< שמואל א 10 >

ויקח שמואל את פך השמן ויצק על ראשו--וישקהו ויאמר--הלוא כי משחך יהוה על נחלתו לנגיד 1
Ndipo Samueli anatenga botolo la mafuta nathira mafutawo pa mutu wa Sauli ndipo anapsompsona nati, “Yehova wakudzoza kuti ukhale mtsogoleri wa anthu ake, Aisraeli. Iwe udzalamulira anthu a Yehova ndiponso udzawapulumutsa mʼmanja mwa adani awo owazungulira. Chizindikiro chakuti Yehova wakudzoza kuti ukhale mtsogoleri wa anthu ake ndi ichi:
בלכתך היום מעמדי ומצאת שני אנשים עם קברת רחל בגבול בנימן בצלצח ואמרו אליך נמצאו האתנות אשר הלכת לבקש והנה נטש אביך את דברי האתנות ודאג לכם לאמר מה אעשה לבני 2
Ukachoka pano lero lino, udzakumana ndi amuna awiri kufupi ndi manda a Rakele ku Zeliza mʼmalire mwa dziko la Benjamini ndipo adzakuwuza kuti, ‘Abulu amene munkafunafuna aja apezeka. Ndipo tsopano abambo ako asiya kuganiza za abulu ndipo akudera nkhawa za iwe.’ Iwo akufunsa kuti, ‘Kodi ndidzachita chiyani mmene mwana wanga sakuoneka?’”
וחלפת משם והלאה ובאת עד אלון תבור ומצאוך שם שלשה אנשים עלים אל האלהים בית אל אחד נשא שלשה גדיים ואחד נשא שלשת ככרות לחם ואחד נשא נבל יין 3
“Ndipo udzapyola pamenepo ndi kufika ku mtengo wa thundu wa ku Tabori. Kumeneko udzakumana ndi anthu atatu akupita kukapereka nsembe ku Nyumba ya Mulungu ku Beteli. Mmodzi adzakhala atanyamula ana ambuzi atatu, wina atanyamula malofu atatu a buledi, ndi winayo atanyamula thumba la vinyo.
ושאלו לך לשלום ונתנו לך שתי לחם ולקחת מידם 4
Adzakupatsa moni ndi kukupatsa malofu awiri a buledi. Iwe udzalandire bulediyo.
אחר כן תבוא גבעת האלהים אשר שם נצבי פלשתים ויהי כבאך שם העיר ופגעת חבל נבאים ירדים מהבמה ולפניהם נבל ותף וחליל וכנור והמה מתנבאים 5
“Pambuyo pake, udzafike ku Gibeyati-Elohimu, kumene kuli gulu la ankhondo la Afilisti. Pamene ukuyandikira mzindawo, udzakumana ndi gulu la aneneri akutsika kuchokera ku phiri, akuyimba zeze, ngʼoma, zitoliro ndi pangwe, ndiponso akulosera.
וצלחה עליך רוח יהוה והתנבית עמם ונהפכת לאיש אחר 6
Kenaka Mzimu wa Yehova udzabwera pa iwe ndi mphamvu, ndipo udzayamba kulosera nawo pamodzi. Ndipo udzasinthika kukhala munthu wina.
והיה כי תבאינה (תבאנה) האתות האלה--לך עשה לך אשר תמצא ידך כי האלהים עמך 7
Zizindikiro izi zikakachitika, dzachite chilichonse manja ako angathe kuchita, pakuti Mulungu ali nawe.
וירדת לפני הגלגל והנה אנכי ירד אליך להעלות עלות לזבח זבחי שלמים שבעת ימים תוחל עד בואי אליך והודעתי לך את אשר תעשה 8
“Tsono tsogola kupita ku Giligala. Ine ndidzabwera ndithu kudzapereka nsembe zopsereza ndi nsembe zachiyanjano. Koma ukandidikire masiku asanu ndi awiri mpaka ine nditabwera kuti ndidzakuwuze zomwe udzachite.”
והיה כהפנתו שכמו ללכת מעם שמואל ויהפך לו אלהים לב אחר ויבאו כל האתות האלה ביום ההוא 9
Sauli akutembenuka kusiyana ndi Samueli, Mulungu anasintha mtima wa Sauli, ndipo zinthu zonsezi zinakwaniritsidwa tsiku lomwelo.
ויבאו שם הגבעתה והנה חבל נבאים לקראתו ותצלח עליו רוח אלהים ויתנבא בתוכם 10
Atafika ku Gibeya, anakumana ndi gulu la aneneri. Mzimu wa Mulungu unabwera pa iye mwamphamvu, nayamba kulosa nawo.
ויהי כל יודעו מאתמול שלשם ויראו והנה עם נבאים נבא ויאמר העם איש אל רעהו מה זה היה לבן קיש--הגם שאול בנביאים 11
Pamene onse amene ankamudziwa kale anamuona akulosera pamodzi ndi aneneri, anafunsana wina ndi mnzake. “Kodi nʼchiyani chachitika ndi mwana wa Kisi? Kodi Sauli alinso mʼgulu la aneneri?”
ויען איש משם ויאמר ומי אביהם על כן היתה למשל הגם שאול בנבאים 12
Munthu wina wa kumeneko anayankha kuti, “Nanga enawa abambo awo ndani?” Kotero kunayambika mwambi wakuti, “Kodi Saulinso ali mʼgulu la aneneri?”
ויכל מהתנבות ויבא הבמה 13
Sauli atasiya kuloserako, anapita ku kachisi ku phiri.
ויאמר דוד שאול אליו ואל נערו אן הלכתם ויאמר לבקש את האתנות ונראה כי אין ונבוא אל שמואל 14
Tsono amalume ake a Sauli anamufunsa ndi mnyamata wake kuti, “Munapita kuti?” Iye anayakha, “Timakafunafuna abulu koma titaona kuti sakupezeka, tinapita kwa Samueli.”
ויאמר דוד שאול הגידה נא לי מה אמר לכם שמואל 15
Amalume ake a Sauli anati, “Chonde, ndifotokozereniko zimene Samueli wakuwuzani.”
ויאמר שאול אל דודו הגד הגיד לנו כי נמצאו האתנות ואת דבר המלוכה לא הגיד לו אשר אמר שמואל 16
Sauli anati, “Iye anatitsimikizira kuti abulu anapezeka.” Koma sanawawuze amalume akewo za nkhani ija ya ufumu imene Samueli anamuwuza.
ויצעק שמואל את העם אל יהוה המצפה 17
Samueli anayitana Aisraeli onse kuti asonkhane pamaso pa Yehova ku Mizipa.
ויאמר אל בני ישראל כה אמר יהוה אלהי ישראל אנכי העליתי את ישראל ממצרים ואציל אתכם מיד מצרים ומיד כל הממלכות הלחצים אתכם 18
Ndipo anawuza Aisraeli onse kuti, “Yehova Mulungu wa Israeli akuti, ‘Ine ndinakutulutsani mʼdziko la Igupto ndi kukupulumutsani mʼdzanja la Igupto ndi mʼdzanja la mafumu onse amene ankakuzunzani.’
ואתם היום מאסתם את אלהיכם אשר הוא מושיע לכם מכל רעותיכם וצרתיכם ותאמרו לו כי מלך תשים עלינו ועתה התיצבו לפני יהוה לשבטיכם ולאלפיכם 19
Koma lero mwamukana Mulungu wanu amene amakupulumutsani mʼmavuto anu onse ndi mʼzowawa zanu. Ndipo mukuti, ‘Ayi, koma mutipatse mfumu yotilamulira.’ Tsopanotu sonkhanani pamaso pa Yehova mwa mafuko ndi mabanja anu.”
ויקרב שמואל את כל שבטי ישראל וילכד שבט בנימן 20
Samueli atasonkhanitsa mafuko onse a Israeli, fuko la Benjamini linasankhidwa.
ויקרב את שבט בנימן למשפחתו ותלכד משפחת המטרי וילכד שאול בן קיש ויבקשהו ולא נמצא 21
Anasonkhanitsa fuko la Benjamini banja ndi banja. Pomaliza anasonkhanitsa banja la Matiri mmodzimmodzi ndipo Sauli mwana wa Kisi anasankhidwa. Koma atamufunafuna, sanamupeze.
וישאלו עוד ביהוה הבא עוד הלם איש ויאמר יהוה הנה הוא נחבא אל הכלים 22
Tsono anthu anafunsanso kwa Yehova kuti, “Kodi munthuyu wabwera kale kuno?” Ndipo Yehova anayankha kuti, “Inde wabisala pakati pa katundu.”
וירצו ויקחהו משם ויתיצב בתוך העם ויגבה מכל העם משכמו ומעלה 23
Iwo anathamanga ndi kukamutenga kumeneko. Atayimirira pakati pa anthu anapezeka kuti anali wamtali kuposa anthu ena mwakuti ankamulekeza mʼmapewa.
ויאמר שמואל אל כל העם הראיתם אשר בחר בו יהוה כי אין כמהו בכל העם וירעו כל העם ויאמרו יחי המלך 24
Samueli anafunsa anthu onse kuti, “Kodi mukumuona munthu amene Yehova wasankha? Palibe wofanana naye pakati pa anthu onse.” Kenaka anthu onse anafuwula kuti, “Mfumu ikhale ndi moyo wautali!”
וידבר שמואל אל העם את משפט המלכה ויכתב בספר וינח לפני יהוה וישלח שמואל את כל העם איש לביתו 25
Samueli anafotokozera anthu ntchito ndi udindo wa mfumu. Pambuyo pake analemba mʼbuku zonse zokhudza ntchito ndi udindo wa mfumu, ndipo bukulo analiyika pamaso pa Yehova. Kenaka Samueli analola aliyense kuti abwerere kupita kwawo.
וגם שאול--הלך לביתו גבעתה וילכו עמו--החיל אשר נגע אלהים בלבם 26
Sauli anapitanso ku mudzi kwawo ku Gibeya, pamodzi ndi anthu amphamvu amene Mulungu anawafewetsa mitima.
ובני בליעל אמרו מה ישענו זה ויבזהו ולא הביאו לו מנחה ויהי כמחריש 27
Koma anthu ena achabechabe anati, “Kodi munthu uyu angathe bwanji kutipulumutsa?” Iwo anayamba kumunyoza Sauliyo, ndipo sankamupatsa ngakhale mphatso. Koma iye sanalabadireko.

< שמואל א 10 >