< עמוס 6 >
הוי השאננים בציון והבטחים בהר שמרון נקבי ראשית הגוים ובאו להם בית ישראל | 1 |
Tsoka kwa amene simukulabadira kanthu ku Ziyoni, ndiponso kwa inu amene mukukhala mwamtendere pa Phiri la Samariya, inu anthu otchuka ochokera ku mtundu wa anthu omveka, kumene Aisraeli amafikako!
עברו כלנה וראו ולכו משם חמת רבה ורדו גת פלשתים הטובים מן הממלכות האלה--אם רב גבולם מגבלכם | 2 |
Pitani ku mzinda wa Kaline mukawuyangʼane; mukapitenso ku Hamati-raba mzinda waukulu uja, ndipo mukatsikirenso ku Gati kwa Afilisti. Kodi mizinda imeneyi ndi yopambana maufumu anu awiriwa? Kodi dziko lawo ndi lalikulu kupambana lanu?
המנדים ליום רע ותגשון שבת חמס | 3 |
Inu simulabadirako kuti tsiku loyipa lidzafika, zochita zanu zimafulumizitsa ulamuliro wankhanza.
השכבים על מטות שן וסרחים על ערשותם ואכלים כרים מצאן ועגלים מתוך מרבק | 4 |
Mumagona pa mabedi owakongoletsa ndi minyanga ya njovu, mumagona pa mipando yanu ya wofuwofu. Mumadya ana ankhosa onona ndi ana angʼombe onenepa.
הפרטים על פי הנבל כדויד חשבו להם כלי שיר | 5 |
Mumayimba azeze anu ndi kumangopeka nyimbo pa zingʼwenyengʼwenye ngati Davide.
השתים במזרקי יין וראשית שמנים ימשחו ולא נחלו על שבר יוסף | 6 |
Mumamwera vinyo mʼzipanda zodzaza ndipo mumadzola mafuta abwino kwambiri, koma simumva chisoni ndi kuwonongeka kwa Yosefe.
לכן עתה יגלו בראש גלים וסר מרזח סרוחים | 7 |
Nʼchifukwa chake inu mudzakhala mʼgulu la anthu oyamba kupita ku ukapolo; maphwando ndi zikondwerero zanu zidzatheratu.
נשבע אדני יהוה בנפשו נאם יהוה אלהי צבאות מתאב אנכי את גאון יעקב וארמנתיו שנאתי והסגרתי עיר ומלאה | 8 |
Ambuye Yehova walumbira mʼdzina lake. Yehova Mulungu Wamphamvuzonse walengeza kuti, “Ndimanyansidwa ndi kunyada kwa Yakobo, ndimadana ndi nyumba zake zaufumu; Ine ndidzawupereka mzindawu pamodzi ndi zonse zili mʼmenemo.”
והיה אם יותרו עשרה אנשים בבית אחד--ומתו | 9 |
Ngati anthu khumi otsala adzabisala mʼnyumba imodzi, nawonso adzafa ndithu.
ונשאו דודו ומסרפו להוציא עצמים מן הבית ואמר לאשר בירכתי הבית העוד עמך ואמר אפס ואמר הס כי לא להזכיר בשם יהוה | 10 |
Ndipo ngati mʼbale wake wa wina wakufayo, woyenera kusamala za maliro, adzafika kudzatulutsa mitembo mʼnyumbamo nʼkufunsa aliyense amene akubisalabe mʼnyumbamo kuti, “Kodi uli ndi wina wamoyo mʼmenemo?” Ndipo munthu wobisalayo ndi kuyankha kuti, “Ayi,” mʼbaleyo adzanena kuti, “Khala chete! Ife tisayerekeze kutchula dzina la Yehova.”
כי הנה יהוה מצוה והכה הבית הגדול רסיסים והבית הקטן בקעים | 11 |
Pakuti Yehova walamula kuti nyumba zikuluzikulu Iye adzazigamulagamula, ndipo nyumba zazingʼono zidzasanduka maduka okhaokha.
הירצון בסלע סוסים אם יחרוש בבקרים כי הפכתם לראש משפט ופרי צדקה ללענה | 12 |
Kodi akavalo amathamanga pa thanthwe? Kodi wina amatipula ndi ngʼombe mʼnyanja? Koma chiweruzo cholungama mwachisandutsa kukhala zinthu zakupha ndipo chipatso cha chilungamo mwachisandutsa kukhala chowawa.
השמחים ללא דבר האמרים--הלוא בחזקנו לקחנו לנו קרנים | 13 |
Inu amene mukunyadira kuti munagonjetsa Lo Debara ndipo mukunena kuti, “Kodi sitinatenge Karinaimu ndi mphamvu zathu zokha?”
כי הנני מקים עליכם בית ישראל נאם יהוה אלהי הצבאות--גוי ולחצו אתכם מלבוא חמת עד נחל הערבה | 14 |
Koma Yehova Mulungu Wamphamvuzonse akulengeza kuti, “Inu nyumba ya Israeli, ndidzakudzutsirani mtundu wina wa anthu umene udzakuzunzani kuchokera ku Lebo Hamati mpaka ku Chigwa cha Araba.”