< דברי הימים ב 9 >
ומלכת שבא שמעה את שמע שלמה ותבוא לנסות את שלמה בחידות בירושלם בחיל כבד מאד וגמלים נשאים בשמים וזהב לרב ואבן יקרה ותבוא אל שלמה ותדבר עמו את כל אשר היה עם לבבה | 1 |
Mfumu yayikazi ya ku Seba itamva za kutchuka kwa Solomoni, inabwera mu Yerusalemu kudzamuyesa ndi mafunso okhwima. Inafika ndi gulu lalikulu la ngamira zonyamula zokometsera zakudya, golide wambiri, ndi miyala yokongola. Inafika kwa Solomoni ndipo inayankhula naye zonse zimene zinali mu mtima mwake.
ויגד לה שלמה את כל דבריה ולא נעלם דבר משלמה אשר לא הגיד לה | 2 |
Solomoni anayankha mafunso ake onse ndipo panalibe kanthu kalikonse kovuta kwa iye komwe sanathe kufotokozera mfumu yayikaziyo.
ותרא מלכת שבא את חכמת שלמה--והבית אשר בנה | 3 |
Mfumu yayikazi ya ku Seba itaona nzeru za Solomoni komanso nyumba yaufumu imene anamanga,
ומאכל שלחנו ומושב עבדיו ומעמד משרתיו ומלבושיהם ומשקיו ומלבושיהם ועליתו אשר יעלה בית יהוה ולא היה עוד בה רוח | 4 |
chakudya cha pa tebulo pake, moyo wa antchito ake ndi zovala zawo; atumiki opereka zakumwa ndi zovala zawo ndiponso nsembe zopsereza zimene ankapereka ku Nyumba ya Yehova, inathedwa nzeru.
ותאמר אל המלך אמת הדבר אשר שמעתי בארצי--על דבריך ועל חכמתך | 5 |
Iyo inati kwa mfumu, “Mbiri imene ndinamva ndili ku dziko kwathu, ya zomwe munachita komanso nzeru zanu ndi yoona.
ולא האמנתי לדבריהם עד אשר באתי ותראינה עיני והנה לא הגד לי חצי מרבית חכמתך יספת על השמועה אשר שמעתי | 6 |
Koma sindinakhulupirire zimene ankanena mpaka nditafika ndi kuona ndi maso anga. Kunena zoona sanandiwuze ngakhale theka lomwe la kuchuluka kwa nzeru zanu, pakuti zaposa zimene ndinamva.
אשרי אנשיך ואשרי עבדיך אלה--העמדים לפניך תמיד ושמעים את חכמתך | 7 |
Ngodala anthu anu! Ngodala atumiki anu amene amayimirira pamaso panu nthawi zonse ndi kumamva nzeru zanu!
יהי יהוה אלהיך ברוך אשר חפץ בך לתתך על כסאו למלך ליהוה אלהיך באהבת אלהיך את ישראל להעמידו לעולם ויתנך עליהם למלך לעשות משפט וצדקה | 8 |
Atamandike Yehova Mulungu wanu amene wakondwera nanu nakukhazikani pa mpando wake waufumu kuti mulamulire mʼmalo mwa Yehova Mulungu wanu. Chifukwa cha chikondi cha Mulungu wanu pa Israeli, ndi khumbo lake kuti akusungeni mpaka muyaya, Iye wayika inu kukhala mfumu yawo kuti mulamulire moyenera ndi mwachilungamo.”
ותתן למלך מאה ועשרים ככר זהב ובשמים לרב מאד--ואבן יקרה ולא היה כבשם ההוא אשר נתנה מלכת שבא למלך שלמה | 9 |
Kenaka iyo inapereka kwa mfumu makilogalamu 4,000 a golide, zonunkhira zambirimbiri ndi miyala yokongola. Nʼkale lomwe sikunaonekenso zonunkhiritsa ngati zomwe mfumu yayikazi ya ku Seba inapereka kwa mfumu Solomoni.
וגם עבדי חירם (חורם) ועבדי שלמה אשר הביאו זהב מאופיר--הביאו עצי אלגומים ואבן יקרה | 10 |
(Anthu a Hiramu ndi anthu a Solomoni anabweretsa golide kuchokera ku Ofiri ndipo anabweretsanso mitengo ya mʼbawa ndi miyala yokongola.
ויעש המלך את עצי האלגומים מסלות לבית יהוה ולבית המלך וכנרות ונבלים לשרים ולא נראו כהם לפנים בארץ יהודה | 11 |
Mfumu inagwiritsa ntchito mitengo ya mʼbawa pokonzera makwerero a Nyumba ya Yehova ndi nyumba yaufumu ndiponso kupangira anthu oyimba apangwe ndi azeze. Zinthu zonga zimenezi sizinaonekeponso mu Yuda).
והמלך שלמה נתן למלכת שבא את כל חפצה אשר שאלה מלבד אשר הביאה אל המלך ותהפך ותלך לארצה היא ועבדיה | 12 |
Mfumu Solomoni inapereka kwa mfumu yayikazi ya ku Seba zonse zimene inazifuna ndi kuzipempha ndipo Solomoni anayipatsa mfumuyo zoposa zimene iyo inabweretsa kwa Solomoni. Ndipo mfumuyo inabwerera ku dziko lake pamodzi ndi atumiki ake.
ויהי משקל הזהב אשר בא לשלמה בשנה אחת--שש מאות וששים ושש ככרי זהב | 13 |
Kulemera kwa golide amene Solomoni amalandira pa chaka kunali makilogalamu 23,000,
לבד מאנשי התרים והסחרים מביאים וכל מלכי ערב ופחות הארץ מביאים זהב וכסף לשלמה | 14 |
osawerengera amene ankabwera ndi anthu ochita malonda ndi osinthanitsa zinthu. Komanso mafumu onse a ku Arabiya ndi abwanamkubwa a mʼdzikomo amabweretsa golide ndi siliva kwa Solomoni.
ויעש המלך שלמה מאתים צנה זהב שחוט שש מאות זהב שחוט יעלה על הצנה האחת | 15 |
Mfumu Solomoni inapanga zishango zazikulu 200 zagolide wosasantha. Mʼchishango chilichonse mumalowa golide wolemera makilogalamu asanu ndi awiri.
ושלש מאות מגנים זהב שחוט--שלש מאות זהב יעלה על המגן האחת ויתנם המלך בבית יער הלבנון | 16 |
Iye anapanganso zishango zingʼonozingʼono 300 zagolide wosasantha ndipo chishango chilichonse chimapangidwa ndi golide wolemera makilogalamu atatu. Mfumu inayika zishangozi mʼnyumba yaufumu yotchedwa Nkhalango ya Lebanoni.
ויעש המלך כסא שן גדול ויצפהו זהב טהור | 17 |
Ndipo mfumu inapanganso mpando waukulu waufumu wa nyanga za njovu ndipo unakutidwa ndi golide woyengeka bwino.
ושש מעלות לכסא וכבש בזהב לכסא מאחזים וידות מזה ומזה על מקום השבת ושנים אריות עמדים אצל הידות | 18 |
Mpando waufumuwo unali ndi makwerero asanu ndi limodzi ndi choyikapo mapazi cholumikizidwa ku mpandowo. Mʼmbali zonse za mpandowo munali zosanjikapo manja, ndi chifanizo cha mkango chitayima posanjikapo manjapo.
ושנים עשר אריות עמדים שם על שש המעלות--מזה ומזה לא נעשה כן לכל ממלכה | 19 |
Mikango khumi ndi iwiri inayimirira pa makwerero asanu ndi imodzi aja. Umodzi mbali ina ya khwerero ndi wina mbali inayo. Palibe mpando wonga uwu umene unapangidwapo mu ufumu wina uliwonse.
וכל כלי משקה המלך שלמה זהב וכל כלי בית יער הלבנון זהב סגור אין כסף נחשב בימי שלמה--למאומה | 20 |
Zikho zonse za mfumu Solomoni zinali zagolide, ndiponso zipangizo zonse za ku nyumba yaufumu ya Nkhalango ya Lebanoni zinali zagolide oyengeka bwino. Panalibe chinthu chopangidwa ndi siliva, chifukwa siliva samayesedwa kanthu mʼnthawi ya Solomoni.
כי אניות למלך הלכות תרשיש עם עבדי חורם אחת לשלוש שנים תבואנה אניות תרשיש נשאות זהב וכסף שנהבים וקופים ותוכיים | 21 |
Mfumu inali ndi sitima zambiri zapamadzi zimene zimayendetsedwa ndi antchito a Hiramu. Zimabwera kamodzi pa zaka zitatu zilizonse zitanyamula golide, siliva ndi nyanga za njovu, ndiponso anyani ndi apusi.
ויגדל המלך שלמה מכל מלכי הארץ--לעשר וחכמה | 22 |
Mfumu Solomoni anapambana mafumu ena onse a dziko lapansi pa chuma ndi nzeru.
וכל מלכי הארץ מבקשים את פני שלמה--לשמע את חכמתו אשר נתן האלהים בלבו | 23 |
Mafumu onse a dziko lapansi ankafunafuna kuonana ndi Solomoni kuti adzamve nzeru zimene Mulungu anayika mu mtima mwake.
והם מביאים איש מנחתו כלי כסף וכלי זהב ושלמות נשק ובשמים סוסים ופרדים--דבר שנה בשנה | 24 |
Chaka ndi chaka, aliyense amene amabwera, amabweretsa mphatso monga zipangizo zasiliva ndi golide, mikanjo, zida zankhondo ndi zokometsera zakudya komanso akavalo ndi abulu.
ויהי לשלמה ארבעת אלפים אריות סוסים ומרכבות ושנים עשר אלף פרשים ויניחם בערי הרכב ועם המלך בירושלם | 25 |
Solomoni anali ndi zipinda 4,000 zodyeramo akavalo ndi magaleta, ndi akavalo 12,000 amene amawasunga mʼmizinda yosungira magaleta ndiponso ena anali ndi iye ku Yerusalemu.
ויהי מושל בכל המלכים--מן הנהר ועד ארץ פלשתים ועד גבול מצרים | 26 |
Iye ankalamulira mafumu onse kuyambira ku mtsinje wa Yufurate mpaka ku dziko la Afilisti, kukafika ku malire a dziko la Igupto.
ויתן המלך את הכסף בירושלם כאבנים ואת הארזים נתן כשקמים אשר בשפלה--לרב | 27 |
Mfumu inasandutsa siliva kukhala wambiri ngati miyala wamba mu Yerusalemu ndipo mikungudza kukhala yochuluka ngati mitengo ya mkuyu ya ku zigwa.
ומוציאים סוסים ממצרים לשלמה ומכל הארצות | 28 |
Solomoni ankayitanitsa akavalo ake kuchokera ku Igupto ndi mayiko ena onse.
ושאר דברי שלמה הראשנים והאחרונים--הלא הם כתובים על דברי נתן הנביא ועל נבואת אחיה השילוני ובחזות יעדי (יעדו) החזה על ירבעם בן נבט | 29 |
Tsono ntchito zina zonse za Solomoni, kuyambira pachiyambi mpaka kumaliza, kodi sizinalembedwa mʼbuku la mbiri la mneneri Natani, ndi mʼbuku la uneneri wa Ahiya wa ku Silo ndi mʼbuku la masomphenya a mlosi Ido, lokamba za Yeroboamu mwana wa Nebati?
וימלך שלמה בירושלם על כל ישראל ארבעים שנה | 30 |
Solomoni analamulira Aisraeli onse ku Yerusalemu zaka makumi anayi.
וישכב שלמה עם אבתיו ויקברהו בעיר דויד אביו וימלך רחבעם בנו תחתיו | 31 |
Ndipo anamwalira nagona ndi makolo ake. Anayikidwa mʼmanda mu mzinda wa Davide abambo ake. Ndipo Rehobowamu, mwana wake, analowa ufumu mʼmalo mwake.