< שמות 6 >
ויאמר יהוה אל משה עתה תראה אשר אעשה לפרעה כי ביד חזקה ישלחם וביד חזקה יגרשם מארצו | 1 |
Yehova anawuza Mose kuti, “Tsopano udzaona zimene ndimuchite Farao: Chifukwa cha dzanja langa lamphamvu adzalola anthu anga kuti atuluke. Chifukwa cha dzanja langa lamphamvu adzawatulutsa mʼdziko lake.”
וידבר אלהים אל משה ויאמר אליו אני יהוה | 2 |
Mulungu anatinso kwa Mose, “Ine ndine Yehova.
וארא אל אברהם אל יצחק ואל יעקב--באל שדי ושמי יהוה לא נודעתי להם | 3 |
Ndinaonekera kwa Abrahamu, kwa Isake ndi kwa Yakobo monga Mulungu Wamphamvuzonse, koma sindinawadziwitse dzina langa kuti ndine Yehova.
וגם הקמתי את בריתי אתם לתת להם את ארץ כנען--את ארץ מגריהם אשר גרו בה | 4 |
Ndinakhazikitsa pangano langa ndi iwo kuwalonjeza kuti ndidzawapatsa dziko la Kanaani kumene anakhalako kale ngati alendo.
וגם אני שמעתי את נאקת בני ישראל אשר מצרים מעבדים אתם ואזכר את בריתי | 5 |
Ndamvanso kubuwula kwa Aisraeli, amene Aigupto awayesa akapolo ndipo ndakumbukira pangano langa.”
לכן אמר לבני ישראל אני יהוה והוצאתי אתכם מתחת סבלת מצרים והצלתי אתכם מעבדתם וגאלתי אתכם בזרוע נטויה ובשפטים גדלים | 6 |
“Nʼchifukwa chake nena kwa Aisraeli kuti, ‘Ine ndine Yehova, ndipo ndidzakutulutsani mʼgoli la Aigupto. Ndidzakumasulani mu ukapolo, ndidzakuwombolani ndi dzanja langa lotambasuka ndi kuchita ntchito zachiweruzo.
ולקחתי אתכם לי לעם והייתי לכם לאלהים וידעתם כי אני יהוה אלהיכם המוציא אתכם מתחת סבלות מצרים | 7 |
Ndidzakutengani kukhala anthu anga, ndipo Ine ndidzakhala Mulungu wanu. Pamenepo inu mudzadziwa kuti Ine ndine Yehova Mulungu wanu amene ndinakutulutsani mʼgoli la Aigupto.
והבאתי אתכם אל הארץ אשר נשאתי את ידי לתת אתה לאברהם ליצחק וליעקב ונתתי אתה לכם מורשה אני יהוה | 8 |
Ndipo ndidzakufikitsani ku dziko limene ndinalumbira kuti ndidzalipereka kwa Abrahamu, kwa Isake ndi kwa Yakobo. Ndidzakupatsani dziko limenelo kuti likhale lanu. Ine ndine Yehova.’”
וידבר משה כן אל בני ישראל ולא שמעו אל משה מקצר רוח ומעבדה קשה | 9 |
Mose anawafotokozera Aisraeli zimenezi, koma iwo sanamumvere chifukwa cha kukhumudwa ndi goli lankhanza.
וידבר יהוה אל משה לאמר | 10 |
Kenaka Yehova anati kwa Mose,
בא דבר אל פרעה מלך מצרים וישלח את בני ישראל מארצו | 11 |
“Pita ukawuze Farao mfumu ya Igupto kuti awalole Aisraeli atuluke mʼdziko lake.”
וידבר משה לפני יהוה לאמר הן בני ישראל לא שמעו אלי ואיך ישמעני פרעה ואני ערל שפתים | 12 |
Koma Mose ananena kwa Yehova kuti, “Ngati Aisraeli sanandimvere, Farao akandimvera chifukwa chiyani, pajatu sinditha kuyankhula bwino?”
וידבר יהוה אל משה ואל אהרן ויצום אל בני ישראל ואל פרעה מלך מצרים--להוציא את בני ישראל מארץ מצרים | 13 |
Ndipo Yehova analamula Mose ndi Aaroni kuti awuze Aisraeli ndi Farao mfumu ya Igupto kuti Aisraeli ayenera kutuluka mʼdziko la Igupto.
אלה ראשי בית אבתם בני ראובן בכר ישראל חנוך ופלוא חצרן וכרמי--אלה משפחת ראובן | 14 |
Atsogoleri a mafuko awo anali awa: Ana a Rubeni mwana wachisamba wa Israeli anali Hanoki, Palu, Hezironi ndi Karimi. Awa anali mafuko a Rubeni.
ובני שמעון ימואל וימין ואהד ויכין וצחר ושאול בן הכנענית אלה משפחת שמעון | 15 |
Ana a Simeoni anali Yemueli, Yamini, Ohadi, Yakini, Zohari ndi Saulo mwana wa kwa mkazi wa Chikanaani. Awa anali mafuko a Simeoni.
ואלה שמות בני לוי לתלדתם--גרשון וקהת ומררי ושני חיי לוי שבע ושלשים ומאת שנה | 16 |
Mayina a ana a Levi pamodzi ndi zidzukulu zawo anali awa: Geresoni, Kohati ndi Merari. Levi anakhala ndi moyo kwa zaka 137.
בני גרשון לבני ושמעי למשפחתם | 17 |
Ana a Geresoni, mwa mafuko awo, anali Libini ndi Simei.
ובני קהת--עמרם ויצהר וחברון ועזיאל ושני חיי קהת שלש ושלשים ומאת שנה | 18 |
Ana a Kohati anali Amramu, Izihari, Hebroni ndi Uzieli. Kohati anakhala ndi moyo zaka 133.
ובני מררי מחלי ומושי אלה משפחת הלוי לתלדתם | 19 |
Ana a Merari anali Mali ndi Musi. Awa anali mafuko a Levi monga mwa mibado yawo.
ויקח עמרם את יוכבד דדתו לו לאשה ותלד לו את אהרן ואת משה ושני חיי עמרם שבע ושלשים ומאת שנה | 20 |
Amramu anakwatira Yokobedi mlongo wa abambo ake, amene anabereka Aaroni ndi Mose. Amramu anakhala ndi moyo kwa zaka 137.
ובני יצהר--קרח ונפג וזכרי | 21 |
Ana a Izihari anali Kora, Nefegi ndi Zikiri.
ובני עזיאל--מישאל ואלצפן וסתרי | 22 |
Ana a Uzieli anali Misaeli, Elizafani ndi Sitiri.
ויקח אהרן את אלישבע בת עמינדב אחות נחשון--לו לאשה ותלד לו את נדב ואת אביהוא את אלעזר ואת איתמר | 23 |
Aaroni anakwatira Eliseba, mwana wamkazi wa Aminadabu, mlongo wa Nasoni ndipo Iye anabereka Nadabu, Abihu, Eliezara ndi Itamara.
ובני קרח אסיר ואלקנה ואביאסף אלה משפחת הקרחי | 24 |
Ana a Kora anali Asiri, Elikana ndi Abiasafu. Awa ndiwo mafuko a Kora.
ואלעזר בן אהרן לקח לו מבנות פוטיאל לו לאשה ותלד לו את פינחס אלה ראשי אבות הלוים--למשפחתם | 25 |
Eliezara mwana wa Aaroni anakwatira mmodzi mwa ana aakazi a Putieli, ndipo anabereka Finehasi. Awa anali atsogoleri a mabanja a Levi, monga mwa mafuko awo.
הוא אהרן ומשה--אשר אמר יהוה להם הוציאו את בני ישראל מארץ מצרים על צבאתם | 26 |
Aaroni ndi Mose ndi aja amene Yehova anawawuza kuti, “Tulutsani Aisraeli mu Igupto mʼmagulu awo.”
הם המדברים אל פרעה מלך מצרים להוציא את בני ישראל ממצרים הוא משה ואהרן | 27 |
Mose ndi Aaroni ndiwo amene anayankhula ndi Farao mfumu ya Igupto kuti atulutse Aisraeli mu Igupto.
ויהי ביום דבר יהוה אל משה--בארץ מצרים | 28 |
Tsopano pamene Yehova anayankhula kwa Mose mu Igupto,
וידבר יהוה אל משה לאמר אני יהוה דבר אל פרעה מלך מצרים את כל אשר אני דבר אליך | 29 |
anati, “Ine ndine Yehova. Umuwuze Farao mfumu ya Igupto zonse zimene Ine ndikuwuze iwe.”
ויאמר משה לפני יהוה הן אני ערל שפתים ואיך ישמע אלי פרעה | 30 |
Koma Mose anati kwa Yehova, “Farao akandimvera bwanji, pakuti ine sinditha kuyankhula bwino?”