< מלכים ב 23 >
וישלח המלך ויאספו אליו כל זקני יהודה וירושלם | 1 |
Pamenepo mfumu inayitanitsa akuluakulu onse a ku Yuda ndi Yerusalemu.
ויעל המלך בית יהוה וכל איש יהודה וכל ישבי ירושלם אתו והכהנים והנביאים וכל העם למקטן ועד גדול ויקרא באזניהם את כל דברי ספר הברית הנמצא בבית יהוה | 2 |
Mfumuyo inapita ku Nyumba ya Yehova pamodzi ndi anthu onse a ku Yuda, ndi onse okhala mu Yerusalemu, ansembe ndi aneneri, ndiponso anthu ena onse kuyambira wamngʼono mpaka wamkulu. Mfumuyo inawerenga mawu onse a mʼBuku la Chipangano limene linapezeka mʼNyumba ya Yehova, anthu onse akumva.
ויעמד המלך על העמוד ויכרת את הברית לפני יהוה ללכת אחר יהוה ולשמר מצותיו ואת עדותיו ואת חקתיו בכל לב ובכל נפש להקים את דברי הברית הזאת הכתבים על הספר הזה ויעמד כל העם בברית | 3 |
Mfumu inayimirira pambali pa chipilala ndi kuchita pangano pamaso pa Yehova kuti idzatsatira Yehova ndi kusunga malamulo, mawu ndi malangizo ake ndi mtima wonse ndi moyo wonse, kukwaniritsa mawu a mʼpanganoli, olembedwa mʼbukuli. Pamenepo anthu onse anadzipereka kutsatira panganoli.
ויצו המלך את חלקיהו הכהן הגדול ואת כהני המשנה ואת שמרי הסף להוציא מהיכל יהוה את כל הכלים העשוים לבעל ולאשרה ולכל צבא השמים וישרפם מחוץ לירושלם בשדמות קדרון ונשא את עפרם בית אל | 4 |
Mfumu inalamula wansembe wamkulu Hilikiya, ansembe othandizana naye ndi alonda a pa khomo kuti achotse mʼNyumba ya Yehova ziwiya zonse zopembedzera Baala ndi Asera ndiponso mafano a zinthu zamlengalenga. Yosiya anazitentha kunja kwa Yerusalemu, ku minda ya ku Chigwa cha Kidroni ndipo phulusa lake anapita nalo ku Beteli.
והשבית את הכמרים אשר נתנו מלכי יהודה ויקטר בבמות בערי יהודה ומסבי ירושלם ואת המקטרים לבעל לשמש ולירח ולמזלות ולכל צבא השמים | 5 |
Iye anachotsa ansembe a mafano amene anayikidwa ndi mafumu a Yuda kuti azifukiza lubani ku malo opembedzera mafano a ku mizinda ya ku Yuda ndi kumalo ozungulira Yerusalemu, amene ankafukiza lubani kwa Baala, dzuwa, mwezi, nyenyezi ndi zinthu zonse zamlengalenga.
ויצא את האשרה מבית יהוה מחוץ לירושלם אל נחל קדרון וישרף אתה בנחל קדרון וידק לעפר וישלך את עפרה על קבר בני העם | 6 |
Anachotsa fano la Asera mʼNyumba ya Yehova napita nalo kunja kwa Yerusalemu, ku Chigwa cha Kidroni, nalitentha kumeneko. Anapera fanolo ndi kukataya phulusa lake pa manda a anthu wamba.
ויתץ את בתי הקדשים אשר בבית יהוה אשר הנשים ארגות שם בתים--לאשרה | 7 |
Iye anagwetsanso tinyumba ta ochita zachiwerewere, timene tinali mʼNyumba ya Yehova, kumene akazi ankalukirako mikanjo yovala popembedza Asera.
ויבא את כל הכהנים מערי יהודה ויטמא את הבמות אשר קטרו שמה הכהנים מגבע עד באר שבע ונתץ את במות השערים אשר פתח שער יהושע שר העיר אשר על שמאול איש בשער העיר | 8 |
Yosiya anabweretsanso ansembe onse kuchokera mʼmizinda ya Yuda, nawononga malo opembedzera mafano, kuyambira ku Geba mpaka ku Beeriseba, kumene ansembe ankafukizako lubani. Anagwetsa nyumba za milungu zimene zinali pa chipata cha Yoswa, bwanamkubwa wa mzindawo, kumanzere kwa chipata cha mzinda.
אך לא יעלו כהני הבמות אל מזבח יהוה בירושלם כי אם אכלו מצות בתוך אחיהם | 9 |
Ngakhale kuti ansembe a ku malo opembedzera mafanowo sanawalole kuti atumikire pa guwa lansembe la Yehova mu Yerusalemu, koma ankadya buledi wopanda yisiti pamodzi ndi ansembe anzawo.
וטמא את התפת אשר בגי בני (בן) הנם לבלתי להעביר איש את בנו ואת בתו באש--למלך | 10 |
Mfumu Yosiya anawononganso Tofeti, amene anali ku Chigwa cha Hinomu, kuti wina aliyense asagwiritse ntchito malowo popereka mwana wake wamwamuna kapena wamkazi pa moto kwa Moleki.
וישבת את הסוסים אשר נתנו מלכי יהודה לשמש מבא בית יהוה אל לשכת נתן מלך הסריס אשר בפרורים ואת מרכבות השמש שרף באש | 11 |
Anachotsa pa chipata cholowera ku Nyumba ya Yehova akavalo amene mafumu a Yuda anawapereka ngati nsembe kwa dzuwa. Akavalo anali pafupi ndi bwalo la chipinda cha mkulu wina wotchedwa Natani-Meleki. Ndipo Yosiya anatentha magaleta opembedzera dzuwa.
ואת המזבחות אשר על הגג עלית אחז אשר עשו מלכי יהודה ואת המזבחות אשר עשה מנשה בשתי חצרות בית יהוה--נתץ המלך וירץ משם והשליך את עפרם אל נחל קדרון | 12 |
Anagwetsa maguwa amene mafumu a Yuda anawamanga pa denga pafupi ndi chipinda chapamwamba cha Ahazi, ndiponso maguwa amene Manase anamanga mʼmabwalo awiri a Nyumba ya Yehova. Yosiya anawachotsa kumeneko nawaphwanya ndi kutaya zidutswa zake mʼChigwa cha Kidroni.
ואת הבמות אשר על פני ירושלם אשר מימין להר המשחית אשר בנה שלמה מלך ישראל לעשתרת שקץ צידנים ולכמוש שקץ מואב ולמלכם תועבת בני עמון--טמא המלך | 13 |
Mfumuyo inawononga malo opembedzera mafano amene ali kummawa kwa Yerusalemu cha kumpoto kwa Phiri la Chiwonongeko. Maguwawa Solomoni mfumu ya Israeli inamangira Asitoreti, fano lalikazi lonyansa la Asidoni, Kemosi, fano lonyansa la Amowabu, ndi Moleki, fano lonyansa la anthu a ku Amoni.
ושבר את המצבות ויכרת את האשרים וימלא את מקומם עצמות אדם | 14 |
Yosiya anaphwanya miyala ya chipembedzo ndiponso anadula mitengo ya fano la Asera ndipo anakwirira malowo ndi mafupa a anthu.
וגם את המזבח אשר בבית אל הבמה אשר עשה ירבעם בן נבט אשר החטיא את ישראל--גם את המזבח ההוא ואת הבמה נתץ וישרף את הבמה הדק לעפר ושרף אשרה | 15 |
Ngakhalenso guwa lansembe la ku Beteli, malo opembedzera mafano amene anapanga Yeroboamu mwana wa Nebati, amene anachimwitsa Israeli, Yosiya anawononga guwalo ndi malo opembedzera mafanowo. Iye anatentha malo opembedzera mafanowo ndi kuwapera ndipo anatenthanso fano la Asera.
ויפן יאשיהו וירא את הקברים אשר שם בהר וישלח ויקח את העצמות מן הקברים וישרף על המזבח ויטמאהו--כדבר יהוה אשר קרא איש האלהים אשר קרא את הדברים האלה | 16 |
Kenaka Yosiya anayangʼanayangʼana ndipo ataona manda amene anali pomwepo, mʼmbali mwa phiri, analamula kuti afukule mandawo ndi kutulutsa mafupa kuti awatenthe paguwapo kuti alidetse, potsatira mawu a Yehova amene munthu wa Mulungu analoseratu za zimenezi.
ויאמר--מה הציון הלז אשר אני ראה ויאמרו אליו אנשי העיר הקבר איש האלהים אשר בא מיהודה ויקרא את הדברים האלה אשר עשית על המזבח בית אל | 17 |
Mfumu inafunsa kuti, “Kodi chizindikiro cha manda chimene ndikuwaonawo ndi chayani?” Anthu a mu mzindamo anayankha kuti, “Ndi chizindikiro cha manda a munthu wa Mulungu wochokera ku Yuda amene ananeneratu zimene inu mwalichita guwa lansembe la Beteli.”
ויאמר הניחו לו איש אל ינע עצמותיו וימלטו עצמותיו--את עצמות הנביא אשר בא משמרון | 18 |
Mfumuyo inati, “Alekeni manda amenewo, munthu asachotse mafupa ake.” Choncho anawasiya mafupa akewo pamodzi ndi mafupa a mneneri wa ku Samariya uja.
וגם את כל בתי הבמות אשר בערי שמרון אשר עשו מלכי ישראל להכעיס--הסיר יאשיהו ויעש להם--ככל המעשים אשר עשה בבית אל | 19 |
Monga momwe Yosiya anachitira ku Beteli, anachotsa ndi kuwononga nyumba za milungu zonse ndi malo opembedzera mafano amene mafumu anamanga mʼmizinda ya ku Samariya omwe anakwiyitsa Yehova.
ויזבח את כל כהני הבמות אשר שם על המזבחות וישרף את עצמות אדם עליהם וישב ירושלם | 20 |
Yosiya anapha ansembe onse amene ankatumikira ku malo opembedzera mafano, anawaphera pa maguwa awo ndi kutentha mafupa awo. Kenaka iye anapita ku Yerusalemu.
ויצו המלך את כל העם לאמר עשו פסח ליהוה אלהיכם--ככתוב על ספר הברית הזה | 21 |
Mfumu inalamula anthu onse kuti, “Chitani Chikondwerero cha Paska kulemekeza Yehova Mulungu wanu, motsatira zomwe zalembedwa mʼBuku la Chipangano.”
כי לא נעשה כפסח הזה מימי השפטים אשר שפטו את ישראל וכל ימי מלכי ישראל--ומלכי יהודה | 22 |
Paska yotere inali isanachitikepo kuyambira nthawi ya oweruza amene anatsogolera Israeli, kapenanso nthawi yonse ya mafumu a Yuda sipanachitikenso Paska ngati imeneyo.
כי אם בשמנה עשרה שנה למלך יאשיהו נעשה הפסח הזה ליהוה--בירושלם | 23 |
Koma mʼchaka cha 18 cha Mfumu Yosiya, Paska imeneyi anachitira Yehova mu Yerusalemu.
וגם את האבות ואת הידענים ואת התרפים ואת הגללים ואת כל השקצים אשר נראו בארץ יהודה ובירושלם--בער יאשיהו למען הקים את דברי התורה הכתבים על הספר אשר מצא חלקיהו הכהן בית יהוה | 24 |
Kuwonjezera apa, Yosiya anachotsa anthu a mawula, woyankhula ndi mizimu ya anthu akufa, milungu ya mʼnyumba, mafano ndiponso zinthu zonse zonyansa zopezeka mu Yuda ndi Yerusalemu. Iye anachita izi pokwaniritsa lamulo lolembedwa mʼbuku limene Hilikiya analipeza mʼNyumba ya Yehova.
וכמהו לא היה לפניו מלך אשר שב אל יהוה בכל לבבו ובכל נפשו ובכל מאדו--ככל תורת משה ואחריו לא קם כמהו | 25 |
Yosiyayo asanalowe ufumu, ngakhale atamwalira, panalibenso mfumu ina yofanana naye imene inatembenukira kwa Yehova monga anachitira, ndi mtima wake wonse, ndi moyo wake wonse, ndi mphamvu zake zonse, motsatira Malamulo onse a Mose.
אך לא שב יהוה מחרון אפו הגדול אשר חרה אפו ביהודה--על כל הכעסים אשר הכעיסו מנשה | 26 |
Komabe Yehova sanachotse mkwiyo wake woopsa, umene anali nawo pa Yuda chifukwa cha zonse zimene anachita Manase poputa mkwiyo wa Mulungu.
ויאמר יהוה גם את יהודה אסיר מעל פני כאשר הסרתי את ישראל ומאסתי את העיר הזאת אשר בחרתי את ירושלם ואת הבית אשר אמרתי יהיה שמי שם | 27 |
Choncho Yehova anati, “Ndidzawachotsanso anthu a ku Yuda pamaso panga monga ndinachotsera anthu a ku Israeli ndipo ndidzawukana mzinda wa Yerusalemu, mzinda umene ndinawusankha, pamodzi ndi Nyumba ino imene ndinati, ‘Dzina langa lidzakhala mʼmenemo.’”
ויתר דברי יאשיהו וכל אשר עשה הלא הם כתובים על ספר דברי הימים--למלכי יהודה | 28 |
Ntchito zina za Yosiya ndi zonse zimene anachita, kodi sizinalembedwe mʼbuku la mbiri ya mafumu a Yuda?
בימיו עלה פרעה נכה מלך מצרים על מלך אשור--על נהר פרת וילך המלך יאשיהו לקראתו וימיתהו במגדו כראתו אתו | 29 |
Yosiya akanali mfumu, Farao wotchedwa Neko, mfumu ya Igupto, anapita ku Mtsinje wa Yufurate kukathandiza mfumu ya ku Asiriya. Mfumu Yosiya anapita kukachita naye nkhondo, koma Neko anakumana naye ndi kumupha ku Megido.
וירכבהו עבדיו מת ממגדו ויבאהו ירושלם ויקברהו בקברתו ויקח עם הארץ את יהואחז בן יאשיהו וימשחו אתו וימליכו אתו תחת אביו | 30 |
Atumiki a Yosiyayo ananyamula mtembo wake mu galeta kuchokera ku Megido mpaka ku Yerusalemu ndipo anamuyika mʼmanda akeake. Ndipo anthu a mʼdzikomo anatenga Yehowahazi mwana wa Yosiya namudzoza, ndipo iye analowa ufumu mʼmalo mwa abambo ake.
בן עשרים ושלש שנה יהואחז במלכו ושלשה חדשים מלך בירושלם ושם אמו חמוטל בת ירמיהו מלבנה | 31 |
Yehowahazi anakhala mfumu ali ndi 23 ndipo analamulira mu Yerusalemu miyezi itatu. Amayi ake anali Hamutali, mwana wa Yeremiya wa ku Libina.
ויעש הרע בעיני יהוה ככל אשר עשו אבתיו | 32 |
Iye anachita zoyipa pamaso pa Yehova monga momwe anachitira makolo ake.
ויאסרהו פרעה נכה ברבלה בארץ חמת במלך (ממלך) בירושלם ויתן ענש על הארץ מאה ככר כסף וככר זהב | 33 |
Farao Neko anamuyika mʼndende ku Ribula mʼdziko la Hamati kuti asalamulirenso mu Yerusalemu. Farao analamula Yuda kuti azikhoma msonkho wa siliva wolemera makilogalamu 3,400, ndiponso golide wolemera makilogalamu 34.
וימלך פרעה נכה את אליקים בן יאשיהו תחת יאשיהו אביו ויסב את שמו יהויקים ואת יהואחז לקח ויבא מצרים וימת שם | 34 |
Farao Neko anayika Eliyakimu mwana wa Yosiya kuti akhale mfumu mʼmalo mwa abambo ake Yosiya, ndipo anasintha dzina lake kukhala Yehoyakimu. Koma iye anatenga Yehowahazi kupita naye ku Igupto ndipo anakafera kumeneko.
והכסף והזהב נתן יהויקים לפרעה--אך העריך את הארץ לתת את הכסף על פי פרעה איש כערכו נגש את הכסף ואת הזהב את עם הארץ לתת לפרעה נכה | 35 |
Yehoyakimu anapereka kwa Farao Neko siliva ndi golide amene anamufuna uja. Koma kuti iye apereke zimenezi, amankhometsa msonkho mʼdziko mwakemo ndipo amalandira siliva ndi golide kuchokera kwa anthu a mʼdzikomo molingana ndi chuma cha munthu aliyense.
בן עשרים וחמש שנה יהויקים במלכו ואחת עשרה שנה מלך בירושלם ושם אמו זבידה (זבודה) בת פדיה מן רומה | 36 |
Yehoyakimu anali wa zaka 25 pamene anakhala mfumu ndipo analamulira mu Yerusalemu zaka 11. Amayi ake anali Zebuda, mwana wa Pedaya wa ku Ruma.
ויעש הרע בעיני יהוה ככל אשר עשו אבתיו | 37 |
Iye anachita zoyipa pamaso pa Yehova monga momwe anachitira makolo ake.