< דברי הימים א 9 >
וכל ישראל התיחשו והנם כתובים על ספר מלכי ישראל ויהודה הגלו לבבל במעלם | 1 |
Aisraeli onse analembedwa potsata mibado yawo mʼbuku la mafumu a Aisraeli. Anthu a ku Yuda anatengedwa kunka ku ukapolo ku Babuloni chifukwa cha kusakhulupirika kwawo.
והיושבים הראשנים אשר באחזתם בעריהם ישראל הכהנים הלוים והנתינים | 2 |
Tsono anthu oyamba kukhala mʼmadera awo anali Aisraeli wamba, ansembe, Alevi ndi otumikira ku Nyumba ya Yehova.
ובירושלם ישבו מן בני יהודה ומן בני בנימן--ומן בני אפרים ומנשה | 3 |
Anthu a ku Yuda, Benjamini ndi Efereimu ndiponso Manase amene anakhala mu Yerusalemu anali awa:
עותי בן עמיהוד בן עמרי בן אמרי בן בנימן (בני מן) בני פרץ בן יהודה | 4 |
Utai mwana wa Amihudi, mwana wa Omuri, mwana wa Imuri, mwana wa Bani, chidzukulu cha Perezi mwana wa Yuda.
ומן השילוני עשיה הבכור ובניו | 5 |
A banja la Siloni: Asaya mwana wake woyamba pamodzi ndi ana ake.
ומן בני זרח יעואל ואחיהם שש מאות ותשעים | 6 |
A banja la Zera: Yeueli. Anthu ochokera ku Yuda analipo 690.
ומן בני בנימן--סלוא בן משלם בן הודויה בן הסנאה | 7 |
A fuko la Benjamini: Salu mwana wa Mesulamu, mwana wa Hodaviya, mwana wa Hasenuya;
ויבניה בן ירחם ואלה בן עזי בן מכרי ומשלם בן שפטיה בן רעואל בן יבניה | 8 |
Ibineya mwana wa Yerohamu; Ela mwana wa Uzi, mwana wa Mikiri; ndi Mesulamu mwana wa Sefatiya, mwana wa Reueli mwana wa Ibiniya.
ואחיהם לתלדותם תשע מאות וחמשים וששה כל אלה אנשים ראשי אבות לבית אבתיהם | 9 |
Anthu ochokera ku Benjamini monga analembedwera mwa mibado yawo, analipo 956. Anthu onsewa anali atsogoleri a mabanja awo.
ומן הכהנים ידעיה ויהויריב ויכין | 10 |
Ansembe: Yedaya, Yehoyaribu; Yakini;
ועזריה בן חלקיה בן משלם בן צדוק בן מריות בן אחיטוב נגיד בית האלהים | 11 |
Azariya mwana wa Hilikiya, mwana wa Mesulamu, mwana wa Zadoki mwana wa Merayoti, mwana wa Ahitubi, wamkulu woyangʼanira Nyumba ya Mulungu;
ועדיה בן ירחם בן פשחור בן מלכיה ומעשי בן עדיאל בן יחזרה בן משלם בן משלמית בן אמר | 12 |
Adaya mwana wa Yerohamu, mwana wa Pasi-Huri, mwana wa Malikiya; ndi Maasai mwana wa Adieli, mwana wa Yahizera, mwana wa Mesulamu, mwana wa Mesilemoti, mwana wa Imeri.
ואחיהם ראשים לבית אבותם אלף ושבע מאות וששים--גבורי חיל מלאכת עבודת בית האלהים | 13 |
Ansembe amene anali atsogoleri a mabanja awo analipo 1,760. Anali anthu amphamvu ndi odziwa kutumikira mʼnyumba ya Mulungu.
ומן הלוים שמעיה בן חשוב בן עזריקם בן חשביה מן בני מררי | 14 |
Alevi: Semaya mwana wa Hasubu, mwana wa Azirikamu, mwana wa Hasabiya, wa mʼbanja la Merari;
ובקבקר חרש וגלל ומתניה בן מיכא בן זכרי בן אסף | 15 |
Bakibakara, Heresi, Galali ndi Mataniya mwana wa Mika, mwana wa Zikiri, mwana wa Asafu;
ועבדיה בן שמעיה בן גלל בן ידותון וברכיה בן אסא בן אלקנה היושב בחצרי נטופתי | 16 |
Obadiya mwana wa Semaya mwana wa Galali, mwana wa Yedutuni ndi Berekiya mwana wa Asa, mwana wa Elikana, amene ankakhala ku midzi ya Anetofati.
והשערים שלום ועקוב וטלמן ואחימן ואחיהם שלום הראש | 17 |
Alonda a pa makomo: Salumu, Akubu, Talimoni, Ahimani ndi abale awo. Mtsogoleri wawo anali Salumu.
ועד הנה בשער המלך מזרחה המה השערים למחנות בני לוי | 18 |
Amenewa amakhala pa chipata cha mfumu kummawa mpaka lero lino. Alonda a gulu la Alevi anali awa:
ושלום בן קורא בן אביסף בן קרח ואחיו לבית אביו הקרחים על מלאכת העבודה שמרי הספים לאהל ואבתיהם על מחנה יהוה שמרי המבוא | 19 |
Salumu mwana wa Kore, mwana wa Ebiyasafu, mwana wa Kora, pamodzi ndi abale ake a ku banja la makolo ake, Akora aja ankanyangʼanira khomo la Tenti monga ankachitira abambo awo polondera khomo la malo okhalapo Yehova.
ופינחס בן אלעזר נגיד היה עליהם לפנים--יהוה עמו | 20 |
Masiku oyamba Finehasi mwana wa Eliezara anali woyangʼanira alonda apakhomo ndipo Yehova anali naye.
זכריה בן משלמיה שער פתח לאהל מועד | 21 |
Zekariya mwana wa Meselemiya anali mlonda woyangʼanira pa chipata cha tenti ya msonkhano.
כלם הברורים לשערים בספים מאתים ושנים עשר המה בחצריהם התיחשם המה יסד דויד ושמואל הראה באמונתם | 22 |
Onse amene anasankhidwa kukhala alonda pa khonde analipo 212. Iwo analembedwa mwa mibado yawo ku midzi yawo. Davide ndi mneneri Samueli ndiwo anawayika mʼmalo awo antchito chifukwa cha kukhulupirika kwawo.
והם ובניהם על השערים לבית יהוה לבית האהל--למשמרות | 23 |
Iwo ndi zidzukulu zawo anali oyangʼanira zipata za nyumba ya Yehova imene imatchedwa Tenti.
לארבע רוחות יהיו השערים מזרח ימה צפונה ונגבה | 24 |
Alonda apakhomowa anali mbali zonse zinayi: kummawa, kumadzulo, kumpoto ndi kummwera.
ואחיהם בחצריהם לבוא לשבעת הימים מעת אל עת--עם אלה | 25 |
Abale awo a ku midzi yawo amabwera nthawi ndi nthawi kudzagwira ntchito yawo kwa masiku asanu ndi awiri.
כי באמונה המה ארבעת גברי השערים--הם הלוים והיו על הלשכות ועל האצרות בית האלהים | 26 |
Koma atsogoleri akuluakulu anayi a alonda, amene anali Alevi, anapatsidwa udindo woyangʼanira zipinda ndi chuma cha nyumba ya Mulungu.
וסביבות בית האלהים ילינו כי עליהם משמרת והם על המפתח ולבקר לבקר | 27 |
Iwo amakhala usiku wonse atayima mozungulira Nyumba ya Mulungu, chifukwa anayenera kuyilondera. Ndipo anali ndi kiyi wotsekulira mmawa uliwonse.
ומהם על כלי העבודה כי במספר יביאום ובמספר יוציאום | 28 |
Ena amayangʼanira zipangizo zimene amagwiritsa ntchito pa ntchito mʼNyumba ya Mulungu. Iwo amaziwerenga zikamalowetsedwa ndi potulutsidwa.
ומהם ממנים על הכלים ועל כל כלי הקדש ועל הסלת והיין והשמן והלבונה והבשמים | 29 |
Ena anapatsidwa udindo wosamalira zipangizo ndi zinthu zina zonse za ku malo opatulika, pamodzi ndi ufa, vinyo, mafuta, lubani ndi zonunkhira.
ומן בני הכהנים רקחי המרקחת לבשמים | 30 |
Koma ansembe ena amasakaniza zonunkhirazo.
ומתתיה מן הלוים הוא הבכור לשלם הקרחי--באמונה על מעשה החבתים | 31 |
Mlevi wotchedwa Matitiya mwana woyamba wa Salumu wa mʼbanja la Kora, anapatsidwa udindo woyangʼanira zophikidwa mʼziwaya.
ומן בני הקהתי מן אחיהם על לחם המערכת להכין שבת שבת | 32 |
Abale ake ena a mʼbanja la Akohati amaphika buledi wa pa Sabata lililonse amene amayikidwa pa tebulo.
ואלה המשררים ראשי אבות ללוים בלשכת--פטירים (פטורים) כי יומם ולילה עליהם במלאכה | 33 |
Atsogoleri a mabanja a Alevi, amene anali ndi luso loyimba, amakhala mʼzipinda za Nyumba ya Mulungu ndipo samagwira ntchito zina chifukwa ankatumikira usana ndi usiku.
אלה ראשי האבות ללוים לתלדותם ראשים אלה ישבו בירושלם | 34 |
Onsewa anali atsogoleri a mabanja a Alevi, akuluakulu monga analembedwera pa mibado yawo, ndipo ankakhala mu Yerusalemu.
ובגבעון ישבו אבי גבעון יעואל (יעיאל) ושם אשתו מעכה | 35 |
Yeiyeli abambo a Gibiyoni ankakhala ku Gibiyoni. Dzina la akazi awo linali Maaka,
ובנו הבכור עבדון וצור וקיש ובעל ונר ונדב | 36 |
ndipo mwana wawo woyamba kubadwa anali Abidoni, motsatana ndi Zuri, Kisi, Baala, Neri, Nadabu,
וגדור ואחיו וזכריה ומקלות | 37 |
Gedori, Ahiyo, Zekariya ndi Mikiloti.
ומקלות הוליד את שמאם ואף הם נגד אחיהם ישבו בירושלם--עם אחיהם | 38 |
Mikiloti anabereka Simeamu. Iwonso ankakhala ndi abale awo ku Yerusalemu.
ונר הוליד את קיש וקיש הוליד את שאול ושאול הוליד את יהונתן ואת מלכישוע ואת אבינדב ואת אשבעל | 39 |
Neri anabereka Kisi, Kisi anabereka Sauli, ndipo Sauli anabereka Yonatani, Maliki-Suwa, Abinadabu ndi Esibaala.
ובן יהונתן מריב בעל ומרי בעל הוליד את מיכה | 40 |
Mwana wa Yonatani anali Meri-Baala, amene anabereka Mika.
ובני מיכה--פיתן ומלך ותחרע | 41 |
Ana a Mika anali: Pitoni, Meleki, Tahireya ndi Ahazi.
ואחז הוליד את יערה ויערה הוליד את עלמת ואת עזמות ואת זמרי וזמרי הוליד את מוצא | 42 |
Ahazi anabereka Yara, Yara anabereka Alemeti, Azimaveti ndi Zimuri, ndipo Zimiri anabereka Moza.
ומוצא הוליד את בנעא ורפיה בנו אלעשה בנו אצל בנו | 43 |
Moza anabereka Bineya. Ana ake anali Refaya, Eleasa ndi Azeli.
ולאצל ששה בנים ואלה שמותם עזריקם בכרו וישמעאל ושעריה ועבדיה וחנן אלה בני אצל | 44 |
Azeli anali ndi ana asanu ndi mmodzi ndipo mayina awo anali awa: Azirikamu, Bokeru, Ismaeli, Seariya, Obadiya ndi Hanani. Awa anali ana a Azeli.