< דברים 28 >

והיה אם שמוע תשמע בקול יהוה אלהיך לשמר לעשות את כל מצותיו אשר אנכי מצוך היום--ונתנך יהוה אלהיך עליון על כל גויי הארץ 1
Ngati mumvera Yehova Mulungu wanu ndi kutsatira mosamalitsa malamulo ake onse amene ndikukupatsani lero lino, Yehova Mulungu wanu adzakukwezani pamwamba pa mitundu yonse ya pa dziko lapansi.
ובאו עליך כל הברכות האלה והשיגך כי תשמע בקול יהוה אלהיך 2
Madalitso awa adzabwera kwa inu ndi kuyenda nanu ngati mumvera Yehova Mulungu wanu:
ברוך אתה בעיר וברוך אתה בשדה 3
Mudzadalitsika mʼmizinda yanu ndi kudalitsika mʼdzikolo.
ברוך פרי בטנך ופרי אדמתך ופרי בהמתך--שגר אלפיך ועשתרות צאנך 4
Yehova adzadalitsa ana anu, zokolola za mʼdziko lanu, ngʼombe zanu pamodzi ndi ziweto zanu zonse.
ברוך טנאך ומשארתך 5
Dengu lanu ndi chiwaya chanu cha buledi zidzadalitsika.
ברוך אתה בבאך וברוך אתה בצאתך 6
Mudzadalitsika pa kulowa kwanu ndi pa kutuluka kwanu.
יתן יהוה את איביך הקמים עליך נגפים לפניך בדרך אחד יצאו אליך ובשבעה דרכים ינוסו לפניך 7
Yehova adzaonetsetsa kuti adani anu amene adzakuwukirani agonjetsedwe pamaso panu. Iwo adzabwera kwa inu kuchokera mbali imodzi koma adzakuthawani ku mbali zisanu ndi ziwiri.
יצו יהוה אתך את הברכה באסמיך ובכל משלח ידך וברכך--בארץ אשר יהוה אלהיך נתן לך 8
Yehova adzatumiza madalitso pa nkhokwe zanu ndi pa chilichonse chimene muchikhudza. Yehova Mulungu wanu adzakudalitsani mʼdziko limene akukupatsani.
יקימך יהוה לו לעם קדוש כאשר נשבע לך כי תשמר את מצות יהוה אלהיך והלכת בדרכיו 9
Yehova Mulungu wanu adzachititsa kuti mukhale anthu ake opatulika, monga momwe analonjezera pa malumbiro ake, ngati musunga malamulo ake ndi kuyenda mʼnjira zake.
וראו כל עמי הארץ כי שם יהוה נקרא עליך ויראו ממך 10
Pamenepo anthu onse a dziko lapansi adzaona kuti mumadziwika ndi dzina la Yehova ndipo adzakuopani.
והותרך יהוה לטובה בפרי בטנך ובפרי בהמתך ובפרי אדמתך--על האדמה אשר נשבע יהוה לאבתיך לתת לך 11
Yehova adzakupambanitsani kwambiri ndipo adzakupatsani ana ambiri, ziweto zambiri, ndi zokolola zochuluka, mʼdziko limene Yehova analumbira kwa makolo anu kuti adzakupatsani.
יפתח יהוה לך את אוצרו הטוב את השמים לתת מטר ארצך בעתו ולברך את כל מעשה ידך והלוית גוים רבים ואתה לא תלוה 12
Yehova adzatsekula kumwamba kumene amasungirako chuma chake, kutumiza mvula mʼdziko lanu pa nthawi yake ndi kudalitsa ntchito yonse ya manja anu. Mudzakongoza mitundu yambiri koma inu simudzakongola kwa aliyense.
ונתנך יהוה לראש ולא לזנב והיית רק למעלה ולא תהיה למטה כי תשמע אל מצות יהוה אלהיך אשר אנכי מצוך היום--לשמר ולעשות 13
Yehova adzakuthandizani kukhala mutu osati mchira. Mukakhala ndi chidwi ndi malamulo a Yehova Mulungu wanu amene ndikukupatsani lero lino ndi kuwatsata mosamalitsa, inu mudzakhala apamwamba nthawi zonse osati apansi.
ולא תסור מכל הדברים אשר אנכי מצוה אתכם היום--ימין ושמאול ללכת אחרי אלהים אחרים--לעבדם 14
Musapatukire ku dzanja lamanja kapena lamanzere pa lamulo lina lililonse limene ndikukupatsani lero lino ndi kumatsatira kapena kuyitumikira milungu ina.
והיה אם לא תשמע בקול יהוה אלהיך לשמר לעשות את כל מצותיו וחקתיו אשר אנכי מצוך היום--ובאו עליך כל הקללות האלה והשיגוך 15
Koma ngati simumvera Yehova Mulungu wanu ndi kusatsata mosamalitsa malamulo ake ndi malangizo ake onse amene ndikukupatsani lero lino, matemberero awa adzabwera pa inu ndikukugonjetsani:
ארור אתה בעיר וארור אתה בשדה 16
Mudzatembereredwa mu mzinda ndi kutembereredwa mʼmudzi.
ארור טנאך ומשארתך 17
Dengu lanu ndi chiwaya chanu cha buledi zidzatembereredwa.
ארור פרי בטנך ופרי אדמתך--שגר אלפיך ועשתרת צאנך 18
Zipatso za mʼmimba mwanu zidzatembereredwa, ndiponso zomera za mʼdziko lanu, ana angʼombe zanu ndi ana ankhosa zanu zidzatembereredwa.
ארור אתה בבאך וארור אתה בצאתך 19
Mudzatembereredwa pa kulowa kwanu ndi pa kutuluka kwanu.
ישלח יהוה בך את המארה את המהומה ואת המגערת בכל משלח ידך אשר תעשה--עד השמדך ועד אבדך מהר מפני רע מעלליך אשר עזבתני 20
Yehova adzakutumizirani matemberero, chisokonezo ndi minyozo pa chilichonse chimene mudzachichita mpaka mudzawonongedwa ndi kukhala bwinja mofulumira chifukwa cha zoyipa zimene mwazichita pa kumutaya Yehova.
ידבק יהוה בך את הדבר--עד כלתו אתך מעל האדמה אשר אתה בא שמה לרשתה 21
Yehova adzakugwetserani mliri wa matenda mpaka atakuwonongani mʼdziko limene mukulowa kukalitengali.
יככה יהוה בשחפת ובקדחת ובדלקת ובחרחר ובחרב ובשדפון ובירקון ורדפוך עד אבדך 22
Yehova adzakukanthani ndi nthenda yowondetsa, ya malungo ndi ya zotupatupa, ndi kutentha kwakukulu ndi chilala, ndi chinsikwi ndi chiwawu zimene zidzakusautsani mpaka mutawonongeka.
והיו שמיך אשר על ראשך נחשת והארץ אשר תחתיך ברזל 23
Mitambo ya pamutu panu idzawuma ngati mkuwa ndipo sidzagwetsa mvula mpaka nthaka yanu idzawuma gwaa ngati chitsulo.
יתן יהוה את מטר ארצך אבק ועפר מן השמים ירד עליך עד השמדך 24
Mʼmalo mwa mvula Yehova adzakupatsani fumbi ndi dothi ndipo lidzakugwerani kuchokera kumwamba mpaka mutawonongeka.
יתנך יהוה נגף לפני איביך--בדרך אחד תצא אליו ובשבעה דרכים תנוס לפניו והיית לזעוה לכל ממלכות הארץ 25
Yehova adzalola kuti adani anu akugonjetseni. Mudzadzera njira imodzi pokalimbana ndi adani anu koma pothawa mudzabalalika mbali zisanu ndi ziwiri. Mudzakhala chinthu chochititsa mantha pakati pa maufumu onse a dziko lapansi.
והיתה נבלתך למאכל לכל עוף השמים ולבהמת הארץ ואין מחריד 26
Mitembo yanu idzadyedwa ndi mbalame zamumlengalenga ndi nyama zakutchire, ndipo palibe amene adzaziyingitse.
יככה יהוה בשחין מצרים ובעפלים (ובטחרים) ובגרב ובחרס--אשר לא תוכל להרפא 27
Yehova adzakusautsani ndi zithupsa za ku Igupto ndi zotupatupa, zipere, ndi mphere zimene simudzachiritsika nazo.
יככה יהוה בשגעון ובעורון ובתמהון לבב 28
Yehova adzakusautsani inu ndi misala, khungu ndi chisokonekero cha maganizo.
והיית ממשש בצהרים כאשר ימשש העור באפלה ולא תצליח את דרכיך והיית אך עשוק וגזול כל הימים--ואין מושיע 29
Masanasana mudzayenda ngati muli mu mdima, kumafufuzira njira ngati wosaona. Mudzakhala olephera pa chilichonse mungachite. Tsiku ndi tsiku mudzaponderezedwa ndi kuberedwa wopanda wokupulumutsani.
אשה תארש ואיש אחר ישגלנה (ישכבנה)--בית תבנה ולא תשב בו כרם תטע ולא תחללנו 30
Mudzachita chinkhoswe ndi mkazi, koma wina adzakulandani ndi kumukwatira. Mudzamanga nyumba koma simudzagonamo. Mudzalima munda wamphesa koma simudzadyako zipatso zake.
שורך טבוח לעיניך ולא תאכל ממנו--חמרך גזול מלפניך ולא ישוב לך צאנך נתנות לאיביך ואין לך מושיע 31
Ngʼombe yanu yamtheno idzaphedwa inu muli pomwepo koma simudzadyako. Bulu wanu adzalandidwa kwa inu mwamakani osabwera nayenso. Nkhosa zanu zidzapatsidwa kwa adani anu, ndipo palibe amene adzazipulumutsa.
בניך ובנתיך נתנים לעם אחר ועיניך ראות וכלות אליהם כל היום ואין לאל ידך 32
Ana anu aamuna ndi aakazi adzaperekedwa kwa anthu a mitundu ina ndipo inu mudzafika potopa ndi kulefuka nʼkudikirira tsiku ndi tsiku kuti mwina anawo abwerako.
פרי אדמתך וכל יגיעך יאכל עם אשר לא ידעת והיית רק עשוק ורצוץ--כל הימים 33
Anthu amene simukuwadziwa adzakudyerani zokolola zanu, ndipo mudzakhala mukuponderezedwa mwankhanza masiku onse.
והיית משגע ממראה עיניך אשר תראה 34
Zimene muzidzaziona zidzakusokonezani mitu.
יככה יהוה בשחין רע על הברכים ועל השקים אשר לא תוכל להרפא--מכף רגלך ועד קדקדך 35
Yehova adzakusautsani ndi zithupsa zaululu ndi zosachiritsika za mʼmawondo ndi mʼmiyendo ndipo zidzafalikira kuchoka kuphazi mpaka kumutu.
יולך יהוה אתך ואת מלכך אשר תקים עליך אל גוי אשר לא ידעת אתה ואבתיך ועבדת שם אלהים אחרים עץ ואבן 36
Yehova adzakuthamangitsirani, inu ndi mafumu anu amene muwayika, ku dziko losadziwika kwa inu ndi kwa makolo anu. Kumeneko mudzakapembedza milungu ina, milungu ya mitengo ndi miyala.
והיית לשמה למשל ולשנינה--בכל העמים אשר ינהגך יהוה שמה 37
Inu mudzakhala chinthu chochititsa mantha kuchisunga ndiponso chinthu chotukwanidwa ndi chonyozeka kwa anthu a mitundu yonse kumene Yehova adzakuthamangitsirani.
זרע רב תוציא השדה ומעט תאסף כי יחסלנו הארבה 38
Mudzadzala mbewu zambiri ku munda koma mudzakolola pangʼono, chifukwa dzombe lidzaziwononga.
כרמים תטע ועבדת ויין לא תשתה ולא תאגר כי תאכלנו התלעת 39
Mudzadzala mpesa ndi kulimirira koma vinyo wake simudzamumwa kapena kukolola mphesazo, chifukwa mphutsi zidzadya mphesazo.
זיתים יהיו לך בכל גבולך ושמן לא תסוך כי ישל זיתך 40
Mudzakhala ndi mitengo ya olivi mʼdziko lanu lonse koma simudzagwiritsa ntchito mafuta ake, chifukwa zipatso zake zidzayoyoka.
בנים ובנות תוליד ולא יהיו לך כי ילכו בשבי 41
Mudzabereka ana aamuna ndi aakazi koma sadzakhala anu, chifukwa adzapita ku ukapolo.
כל עצך ופרי אדמתך יירש הצלצל 42
Magulumagulu a dzombe adzawononga mitengo yanu ndi mbewu za mʼdziko lanu.
הגר אשר בקרבך יעלה עליך מעלה מעלה ואתה תרד מטה מטה 43
Mlendo wokhala pakati panu adzatukuka kuposa inu, koma inuyo mudzaloweralowera pansi.
הוא ילוך ואתה לא תלונו הוא יהיה לראש ואתה תהיה לזנב 44
Iye adzakubwereketsani, koma inu simudzatha kubwereketsa. Iye adzakhala mutu ndipo inu mudzakhala mchira.
ובאו עליך כל הקללות האלה ורדפוך והשיגוך עד השמדך כי לא שמעת בקול יהוה אלהיך--לשמר מצותיו וחקתיו אשר צוך 45
Matemberero onsewa adzabwera pa inu. Adzakulondolani ndi kukugonjetsani mpaka mutawonongeka, chifukwa simunamvere Yehova Mulungu wanu ndi kusunga malamulo ndi malangizo amene anakupatsani.
והיו בך לאות ולמופת ובזרעך עד עולם 46
Matemberero amenewa adzakhala chizindikiro ndi chozizwitsa kwa inu ndi zidzukulu zanu mpaka kalekale.
תחת אשר לא עבדת את יהוה אלהיך בשמחה ובטוב לבב--מרב כל 47
Pakuti inu simunatumikire Yehova Mulungu wanu pa nthawi imene zinthu zinkakuyenderani bwino,
ועבדת את איביך אשר ישלחנו יהוה בך ברעב ובצמא ובעירם ובחסר כל ונתן על ברזל על צוארך עד השמידו אתך 48
chomwecho pa nthawi ya njala ndi ludzu, ya maliseche ndi umphawi woopsa, mudzatumikira adani amene Yehova adzakutumizirani. Iye adzayika goli lachitsulo mʼkhosi mwanu kufikira atakuwonongani.
ישא יהוה עליך גוי מרחק מקצה הארץ כאשר ידאה הנשר גוי אשר לא תשמע לשנו 49
Yehova adzakutumizirani mtundu wa anthu kuchokera kutali kumapeto kwa dziko lapansi nudzachita ngati mphungu yowulukira pansi, mtundu wa anthu umene chiyankhulo chawo simudzachimva,
גוי עז פנים אשר לא ישא פנים לזקן ונער לא יחן 50
mtundu wooneka wochititsa mantha, wopanda ulemu kwa okalamba kapena chisoni kwa ana.
ואכל פרי בהמתך ופרי אדמתך עד השמדך אשר לא ישאיר לך דגן תירוש ויצהר שגר אלפיך ועשתרת צאנך--עד האבידו אתך 51
Iwo adzagwira ana a ziweto zanu, natenga zokolola za mʼdziko lanu kufikira mutawonongeka. Iwo sadzakusiyirani tirigu, vinyo watsopano kapena mafuta a olivi, kapena mwana wangʼombe aliyense kapena mwana wankhosa mpaka mutasanduka bwinja.
והצר לך בכל שעריך עד רדת חמתיך הגבהת והבצרות אשר אתה בטח בהן בכל ארצך והצר לך בכל שעריך בכל ארצך אשר נתן יהוה אלהיך לך 52
Iwo adzathira nkhondo mizinda yonse mʼdziko lanu lonse mpaka malinga anu ataliatali omwe mumadalira aja atagwa. Adzathira nkhondo mizinda yonse ya mʼdziko limene Yehova Mulungu wanu akukupatsani.
ואכלת פרי בטנך בשר בניך ובנתיך אשר נתן לך יהוה אלהיך--במצור ובמצוק אשר יציק לך איבך 53
Chifukwa cha zosautsa zimene mdani wanu adzabweretsa pa nthawi yokuthirani nkhondo, inu mudzadya ana anu, mnofu wa ana anu aamuna ndi aakazi amene Yehova Mulungu wanu wakupatsani.
האיש הרך בך והענג מאד--תרע עינו באחיו ובאשת חיקו וביתר בניו אשר יותיר 54
Ngakhale munthu woleza mtima ndi wachifundo kwambiri pakati panu sadzakhala ndi chifundo pa mʼbale wake weniweni kapena mkazi wake amene iye amamukonda kapena ana ake otsalawo,
מתת לאחד מהם מבשר בניו אשר יאכל מבלי השאיר לו כל--במצור ובמצוק אשר יציק לך איבך בכל שעריך 55
ndipo sadzagawirako aliyense wa iwo mnofu wa ana ake amene akudyawo. Kadzakhala kali komweko basi kamene kamutsalira chifukwa cha msautso umene mdani wanu adzagwetsa pa nthawi yothira nkhondo mizinda yanu yonse.
הרכה בך והענגה אשר לא נסתה כף רגלה הצג על הארץ מהתענג ומרך--תרע עינה באיש חיקה ובבנה ובבתה 56
Mayi woleza mtima ndi wachifundo kwambiri pakati panu, uja woti sangayerekeze kuponda pansi, adzabisira mwamuna wake amene amamukonda ndi ana ake omwe aamuna ndi aakazi
ובשליתה היוצת מבין רגליה ובבניה אשר תלד כי תאכלם בחסר כל בסתר--במצור ובמצוק אשר יציק לך איבך בשעריך 57
zotsalira za uchembere zochoka mʼmimba mwake ndi ana amene wabereka. Pakuti adzafuna kuti adye zimenezi yekha mobisa pa nthawi yothiridwa nkhondo chifukwa cha masautso amene mdani wanu adzagwetsa pa inu mʼmizinda yanu.
אם לא תשמר לעשות את כל דברי התורה הזאת הכתבים בספר הזה ליראה את השם הנכבד והנורא הזה--את יהוה אלהיך 58
Ngati simutsata mosamalitsa mawu onse a malamulo awa amene alembedwa mʼbuku lino, komanso ngati simuopa dzina la ulemerero ndi loopsa, dzina la Yehova Mulungu wanu,
והפלא יהוה את מכתך ואת מכות זרעך מכות גדלת ונאמנות וחלים רעים ונאמנים 59
Yehova adzatumiza pa inu ndi zidzukulu zanu miliri yoopsa, zosautsa zowawa ndi zokhalitsa, ndi matenda aakulu ndi ovuta kuchiritsika.
והשיב בך את כל מדוה מצרים אשר יגרת מפניהם ודבקו בך 60
Adzakubweretserani matenda onse a ku Igupto aja mumawaopawa ndipo adzakukanirirani.
גם כל חלי וכל מכה אשר לא כתוב בספר התורה הזאת--יעלם יהוה עליך עד השמדך 61
Yehova adzakubweretseraninso mtundu uliwonse wa matenda ndi zosautsa zimene sizinalembedwe mʼbuku la malamulo lino, mpaka mutawonongeka.
ונשארתם במתי מעט תחת אשר הייתם ככוכבי השמים לרב כי לא שמעת בקול יהוה אלהיך 62
Inu aja munali ochuluka ngati nyenyezi zakumwamba mudzatsala ochepa chabe chifukwa simunamvere Yehova Mulungu wanu.
והיה כאשר שש יהוה עליכם להיטיב אתכם ולהרבות אתכם--כן ישיש יהוה עליכם להאביד אתכם ולהשמיד אתכם ונסחתם מעל האדמה אשר אתה בא שמה לרשתה 63
Monga kunamukomera Yehova kukulemeretsani ndi kukuchulukitsani, momwemonso kudzamukondweretsa kukunthani ndi kukuwonongani. Inu mudzazulidwa kukuchotsani mʼdziko limene mukulowa kukalitengali.
והפיצך יהוה בכל העמים מקצה הארץ ועד קצה הארץ ועבדת שם אלהים אחרים אשר לא ידעת אתה ואבתיך--עץ ואבן 64
Kenaka Yehova adzakubalalitsani pakati pa anthu a mitundu yonse, kuchokera ku mapeto a dziko kufika ku mapeto ena. Kumeneko mudzapembedza milungu ina, milungu ya mitengo ndi ya miyala, imene inu eni kapena makolo anu sanayidziwepo.
ובגוים ההם לא תרגיע ולא יהיה מנוח לכף רגלך ונתן יהוה לך שם לב רגז וכליון עינים ודאבון נפש 65
Pakati pa mitundu ya anthu imeneyi simudzapeza mpata, popanda malo woti nʼkuyikapo phazi. Kumeneko Yehova adzakupatsani moyo wa nkhawa, maso otopa ndi chiyembekezo, ndi mtima wosakhazikika.
והיו חייך תלאים לך מנגד ופחדת לילה ויומם ולא תאמין בחייך 66
Inu mudzakhala osakhazikika mopitirira, odzazidwa ndi mantha usiku ndi usana womwe, osowa chitsimikizo cha pa moyo wanu.
בבקר תאמר מי יתן ערב ובערב תאמר מי יתן בקר--מפחד לבבך אשר תפחד וממראה עיניך אשר תראה 67
Mmawa muzidzati, “Chikhala anali madzulo!” ndipo madzulo mudzati, “Chikhala unali mmawa!” Mudzanena zimenezi chifukwa cha mantha amene adzakhale mu mtima mwanu ndi chifukwa cha zomwe muzidzaziona.
והשיבך יהוה מצרים באניות בדרך אשר אמרתי לך לא תסיף עוד לראתה והתמכרתם שם לאיביך לעבדים ולשפחות ואין קנה 68
Yehova adzakubwezani ku Igupto pa sitima zapamadzi paulendo umene Ine ndinati musawuyendenso. Kumeneko mudzadzitsatsa nokha kwa adani anu monga akapolo aamuna ndi aakazi, koma palibe amene adzakuguleni.

< דברים 28 >