< דברי הימים ב 4 >

ויעש מזבח נחשת--עשרים אמה ארכו ועשרים אמה רחבו ועשר אמות קומתו 1
Solomoni anapanga guwa lamkuwa limene mulitali mwake linali mamita asanu ndi anayi, mulifupi mwakenso mamita asanu ndi anayi ndipo msinkhu wake unali mamita anayi ndi theka.
ויעש את הים מוצק עשר באמה משפתו אל שפתו עגול סביב וחמש באמה קומתו וקו שלשים באמה יסב אתו סביב 2
Kenaka iye anapanga mbiya yayikulu yachitsulo. Inali yozungulira ndipo pakamwa pake panali pa mamita anayi ndi theka, poyeza modutsa pakati pake. Msinkhu wake unali wopitirirapo mamita awiri. Thunthu lake linali mamita 13.
ודמות בקרים תחת לו סביב סביב סובבים אתו עשר באמה מקיפים את הים סביב שנים טורים הבקר יצוקים במצקתו 3
Mʼmunsi mwa mkombero wa mbiyayo anajambulamo zithunzi zangʼombe zazimuna mozungulira, zithunzi khumi pa theka la mita. Ngʼombezo zimajambulidwa mʼmizere iwiri ndipo anazipangira kumodzi ndi mbiyayo.
עומד על שנים עשר בקר שלשה פנים צפונה ושלושה פנים ימה ושלשה פנים נגבה ושלשה פנים מזרחה והים עליהם מלמעלה וכל אחריהם ביתה 4
Mbiyayo anayisanjika pa ngʼombe zamkuwa khumi ndi ziwiri, zitatu zoyangʼana kumpoto, zitatu zoyangʼana kumadzulo, zitatu zoyangʼana kummwera ndipo zitatu zoyangʼana kummawa. Mbiyayo inakhazikika pamwamba pa ngʼombezo, ndipo miyendo yake yonse yakumbuyo ya ngʼombezo inkaloza mʼkati.
ועביו טפח--ושפתו כמעשה שפת כוס פרח שושנה מחזיק בתים שלשת אלפים יכיל 5
Mbiyayo inali yochindikala ngati chikhatho ndipo mkombero wake unali ngati mkombero wa chikho, ngati duwa lokongola kwambiri. Mʼmbiyamo munkalowa madzi okwana malita 60,000.
ויעש כיורים עשרה ויתן חמשה מימין וחמשה משמאול לרחצה בהם את מעשה העולה ידיחו בם והים לרחצה לכהנים בו 6
Kenaka anapanga mabeseni khumi otsukira zinthu ndipo asanu amawayika mbali ya kummwera, asanu mbali ya kumpoto. Mʼmenemo amatsukiramo zinthu zimene zimagwiritsidwa ntchito pa nsembe zopsereza koma mbiyamo ndi mʼmene ankasambiramo ansembe.
ויעש את מנרות הזהב עשר--כמשפטם ויתן בהיכל חמש מימין וחמש משמאול 7
Solomoni anapanga zoyikapo nyale khumi zagolide monga momwe kunalembedwera ndipo anaziyika mʼNyumba ya Mulungu, zisanu mbali ya kummwera, ndi zisanu mbali ya kumpoto.
ויעש שלחנות עשרה וינח בהיכל חמשה מימין וחמשה משמאול ויעש מזרקי זהב מאה 8
Iye anapanga matebulo khumi ndipo anawayika mʼNyumba ya Mulungu, asanu mbali ya kummwera ndi asanu mbali ya kumpoto. Iye anapanganso mabeseni agolide okwanira 100.
ויעש חצר הכהנים והעזרה הגדולה ודלתות לעזרה ודלתותיהם צפה נחשת 9
Iye anapanga bwalo la ansembe, bwalo lalikulu ndi zitseko za bwalolo ndipo anakuta zitsekozo ndi mkuwa.
ואת הים נתן מכתף הימנית קדמה--ממול נגבה 10
Anayika mbiya ija mbali yakummwera pamene mbali ya kummawa ndi kummwera zimakumana.
ויעש חורם--את הסירות ואת היעים ואת המזרקות ויכל חירם (חורם) לעשות את המלאכה אשר עשה למלך שלמה בבית האלהים 11
Iye anapanganso miphika ndi mafosholo ndi mabeseni owazira magazi. Kotero Hiramu anatsiriza ntchito yonse ya ku Nyumba ya Mulungu imene ankagwirira Mfumu Solomoni:
עמודים שנים והגלות והכתרות על ראש העמודים שתים והשבכות שתים--לכסות את שתי גלות הכתרות אשר על ראש העמודים 12
Nsanamira ziwiri; mbale ziwiri za mitu yapamwamba pa nsanamirazo; maukonde awiri okongoletsera mbale ziwiri za mitu yapamwamba pa nsanamirazo;
ואת הרמונים ארבע מאות לשתי השבכות שנים טורים רמונים לשבכה האחת--לכסות את שתי גלות הכתרות אשר על פני העמודים 13
makangadza 400 a maukonde awiri okongoletserawo (mizere iwiri ya makangadza pa ukonde uliwonse, kukongoletsa mbale za mitu yapamwamba pa nsanamira);
ואת המכנות עשה ואת הכירות עשה על המכנות 14
miyendo pamodzi ndi mabeseni ake;
את הים אחד ואת הבקר שנים עשר תחתיו 15
mbiya pamodzi ndi ngʼombe khumi ndi ziwiri zazimuna zosanjikapo mbiyayo.
ואת הסירות ואת היעים ואת המזלגות ואת כל כליהם עשה חורם אביו למלך שלמה לבית יהוה--נחשת מרוק 16
Miphika, mafosholo, mafoloko otengera nyama ndi ziwiya zina zonse. Zipangizo zonse zimene Hiramu Abi anapangira Mfumu Solomoni za mʼNyumba ya Yehova zinali zamkuwa wonyezimira.
בככר הירדן יצקם המלך בעבי האדמה בין סכות ובין צרדתה 17
Mfumu inapangitsa zimenezi mʼchigwa cha Yorodani, ku malo amtapo amene anali pakati pa Sukoti ndi Zaretani.
ויעש שלמה כל הכלים האלה לרב מאד כי לא נחקר משקל הנחשת 18
Zinthu zonse zimene Solomoni anapanga zinali zochuluka kwambiri kotero kuti kulemera kwa mkuwa sikunadziwike.
ויעש שלמה--את כל הכלים אשר בית האלהים ואת מזבח הזהב ואת השלחנות ועליהם לחם הפנים 19
Solomoni anapanganso ziwiya zonse zimene zinali mʼNyumba ya Mulungu: guwa lansembe lagolide; matebulo pamene ankayikapo buledi woperekedwa kwa Mulungu;
ואת המנרות ונרתיהם לבערם כמשפט לפני הדביר--זהב סגור 20
zoyikapo nyale zagolide ndi nyale zake zagolide weniweni, kuti ziziyaka mʼkati mwenimweni mwa malo opatulika monga analembera,
והפרח והנרות והמלקחים זהב הוא מכלות זהב 21
maluwa agolide, nyale ndi mbaniro. (Zinali zagolide mmodzi);
והמזמרות והמזרקות והכפות והמחתות זהב סגור ופתח הבית דלתותיו הפנימיות לקדש הקדשים ודלתי הבית להיכל--זהב 22
zozimitsira nyale zagolide weniweni, mbale zowazira magazi, mbale ndi zofukizira; ndiponso zitseko zagolide za Nyumba ya Mulungu, chitseko cha ku Malo Opatulika Kwambiri ndi zitseko za ku chipinda chachikulu.

< דברי הימים ב 4 >