< דברי הימים ב 21 >

וישכב יהושפט עם אבתיו ויקבר עם אבתיו בעיר דויד וימלך יהורם בנו תחתיו 1
Yehosafati anamwalira nayikidwa mʼmanda pamodzi ndi makolo ake mu mzinda wa Davide. Ndipo Yehoramu mwana wake analowa ufumu mʼmalo mwake.
ולו אחים בני יהושפט עזריה ויחיאל וזכריהו ועזריהו ומיכאל ושפטיהו כל אלה בני יהושפט מלך ישראל 2
Abale ake a Yehoramu, ana aamuna a Yehosafati, anali Azariya, Yehieli, Zekariya, Azariyahu, Mikayeli ndi Sefatiya. Onsewa anali ana a Yehosafati mfumu ya Israeli.
ויתן להם אביהם מתנות רבות לכסף ולזהב ולמגדנות עם ערי מצרות ביהודה ואת הממלכה נתן ליהורם כי הוא הבכור 3
Abambo awo anawapatsa mphatso zambiri za siliva, golide ndi zinthu zina zamtengowapatali komanso mizinda yotetezedwa ya Yuda. Koma iye anapereka ufumu kwa Yehoramu chifukwa anali mwana wake woyamba kubadwa.
ויקם יהורם על ממלכת אביו ויתחזק ויהרג את כל אחיו בחרב וגם משרי ישראל 4
Yehoramu atakhazikika pa ufumu wa abambo ake, iye anapha abale ake ndi lupanga pamodzi ndi atsogoleri ena a Israeli.
בן שלשים ושתים שנה יהורם במלכו ושמונה שנים מלך בירושלם 5
Yehoramu anali wa zaka 32 pamene anakhala mfumu, ndipo analamulira mu Yerusalemu zaka zisanu ndi zitatu.
וילך בדרך מלכי ישראל כאשר עשו בית אחאב--כי בת אחאב היתה לו אשה ויעש הרע בעיני יהוה 6
Iye anayenda mʼnjira za mafumu a Israeli, monga mmene linachitira banja la Ahabu, pakuti anakwatira mwana wa Ahabu. Ndipo anachita zoyipa pamaso pa Yehova.
ולא אבה יהוה להשחית את בית דויד--למען הברית אשר כרת לדויד וכאשר אמר לתת לו ניר ולבניו--כל הימים 7
Komabe, chifukwa cha pangano limene Yehova anachita ndi Davide, Yehova sanafune kuwononga banja la Davide. Iye analonjeza kusungira nyale Davide ndi zidzukulu zake mpaka muyaya.
בימיו פשע אדום מתחת יד יהודה וימליכו עליהם מלך 8
Pa nthawi ya Yehoramu, Edomu anawukira Yuda ndipo anadzisankhira mfumu.
ויעבר יהורם עם שריו וכל הרכב עמו ויהי קם לילה ויך את אדום הסובב אליו ואת שרי הרכב 9
Choncho Yehoramu anapita kumeneko pamodzi ndi atsogoleri ake ndi magaleta ake onse. Aedomu anamuzungulira pamodzi ndi atsogoleri ake koma iye ananyamuka ndi kuthawa usiku.
ויפשע אדום מתחת יד יהודה עד היום הזה--אז תפשע לבנה בעת ההיא מתחת ידו כי עזב את יהוה אלהי אבתיו 10
Mpaka lero lino Edomu ndi wowukira ulamuliro wa Yuda. Pa nthawi yomweyi, mzinda wa Libina unawukiranso chifukwa Yehoramu anasiya Yehova, Mulungu wa makolo ake.
גם הוא עשה במות בהרי יהודה ויזן את ישבי ירושלם וידח את יהודה 11
Iye anamanganso malo opembedzerapo mafano mʼmapiri a Yuda ndipo anachititsa anthu a mu Yerusalemu kukhala osakhulupirika. Choncho anasocheretsa anthu a ku Yuda.
ויבא אליו מכתב מאליהו הנביא לאמר כה אמר יהוה אלהי דויד אביך--תחת אשר לא הלכת בדרכי יהושפט אביך ובדרכי אסא מלך יהודה 12
Yehoramu analandira kalata yochokera kwa mneneri Eliya yonena kuti, “Yehova Mulungu wa Davide abambo ako akuti, ‘Iwe sunayende mʼnjira ya Yehosafati abambo ako kapena Asa mfumu ya Yuda.
ותלך בדרך מלכי ישראל ותזנה את יהודה ואת ישבי ירושלם כהזנות בית אחאב וגם את אחיך בית אביך הטובים ממך הרגת 13
Koma wayenda mʼnjira za mafumu a Israeli ndipo watsogolera anthu a ku Yuda ndi Yerusalemu kukhala osakhulupirika, monga linachitira banja la Ahabu. Waphanso abale ako, abale a banja la abambo ako, anthu amene anali abwino kuposa iweyo.
הנה יהוה נגף מגפה גדולה--בעמך ובבניך ובנשיך ובכל רכושך 14
Kotero tsono Yehova ali pafupi kukantha anthu ako, ana ako, akazi ako ndi zinthu zako zonse, ndi chilango chachikulu.
ואתה בחליים רבים במחלה מעיך עד יצאו מעיך מן החלי ימים על ימים 15
Ndipo iwe udzadwala nthenda yoopsa yamʼmimba, mpaka nthendayo idzachititsa matumbo ako kutuluka.’”
ויער יהוה על יהורם את רוח הפלשתים והערבים אשר על יד כושים 16
Yehova anamuutsira Yehoramuyo mkwiyo wa Afilisti ndi Aarabu amene amakhala pafupi ndi Akusi.
ויעלו ביהודה ויבקעוה וישבו את כל הרכוש הנמצא לבית המלך וגם בניו ונשיו ולא נשאר לו בן כי אם יהואחז קטן בניו 17
Iwo anathira nkhondo Yuda. Analowanso ndi kutenga katundu yense amene anamupeza mʼnyumba ya mfumu pamodzi ndi ana ake ndi akazi ake. Palibe mwana amene anatsala kupatula mwana wake wamngʼono kwambiri, Ahaziya.
ואחרי כל זאת--נגפו יהוה במעיו לחלי לאין מרפא 18
Izi zonse zitachitika, Yehova anakantha Yehoramu ndi nthenda yamʼmimba imene inali yosachiritsika.
ויהי לימים מימים וכעת צאת הקץ לימים שנים יצאו מעיו עם חליו וימת בתחלאים רעים ולא עשו לו עמו שרפה כשרפת אבתיו 19
Patapita nthawi, kumapeto kwa chaka chachiwiri, matumbo ake anatuluka chifukwa cha nthendayo, ndipo anafa imfa yopweteka kwambiri. Anthu ake sanasonkhe moto kumuchitira ulemu, monga anachitira ndi makolo ake.
בן שלשים ושתים היה במלכו ושמונה שנים מלך בירושלם וילך בלא חמדה ויקברהו בעיר דויד ולא בקברות המלכים 20
Yehoramu anali wa zaka 32 pamene anakhala mfumu. Iyeyo analamulira mu Yerusalemu zaka zisanu ndi zitatu. Ndipo anamwalira popanda odandawula, nayikidwa mʼmanda mu mzinda wa Davide, koma osati mʼmanda a mafumu.

< דברי הימים ב 21 >