< עמוס 9 >

ראיתי את אדני נצב על המזבח ויאמר הך הכפתור וירעשו הספים ובצעם בראש כלם ואחריתם בחרב אהרג לא ינוס להם נס ולא ימלט להם פליט 1
Ine ndinaona Ambuye atayima pambali pa guwa lansembe, ndipo anati: “Kantha mitu ya nsanamira kuti ziwundo za nyumba zigwedezeke. Muzigwetsere pa mitu ya anthu onse, onse amene atsalira ndidzawapha ndi lupanga. Palibe ndi mmodzi yemwe amene adzathawe, palibe amene adzapulumuke.
אם יחתרו בשאול משם ידי תקחם ואם יעלו השמים--משם אורידם (Sheol h7585) 2
Ngakhale atakumba pansi mpaka ku malo a anthu akufa, dzanja langa lidzawatulutsa kumeneko. Ngakhale atakwera kumwamba Ine ndidzawatsakamutsa kumeneko. (Sheol h7585)
ואם יחבאו בראש הכרמל משם אחפש ולקחתים ואם יסתרו מנגד עיני בקרקע הים--משם אצוה את הנחש ונשכם 3
Ngakhale atakabisala pamwamba pa phiri la Karimeli, Ine ndidzawasaka kumeneko ndi kuwagwira. Ngakhale atakabisala pansi pa nyanja yayikulu, ndidzalamula njoka kuti iwalume kumeneko.
ואם ילכו בשבי לפני איביהם משם אצוה את החרב והרגתם ושמתי עיני עליהם לרעה ולא לטובה 4
Ngakhale adani awo awakusire ku ukapolo, ndidzalamula lupanga kuti liwaphe kumeneko. Ndidzawayangʼanitsitsa kuti zoyipa ziwagwere; osati zabwino.”
ואדני יהוה הצבאות הנוגע בארץ ותמוג ואבלו כל יושבי בה ועלתה כיאר כלה ושקעה כיאר מצרים 5
Ambuye Yehova Wamphamvuzonse amene amakhudza dziko lapansi ndipo dzikolo limasungunuka, onse amene amakhala mʼmenemo amalira. Dziko lonse lidzadzaza ngati mtsinje wa Nailo, kenaka nʼkuphwera ngati mtsinje wa ku Igupto.
הבונה בשמים מעלותו ואגדתו על ארץ יסדה הקרא למי הים וישפכם על פני הארץ--יהוה שמו 6
Iye amene amamanga malo ake okhalamo kumwamba, ndi kuyika maziko ake pa dziko lapansi, Iye amene amayitana madzi a ku nyanja ndikuwakhuthulira pa dziko lapansi, dzina lake ndiye Yehova.
הלוא כבני כשיים אתם לי בני ישראל נאם יהוה הלוא את ישראל העליתי מארץ מצרים ופלשתיים מכפתור וארם מקיר 7
“Kodi kwa Ine, inu Aisraeli, simuli chimodzimodzi ndi Akusi?” Akutero Yehova. “Kodi sindine amene ndinatulutsa Israeli ku Igupto, Afilisti ku Kafitori ndi Aaramu ku Kiri?
הנה עיני אדני יהוה בממלכה החטאה והשמדתי אתה מעל פני האדמה אפס כי לא השמיד אשמיד את בית יעקב--נאם יהוה 8
“Taonani, maso a Ambuye Yehova ali pa ufumu wochimwawu. Ndidzawufafaniza pa dziko lapansi. Komabe sindidzawononga kotheratu nyumba ya Yakobo,” akutero Yehova.
כי הנה אנכי מצוה והנעותי בכל הגוים את בית ישראל כאשר ינוע בכברה ולא יפול צרור ארץ 9
“Pakuti ndidzalamula, ndipo ndidzagwedeza nyumba ya Israeli pakati pa mitundu yonse ya anthu monga momwe amasefera ufa mʼsefa, koma palibe nʼkamwala kamodzi komwe kamene kadzagwe pansi.
בחרב ימותו כל חטאי עמי האמרים לא תגיש ותקדים בעדינו--הרעה 10
Anthu onse ochimwa pakati pa anthu anga adzaphedwa ndi lupanga, onse amene amanena kuti, ‘Tsoka silidzatigwera ife kapena kutiwononga.’
ביום ההוא אקים את סכת דויד הנפלת וגדרתי את פרציהן והרסתיו אקים ובניתיה כימי עולם 11
“Tsiku limenelo ndidzabwezeretsa nyumba ya Davide imene inagwa. Ndidzakonzanso malo amene anagumuka, ndi kuyimanganso monga inalili poyamba,
למען יירשו את שארית אדום וכל הגוים אשר נקרא שמי עליהם נאם יהוה עשה זאת 12
kuti adzatengenso otsala a Edomu ndi mitundu yonse imene imatchedwa ndi dzina langa,” akutero Yehova amene adzachita zinthu izi.
הנה ימים באים נאם יהוה ונגש חורש בקצר ודרך ענבים במשך הזרע והטיפו ההרים עסיס וכל הגבעות תתמוגגנה 13
Yehova akunena kuti “Nthawi ikubwera pamene mlimi wotipula adzapyola wokolola ndipo woponda mphesa adzapyola wodzala mbewu. Mapiri adzachucha vinyo watsopano ndi kuyenderera pa zitunda zonse.
ושבתי את שבות עמי ישראל ובנו ערים נשמות וישבו ונטעו כרמים ושתו את יינם ועשו גנות ואכלו את פריהם 14
Ndidzawabwezeranso pabwino anthu anga Aisraeli; mizinda imene inali mabwinja idzamangidwanso ndipo azidzakhalamo. Adzalima minda ya mpesa ndipo adzamwa vinyo wake; adzalima minda ndipo adzadya zipatso zake.
ונטעתים על אדמתם ולא ינתשו עוד מעל אדמתם אשר נתתי להם--אמר יהוה אלהיך 15
Ndidzakhazika Aisraeli mʼdziko mwawo, ndipo sadzachotsedwamonso mʼdziko limene Ine ndawapatsa,” akutero Yehova Mulungu wako.

< עמוס 9 >