< מלכים ב 3 >

ויהורם בן אחאב מלך על ישראל בשמרון בשנת שמנה עשרה ליהושפט מלך יהודה וימלך שתים עשרה שנה 1
Yoramu mwana wa Ahabu anakhala mfumu ya Israeli ku Samariya mʼchaka cha 18 cha Yehosafati mfumu ya ku Yuda ndipo analamulira zaka khumi ndi ziwiri.
ויעשה הרע בעיני יהוה--רק לא כאביו וכאמו ויסר את מצבת הבעל אשר עשה אביו 2
Iye anachita zoyipa pamaso pa Yehova koma sizinafanane ndi zimene anachita abambo ndi amayi ake. Iye anachotsa fano la mwala la Baala limene abambo ake anapanga.
רק בחטאות ירבעם בן נבט אשר החטיא את ישראל--דבק לא סר ממנה 3
Komabe anawumirira kuchita machimo a Yeroboamu mwana wa Nebati, amene anachimwitsa nawo Israeli ndipo sanafune kuwaleka.
ומישע מלך מואב היה נקד והשיב למלך ישראל מאה אלף כרים ומאה אלף אילים צמר 4
Tsono Mesa, mfumu ya ku Mowabu ankaweta nkhosa, ndipo iye ankayenera kumapereka kwa mfumu ya ku Israeli chaka ndi chaka ana ankhosa onenepa okwanira 100,000 pamodzi ndi ubweya wankhosa 100,000 zazimuna.
ויהי כמות אחאב ויפשע מלך מואב במלך ישראל 5
Koma atamwalira Ahabu, mfumu ya ku Mowabu inawukira mfumu ya ku Israeli.
ויצא המלך יהורם ביום ההוא--משמרון ויפקד את כל ישראל 6
Choncho nthawi imeneyi mfumu Yoramu inatuluka mu Samariya ndi kukasonkhanitsa Aisraeli onse.
וילך וישלח אל יהושפט מלך יהודה לאמר מלך מואב פשע בי--התלך אתי אל מואב למלחמה ויאמר אעלה כמוני כמוך כעמי כעמך כסוסי כסוסיך 7
Yoramu anatumizanso uthenga uwu kwa Yehosafati mfumu ya ku Yuda: “Mfumu ya ku Mowabu yandiwukira. Kodi ungapite nane kukamenyana ndi Mowabu?” Iye anayankha kuti, “Ine ndidzapita nawe. Iwe ndi ine ndife anthu amodzi, anthu anga ali ngati anthu ako, akavalo anga ali ngati akavalo ako.”
ויאמר אי זה הדרך נעלה ויאמר דרך מדבר אדום 8
Yehosafati anafunsa kuti, “Kodi tidzera njira iti popita ku nkhondoko?” Yoramu anayankha kuti, “Tidzera ku Chipululu cha Edomu.”
וילך מלך ישראל ומלך יהודה ומלך אדום ויסבו דרך שבעת ימים ולא היה מים למחנה ולבהמה אשר ברגליהם 9
Choncho mfumu ya ku Israeli inanyamuka pamodzi ndi mfumu ya ku Yuda ndi ya ku Edomu. Ndipo atayenda mozungulira mʼchipululu kwa masiku asanu ndi awiri, asilikali analibe madzi woti amwe kapena kumwetsa nyama zawo zosenza katundu.
ויאמר מלך ישראל אהה--כי קרא יהוה לשלשת המלכים האלה לתת אותם ביד מואב 10
Mfumu inafuwula kuti, “Nʼchiyani chomwe chikutichitikira! Kodi Yehova wasonkhanitsa mafumu atatu pamodzi kuti atipereke mʼmanja mwa Amowabu?”
ויאמר יהושפט האין פה נביא ליהוה ונדרשה את יהוה מאותו ויען אחד מעבדי מלך ישראל ויאמר פה אלישע בן שפט אשר יצק מים על ידי אליהו 11
Koma mfumu Yehosafati inafunsa kuti, “Kodi kuno kulibe mneneri wa Yehova woti tingakafunse kwa Yehova kudzera mwa iyeyo?” Mtsogoleri wa ankhondo wa mfumu ya ku Israeli anayankha kuti, “Alipo, Elisa mwana wa Safati. Iye anali mtumiki wa Eliya.”
ויאמר יהושפט יש אותו דבר יהוה וירדו אליו מלך ישראל ויהושפט--ומלך אדום 12
Yehosafati anati, “Yehova amayankhula kudzera mwa iye.” Choncho mfumu ya ku Israeli pamodzi ndi Yehosafati ndiponso mfumu ya ku Edomu anapita kwa Elisa.
ויאמר אלישע אל מלך ישראל מה לי ולך--לך אל נביאי אביך ואל נביאי אמך ויאמר לו מלך ישראל אל כי קרא יהוה לשלשת המלכים האלה לתת אותם ביד מואב 13
Elisa ananena kwa mfumu ya ku Israeli kuti, “Pali ubale wanji pakati pa inu ndi ine? Pitani kwa aneneri a abambo ndi amayi anu.” Mfumu ya ku Israeli inayankha kuti, “Ayi, pakuti ndi Yehova amene anatisonkhanitsa ife mafumu atatu pamodzi kuti atipereke mʼmanja mwa Amowabu.”
ויאמר אלישע חי יהוה צבאות אשר עמדתי לפניו כי לולי פני יהושפט מלך יהודה אני נשא--אם אביט אליך ואם אראך 14
Elisa anati, “Pali Yehova Wamphamvuzonse amene ndimamutumikira, pakanapanda kuti ndimamuchitira ulemu Yehosafati mfumu ya ku Yuda, sindikanakulabadirani kapena kukuyangʼanani nʼkomwe.
ועתה קחו לי מנגן והיה כנגן המנגן ותהי עליו יד יהוה 15
Koma tsopano ndiyitanireni munthu wodziwa kuyimba bwino zeze.” Munthuyo akuyimba zeze, mphamvu ya Yehova inafika pa Elisa,
ויאמר כה אמר יהוה עשה הנחל הזה גבים גבים 16
ndipo anati, “Yehova akuti, ‘Kumbani ngalande mʼchigwa chonse.’
כי כה אמר יהוה לא תראו רוח ולא תראו גשם והנחל ההוא ימלא מים ושתיתם אתם ומקניכם ובהמתכם 17
Pakuti Yehova akunena kuti, ‘Simudzaona mphepo kapena mvula, komabe chigwa ichi chopanda madzi chidzadzaza ndi madzi, ndipo inu mudzamwa pamodzi ndi ngʼombe zanu ndiponso nyama zanu zonse.’
ונקל זאת בעיני יהוה ונתן את מואב בידכם 18
Izi ndi zosavuta pamaso pa Yehova. Ndipo adzaperekanso Amowabu mʼmanja mwanu.
והכיתם כל עיר מבצר וכל עיר מבחור וכל עץ טוב תפילו וכל מעיני מים תסתמו וכל החלקה הטובה תכאבו באבנים 19
Mudzagonjetsa mizinda yawo yonse yotetezedwa ndiponso mizinda yawo ikuluikulu. Mudzagwetsa mtengo wabwino uliwonse, mudzatseka akasupe onse amadzi, ndiponso mudzawononga minda yawo yonse yachonde poponyamo miyala.”
ויהי בבקר כעלות המנחה והנה מים באים מדרך אדום ותמלא הארץ את המים 20
Mmawa mwake, nthawi yopereka nsembe ili pafupi, anangoona madzi akutuluka kuchokera ku Edomu, ndipo malo onse anadzaza ndi madzi.
וכל מואב שמעו כי עלו המלכים להלחם בם ויצעקו מכל חגר חגרה ומעלה ויעמדו על הגבול 21
Tsono nʼkuti Amowabu onse atamva kuti mafumu abwera kudzachita nawo nkhondo. Kotero, anayitana munthu aliyense, wamkulu ndi wamngʼono amene ankatha kugwira chida chankhondo ndipo anakayima ku malire a dziko lawo.
וישכימו בבקר והשמש זרחה על המים ויראו מואב מנגד את המים אדמים כדם 22
Amowabu atadzuka mmamawa, dzuwa likuwala pa madziwo, anaona madziwo akuoneka wofiira ngati magazi patsogolo pawo.
ויאמרו דם זה החרב נחרבו המלכים ויכו איש את רעהו ועתה לשלל מואב 23
Ndipo iwo anati, “Taonani magazi! Mafumu aja amenyana okhaokha ndipo aphana. Amowabu, tsopano ndi nthawi yofunkha!”
ויבאו אל מחנה ישראל ויקמו ישראל ויכו את מואב וינסו מפניהם ויבו (ויכו) בה והכות את מואב 24
Koma Amowabu atafika ku misasa ya Israeli, Aisraeli ananyamuka ndi kumenyana nawo mpaka anathawa. Ndipo Aisraeli analowa mʼdzikolo ndi kupha Amowabu.
והערים יהרסו וכל חלקה טובה ישליכו איש אבנו ומלאוה וכל מעין מים יסתמו וכל עץ טוב יפילו עד השאיר אבניה בקיר חרשת ויסבו הקלעים ויכוה 25
Aisraeli anagumula mizinda yawo ndipo munthu aliyense anaponya mwala pa munda uliwonse wachonde mpaka utadzaza ndi miyala. Iwo anatseka akasupe onse amadzi ndiponso anadula mtengo wabwino uliwonse. Mzinda wa Kiri Hareseti wokha ndiye unatsala wotetezedwa koma anthu oponya miyala anawuzungulira nawuthiranso nkhondo.
וירא מלך מואב כי חזק ממנו המלחמה ויקח אותו שבע מאות איש שלף חרב להבקיע אל מלך אדום--ולא יכלו 26
Mfumu ya ku Mowabu itaona kuti nkhondo ikumulaka, inatenga anthu 700 a malupanga kuti athawe modutsa mfumu ya ku Edomu, koma inalephera.
ויקח את בנו הבכור אשר ימלך תחתיו ויעלהו עלה על החמה ויהי קצף גדול על ישראל ויסעו מעליו וישבו לארץ 27
Choncho inatenga mwana wake wamwamuna woyamba kubadwa, amene akanalowa ufumu mʼmalo mwake, ndi kumupereka nsembe pa khoma la mzinda. Zimenezi zinachititsa kuti mkwiyo ndi ukali wa Amowabu ukule kwambiri pa Aisraeli ndipo Aisraeliwo anathawa nabwerera ku dziko la kwawo.

< מלכים ב 3 >