< שמואל א 6 >
ויהי ארון יהוה בשדה פלשתים שבעה חדשים | 1 |
Bokosi la Yehova linakhala mʼdziko la Afilisti kwa miyezi isanu ndi iwiri.
ויקראו פלשתים לכהנים ולקסמים לאמר מה נעשה לארון יהוה הודענו במה נשלחנו למקומו | 2 |
Tsono Afilisti anayitana ansembe ndi amawula ndipo anati, “Tichite nalo chiyani Bokosi la Yehova? Tiwuzeni momwe tidzalitumizira ku malo ake.”
ויאמרו אם משלחים את ארון אלהי ישראל אל תשלחו אתו ריקם--כי השב תשיבו לו אשם אז תרפאו ונודע לכם למה לא תסור ידו מכם | 3 |
Iwo anayankha kuti, “Ngati mufuna kubweza Bokosi la Mulungu wa Israeli, musalitumize wopanda kanthu, koma muyesetse kulitumiza pamodzi ndi nsembe yopepesera machimo. Mukatero mudzachiritsidwa, ndipo mudzadziwa chifukwa chiyani chilango cha Yehova sichikukuchokani.”
ויאמרו מה האשם אשר נשיב לו ויאמרו מספר סרני פלשתים חמשה עפלי (טחרי) זהב וחמשה עכברי זהב כי מגפה אחת לכלם ולסרניכם | 4 |
Afilisti anafunsanso kuti “Kodi ife tipereke nsembe yanji yopepesera machimo?” Iwo anayankha kuti, “Mupereke zifanizo zagolide za zithupsa zisanu ndi zamakoswe asanu malingana ndi chiwerengero cha akalonga a Afilisti popeza mliri womwewo wagwera inu ndi akalonga anu.
ועשיתם צלמי עפליכם (טחריכם) וצלמי עכבריכם המשחיתם את הארץ ונתתם לאלהי ישראל כבוד אולי יקל את ידו מעליכם ומעל אלהיכם ומעל ארצכם | 5 |
Mupange zifanizo za zithupsa zisanu ndi za makoswe asanu amene akuwononga dziko lanu ndipo mupereke ulemu kwa Israeli. Mwina adzaleka kuzunza inu, milungu yanu ndi dziko lanu.
ולמה תכבדו את לבבכם כאשר כבדו מצרים ופרעה את לבם הלוא כאשר התעלל בהם וישלחום וילכו | 6 |
Nʼchifukwa chiyani mukuwumitsa mitima monga anachita Aigupto ndi Farao? Mulungu atawalanga anthu a ku Igupto aja kodi suja anawalola Aisraeli kuti azipita ndipo anapitadi?
ועתה קחו ועשו עגלה חדשה אחת ושתי פרות עלות אשר לא עלה עליהם על ואסרתם את הפרות בעגלה והשיבתם בניהם מאחריהם הביתה | 7 |
“Tsopano konzani galeta latsopano limodzi ndiponso ngʼombe ziwiri zazikazi zamkaka zimene sizinavalepo goli. Muzimangirire ngʼombezo ku ngoloyo, koma ana awo muwachotse ndi kuwasiya kwanu.
ולקחתם את ארון יהוה ונתתם אתו אל העגלה ואת כלי הזהב אשר השבתם לו אשם תשימו בארגז מצדו ושלחתם אתו והלך | 8 |
Mutenge Bokosi la Yehova ndi kuliyika pa galetapo ndipo pambali pake pakhale Bokosi, mʼmene muyikemonso zinthu zagolide zomwe mukutumiza kwa Iye monga nsembe yopepesera machimo. Kenaka, mulisiye lizipita.
וראיתם אם דרך גבולו יעלה בית שמש--הוא עשה לנו את הרעה הגדולה הזאת ואם לא וידענו כי לא ידו נגעה בנו--מקרה הוא היה לנו | 9 |
Koma muziliyangʼana. Ngati lilondola njira yopita kwawo kwa Bokosilo mpaka ku Beti-Semesi ndiye kuti amene watichita zoyipa zazikulu zoterezi ndi Mulungu wa Israeli. Koma ngati silitero, ife tidzadziwa kuti sanali Mulungu wa Israeli amene watizunza koma kuti zinangochitika mwatsoka.”
ויעשו האנשים כן ויקחו שתי פרות עלות ויאסרום בעגלה ואת בניהם כלו בבית | 10 |
Anthu aja anachitadi zimenezi. Anatenga ngʼombe zamkaka ziwiri nazimanga ku galeta lija. Koma ana awo anawatsekera mʼkhola.
וישמו את ארון יהוה אל העגלה ואת הארגז ואת עכברי הזהב ואת צלמי טחריהם | 11 |
Tsono anayika Bokosi la Yehova pa galeta pamodzi ndi bokosi limene munali makoswe agolide ndi zifanizo zawo za zithupsa.
וישרנה הפרות בדרך על דרך בית שמש במסלה אחת הלכו הלך וגעו ולא סרו ימין ושמאול וסרני פלשתים הלכים אחריהם עד גבול בית שמש | 12 |
Ngʼombe zija zinapita molunjika kutsata msewu wopita ku Beti Semesi zikulira njira yonse. Sizinakhotere kumanja kapena kumanzere. Akalonga a Afilisti anazitsatira mpaka mʼmalire a Beti-Semesi.
ובית שמש קצרים קציר חטים בעמק וישאו את עיניהם ויראו את הארון וישמחו לראות | 13 |
Nthawi imeneyi anthu a ku Beti-Semesi amakolola tirigu mʼchigwa ndipo pamene anayangʼana ndi kuona Bokosi la Chipangano likubwera anakondwa.
והעגלה באה אל שדה יהושע בית השמשי ותעמד שם ושם אבן גדולה ויבקעו את עצי העגלה ואת הפרות העלו עלה ליהוה | 14 |
Galeta lija linafika ku munda wa Yoswa ku Beti-Semesi ndipo linayima. Kumeneko kunali mwala waukulu. Tsono anthu anawaza nkhuni galetalo, ndipo anapha ngʼombe zija ndi kuzipereka ngati nsembe zopsereza kwa Yehova.
והלוים הורידו את ארון יהוה ואת הארגז אשר אתו אשר בו כלי זהב וישמו אל האבן הגדולה ואנשי בית שמש העלו עלות ויזבחו זבחים ביום ההוא--ליהוה | 15 |
Alevi nʼkuti atatsitsa Bokosi la Yehova, pamodzi ndi bokosi mmene munali zinthu zagolide, ndipo anawayika pa mwala uja waukulu. Tsiku limenelo anthu a ku Beti-Semesi anapereka nsembe yopsereza ndi nsembe zina kwa Yehova.
וחמשה סרני פלשתים ראו וישבו עקרון ביום ההוא | 16 |
Atsogoleri asanu a Afilisti ataona izi anabwerera ku Ekroni tsiku lomwelo.
ואלה טחרי הזהב אשר השיבו פלשתים אשם ליהוה לאשדוד אחד לעזה אחד לאשקלון אחד לגת אחד לעקרון אחד | 17 |
Zifanizo zagolide za zithupsa zimene Afilisti anatumiza ngati nsembe zopepesera machimo kwa Yehova zinkayimirira mizinda isanu iyi motere: chimodzi cha ku Asidodi, china cha ku Gaza ndi zina za ku Asikeloni, Gati ndi Ekroni.
ועכברי הזהב מספר כל ערי פלשתים לחמשת הסרנים--מעיר מבצר ועד כפר הפרזי ועד אבל הגדולה אשר הניחו עליה את ארון יהוה עד היום הזה בשדה יהושע בית השמשי | 18 |
Ndipo chiwerengero cha zifanizo za makoswe chinali chofanana ndi chiwerengero cha mizinda ya akalonga asanu a Afilisti. Mizindayi inali yotetezedwa bwino ndi ina yapamtetete. Mwala waukulu umene anayikapo Bokosi la Chipangano la Yehova mʼmunda mwa Yoswa ku Beti-Semesi uli ngati mboni mpaka lero.
ויך באנשי בית שמש כי ראו בארון יהוה ויך בעם שבעים איש חמשים אלף איש ויתאבלו העם כי הכה יהוה בעם מכה גדולה | 19 |
Yehova anakantha amuna a ku Beti-Semesi 70 chifukwa anasuzumira mʼBokosi la Chipangano cha Yehova. Ndipo anzawo analira chifukwa Yehova anawalanga kwambiri.
ויאמרו אנשי בית שמש מי יוכל לעמד לפני יהוה האלהים הקדוש הזה ואל מי יעלה מעלינו | 20 |
Tsono anthu a ku Beti-Semesi anafunsa, “Ndani angathe kuyima pamaso pa Yehova Mulungu Woyera? Bokosi la Chipanganoli lipita kuti likachoka pano?”
וישלחו מלאכים אל יושבי קרית יערים לאמר השבו פלשתים את ארון יהוה--רדו העלו אתו אליכם | 21 |
Tsono iwo anatumiza a mithenga kwa anthu a ku Kiriati-Yearimu kuti, “Afilisti atibwezera Bokosi la Yehova. Bwerani kuno mudzalitenge, mupite nalo kwanuko.”