< שמות 10 >
ויאמר יהוה אל משה בא אל פרעה כי אני הכבדתי את לבו ואת לב עבדיו למען שתי אתתי אלה בקרבו | 1 |
Kenaka Yehova anati kwa Mose, “Pita kwa Farao, pakuti Ine ndawumitsa mtima wake ndi mitima ya nduna zake kuti ndichite zizindikiro zozizwitsa pakati pawo
ולמען תספר באזני בנך ובן בנך את אשר התעללתי במצרים ואת אתתי אשר שמתי בם וידעתם כי אני יהוה | 2 |
kuti inu mudzawuze ana ndi zidzukulu zanu za mmene ndinawakhawulitsira Aigupto ndi zizindikiro zozizwitsa zimene ndinachita pakati pawo ndiponso kuti inu mudziwe kuti ine ndine Yehova.”
ויבא משה ואהרן אל פרעה ויאמרו אליו כה אמר יהוה אלהי העברים עד מתי מאנת לענת מפני שלח עמי ויעבדני | 3 |
Ndipo Mose ndi Aaroni anapita kwa Farao ndi kukanena kuti, “Yehova Mulungu wa Ahebri, akuti: ‘Kodi udzakanabe kudzichepetsa pamaso panga mpaka liti? Alole anthu anga apite kuti akandipembedze.
כי אם מאן אתה לשלח את עמי--הנני מביא מחר ארבה בגבלך | 4 |
Ngati ukana kuwalola, ndigwetsa dzombe mʼdziko lako lino mawa.
וכסה את עין הארץ ולא יוכל לראת את הארץ ואכל את יתר הפלטה הנשארת לכם מן הברד ואכל את כל העץ הצמח לכם מן השדה | 5 |
Dzombeli lidzakuta nthaka yonse moti sidzaoneka konse. Lidzadya kalikonse kakangʼono kamene sikanawonongedwe ndi matalala aja, kuphatikizapo mitengo yonse imene ikumera mʼminda yanu.
ומלאו בתיך ובתי כל עבדיך ובתי כל מצרים אשר לא ראו אבתיך ואבות אבתיך מיום היותם על האדמה עד היום הזה ויפן ויצא מעם פרעה | 6 |
Dzombeli lidzadzaza nyumba zako ndi za nduna zako ndiponso za Aigupto onse, chinthu chimene ngakhale makolo anu kapena makolo awo sanachionepo kuyambira tsiku limene anakhala mʼdzikoli mpaka lero.’” Ndipo Mose ndi Aaroni anatembenuka ndi kumusiya Farao.
ויאמרו עבדי פרעה אליו עד מתי יהיה זה לנו למוקש--שלח את האנשים ויעבדו את יהוה אלהיהם הטרם תדע כי אבדה מצרים | 7 |
Nduna za Farao zinamufunsa kuti, “Kodi munthu uyu adzativutitsa mpaka liti? Aloleni anthuwa apite, kuti akapembedze Yehova Mulungu wawo. Kodi simukuona kuti dziko la Igupto lawonongeka?”
ויושב את משה ואת אהרן אל פרעה ויאמר אלהם לכו עבדו את יהוה אלהיכם מי ומי ההלכים | 8 |
Choncho Mose ndi Aaroni anayitanidwanso kwa Farao ndipo anati, “Pitani kapembedzeni Yehova Mulungu wanu. Koma ndani amene adzapite?”
ויאמר משה בנערינו ובזקנינו נלך בבנינו ובבנותנו בצאננו ובבקרנו נלך--כי חג יהוה לנו | 9 |
Mose anayankha kuti, “Ife tidzapita tonse pamodzi; angʼonoangʼono ndi akuluakulu, ana athu aamuna ndi aakazi, ndiponso ziweto zathu ndi ngʼombe chifukwa tikakhala ndi chikondwerero cha kwa Yehova.”
ויאמר אלהם יהי כן יהוה עמכם כאשר אשלח אתכם ואת טפכם ראו כי רעה נגד פניכם | 10 |
Farao anati, “Yehova akhale ndi inu ngati ndingakuloleni kupita pamodzi ndi akazi ndi ana anu! Zikuoneka kuti mwakonzeka kuchita choyipa.
לא כן לכו נא הגברים ועבדו את יהוה--כי אתה אתם מבקשים ויגרש אתם מאת פני פרעה | 11 |
Ndakana! Amuna okha ndiwo apite ndi kukapembedza Yehova pakuti izi ndi zimene mwakhala mukupempha.” Kenaka Mose ndi Aaroni anathamangitsidwa pamaso pa Farao.
ויאמר יהוה אל משה נטה ידך על ארץ מצרים בארבה ויעל על ארץ מצרים ויאכל את כל עשב הארץ את כל אשר השאיר הברד | 12 |
Ndipo Yehova anati kwa Mose, “Tambalitsa dzanja lako pa dziko la Igupto kuti dzombe lidze pa dziko la Igupto ndi kuwononga chilichonse chimene chikumera mʼminda ndi chilichonse chimene chinatsala pa nthawi ya matalala.”
ויט משה את מטהו על ארץ מצרים ויהוה נהג רוח קדים בארץ כל היום ההוא וכל הלילה הבקר היה--ורוח הקדים נשא את הארבה | 13 |
Kotero Mose anakweza ndodo yake pa dziko la Igupto, ndipo Yehova anawutsa mphepo ya kummawa imene inawomba pa dziko usana ndi usiku wonse. Mmene kumacha nʼkuti mphepoyo itabweretsa dzombe.
ויעל הארבה על כל ארץ מצרים וינח בכל גבול מצרים כבד מאד--לפניו לא היה כן ארבה כמהו ואחריו לא יהיה כן | 14 |
Dzombelo linafika pa dziko lonse la Igupto ndi kukhala dera lililonse la dzikolo. Dzombe lambiri ngati limenelo silinakhaleponso nʼkale lonse ndipo silidzakhalapo ngakhale mʼtsogolo.
ויכס את עין כל הארץ ותחשך הארץ ויאכל את כל עשב הארץ ואת כל פרי העץ אשר הותיר הברד ולא נותר כל ירק בעץ ובעשב השדה בכל ארץ מצרים | 15 |
Dzombelo linaphimba nthaka yonse mpaka kuoneka kuti bii. Linadya zonse zimene zinatsala nthawi ya matalala, zomera za mʼmunda ndi zipatso. Panalibe chobiriwira chilichonse chimene chinatsala pa mtengo kapena pa chomera chilichonse mʼdziko lonse la Igupto.
וימהר פרעה לקרא למשה ולאהרן ויאמר חטאתי ליהוה אלהיכם--ולכם | 16 |
Mwamsangamsanga, Farao anayitanitsa Mose ndi Aaroni ndipo anati, “Ine ndachimwira Yehova Mulungu wanu ndiponso inu.
ועתה שא נא חטאתי אך הפעם והעתירו ליהוה אלהיכם ויסר מעלי רק את המות הזה | 17 |
Tsopano ndikhululukirenso tchimo langa kano konkha ndipo pempherani kwa Yehova Mulungu wanu kuti andichotsere mliri wosakazawu.”
ויצא מעם פרעה ויעתר אל יהוה | 18 |
Mose anachoka kwa Farao nakapemphera kwa Yehova.
ויהפך יהוה רוח ים חזק מאד וישא את הארבה ויתקעהו ימה סוף לא נשאר ארבה אחד בכל גבול מצרים | 19 |
Ndipo Yehova anasintha mphepo ija kuti ikhale ya mphamvu yochokera ku madzulo, ndipo inanyamula dzombe lija nʼkulikankhira mʼNyanja Yofiira. Panalibe dzombe ndi limodzi lomwe limene linatsala mu Igupto.
ויחזק יהוה את לב פרעה ולא שלח את בני ישראל | 20 |
Koma Yehova anawumitsa mtima wa Farao, ndipo sanalole kuti Aisraeli apite.
ויאמר יהוה אל משה נטה ידך על השמים ויהי חשך על ארץ מצרים וימש חשך | 21 |
Kenaka Yehova anati kwa Mose, “Tambasulira dzanja lako kumwamba kuti kukhale mdima umene udzaphimba dziko lonse la Igupto, mdima wandiweyani.”
ויט משה את ידו על השמים ויהי חשך אפלה בכל ארץ מצרים שלשת ימים | 22 |
Choncho Mose anakweza dzanja lake kumwamba ndipo mdima wandiweyani unaphimba dziko lonse la Igupto kwa masiku atatu.
לא ראו איש את אחיו ולא קמו איש מתחתיו--שלשת ימים ולכל בני ישראל היה אור במושבתם | 23 |
Palibe amene anatha kuona mnzake kapena kuchoka pa khomo pake kwa masiku atatu. Koma kumalo kumene kumakhala Aisraeli kunali kowala.
ויקרא פרעה אל משה ויאמר לכו עבדו את יהוה--רק צאנכם ובקרכם יצג גם טפכם ילך עמכם | 24 |
Kenaka Farao anayitanitsa Mose ndi Aaroni nati, “Pitani kapembedzeni Yehova. Ngakhale akazi ndi ana anu apite pamodzi ndi inu. Koma musatenge ziweto zanu ndi ngʼombe zanu.”
ויאמר משה גם אתה תתן בידנו זבחים ועלת ועשינו ליהוה אלהינו | 25 |
Koma Mose anati, “Ndiye inu mutipatse nsembe zopsereza zoti tikapereke kwa Yehova Mulungu wathu.
וגם מקננו ילך עמנו לא תשאר פרסה--כי ממנו נקח לעבד את יהוה אלהינו ואנחנו לא נדע מה נעבד את יהוה עד באנו שמה | 26 |
Koma ayi, ife tipita ndi ziweto zathu. Palibe chiweto chilichonse chimene chitatsale kuno, popeza tikasankha komweko ziweto zokapembedzera Yehova. Sitingadziwe zimene tikagwiritse ntchito popembedza Yehova mpaka titakafika kumeneko.”
ויחזק יהוה את לב פרעה ולא אבה לשלחם | 27 |
Koma Yehova anawumitsa mtima wa Farao ndipo sanafune kuwalola kuti apite.
ויאמר לו פרעה לך מעלי השמר לך אל תסף ראות פני--כי ביום ראתך פני תמות | 28 |
Farao anati kwa Mose, “Choka pamaso panga! Uwonetsetse kuti usadzaonekerenso pamaso panga! Tsiku limene ndidzakuonenso udzafa.”
ויאמר משה כן דברת לא אסף עוד ראות פניך | 29 |
Mose anayankha kuti, “Monga momwe mwaneneramu, Ine sindidzaonekeranso pamaso panu.”