruza milandu.
בחקותי יהלך ומשפטי שמר לעשות אמת צדיק הוא חיה יחיה נאם אדני יהוה | 9 |
Iye amatsatira malangizo anga, ndipo amasunga malamulo anga mokhulupirika. Munthu ameneyo ndi wolungama; iye adzakhala ndithu ndi moyo, akutero Ambuye Yehova.
והוליד בן פריץ שפך דם ועשה אח מאחד מאלה | 10 |
“Tiyerekeze kuti munthu wolungama chotere wabala mwana chimbalangondo amene amakhalira kupha anthu ndi kuchita zinthu zina zotere.
והוא את כל אלה לא עשה--כי גם אל ההרים אכל ואת אשת רעהו טמא | 11 |
Iye nʼkumachita zinthu zimene ngakhale abambo ake sanachitepo. “Amadyera nawo ku mapiri achipembedzo. Amayipitsa mkazi wa mnzake.
עני ואביון הונה--גזלות גזל חבל לא ישיב ואל הגלולים נשא עיניו תועבה עשה | 12 |
Iye amapondereza munthu wosauka ndi wosowa. Amalanda zinthu za osauka. Sabweza chikole cha munthu wa ngongole. Iye amatembenukira ku mafano nachita zonyansa.
בנשך נתן ותרבית לקח וחי לא יחיה את כל התועבות האלה עשה--מות יומת דמיו בו יהיה | 13 |
Iye amakongoletsa mwa katapira ndipo amalandira chiwongoladzanja chachikulu. Kodi munthu wotereyu nʼkukhala ndi moyo? Ayi ndithu! Chifukwa wachita zinthu zonyansa zonsezi, adzaphedwa ndipo adzalandira chilango chomuyenera.
והנה הוליד בן וירא את כל חטאת אביו אשר עשה ויראה ולא יעשה כהן | 14 |
“Tsono tiyerekeze kuti munthu woyipa uyu wabala mwana amene amaona machimo onse amene abambo ake ankachita. Ngakhale amaona koma osatsanzira ntchito zake zoyipazo.
על ההרים לא אכל ועיניו לא נשא אל גלולי בית ישראל את אשת רעהו לא טמא | 15 |
“Sadyera nawo pa mapiri achipembedzo. Sapembedza mafano a ku Israeli. Sayipitsa mkazi wa mnzake.
ואיש לא הונה--חבל לא חבל וגזלה לא גזל לחמו לרעב נתן וערום כסה בגד | 16 |
Sapondereza munthu wina aliyense. Satenga chikole akabwereketsa chinthu. Salanda zinthu za osauka. Salanda zinthu za munthu. Amapereka chakudya kwa anthu anjala. Amapereka zovala kwa anthu aumphawi.
מעני השיב ידו נשך ותרבית לא לקח--משפטי עשה בחקותי הלך הוא לא ימות בעון אביו--חיה יחיה | 17 |
Amadziletsa kuchita zoyipa. Sakongoletsa kuti apezepo phindu. Salandira chiwongoladzanja. Amasunga malangizo anga ndi kumvera malamulo anga. Munthu wotereyo sadzafa chifukwa cha machimo a abambo ake. Adzakhala ndi moyo ndithu.
אביו כי עשק עשק גזל גזל אח ואשר לא טוב עשה בתוך עמיו והנה מת בעונו | 18 |
Koma abambo ake, popeza kuti anazunza anthu ena ndi kubera mʼbale wawo ndiponso popeza kuti sanachitire zabwino anansi ake, adzafera machimo ake omwe.
ואמרתם מדע לא נשא הבן בעון האב והבן משפט וצדקה עשה את כל חקותי שמר ויעשה אתם--חיה יחיה | 19 |
“Mwina inu mukhoza kufunsa kuti, ‘Nʼchifukwa chiyani mwana salangidwa chifukwa cha kulakwa kwa abambo ake? Ayi, mwanayo adzakhala ndi moyo chifukwa ankachita zolungama ndi zolondola ndipo ankasamala kumvera malamulo anga onse.
הנפש החטאת היא תמות בן לא ישא בעון האב ואב לא ישא בעון הבן--צדקת הצדיק עליו תהיה ורשעת רשע (הרשע) עליו תהיה | 20 |
Munthu wochimwa ndiye amene adzafe. Mwana sadzapezeka wolakwa chifukwa cha abambo ake, kapena abambo kupezeka wolakwa chifukwa cha mwana wawo. Chilungamo cha munthu wolungama ndicho chidzamupulutse, ndipo kuyipa kwa munthu wochimwa ndiko kudzamuwonongetse.
והרשע כי ישוב מכל חטאתו אשר עשה ושמר את כל חקותי ועשה משפט וצדקה--חיה יחיה לא ימות | 21 |
“‘Munthu woyipa akatembenuka mtima ndi kusiya machimo amene ankachita ndi kuyamba kumvera malamulo anga ndi kumachita zolungama ndi zokhulupirika, ndiye kuti adzakhala ndi moyo. Sadzafa ayi.
כל פשעיו אשר עשה לא יזכרו לו בצדקתו אשר עשה יחיה | 22 |
Zoyipa zake zonse zidzakhululukidwa. Chifukwa cha zinthu zolungama zimene anazichita adzakhala ndi moyo.
החפץ אחפץ מות רשע נאם אדני יהוה הלוא בשובו מדרכיו וחיה | 23 |
Kodi Ine ndimakondwera ndi imfa ya munthu woyipa? Ayi, ndimakondwera pamene woyipa watembenuka mtima kuti akhale ndi moyo. Akutero Ambuye Yehova.
ובשוב צדיק מצדקתו ועשה עול ככל התועבות אשר עשה הרשע יעשה וחי--כל צדקתו אשר עשה לא תזכרנה במעלו אשר מעל ובחטאתו אשר חטא בם ימות | 24 |
“‘Koma ngati munthu wolungama apatuka kusiya zachilungamo ndi kuyamba kuchita tchimo ndi zonyansa za mtundu uliwonse zimene amachita anthu oyipa, kodi munthu wotereyu nʼkukhala ndi moyo? Ayi ndithu, zolungama zake zonse sizidzakumbukiridwa. Iye adzayenera kufa chifukwa cha machimo amene anachita.
ואמרתם לא יתכן דרך אדני שמעו נא בית ישראל הדרכי לא יתכן הלא דרכיכם לא יתכנו | 25 |
“Komabe inu mukunena kuti, ‘Zimene Ambuye amachita ndi zopanda chilungamo.’ Tamvani tsono inu Aisraeli: Kodi zochita zanga ndizo zosalungama? Kodi si zochita zanu zimene ndi zosalungama?
בשוב צדיק מצדקתו ועשה עול ומת עליהם בעולו אשר עשה ימות | 26 |
Ngati munthu wolungama atembenuka kusiya chilungamo chake ndi kuchita tchimo, iye adzafa chifukwa cha tchimolo.
ובשוב רשע מרשעתו אשר עשה ויעש משפט וצדקה--הוא את נפשו יחיה | 27 |
Koma ngati munthu woyipa aleka zoyipa zake zimene anazichita ndi kuyamba kuchita zimene ndi zolungama ndi zolondola, iye adzapulumutsa moyo wake.
ויראה וישוב (וישב) מכל פשעיו אשר עשה--חיו יחיה לא ימות | 28 |
Popeza waganizira za zolakwa zonse ankachita ndipo wazileka, iye adzakhala ndi moyo ndithu; sadzafa.
ואמרו בית ישראל לא יתכן דרך אדני הדרכי לא יתכנו בית ישראל--הלא דרכיכם לא יתכן | 29 |
Komabe Aisraeli akunena kuti, ‘Zimene Ambuye amachita ndi zopanda chilungamo.’ Kodi zochita zanga ndizo zopanda chilungamo, inu Aisraeli? Kodi si zochita zanu zimene ndi zopanda chilungamo?
לכן איש כדרכיו אשפט אתכם בית ישראל--נאם אדני יהוה שובו והשיבו מכל פשעיכם ולא יהיה לכם למכשול עון | 30 |
“Chifukwa chake Ine Ambuye Yehova ndikuti: inu Aisraeli, Ine ndidzakuweruzani aliyense wa inu molingana ndi ntchito zake. Lapani! Lekani zoyipa zanu kuti musawonongeke nazo.
השליכו מעליכם את כל פשעיכם אשר פשעתם בם ועשו לכם לב חדש ורוח חדשה ולמה תמתו בית ישראל | 31 |
Tayani zolakwa zanu zonse zimene munandichimwira nazo ndipo khalani ndi mtima watsopano ndi mzimu watsopano. Kodi muferanji inu Aisraeli?
כי לא אחפץ במות המת נאם אדני יהוה והשיבו וחיו | 32 |
Ine sindikondwera ndi imfa ya munthu aliyense, akutero Ambuye Yehova. Chifukwa chake, lapani kuti mukhale ndi moyo.”