< דברים 2 >
ונפן ונסע המדברה דרך ים סוף כאשר דבר יהוה אלי ונסב את הר שעיר ימים רבים | 1 |
Kenaka tinabwerera ndi kuyamba ulendo wolowera ku chipululu motsatira njira ya ku Nyanja Yofiira, monga mmene Yehova anatilamulira. Kwa nthawi yayitali tinayendayenda cha ku dziko la mapiri la Seiri.
Ndipo Yehova anati kwa ine,
רב לכם סב את ההר הזה פנו לכם צפנה | 3 |
“Mwazungulira mokwanira dziko la mapiri, tsopano tembenukirani kumpoto.
ואת העם צו לאמר אתם עברים בגבול אחיכם בני עשו הישבים בשעיר וייראו מכם ונשמרתם מאד | 4 |
Apatse anthu malamulo awa: ‘Muli pafupi kudutsa mʼchigawo cha abale anu adzukulu a Esau okhala ku Seiri. Iwowa adzachita nanu mantha koma musamale kwambiri.
אל תתגרו בם--כי לא אתן לכם מארצם עד מדרך כף רגל כי ירשה לעשו נתתי את הר שעיר | 5 |
Musayambane nawo popeza sindidzakupatsani gawo lina lililonse la dziko lawo ngakhale poti mungoyika phazi. Ndamupatsa Esau dziko lamapiri la Seiri kuti likhale lakelake.
אכל תשברו מאתם בכסף ואכלתם וגם מים תכרו מאתם בכסף--ושתיתם | 6 |
Inu muyenera kuwalipira ndi siliva pa chakudya chimene mudye ndi madzi amene mumwe.’”
כי יהוה אלהיך ברכך בכל מעשה ידך--ידע לכתך את המדבר הגדל הזה זה ארבעים שנה יהוה אלהיך עמך--לא חסרת דבר | 7 |
Yehova Mulungu wanu wakudalitsani mʼntchito zonse za manja anu. Iye wakuyangʼanirani pa ulendo wanu wodutsa mʼchipululu chachikulu. Yehova Mulungu wanu wakhala nanu mʼzaka makumi anayi, ndipo simunasowe kalikonse.
ונעבר מאת אחינו בני עשו הישבים בשעיר מדרך הערבה מאילת ומעצין גבר ונפן ונעבר דרך מדבר מואב | 8 |
Choncho tinapitiriza ulendo modutsa abale athu, adzukulu a Esau okhala ku Seiri. Tinapatukira njira ya ku Araba imene imachokera ku Elati ndi Ezioni Geberi ndipo tinayenda njira ya ku chipululu cha Mowabu.
ויאמר יהוה אלי אל תצר את מואב ואל תתגר בם מלחמה כי לא אתן לך מארצו ירשה--כי לבני לוט נתתי את ער ירשה | 9 |
Ndipo Yehova anati kwa ine, “Musawavutitse Amowabu kapena kuwaputa kuti muchite nawo nkhondo popeza sindidzakupatsani gawo lina lililonse la dziko lawo. Ndinapereka Ari kwa adzukulu a Loti ngati chuma chawo.”
האמים לפנים ישבו בה--עם גדול ורב ורם כענקים | 10 |
(Aemi, anthu amphamvu ndi ochuluka komanso ataliatali ngati Aanaki amakhala kumeneko.
רפאים יחשבו אף הם כענקים והמאבים יקראו להם אמים | 11 |
Ngati Aanaki, nawonso ankawayesa kuti anali Arefai, koma Amowabu ankawatcha iwo Aemi.
ובשעיר ישבו החרים לפנים ובני עשו יירשום וישמידום מפניהם וישבו תחתם כאשר עשה ישראל לארץ ירשתו אשר נתן יהוה להם | 12 |
Ahori amakhala ku Seiri koma adzukulu a Esau anawapirikitsa. Iwo anawononga Ahori pamaso pawo nawakhalira pamalo pawo monga Aisraeli anachitira mʼdziko limene Yehova anawapatsa ngati chuma chawo).
עתה קמו ועברו לכם--את נחל זרד ונעבר את נחל זרד | 13 |
Ndipo Yehova anati, “Tsopano nyamukani ndipo muwoloke Chigwa cha Zeredi.” Choncho tinawoloka chigwacho.
והימים אשר הלכנו מקדש ברנע עד אשר עברנו את נחל זרד שלשים ושמנה שנה--עד תם כל הדור אנשי המלחמה מקרב המחנה כאשר נשבע יהוה להם | 14 |
Panapita zaka 38 kuchokera pa nthawi imene tinachoka ku Kadesi Barinea mpaka pamene tinawoloka Chigwa cha Zeredi. Pa nthawi imeneyi nʼkuti mʼbado wonse wa anthu ankhondowo utawonongeka ku msasa monga Yehova anawalumbirira.
וגם יד יהוה היתה בם להמם מקרב המחנה עד תמם | 15 |
Dzanja la Yehova linatsutsana nawo mpaka wonse anathera ku msasa.
ויהי כאשר תמו כל אנשי המלחמה למות--מקרב העם | 16 |
Tsono atafa munthu wotsiriza mwa anthu ankhondowo,
אתה עבר היום את גבול מואב את ער | 18 |
“Lero mudutsa malire a Mowabu ku Ari podzera ku Ari.
וקרבת מול בני עמון--אל תצרם ואל תתגר בם כי לא אתן מארץ בני עמון לך ירשה--כי לבני לוט נתתיה ירשה | 19 |
Mukafika kwa Aamoni, musawavutitse kapena kuwaputa, popeza sindidzakupatsani gawo lililonse la dziko la Aamoni. Ine ndalipereka dzikoli ngati chuma kwa adzukulu a Loti.”
ארץ רפאים תחשב אף הוא רפאים ישבו בה לפנים והעמנים יקראו להם זמזמים | 20 |
(Ilinso ankaliyesa dziko la Arefai amene ankakhala kumeneko. Koma Aamoni ankawatcha iwo Azamuzumi.
עם גדול ורב ורם כענקים וישמידם יהוה מפניהם ויירשם וישבו תחתם | 21 |
Iwo anali anthu amphamvu ndiponso ochuluka, ataliatali ngati Aanaki. Yehova anawawononga ndi kuwachotsa pamaso pa Aamoni, amene anawapirikitsa nawakhalira pa malo pawo.
כאשר עשה לבני עשו הישבים בשעיר--אשר השמיד את החרי מפניהם ויירשם וישבו תחתם עד היום הזה | 22 |
Yehova anachitanso chimodzimodzi ndi adzukulu a Esau omwe anakhazikika ku Seiri atawononga Ahori powachotsa pamaso pawo. Iwo anawapirikitsa Ahoriwo ndi kuwakhalira pamalo pawo mpaka lero.
והעוים הישבים בחצרים עד עזה--כפתרים היצאים מכפתר השמידם וישבו תחתם | 23 |
Ndipo za Aavi omwe ankakhala mʼmidzi yofika mpaka ku Gaza, anagonjetsedwa ndi Akafitori wochokera ku Akafitori nakhala pamalo pawo).
קומו סעו ועברו את נחל ארנן--ראה נתתי בידך את סיחן מלך חשבון האמרי ואת ארצו החל רש והתגר בו מלחמה | 24 |
“Tsopano nyamukani, muwoloke khwawa la Arinoni. Taona ndapereka mʼmanja mwako Sihoni Mwamori mfumu ya Hesiboni ndi dziko lake lonse. Yambapo kutenga chuma chake ndi kumenyana naye nkhondo.
היום הזה אחל תת פחדך ויראתך על פני העמים תחת כל השמים--אשר ישמעון שמעך ורגזו וחלו מפניך | 25 |
Lero lomwe lino ndidzayamba kuyika chiopsezo ndi mantha pa mitundu yonse pansi pa thambo kuti akuope. Iwowo adzamva zambiri yako ndipo adzanjenjemera ndi kuwawidwa mtima chifukwa cha iwe.”
ואשלח מלאכים ממדבר קדמות אל סיחון מלך חשבון דברי שלום לאמר | 26 |
Ine ndinatuma amithenga kuchokera ku chipululu cha Kedemoti kupita kwa Sihoni mfumu ya Hesiboni kukanena mawu ofuna mtendere ndipo ndinati,
אעברה בארצך בדרך בדרך אלך לא אסור ימין ושמאול | 27 |
“Tiloleni tidutse mʼdziko mwanu. Ife tidzangodutsa ndi msewu waukulu, ndipo sitidzapatukira kumanja kapena kumanzere.
אכל בכסף תשברני ואכלתי ומים בכסף תתן לי ושתיתי רק אעברה ברגלי | 28 |
Mutigulitse chakudya kuti tidye ndi madzi kuti timwe pa mtengo wa siliva. Mungotilola kuti tidutse, tikuyenda pansi
כאשר עשו לי בני עשו הישבים בשעיר והמואבים הישבים בער--עד אשר אעבר את הירדן אל הארץ אשר יהוה אלהינו נתן לנו | 29 |
monga mmene anatichitira adzukulu a Esau okhala ku Seiri ndi Amowabu okhala ku Ari mpaka titawoloka Yorodani kufika ku dziko limene Yehova Mulungu wathu akutipatsa.”
ולא אבה סיחן מלך חשבון העברנו בו כי הקשה יהוה אלהיך את רוחו ואמץ את לבבו למען תתו בידך כיום הזה | 30 |
Koma Sihoni mfumu ya Hesiboni sanalole kuti tidutse. Popeza Yehova Mulungu wanu analimbitsa mzimu wake, nawumitsa mtima wake kuti amupereke mʼmanja mwanu monga wachitira lero lino.
ויאמר יהוה אלי ראה החלתי תת לפניך את סיחן ואת ארצו החל רש לרשת את ארצו | 31 |
Yehova anati kwa ine, “Taona ndayamba kumupereka Sihoni ndi dziko lake kwa iwe. Tsopano yamba kugonjetsa ndi kulanda dziko lake.”
ויצא סיחן לקראתנו הוא וכל עמו למלחמה--יהצה | 32 |
Sihoni ndi ankhondo ake atabwera kudzakumana nafe mwankhondo pa Yahazi,
ויתנהו יהוה אלהינו לפנינו ונך אתו ואת בנו ואת כל עמו | 33 |
Yehova Mulungu anamupereka iye kwa ife ndipo tinankantha, pamodzi ndi ana ake aamuna ndi gulu lake lonse lankhondo.
ונלכד את כל עריו בעת ההוא ונחרם את כל עיר מתם והנשים והטף לא השארנו שריד | 34 |
Pa nthawi imeneyi tinamulanda mizinda yake yonse ndi kuyiwononga kwathunthu, amuna, akazi ndi ana. Palibe amene anapulumuka.
רק הבהמה בזזנו לנו ושלל הערים אשר לכדנו | 35 |
Koma ziweto ndi zinthu zonse zimene tinalanda mʼmizinda imene tinagonjetsayo, tinazitenga kukhala zathu.
מערער אשר על שפת נחל ארנן והעיר אשר בנחל ועד הגלעד לא היתה קריה אשר שגבה ממנו את הכל נתן יהוה אלהינו לפנינו | 36 |
Kuchokera ku Aroeri mʼmphepete mwa mtsinje wa Arinoni ndi ku mzinda wa ku mtsinjeko mpaka kukafika ku Giliyadi, panalibe ndi mzinda ndi umodzi omwe umene unatikanika kuwugonjetsa. Yehova Mulungu wathu anatipatsa onsewo.
רק אל ארץ בני עמון לא קרבת כל יד נחל יבק וערי ההר וכל אשר צוה יהוה אלהינו | 37 |
Molingana ndi lamulo la Yehova Mulungu wathu, simunalowerere dziko lililonse la Aamoni, ngakhale dera lonse la ku mtsinje wa Yaboki kapena dera lozungulira dera la ku mizinda ya ku mapiri.