< Κατα Μαρκον 16 >
1 Καὶ διαγενομένου τοῦ Σαββάτου, ἡ Μαρία ἡ Μαγδαληνὴ, καὶ Μαρία ἡ τοῦ Ἰακώβου, καὶ Σαλώμη, ἠγόρασαν ἀρώματα, ἵνα ἐλθοῦσαι ἀλείψωσιν αὐτόν.
Litapita tsiku la Sabata, Mariya Magadalena, ndi amayi ake a Yakobo, ndi Salome anagula zonunkhiritsa ndi cholinga chakuti apite akadzoze thupi la Yesu.
2 Καὶ λίαν πρωῒ μιᾷ τῶν σαββάτων, ἔρχονται ἐπὶ τὸ μνημεῖον, ἀνατείλαντος τοῦ ἡλίου.
Mmamawa, tsiku loyamba la Sabata, dzuwa litangotuluka kumene, anali pa ulendo wopita ku manda
3 Καὶ ἔλεγον πρὸς ἑαυτάς, “Τίς ἀποκυλίσει ἡμῖν τὸν λίθον ἐκ τῆς θύρας τοῦ μνημείου;”
ndipo anafunsana wina ndi mnzake kuti, “Kodi akatikugudubuzira mwala pa khomo la manda ndani?”
4 Καὶ ἀναβλέψασαι θεωροῦσιν ὅτι ἀποκεκύλισται ὁ λίθος, ἦν γὰρ μέγας σφόδρα.
Koma atakweza maso awo, anaona kuti mwala umene unali waukulu kwambiri wagubuduzidwa kale.
5 Καὶ εἰσελθοῦσαι εἰς τὸ μνημεῖον, εἶδον νεανίσκον καθήμενον ἐν τοῖς δεξιοῖς, περιβεβλημένον στολὴν λευκήν, καὶ ἐξεθαμβήθησαν.
Atalowa mʼmanda, anaona mnyamata atavala mwinjiro woyera atakhala ku mbali ya kumanja, ndipo iwo anachita mantha.
6 Ὁ δὲ λέγει αὐταῖς, “Μὴ ἐκθαμβεῖσθε. ˚Ἰησοῦν ζητεῖτε τὸν Ναζαρηνὸν, τὸν ἐσταυρωμένον. Ἠγέρθη! Οὐκ ἔστιν ὧδε· ἴδε, ὁ τόπος ὅπου ἔθηκαν αὐτόν.
Iye anati, “Musaope. Kodi mukufuna Yesu wa ku Nazareti, amene anapachikidwa? Wauka! Sali muno. Onani malo amene anamugonekapo.
7 Ἀλλὰ ὑπάγετε, εἴπατε τοῖς μαθηταῖς αὐτοῦ καὶ τῷ Πέτρῳ, ὅτι ‘Προάγει ὑμᾶς εἰς τὴν Γαλιλαίαν· ἐκεῖ αὐτὸν ὄψεσθε, καθὼς εἶπεν ὑμῖν.’”
Koma pitani, kawuzeni ophunzira ake ndi Petro kuti, ‘Iye watsogola kupita ku Galileya. Kumeneko mukamuona Iye monga momwe anakuwuzirani.’”
8 Καὶ ἐξελθοῦσαι, ἔφυγον ἀπὸ τοῦ μνημείου, εἶχεν γὰρ αὐτὰς τρόμος καὶ ἔκστασις, καὶ οὐδενὶ οὐδὲν εἶπον, ἐφοβοῦντο γάρ.
Akunjenjemera ndi kudabwa, amayiwo anatuluka ndipo anathawa ku mandako. Sananene china chilichonse kwa aliyense, chifukwa anachita mantha.
(note: The most reliable and earliest manuscripts do not include Mark 16:9-20.) Yesu atauka kwa akufa mmawa pa tsiku loyamba la Sabata, anayamba kuonekera kwa Mariya Magadalena, amene anatulutsa mwa iye ziwanda zisanu ndi ziwiri.
Iye anapita ndi kukawawuza amene anali ndi Yesu, amene ankakhuza maliro ndi kulira.
Atamva kuti Yesu ali moyo ndikuti amuona, iwo sanakhulupirire.
Zitatha izi Yesu anaonekera mʼmaonekedwe ena kwa awiri a iwo amene anali ku dera la ku mudzi.
Iwo anabwerera ndi kudzawawuza enawo; koma iwo sanakhulupirirebe.
Pambuyo pake Yesu anaonekera kwa khumi ndi mmodziwo pamene ankadya; anawadzudzula chifukwa chopanda chikhulupiriro ndi kukanitsitsa kwawo kuti akhulupirire amene anamuona Iye atauka.
Anati kwa iwo, “Pitani mʼdziko lonse lapansi ndipo mukalalikire Uthenga Wabwino kwa zolengedwa zonse.
Aliyense amene akakhulupirire nabatizidwa adzapulumuka, koma amene sakakhulupirira adzalangidwa.
Tsono zizindikiro izi zidzawatsata amene adzakhulupirira: Mʼdzina langa adzatulutsa ziwanda; adzayankhula malilime atsopano;
adzanyamula njoka ndi manja awo; ndipo pamene adzamwa mankhwala akupha, sadzawapweteka nʼpangʼonongʼono pomwe; adzasanjika manja awo pa anthu odwala ndipo odwalawo adzachira.”
Ambuye Yesu atatha kuyankhulana nawo, anatengedwa kupita kumwamba ndipo anakhala kudzanja lamanja la Mulungu.
Pamenepo ophunzira aja anapita ndi kukalalikira ponseponse, ndipo Ambuye anagwira nawo ntchito pamodzi, ndipo anatsimikizira mawuwo ndi zizindikiro zimene ankachita.