< עמוס 1 >

דברי עמוס אשר היה בנקדים מתקוע אשר חזה על ישראל בימי עזיה מלך יהודה ובימי ירבעם בן יואש מלך ישראל--שנתים לפני הרעש 1
Mawu a Amosi, mmodzi mwa anthu oweta nkhosa ku Tekowa. Zimene iye anaona mʼmasomphenya zokhudza Israeli patatsala zaka ziwiri kuti chivomerezi chichitike, nthawi imene Uziya anali mfumu ya Yuda ndipo Yeroboamu mwana wa Yowasi anali mfumu ya Israeli.
ויאמר--יהוה מציון ישאג ומירושלם יתן קולו ואבלו נאות הרעים ויבש ראש הכרמל 2
Amosi anati: “Yehova akubangula mu Ziyoni ndipo akumveka ngati bingu mu Yerusalemu; msipu wa abusa ukulira, ndipo pamwamba pa Karimeli pakuwuma.”
כה אמר יהוה על שלשה פשעי דמשק ועל ארבעה לא אשיבנו על דושם בחרצות הברזל את הגלעד 3
Yehova akuti, “Chifukwa anthu a ku Damasiko akunka nachimwirachimwira, Ine sindileka kuwalanga. Popeza anapuntha Giliyadi ndi zopunthira za mano achitsulo,
ושלחתי אש בבית חזאל ואכלה ארמנות בן הדד 4
Ine ndidzatumiza moto pa nyumba ya Hazaeli umene udzanyeketsa nyumba zaufumu za Beni-Hadadi.
ושברתי בריח דמשק והכרתי יושב מבקעת און ותומך שבט מבית עדן וגלו עם ארם קירה אמר יהוה 5
Ndidzathyola chipata cha Damasiko; ndidzawononga mfumu yokhala ku Chigwa cha Aveni, ndiponso iye amene akugwira ndodo yaufumu mu Beti-Edeni. Anthu a ku Aramu adzapita ku ukapolo ku Kiri,” akutero Yehova.
כה אמר יהוה על שלשה פשעי עזה ועל ארבעה לא אשיבנו על הגלותם גלות שלמה להסגיר לאדום 6
Yehova akuti, “Chifukwa anthu a ku Gaza akunka nachimwirachimwira, Ine sindileka kuwalanga. Popeza anatenga ukapolo mtundu wathunthu ndi kuwugulitsa ku Edomu,
ושלחתי אש בחומת עזה ואכלה ארמנתיה 7
ndidzatumiza moto pa makoma a Gaza umene udzanyeketsa nyumba zake zaufumu.
והכרתי יושב מאשדוד ותומך שבט מאשקלון והשיבותי ידי על עקרון ואבדו שארית פלשתים--אמר אדני יהוה 8
Ndidzawononga mfumu ya ku Asidodi komanso amene akugwira ndodo yaufumu ku Asikeloni. Ndidzalanga Ekroni, mpaka wotsala mwa Afilisti atafa,” akutero Ambuye Yehova.
כה אמר יהוה על שלשה פשעי צר ועל ארבעה לא אשיבנו על הסגירם גלות שלמה לאדום ולא זכרו ברית אחים 9
Yehova akuti, “Chifukwa anthu a ku Turo akunka nachimwirachimwira, Ine sindileka kuwalanga. Popeza iwo anagulitsa mtundu wathunthu ku ukapolo ku Edomu, osasunga pangano laubale lija,
ושלחתי אש בחומת צר ואכלה ארמנותיה 10
Ine ndidzatumiza moto pa makoma a Turo umene udzanyeketsa nyumba zake zaufumu.”
כה אמר יהוה על שלשה פשעי אדום ועל ארבעה לא אשיבנו על רדפו בחרב אחיו ושחת רחמיו ויטרף לעד אפו ועברתו שמרה נצח 11
Yehova akuti, “Chifukwa anthu a ku Edomu akunka nachimwirachimwira, Ine sindileka kuwalanga. Popeza anathamangitsa mʼbale wake ndi lupanga, popanda nʼchifundo chomwe. Popeza mkwiyo wake unakulabe ndipo ukali wake sunatonthozeke,
ושלחתי אש בתימן ואכלה ארמנות בצרה 12
Ine ndidzatumiza moto pa Temani umene udzanyeketsa nyumba zaufumu za Bozira.”
כה אמר יהוה על שלשה פשעי בני עמון ועל ארבעה לא אשיבנו על בקעם הרות הגלעד למען הרחיב את גבולם 13
Yehova akuti, “Chifukwa anthu a ku Amoni akunka nachimwirachimwira, Ine sindileka kuwalanga. Popeza anatumbula akazi oyembekezera a ku Giliyadi nʼcholinga choti akuze malire awo,
והצתי אש בחומת רבה ואכלה ארמנותיה בתרועה ביום מלחמה בסער ביום סופה 14
Ine ndidzayatsa moto pa makoma a ku Raba umene udzanyeketsa nyumba zake zaufumu. Padzakhala kulira kwakukulu pa tsiku la nkhondoyo, kumenyana kudzakhala kwafumbi ngati mkuntho wa kamvuluvulu.
והלך מלכם בגולה הוא ושריו יחדו אמר יהוה 15
Mfumu yawo idzatengedwa kupita ku ukapolo, iyo pamodzi ndi akuluakulu ake,” akutero Yehova.

< עמוס 1 >