< קֹהֶלֶת 5 >

שמר רגליך (רגלך) כאשר תלך אל בית האלהים וקרוב לשמע מתת הכסילים זבח כי אינם יודעים לעשות רע 1
Uzisamala mayendedwe ako pamene ukupita ku nyumba ya Mulungu. Upite pafupi kuti ukamvetsere mʼmalo mopereka nsembe ya zitsiru zimene sizizindikira kuti zikuchita zolakwa.
אל תבהל על פיך ולבך אל ימהר להוציא דבר--לפני האלהים כי האלהים בשמים ואתה על הארץ על כן יהיו דבריך מעטים 2
Usamafulumire kuyankhula, usafulumire mu mtima mwako kunena chilichonse pamaso pa Mulungu. Mulungu ali kumwamba ndipo iwe uli pa dziko lapansi, choncho mawu ako akhale ochepa.
כי בא החלום ברב ענין וקול כסיל ברב דברים 3
Kuchuluka kwa mavuto mu mtima kumabweretsa maloto oyipa, ndipo kuchuluka kwa mawu kumadzetsa uchitsiru.
כאשר תדר נדר לאלהים אל תאחר לשלמו--כי אין חפץ בכסילים את אשר תדר שלם 4
Pamene ulumbira kwa Mulungu usachedwe kukwaniritsa chimene walumbiracho. Iye sakondweretsedwa ndi chitsiru; kwaniritsa lumbiro lako.
טוב אשר לא תדר--משתדור ולא תשלם 5
Kuli bwino kusalumbira kusiyana ndi kulumbira koma osakwaniritsa lumbirolo.
אל תתן את פיך לחטיא את בשרך ואל תאמר לפני המלאך כי שגגה היא למה יקצף האלהים על קולך וחבל את מעשה ידיך 6
Pakamwa pako pasakuchimwitse. Ndipo usanene kwa mthenga wa mʼNyumba ya Mulungu kuti, “Ndinalakwitsa polumbira.” Chifukwa chiyani ukufuna Mulungu akwiye ndi mawu ako ndiponso ntchito ya manja ako?
כי ברב חלמות והבלים ודברים הרבה כי את האלהים ירא 7
Maloto ochuluka ndi mawu ochuluka ndi zinthu zopandapake. Kotero lemekeza Mulungu.
אם עשק רש וגזל משפט וצדק תראה במדינה--אל תתמה על החפץ כי גבה מעל גבה שמר וגבהים עליהם 8
Ngati uwona anthu osauka akuzunzika mʼdziko, ndiponso anthu ena akupsinja anzawo ndi kuwalanda ufulu wawo, usadabwe ndi zinthu zimenezi; pakuti woyangʼanira ali naye wina womuyangʼanira wamkulu, ndipo pamwamba pa awiriwa pali ena akuluakulu owaposa.
ויתרון ארץ בכל היא (הוא)--מלך לשדה נעבד 9
Anthu onse amatengako zokolola za mʼminda: koma ndi mfumu yokha imene imapeza phindu la mindayi.
אהב כסף לא ישבע כסף ומי אהב בהמון לא תבואה גם זה הבל 10
Aliyense amene amakonda ndalama sakhutitsidwa ndi ndalamazo; aliyense amene amakonda chuma sakhutitsidwa ndi zimene amapeza. Izinso ndi zopandapake.
ברבות הטובה רבו אוכליה ומה כשרון לבעליה כי אם ראית (ראות) עיניו 11
Chuma chikachuluka akudya nawo chumacho amachulukanso. Nanga mwini wake amapindulapo chiyani kuposa kumangochiyangʼana ndi maso ake?
מתוקה שנת העבד אם מעט ואם הרבה יאכל והשבע לעשיר--איננו מניח לו לישון 12
Wantchito amagona tulo tabwino ngakhale adye pangʼono kapena kudya kwambiri, koma munthu wolemera, chuma sichimulola kuti agone.
יש רעה חולה ראיתי תחת השמש עשר שמור לבעליו לרעתו 13
Ine ndinaona choyipa chomvetsa chisoni pansi pano: chuma chokundikidwa chikupweteka mwini wake yemwe,
ואבד העשר ההוא בענין רע והוליד בן ואין בידו מאומה 14
kapena chuma chowonongedwa pa nthawi yatsoka, kotero kuti pamene wabereka mwana alibe kanthu koti amusiyire.
כאשר יצא מבטן אמו ערום ישוב ללכת כשבא ומאומה לא ישא בעמלו שילך בידו 15
Munthu anabadwa wamaliseche kuchokera mʼmimba mwa amayi ake, ndipo monga iye anabadwira, adzapitanso choncho. Pa zonse zimene iye anakhetsera thukuta palibe nʼchimodzi chomwe chimene adzatenge mʼmanja mwake.
וגם זה רעה חולה כל עמת שבא כן ילך ומה יתרון לו שיעמל לרוח 16
Izinso ndi zoyipa kwambiri: munthu adzapita monga momwe anabwerera, ndipo iye amapindula chiyani, pakuti amagwira ntchito yolemetsa yopanda phindu?
גם כל ימיו בחשך יאכל וכעס הרבה וחליו וקצף 17
Masiku ake onse ndi odzaza ndi mdima, kukhumudwa kwakukulu, masautso ndi nkhawa.
הנה אשר ראיתי אני טוב אשר יפה לאכול ולשתות ולראות טובה בכל עמלו שיעמל תחת השמש מספר ימי חיו אשר נתן לו האלהים--כי הוא חלקו 18
Tsono ndinazindikira kuti nʼchabwino ndi choyenera kuti munthu azidya ndi kumwa, ndi kukhutitsidwa ndi ntchito yake yolemetsa imene amayigwira pansi pano pa nthawi yake yochepa imene Mulungu amamupatsa, poti ichi ndiye chake.
גם כל האדם אשר נתן לו האלהים עשר ונכסים והשליטו לאכל ממנו ולשאת את חלקו ולשמח בעמלו--זה מתת אלהים היא 19
Komatu pamene Mulungu apereka chuma kwa munthu aliyense ndi zinthu zina, ndi kulola kuti akondwere ndi chumacho, munthuyo alandire chumacho ndi kusangalala ndi ntchito yake, imene ndi mphatso yochokera kwa Mulungu.
כי לא הרבה יזכר את ימי חייו כי האלהים מענה בשמחת לבו 20
Munthu wotereyu saganizirapo za masiku a moyo wake, chifukwa Mulungu amamutanganidwitsa ndi chisangalalo cha mu mtima mwake.

< קֹהֶלֶת 5 >