< דברים 1 >
אלה הדברים אשר דבר משה אל כל ישראל בעבר הירדן במדבר בערבה מול סוף בין פארן ובין תפל ולבן וחצרת--ודי זהב | 1 |
Awa ndi mawu amene Mose anayankhula kwa Aisraeli onse mʼchipululu kummawa kwa Yorodani, ku Araba moyangʼanana ndi Sufi, pakati pa Parani ndi Tofeli, Labani, Heziroti ndi Dizahabu.
אחד עשר יום מחרב דרך הר שעיר עד קדש ברנע | 2 |
(Kuyenda kuchokera ku Horebu kukafika ku Kadesi Barinea kudzera njira ya ku Phiri la Seiri ndi ulendo wa masiku khumi ndi limodzi).
ויהי בארבעים שנה בעשתי עשר חדש באחד לחדש דבר משה אל בני ישראל ככל אשר צוה יהוה אתו אלהם | 3 |
Mʼchaka cha makumi anayi, pa tsiku loyamba la mwezi 11, Mose anafotokozera Aisraeli zonse zimene Yehova anamulamula zokhudza iwowo.
אחרי הכתו את סיחן מלך האמרי אשר יושב בחשבון--ואת עוג מלך הבשן אשר יושב בעשתרת באדרעי | 4 |
Apa nʼkuti atagonjetsa Sihoni mfumu ya Aamori, amene amalamulira ku Hesiboni, ndipo pa Ederi anagonjetsa Ogi mfumu ya ku Basani, amene amalamulira mu Asiteroti.
בעבר הירדן בארץ מואב הואיל משה באר את התורה הזאת לאמר | 5 |
Chakummawa kwa Yorodani mʼchigawo cha Mowabu, Mose anayamba kufotokozera lamulo ili kunena kuti:
יהוה אלהינו דבר אלינו בחרב לאמר רב לכם שבת בהר הזה | 6 |
Ku Horebu, Yehova Mulungu wathu anati kwa ife, “Mwakhalitsa pa phiri lino.
פנו וסעו לכם ובאו הר האמרי ואל כל שכניו בערבה בהר ובשפלה ובנגב ובחוף הים--ארץ הכנעני והלבנון עד הנהר הגדל נהר פרת | 7 |
Sasulani msasa ndipo pitani ku dziko la mapiri la Aamori. Pitani kwa anthu onse oyandikana nawo ku Araba, ku mapiri, mʼmbali mwa mapiri a ku madzulo, ku Negevi ndiponso mʼmbali mwa nyanja, ku dziko la Akanaani ndi ku Lebanoni mpaka ku mtsinje waukulu wa Yufurate.
ראה נתתי לפניכם את הארץ באו ורשו את הארץ אשר נשבע יהוה לאבתיכם לאברהם ליצחק וליעקב לתת להם ולזרעם אחריהם | 8 |
Taonani, Ine ndakupatsani dziko ili. Lowani ndi kulilanda dziko limene Yehova analumbira kuti adzapereka kwa makolo anu, Abrahamu, Isake ndi Yakobo komanso kwa zidzukulu zawo.”
ואמר אלכם בעת ההוא לאמר לא אוכל לבדי שאת אתכם | 9 |
Pa nthawi imeneyi ine ndinati kwa inu, “Inu ndinu katundu olemera kwambiri woti sindingathe kumunyamula ndekha.
יהוה אלהיכם הרבה אתכם והנכם היום ככוכבי השמים לרב | 10 |
Yehova Mulungu wanu wakuchulukitsani kotero kuti lero lino ndinu ochuluka ngati nyenyezi za kumwamba.
יהוה אלהי אבותכם יסף עליכם ככם--אלף פעמים ויברך אתכם כאשר דבר לכם | 11 |
Yehova Mulungu wa makolo anu wachulukitsa chiwerengero chanu ndipo wakudalitsani monga momwe analonjezera!
איכה אשא לבדי טרחכם ומשאכם וריבכם | 12 |
Koma nanga ndekha ndidzasenza bwanji zovuta ndi zipsinjo zanu komanso milandu yanu?
הבו לכם אנשים חכמים ונבנים וידעים--לשבטיכם ואשימם בראשיכם | 13 |
Sankhani amuna ena anzeru, ozindikira ndi amene mumawalemekeza kuchokera ku mtundu uliwonse wa mitundu yanu, ndipo ndidzawayika kuti akulamulireni.”
ותענו אתי ותאמרו טוב הדבר אשר דברת לעשות | 14 |
Inu munandiyankha kuti, “Maganizo amenewa ndi abwino kuwachita.”
ואקח את ראשי שבטיכם אנשים חכמים וידעים ואתן אותם ראשים עליכם שרי אלפים ושרי מאות ושרי חמשים ושרי עשרת ושטרים לשבטיכם | 15 |
Choncho ndinatenga anthu otsogolera mafuko anu, anzeru ndi omwe mumawalemekeza, ndipo ndinawayika kuti azikulamulirani mʼmagulu a 1,000, ena 100, ena makumi asanu ndi ena khumi, kuti akhalenso ngati akapitawo a mafuko.
ואצוה את שפטיכם בעת ההוא לאמר שמע בין אחיכם ושפטתם צדק בין איש ובין אחיו ובין גרו | 16 |
Ndipo pa nthawi imeneyo ndinawawuza olamula anu kuti, “Muzimva milandu ya pakati pa abale anu ndi kuweruza mosakondera, kaya mlanduwo uli pakati pa Aisraeli okhaokha kapena mmodzi wa iwo ndi mlendo.
לא תכירו פנים במשפט כקטן כגדל תשמעון--לא תגורו מפני איש כי המשפט לאלהים הוא והדבר אשר יקשה מכם תקרבון אלי ושמעתיו | 17 |
Osamayangʼana nkhope poweruza koma muzimvetsera aangʼono ndi aakulu omwe chimodzimodzi. Musamaope munthu aliyense, pakuti chiweruzo ndi cha Mulungu. Muzindibweretsera mlandu uliwonse wovuta ndipo ndidzaumva.”
ואצוה אתכם בעת ההוא את כל הדברים אשר תעשון | 18 |
Ndipo nthawi imeneyo ndinakuwuzani chilichonse chimene munayenera kuchita.
ונסע מחרב ונלך את כל המדבר הגדול והנורא ההוא אשר ראיתם דרך הר האמרי כאשר צוה יהוה אלהינו אתנו ונבא עד קדש ברנע | 19 |
Tsono monga Yehova Mulungu wathu anatilamulira, tinanyamuka kuchoka ku Horebu ndi kupita cha ku dziko lamapiri la Aamori kudzera ku chipululu chachikulu ndi choopsa chija munachionachi, kotero kuti tinakafika ku Kadesi Barinea.
ואמר אלכם באתם עד הר האמרי אשר יהוה אלהינו נתן לנו | 20 |
Ndipo ndinati kwa inu, “Mwafika ku dziko la mapiri la Aamori, limene Yehova Mulungu wathu akutipatsa.
ראה נתן יהוה אלהיך לפניך--את הארץ עלה רש כאשר דבר יהוה אלהי אבתיך לך--אל תירא ואל תחת | 21 |
Taonani, Yehova Mulungu wanu wakupatsani dzikoli. Pitani ndi kulitenga monga Yehova, Mulungu wa makolo anu anakuwuzirani. Musaope kapenanso kugwa mphwayi.”
ותקרבון אלי כלכם ותאמרו נשלחה אנשים לפנינו ויחפרו לנו את הארץ וישבו אתנו דבר--את הדרך אשר נעלה בה ואת הערים אשר נבא אליהן | 22 |
Tsono nonse munabwera kwa ine ndi kuti, “Tiyeni titumize anthu ayambe apita kuti akazonde dzikolo ndi kutibweretsera mawu pa za njira yomwe tidzere ndi za mizinda imene tikafikireko.”
וייטב בעיני הדבר ואקח מכם שנים עשר אנשים איש אחד לשבט | 23 |
Ndinaona kuti maganizo amenewa anali abwino, choncho ndinasankha anthu khumi ndi awiri, mmodzi ku fuko lililonse.
ויפנו ויעלו ההרה ויבאו עד נחל אשכל וירגלו אתה | 24 |
Iwo ananyamuka napita mʼdziko la mapiri, ndipo anafika ku Chigwa cha Esikolo ndi kukazonda dzikolo.
ויקחו בידם מפרי הארץ ויורדו אלינו וישבו אתנו דבר ויאמרו טובה הארץ אשר יהוה אלהינו נתן לנו | 25 |
Pobwerera anatitengerako zipatso za mʼdzikomo ndipo anatipatsa mawu akuti, “Dziko limene Yehova Mulungu wathu akutipatsa ndi labwino.”
ולא אביתם לעלת ותמרו את פי יהוה אלהיכם | 26 |
Koma inu simunafune kupitako ndipo munawukira lamulo la Yehova Mulungu wanu.
ותרגנו באהליכם ותאמרו בשנאת יהוה אתנו הוציאנו מארץ מצרים--לתת אתנו ביד האמרי להשמידנו | 27 |
Inu munanyinyirika mʼmatenti anu nʼkumati, “Mulungu amatida nʼchifukwa chake anatitulutsa ku Igupto kuti atipereke mʼmanja mwa Aamori kuti atiwononge.
אנה אנחנו עלים אחינו המסו את לבבנו לאמר עם גדול ורם ממנו ערים גדלת ובצורת בשמים וגם בני ענקים ראינו שם | 28 |
Tigwire mtengo wanji? Abale athu anatitayitsa mtima. Iwo akuti, ‘Anthuwo ndi amphamvu ndi aatali kuposa ife, mizindayo ndi yayikulu ndipo mipanda yake ndi yayitali yofika kumwamba. Ife tinaonanso Aanaki kumeneko.’”
ואמר אלכם לא תערצון ולא תיראון מהם | 29 |
Ndipo ine ndinati kwa inu, “Musachite mantha kapena kuwaopa.
יהוה אלהיכם ההלך לפניכם הוא ילחם לכם ככל אשר עשה אתכם במצרים--לעיניכם | 30 |
Yehova Mulungu wanu, amene akukutsogolerani, adzakumenyerani nkhondo monga muja anachitira ku Igupto inu mukuona,
ובמדבר אשר ראית אשר נשאך יהוה אלהיך כאשר ישא איש את בנו--בכל הדרך אשר הלכתם עד באכם עד המקום הזה | 31 |
ndi mʼchipululu muja. Kumeneko munaona mmene Yehova Mulungu wanu anakunyamulirani monga abambo anyamulira mwana wawo, njira yonse yomwe munayenda mpaka munafika pamalo ano.”
ובדבר הזה--אינכם מאמינם ביהוה אלהיכם | 32 |
Ngakhale zinali choncho, simunadalire Yehova Mulungu wanu
ההלך לפניכם בדרך לתור לכם מקום--לחנתכם באש לילה לראתכם בדרך אשר תלכו בה ובענן יומם | 33 |
amene anakutsogolerani pa ulendo wanu, ndi moto nthawi ya usiku ndi mtambo nthawi ya masana, kukufunirani malo woti mumange msasa ndi kukuonetsani njira yoti muyendemo.
וישמע יהוה את קול דבריכם ויקצף וישבע לאמר | 34 |
Yehova atamva zimene munanena anakwiya nalumbira kuti,
אם יראה איש באנשים האלה הדור הרע הזה--את הארץ הטובה אשר נשבעתי לתת לאבתיכם | 35 |
“Palibe ndi mmodzi yemwe mwa mʼbado woyipawu amene adzaona dziko labwino limene ndinalumbira kupatsa makolo anu,
זולתי כלב בן יפנה הוא יראנה ולו אתן את הארץ אשר דרך בה ולבניו--יען אשר מלא אחרי יהוה | 36 |
kupatula Kalebe mwana wa Yefune. Iye adzaliona, ndipo ndidzamupatsa iye ndi adzukulu ake, dziko limene adzapondamo popeza anatsata Yehova ndi mtima wake wonse.”
גם בי התאנף יהוה בגללכם לאמר גם אתה לא תבא שם | 37 |
Chifukwa cha inu, Yehova anakwiyiranso ine ndipo anati, “Iwenso sudzalowa mʼdzikomo.
יהושע בן נון העמד לפניך הוא יבא שמה אתו חזק כי הוא ינחלנה את ישראל | 38 |
Koma Yoswa mwana wa Nuni amene amakuthandiza, adzalowa mʼdzikomo. Umulimbikitse chifukwa adzatsogolera Israeli kukalandira dzikolo.
וטפכם אשר אמרתם לבז יהיה ובניכם אשר לא ידעו היום טוב ורע--המה יבאו שמה ולהם אתננה והם יירשוה | 39 |
Ndipo angʼonoangʼono amene munati adzagwidwa ukapolo, ana anu amene sanadziwe kusiyanitsa chabwino ndi choyipa, amenewo adzalowa mʼdzikolo. Ndidzalipereka kwa iwo ndipo lidzakhala lawo.
ואתם פנו לכם וסעו המדברה דרך ים סוף | 40 |
Koma inu, tembenukani nyamukani kulowera cha ku chipululu kutsatira njira ya ku Nyanja Yofiira.”
ותענו ותאמרו אלי חטאנו ליהוה--אנחנו נעלה ונלחמנו ככל אשר צונו יהוה אלהינו ותחגרו איש את כלי מלחמתו ותהינו לעלת ההרה | 41 |
Ndipo inuyo munati, “Tachimwa pamaso pa Yehova. Tipita ndi kukachita nkhondo monga Yehova Mulungu wathu watilamulira.” Choncho aliyense wa inu anavala zankhondo, ndi kuganiza kuti nʼkosavuta kupita mʼdziko la mapiri lija.
ויאמר יהוה אלי אמר להם לא תעלו ולא תלחמו--כי אינני בקרבכם ולא תנגפו לפני איביכם | 42 |
Koma Yehova anandiwuza kuti, “Awuze anthuwa kuti, ‘Musapite kukachita nkhondo chifukwa Ine sindidzakhala nanu. Mudzagonjetsedwa ndi adani anu.’”
ואדבר אליכם ולא שמעתם ותמרו את פי יהוה ותזדו ותעלו ההרה | 43 |
Choncho ndinakuwuzani koma simunamve. Inu munawukira lamulo la Yehova ndipo mwamwano munayenda kulowa mʼdziko la mapiri.
ויצא האמרי הישב בהר ההוא לקראתכם וירדפו אתכם כאשר תעשינה הדברים ויכתו אתכם בשעיר עד חרמה | 44 |
Aamori amene ankakhala mʼmapiriwo anatuluka kukakumana nanu ndipo anakuthamangitsani ngati gulu la njuchi ndipo anakukanthani kuchokera ku Seiri, njira yonse mpaka ku Horima.
ותשבו ותבכו לפני יהוה ולא שמע יהוה בקלכם ולא האזין אליכם | 45 |
Munabwererako mukulira pamaso pa Yehova, koma Iye sanalabadire kulira kwanuko ndipo sanakumvetsereni.
ותשבו בקדש ימים רבים כימים אשר ישבתם | 46 |
Pamenepo munakhala ku Kadesi masiku ambiri kwa nthawi yayitali ndithu.