< מלכים ב 16 >
בשנת שבע עשרה שנה לפקח בן רמליהו מלך אחז בן יותם מלך יהודה | 1 |
Mʼchaka cha 17 cha Peka mwana wa Remaliya, Ahazi mwana wa Yotamu mfumu ya Yuda anayamba kulamulira.
בן עשרים שנה אחז במלכו ושש עשרה שנה מלך בירושלם ולא עשה הישר בעיני יהוה אלהיו--כדוד אביו | 2 |
Ahazi anakhala mfumu ali ndi zaka makumi awiri ndipo analamulira mu Yerusalemu zaka 16. Iye sanachite zabwino pamaso pa Yehova Mulungu wake monga momwe Davide kholo lake ankachitira.
וילך בדרך מלכי ישראל וגם את בנו העביר באש כתעבות הגוים אשר הוריש יהוה אתם מפני בני ישראל | 3 |
Iye anayenda mʼnjira ya mafumu a Israeli mpaka kupereka mwana wake wamwamuna pa moto ngati nsembe yopsereza, potsatira zonyansa za anthu a mitundu imene Yehova anayipirikitsa mʼdzikomo Aisraeli asanafike.
ויזבח ויקטר בבמות ועל הגבעות ותחת כל עץ רענן | 4 |
Iyeyo ankapereka nsembe ndi kufukiza lubani pa malo opembedzera mafano, pa mapiri ndi pansi pa mtengo uliwonse wa masamba ambiri.
אז יעלה רצין מלך ארם ופקח בן רמליהו מלך ישראל ירושלם--למלחמה ויצרו על אחז ולא יכלו להלחם | 5 |
Ndipo Rezini mfumu ya Aramu ndi Peka mwana wa Remaliya mfumu ya Israeli anapita kukachita naye nkhondo ku Yerusalemu ndipo anazinga Ahazi, koma sanathe kumugonjetsa.
בעת ההיא השיב רצין מלך ארם את אילת לארם וינשל את היהודים מאילות וארמים (ואדמים) באו אילת וישבו שם עד היום הזה | 6 |
Nthawi imeneyo Rezini mfumu ya Aramu anatenganso Elati ndi kumubwezera kwa Aaramu, nathamangitsa anthu a ku Yuda mu Elatimo. Aedomu anapita kukakhala ku Elati ndipo akukhalako mpaka lero lino.
וישלח אחז מלאכים אל תגלת פלסר מלך אשור לאמר עבדך ובנך אני עלה והושעני מכף מלך ארם ומכף מלך ישראל הקומים עלי | 7 |
Ahazi anatuma amithenga kwa Tigilati-Pileseri mfumu ya ku Asiriya kuti, “Ine ndine mtumiki wanu ndipo ndili pansi panu. Bwerani mudzandipulumutse mʼdzanja la mfumu ya Aramu ndiponso mʼdzanja la mfumu ya Israeli amene akundithira nkhondo.”
ויקח אחז את הכסף ואת הזהב הנמצא בית יהוה ובאצרות בית המלך וישלח למלך אשור שחד | 8 |
Ndipo Ahazi anatenga siliva ndi golide amene anamupeza mʼNyumba ya Yehova ndi mosungira chuma cha nyumba ya mfumu ndi kutumiza ngati mphatso kwa mfumu ya ku Asiriya.
וישמע אליו מלך אשור ויעל מלך אשור אל דמשק ויתפשה ויגלה קירה ואת רצין המית | 9 |
Mfumu ya ku Asiriya inamvera pokathira nkhondo mzinda wa Damasiko ndi kuwulanda. Anthu a mu mzindamo anawatumiza ku Kiri ndipo anapha Rezini.
וילך המלך אחז לקראת תגלת פלאסר מלך אשור דומשק וירא את המזבח אשר בדמשק וישלח המלך אחז אל אוריה הכהן את דמות המזבח ואת תבניתו--לכל מעשהו | 10 |
Kenaka mfumu Ahazi inapita ku Damasiko kukakumana ndi Tigilati-Pileseri mfumu ya ku Asiriya. Iye anaona guwa lansembe ku Damasiko kuja ndipo anatumiza chitsanzo chake kwa wansembe Uriya, osasiyapo nʼkanthu komwe kuti athe kulimanga.
ויבן אוריה הכהן את המזבח ככל אשר שלח המלך אחז מדמשק כן עשה אוריה הכהן עד בוא המלך אחז מדמשק | 11 |
Choncho wansembe Uriya anamanga guwa lansembe molingana ndi chitsanzo chimene anamutumizira Mfumu Ahazi kuchokera ku Damasiko ndipo anatsiriza kumanga guwalo Ahazi asabwere kuchokera ku Damasiko kuja.
ויבא המלך מדמשק וירא המלך את המזבח ויקרב המלך על המזבח ויעל עליו | 12 |
Mfumu itabwera kuchokera ku Damasiko kuja ndi kuona guwalo, inasendera pafupi ndi kupereka nsembe paguwapo.
ויקטר את עלתו ואת מנחתו ויסך את נסכו ויזרק את דם השלמים אשר לו על המזבח | 13 |
Mfumu inapereka nsembe yopsereza ndi nsembe ya chakudya. Inapereka nsembe yachakumwa ndi kuwaza magazi a nsembe yake yachiyanjano paguwapo.
ואת המזבח הנחשת אשר לפני יהוה ויקרב מאת פני הבית מבין המזבח ומבין בית יהוה ויתן אתו על ירך המזבח צפונה | 14 |
Guwa lamkuwa limene linali pamaso pa Yehova analichotsa kutsogolo kwa nyumbayo, kulichotsa pakati pa guwa latsopano ndi Nyumba ya Yehova ndi kukaliyika cha kumpoto kwa guwa latsopanolo.
ויצוהו (ויצוה) המלך אחז את אוריה הכהן לאמר על המזבח הגדול הקטר את עלת הבקר ואת מנחת הערב ואת עלת המלך ואת מנחתו ואת עלת כל עם הארץ ומנחתם ונסכיהם וכל דם עלה וכל דם זבח עליו תזרק ומזבח הנחשת יהיה לי לבקר | 15 |
Pamenepo Mfumu Ahazi inalamula wansembe Uriya kuti, “Pa guwa lalikulu latsopano uziperekapo nsembe yopsereza ya mmawa ndi nsembe ya chakudya ya madzulo, nsembe yopsereza ya mfumu ndi nsembe yake ya chakudya ndiponso nsembe za anthu onse a mʼdziko, za chakudya ndi chakumwa. Pa guwali uziwazapo magazi a nsembe zonse zopsereza ndi nsembe zina zonse. Koma ine ndizigwiritsa ntchito guwa lansembe lamkuwa pofuna kufunsira nzeru.”
ויעש אוריה הכהן ככל אשר צוה המלך אחז | 16 |
Ndipo wansembe Uriya anachita monga analamulira Mfumu Ahazi.
ויקצץ המלך אחז את המסגרות המכונת ויסר מעליהם ואת (את) הכיר ואת הים הורד מעל הבקר הנחשת אשר תחתיה ויתן אתו על מרצפת אבנים | 17 |
Mfumu Ahazi anachotsa maferemu a maphaka nachotsapo mabeseni. Iye anatsitsa mbiya yayikulu imene inali pamwamba pa ngʼombe zamkuwa ndipo anayika pansi pa chiwundo cha miyala.
ואת מיסך (מוסך) השבת אשר בנו בבית ואת מבוא המלך החיצונה--הסב בית יהוה מפני מלך אשור | 18 |
Iye anachotsa kadenga ka pa Sabata kamene kanamangidwa mʼkati mwa Nyumba ya Yehova ndiponso anatseka chipata cholowera mfumu cha kunja kwa nyumba ya Yehova pofuna kukondweretsa mfumu ya ku Asiriya.
ויתר דברי אחז אשר עשה הלא הם כתובים על ספר דברי הימים--למלכי יהודה | 19 |
Ntchito zina za Ahazi ndi zonse zimene anachita, kodi sizinalembedwe mʼbuku la mbiri ya mafumu a Yuda?
וישכב אחז עם אבתיו ויקבר עם אבתיו בעיר דוד וימלך חזקיהו בנו תחתיו | 20 |
Ahazi anamwalira ndipo anayikidwa mʼmanda pamodzi ndi makolo ake mu Mzinda wa Davide. Ndipo Hezekiya mwana wake analowa ufumu mʼmalo mwake.