< דברי הימים ב 31 >
וככלות כל זאת יצאו כל ישראל הנמצאים לערי יהודה וישברו המצבות ויגדעו האשרים וינתצו את הבמות ואת המזבחות מכל יהודה ובנימן ובאפרים ומנשה עד לכלה וישובו כל בני ישראל איש לאחזתו--לעריהם | 1 |
Zonse zitatha, Aisraeli onse amene anali kumeneko anapita ku mizinda ya ku Yuda, nakaphwanya miyala yachipembedzo ndi kudula mitengo ya mafano a Asera. Iwo anakawononga malo achipembedzo ndi maguwa ansembe amene anali mʼdziko lonse la Yuda, Benjamini, Efereimu ndi Manase. Atawononga zonsezi, Aisraeli anabwerera ku mizinda yawo ndi ku malo awo.
ויעמד יחזקיהו את מחלקות הכהנים והלוים על מחלקותם איש כפי עבדתו לכהנים וללוים לעלה ולשלמים--לשרת ולהדות ולהלל בשערי מחנות יהוה | 2 |
Hezekiya anakhazikitsa magulu a ansembe ndi Alevi, gulu lililonse monga mwa ntchito zawo ngati ansembe kapena Alevi, kupereka nsembe zopsereza ndi nsembe zachiyanjano, kutumikira, kuyamikira ndi kuyimba matamando pa zipata za ku malo okhala Yehova.
ומנת המלך מן רכושו לעלות לעלות הבקר והערב והעלות לשבתות ולחדשים ולמעדים--ככתוב בתורת יהוה | 3 |
Kuchokera pa chuma chake, mfumu inapereka nsembe zopsereza za mmawa ndi madzulo ndiponso nsembe zopsereza za pa Chikondwerero cha Masabata, Chikondwerero cha Mwezi Watsopano ndipo inakhazikitsa zikondwerero monga zinalembedwera mʼmalamulo a Yehova.
ויאמר לעם ליושבי ירושלם לתת מנת הכהנים והלוים--למען יחזקו בתורת יהוה | 4 |
Iyo inalamula anthu amene amakhala mu Yerusalemu kupereka gawo lawo kwa ansembe ndi Alevi kuti iwowo adzipereke ku malamulo a Yehova.
וכפרץ הדבר הרבו בני ישראל ראשית דגן תירוש ויצהר ודבש וכל תבואת שדה ומעשר הכל לרב הביאו | 5 |
Lamuloli atangolilengeza, Aisraeli anapereka mowolowamanja zipatso zoyamba kucha za tirigu, vinyo watsopano, mafuta ndi uchi ndi zonse zomwe nthaka yawo inabereka. Anabweretsa zochuluka kwambiri, chakhumi cha chilichonse.
ובני ישראל ויהודה היושבים בערי יהודה--גם הם מעשר בקר וצאן ומעשר קדשים המקדשים ליהוה אלהיהם הביאו ויתנו ערמות ערמות | 6 |
Aisraeli ndi Ayuda amene amakhala mʼmizinda ya Yuda anabweretsanso chakhumi cha ngʼombe zawo ndi nkhosa ndi chakhumi cha zinthu zoyera zoperekedwa kwa Yehova Mulungu wawo, ndipo anaziyika mʼmilumilu.
בחדש השלשי החלו הערמות ליסוד ובחדש השביעי כלו | 7 |
Anayamba kuchita izi mwezi wachitatu ndipo anatsiriza mwezi wachisanu ndi chiwiri.
ויבאו יחזקיהו והשרים ויראו את הערמות ויברכו את יהוה ואת עמו ישראל | 8 |
Hezekiya ndi akuluakulu ake atabwera ndi kuona miluyo, anatamanda Yehova ndi kudalitsa anthu ake, Aisraeli.
וידרש יחזקיהו על הכהנים והלוים--על הערמות | 9 |
Hezekiya anafunsa ansembe ndi Alevi za miluyi;
ויאמר אליו עזריהו הכהן הראש--לבית צדוק ויאמר מהחל התרומה לביא בית יהוה אכול ושבוע והותר עד לרוב--כי יהוה ברך את עמו והנותר את ההמון הזה | 10 |
ndipo Azariya, mkulu wa ansembe, ochokera ku banja la Zadoki anayankha kuti, “Kuyambira pamene anthu anayamba kubweretsa zopereka zawo ku Nyumba ya Yehova ife takhala ndi zokwanira kudya ndi zina zambiri zosunga, chifukwa Yehova wadalitsa anthu ake, ndipo mulu umenewu ndiye zotsala.”
ויאמר יחזקיהו להכין לשכות בבית יהוה--ויכינו | 11 |
Hezekiya analamula kuti akonze zipinda zosungiramo za mʼNyumba ya Yehova, ndipo izi zinachitika.
ויביאו את התרומה והמעשר והקדשים באמונה ועליהם נגיד כונניהו (כנניהו) הלוי ושמעי אחיהו משנה | 12 |
Ndipo iwo mokhulupirika anabweretsa zopereka, chakhumi ndi mphatso zopatulika. Konaniya Mlevi ndiye amayangʼanira zinthu zimenezi ndipo mʼbale wake Simei ndiye anali wachiwiri wake.
ויחיאל ועזזיהו ונחת ועשהאל וירימות ויוזבד ואליאל ויסמכיהו ומחת ובניהו--פקידים מיד כונניהו (כנניהו) ושמעי אחיו במפקד יחזקיהו המלך ועזריהו נגיד בית האלהים | 13 |
Yehieli, Azaziya, Nahati, Asaheli, Yerimoti, Yozabadi, Elieli, Isimakiya, Mahati ndi Benaya anali oyangʼanira motsogozedwa ndi Konaniya ndi Simei, mʼbale wake. Iwowa anasankhidwa ndi mfumu Hezekiya ndi Azariya mkulu woyangʼanira Nyumba ya Mulungu.
וקורא בן ימנה הלוי השוער למזרחה על נדבות האלהים--לתת תרומת יהוה וקדשי הקדשים | 14 |
Kore mwana wa Imuna Mlevi, mlonda wa Chipata Chakummawa, amayangʼanira zopereka zaufulu kwa Mulungu, ankagawa zopereka za kwa Yehova ndiponso mphatso zopatulika.
ועל ידו עדן ומנימן וישוע ושמעיהו אמריהו ושכניהו בערי הכהנים--באמונה לתת לאחיהם במחלקות כגדול כקטן | 15 |
Edeni, Miniyamini, Yesuwa, Semaya, Amariya, Sekaniya amamuthandiza mokhulupirika mʼmizinda yonse a ansembe kugawira kwa ansembe anzawo monga mwa magulu awo, aakulu ndi aangʼono omwe.
מלבד התיחשם לזכרים מבן שלוש שנים ולמעלה לכל הבא לבית יהוה לדבר יום ביומו--לעבודתם במשמרותם כמחלקותיהם | 16 |
Kuwonjezera apa, amagawira ana aamuna a zaka zitatu kapena kupitirira amene mayina awo anali mʼmbiri ya mibado yawo, amene adzalowe mʼNyumba ya Yehova kugwira ntchito za tsiku ndi tsiku za magulu awo, molingana ndi udindo ndi magulu awo.
ואת התיחש הכהנים לבית אבותיהם והלוים מבן עשרים שנה ולמעלה--במשמרותיהם במחלקותיהם | 17 |
Ndipo anazigawa kwa ansembe amene analembetsa mayina awo mwa mbiri ya mabanja awo, chimodzimodzinso Alevi amene anali ndi zaka makumi awiri kapena kupitirira molingana ndi udindo wawo ndi magulu awo.
ולהתיחש בכל טפם נשיהם ובניהם ובנותיהם--לכל קהל כי באמונתם יתקדשו קדש | 18 |
Iwo anaphatikizanso ana onse aangʼono, akazi ndiponso ana aamuna ndi ana aakazi a gulu lonse amene analembedwa mʼmbiri ya mibado yawo iyi, pakuti anakhulupirika pa kudzipatula okha.
ולבני אהרן הכהנים בשדי מגרש עריהם בכל עיר ועיר אנשים אשר נקבו בשמות--לתת מנות לכל זכר בכהנים ולכל התיחש בלוים | 19 |
Kunena za ansembe, zidzukulu za Aaroni, amene amakhala mʼminda yozungulira mizinda yawo kapena mzinda wina uliwonse, anthu anasankhidwa mowatchula mayina kuti azipereka magawo kwa munthu wamwamuna aliyense pakati pawo ndiponso kwa onse amene analembedwa mʼmbiri ya mibado ya Alevi.
ויעש כזאת יחזקיהו בכל יהודה ויעש הטוב והישר והאמת לפני יהוה אלהיו | 20 |
Izi ndi zimene Hezekiya anachita mu Yuda monse, kuchita zabwino, zolungama ndi zokhulupirika pamaso pa Yehova Mulungu wake.
ובכל מעשה אשר החל בעבודת בית האלהים ובתורה ובמצוה לדרש לאלהיו--בכל לבבו עשה והצליח | 21 |
Pa chilichonse chimene anachita pa ntchito ya Nyumba ya Mulungu ndi pa kumvera malangizo ndi malamulo, iye anafunafuna Mulungu wake ndipo anagwira ntchito ndi mtima wake wonse. Ndipo zinthu zimamuyendera bwino.