< דברי הימים ב 17 >
וימלך יהושפט בנו תחתיו ויתחזק על ישראל | 1 |
Yehosafati mwana wake analowa ufumu mʼmalo mwake ndipo anadzilimbitsa pofuna kulimbana ndi Israeli.
ויתן חיל--בכל ערי יהודה הבצרות ויתן נציבים בארץ יהודה ובערי אפרים אשר לכד אסא אביו | 2 |
Iye anayika magulu a asilikali mʼmizinda yonse yotetezedwa ya Yuda, ndipo anamanga maboma mu Yuda ndi mʼmizinda yonse ya Efereimu imene Asa abambo ake analanda.
ויהי יהוה עם יהושפט כי הלך בדרכי דויד אביו הראשנים ולא דרש לבעלים | 3 |
Yehova anali ndi Yehosafati chifukwa mʼzaka zoyambirira anatsatira makhalidwe a Davide abambo ake. Iye sanafunsire kwa Abaala.
כי לאלהי אביו דרש ובמצותיו הלך ולא כמעשה ישראל | 4 |
Koma anafunafuna Mulungu wa abambo ake ndipo anatsatira malamulo ake osati zochita za Israeli.
ויכן יהוה את הממלכה בידו ויתנו כל יהודה מנחה ליהושפט ויהי לו עשר וכבוד לרב | 5 |
Yehova anakhazikitsa kolimba ufumuwo mʼmanja mwake ndipo Ayuda onse anabweretsa mphatso kwa Yehosafati, kotero kuti anali ndi chuma ndi ulemu wambiri.
ויגבה לבו בדרכי יהוה ועוד הסיר את הבמות ואת האשרים--מיהודה | 6 |
Mtima wake anawupereka kutsatira Yehova, kuwonjezera apo, anachotsa malo onse achipembedzo ndi mafano a Asera mu Yuda.
ובשנת שלוש למלכו שלח לשריו לבן חיל ולעבדיה ולזכריה ולנתנאל ולמיכיהו--ללמד בערי יהודה | 7 |
Mʼchaka chachitatu cha ufumu wake, iye anatuma akuluakulu ake Beni-Haili, Obadiya, Zekariya, Netaneli ndi Mikaya kukaphunzitsa mʼmizinda ya Yuda.
ועמהם הלוים שמעיהו ונתניהו וזבדיהו ועשהאל ושמרימות (ושמירמות) ויהונתן ואדניהו וטוביהו וטוב אדוניה--הלוים ועמהם אלישמע ויהורם הכהנים | 8 |
Pamodzi ndi iwo panali Alevi ena: Semaya, Netaniya, Zebadiya, Asaheli, Semiramoti, Yonatani, Adoniya, Tobiya ndi Tobu-Adoniya ndiponso ansembe Elisama ndi Yehoramu.
וילמדו ביהודה ועמהם ספר תורת יהוה ויסבו בכל ערי יהודה וילמדו בעם | 9 |
Iwo anaphunzitsa mu Yuda monse atatenga Buku la Malamulo a Yehova iwo anayenda mʼmizinda yonse ya ku Yuda ndipo anaphunzitsa anthu.
ויהי פחד יהוה על כל ממלכות הארצות אשר סביבות יהודה ולא נלחמו עם יהושפט | 10 |
Kuopsa kwa Yehova kunali pa maufumu onse a mayiko oyandikana ndi Yuda, kotero kuti sanachite nkhondo ndi Yehosafati.
ומן פלשתים מביאים ליהושפט מנחה--וכסף משא גם הערביאים מביאים לו צאן אילים שבעת אלפים ושבע מאות ותישים שבעת אלפים ושבע מאות | 11 |
Afilisti ena anabweretsa kwa Yehosafati mphatso ndi siliva ngati msonkho, ndipo Aarabu anabweretsa ziweto: nkhosa zazimuna 7,700 ndi mbuzi 7,700.
ויהי יהושפט הלך וגדל עד למעלה ויבן ביהודה בירניות וערי מסכנות | 12 |
Mphamvu za Yehosafati zinkakulirakulira. Iye anamanga malo otetezedwa ndi mizinda yosungiramo chuma mu Yuda
ומלאכה רבה היה לו בערי יהודה ואנשי מלחמה גבורי חיל בירושלם | 13 |
ndipo anali ndi katundu wambiri mʼmizinda ya Yuda. Iye anayikanso asilikali odziwa bwino nkhondo mu Yerusalemu.
ואלה פקדתם לבית אבותיהם ליהודה שרי אלפים-- עדנה השר ועמו גבורי חיל שלש מאות אלף | 14 |
Chiwerengero chawo potsata mabanja awo chinali chotere: kuchokera ku Yuda, atsogoleri a magulu 1,000; mtsogoleri Adina, anali ndi anthu 300,000 odziwa nkhondo;
ועל ידו יהוחנן השר ועמו מאתים ושמונים אלף | 15 |
otsatana naye, mtsogoleri Yehohanani, anali ndi anthu 280,000;
ועל ידו עמסיה בן זכרי המתנדב ליהוה ועמו מאתים אלף גבור חיל | 16 |
otsatana naye, Amasiya mwana wa Zikiri amene anadzipereka yekha kutumikira Yehova, anali ndi anthu 200,000.
ומן בנימן--גבור חיל אלידע ועמו נשקי קשת ומגן מאתים אלף | 17 |
Kuchokera ku Benjamini: Eliada, msilikali wolimba mtima, anali ndi anthu 200,000 amene anali ndi mauta ndi zishango;
ועל ידו יהוזבד ועמו מאה ושמונים אלף חלוצי צבא | 18 |
otsatana naye, Yehozabadi, anali ndi anthu 180,000 okonzekera nkhondo.
אלה המשרתים את המלך מלבד אשר נתן המלך בערי המבצר--בכל יהודה | 19 |
Awa ndi anthu amene ankatumikira mfumu osawerengera amene anawayika mʼmizinda yotetezedwa mʼdziko lonse la Yuda.