< Κατα Ματθαιον 14 >
1 Ἐν ἐκείνῳ τῷ καιρῷ ἤκουσεν Ἡρῴδης ὁ τετραάρχης τὴν ἀκοὴν Ἰησοῦ,
Pa nthawi imeneyo Mfumu Herode anamva za mbiri ya Yesu.
2 καὶ εἶπεν τοῖς παισὶν αὐτοῦ Οὗτός ἐστιν Ἰωάνης ὁ Βαπτιστής· αὐτὸς ἠγέρθη ἀπὸ τῶν νεκρῶν, καὶ διὰ τοῦτο αἱ δυνάμεις ἐνεργοῦσιν ἐν αὐτῷ.
Ndipo iye anati kwa antchito ake, “Uyu ndi Yohane Mʼbatizi; iye wauka kwa akufa! Ichi ndi chifukwa chake mphamvu zodabwitsa zikugwira ntchito mwa iye.”
3 Ὁ γὰρ Ἡρῴδης κρατήσας τὸν Ἰωάνην ἔδησεν καὶ ἐν φυλακῇ ἀπέθετο διὰ Ἡρῳδιάδα τὴν γυναῖκα Φιλίππου τοῦ ἀδελφοῦ αὐτοῦ·
Pakuti Herode anamugwira Yohane ndi kumumanga ndipo anamuyika mʼndende chifukwa cha Herodia mkazi wa mʼbale wake Filipo.
4 ἔλεγεν γὰρ ὁ Ἰωάνης αὐτῷ Οὐκ ἔξεστίν σοι ἔχειν αὐτήν.
Chifukwa Yohane anakhala akunena kwa iye kuti, “Sichololedwa kwa inu kutenga mkaziyo.”
5 καὶ θέλων αὐτὸν ἀποκτεῖναι ἐφοβήθη τὸν ὄχλον, ὅτι ὡς προφήτην αὐτὸν εἶχον.
Herode anafuna kupha Yohane koma iye anaopa anthu chifukwa anamuyesa iye mneneri.
6 γενεσίοις δὲ γενομένοις τοῦ Ἡρῴδου ὠρχήσατο ἡ θυγάτηρ τῆς Ἡρῳδιάδος ἐν τῷ μέσῳ καὶ ἤρεσεν τῷ Ἡρῴδῃ,
Pa tsiku lokumbukira kubadwa kwa Herode, mwana wamkazi wa Herodia anavina pamaso pa anthu ndipo anasangalatsa kwambiri.
7 ὅθεν μεθ’ ὅρκου ὡμολόγησεν αὐτῇ δοῦναι ὃ ἐὰν αἰτήσηται.
Kotero Herode analonjeza ndi lumbiro kumupatsa chilichonse chimene mwanayo angamupemphe.
8 ἡ δὲ προβιβασθεῖσα ὑπὸ τῆς μητρὸς αὐτῆς Δός μοι, φησίν, ὧδε ἐπὶ πίνακι τὴν κεφαλὴν Ἰωάνου τοῦ Βαπτιστοῦ.
Ndipo atamupangira amayi ake anati, “Mundipatse pomwe pano mutu wa Yohane Mʼbatizi mʼmbale.”
9 καὶ λυπηθεὶς ὁ βασιλεὺς διὰ τοὺς ὅρκους καὶ τοὺς συνανακειμένους ἐκέλευσεν δοθῆναι,
Mfumuyo inamva chisoni koma chifukwa cha lumbiro lake ndi alendo amene anali pa phwando lake analamulira kuti chofuna chake chipatsidwe;
10 καὶ πέμψας ἀπεκεφάλισεν Ἰωάνην ἐν τῇ φυλακῇ.
ndipo anakadula mutu wa Yohane mʼndende.
11 καὶ ἠνέχθη ἡ κεφαλὴ αὐτοῦ ἐπὶ πίνακι καὶ ἐδόθη τῷ κορασίῳ, καὶ ἤνεγκεν τῇ μητρὶ αὐτῆς.
Mutu wake anawubweretsa mʼmbale ndi kumupatsa mtsikanayo amene anawutengera kwa amayi ake.
12 καὶ προσελθόντες οἱ μαθηταὶ αὐτοῦ ἦραν τὸ πτῶμα καὶ ἔθαψαν αὐτόν, καὶ ἐλθόντες ἀπήγγειλαν τῷ Ἰησοῦ.
Ophunzira a Yohane anabwera nadzatenga mtembo wake ndi kukawuyika mʼmanda. Pomwepo iwo anapita kukamuwuza Yesu.
13 Ἀκούσας δὲ ὁ Ἰησοῦς ἀνεχώρησεν ἐκεῖθεν ἐν πλοίῳ εἰς ἔρημον τόπον κατ’ ἰδίαν· καὶ ἀκούσαντες οἱ ὄχλοι ἠκολούθησαν αὐτῷ πεζῇ ἀπὸ τῶν πόλεων.
Yesu atamva zimene zinachitika, anachoka pa bwato mwachinsinsi kupita kumalo a yekha. Magulu a anthu atamva izi anamutsatira Iye poyenda pansi kuchokera ku mizinda.
14 Καὶ ἐξελθὼν εἶδεν πολὺν ὄχλον, καὶ ἐσπλαγχνίσθη ἐπ’ αὐτοῖς καὶ ἐθεράπευσεν τοὺς ἀρρώστους αὐτῶν.
Yesu atafika ku mtunda, ndi kuona gulu lalikulu la anthu, Iye anamva nawo chifundo ndipo anachiritsa odwala awo.
15 ὀψίας δὲ γενομένης προσῆλθον αὐτῷ οἱ μαθηταὶ λέγοντες Ἔρημός ἐστιν ὁ τόπος καὶ ἡ ὥρα ἤδη παρῆλθεν· ἀπόλυσον οὖν τοὺς ὄχλους, ἵνα ἀπελθόντες εἰς τὰς κώμας ἀγοράσωσιν ἑαυτοῖς βρώματα.
Kutayamba mdima, ophunzira anabwera kwa Iye nati, “Kuno ndi kutchire ndipo kwayamba kale kuda. Awuzeni anthu azipita kuti afike ku midzi ndi kukadzigulira zakudya.”
16 ὁ δὲ Ἰησοῦς εἶπεν αὐτοῖς Οὐ χρείαν ἔχουσιν ἀπελθεῖν· δότε αὐτοῖς ὑμεῖς φαγεῖν.
Yesu anawayankha kuti, “Sikofunika kuti azipita. Inuyo muwapatse kanthu kuti adye.”
17 οἱ δὲ λέγουσιν αὐτῷ Οὐκ ἔχομεν ὧδε εἰ μὴ πέντε ἄρτους καὶ δύο ἰχθύας.
Iwo anayankha kuti, “Tili ndi malofu asanu okha a buledi ndi nsomba ziwiri.”
18 ὁ δὲ εἶπεν· Φέρετέ μοι ὧδε αὐτούς.
Koma Iye anati, “Bweretsani kwa Ine.”
19 καὶ κελεύσας τοὺς ὄχλους ἀνακλιθῆναι ἐπὶ τοῦ χόρτου, λαβὼν τοὺς πέντε ἄρτους καὶ τοὺς δύο ἰχθύας, ἀναβλέψας εἰς τὸν οὐρανὸν εὐλόγησεν, καὶ κλάσας ἔδωκεν τοῖς μαθηταῖς τοὺς ἄρτους, οἱ δὲ μαθηταὶ τοῖς ὄχλοις.
Analamula anthu kuti akhale pansi pa udzu ndipo anatenga buledi musanu ndi nsomba ziwiri nayangʼana kumwamba, nayamika nagawa bulediyo. Kenaka anapereka bulediyo kwa ophunzira ake ndipo ophunzirawo anagawira anthu.
20 καὶ ἔφαγον πάντες καὶ ἐχορτάσθησαν, καὶ ἦραν τὸ περισσεῦον τῶν κλασμάτων δώδεκα κοφίνους πλήρεις.
Onse anadya nakhuta ndipo ophunzira anatola zotsalira ndi kudzaza madengu khumi ndi awiri.
21 οἱ δὲ ἐσθίοντες ἦσαν ἄνδρες ὡσεὶ πεντακισχίλιοι χωρὶς γυναικῶν καὶ παιδίων.
Chiwerengero cha amene anadya kupatulako amayi ndi ana chinali pafupifupi amuna 5,000.
22 Καὶ εὐθέως ἠνάγκασεν τοὺς μαθητὰς ἐμβῆναι εἰς τὸ πλοῖον καὶ προάγειν αὐτὸν εἰς τὸ πέραν, ἕως οὗ ἀπολύσῃ τοὺς ὄχλους.
Nthawi yomweyo anawawuza ophunzira ake kuti alowe mʼbwato ndi kuti atsogole kupita kutsidya lina pamene Iye ankawuza anthu kuti azipita kwawo.
23 καὶ ἀπολύσας τοὺς ὄχλους ἀνέβη εἰς τὸ ὄρος κατ’ ἰδίαν προσεύξασθαι. ὀψίας δὲ γενομένης μόνος ἦν ἐκεῖ.
Atatha kuwawuza kuti azipita kwawo, Iye anakwera ku phiri yekha kukapemphera. Pamene kumada anali kumeneko yekha.
24 τὸ δὲ πλοῖον ἤδη σταδίους πολλοὺς ἀπὸ τῆς γῆς ἀπεῖχεν, βασανιζόμενον ὑπὸ τῶν κυμάτων, ἦν γὰρ ἐναντίος ὁ ἄνεμος.
Pamenepo nʼkuti bwato litapita patali pangʼono kuchokera ku mtunda ndipo linavutika ndi mafunde chifukwa mphepo inkawomba mokumana nalo.
25 τετάρτῃ δὲ φυλακῇ τῆς νυκτὸς ἦλθεν πρὸς αὐτοὺς περιπατῶν ἐπὶ τὴν θάλασσαν.
Pa ora lachinayi usiku, Yesu anabwera kwa iwo akuyendabe pa nyanja.
26 οἱ δὲ μαθηταὶ ἰδόντες αὐτὸν ἐπὶ τῆς θαλάσσης περιπατοῦντα ἐταράχθησαν λέγοντες ὅτι Φάντασμά ἐστιν, καὶ ἀπὸ τοῦ φόβου ἔκραξαν.
Ophunzira atamuona akuyenda pa nyanja, anaopa nati, “Ndi mzukwa!” Ndipo analira chifukwa cha mantha.
27 εὐθὺς δὲ ἐλάλησεν ὁ Ἰησοῦς αὐτοῖς λέγων Θαρσεῖτε, ἐγώ εἰμι· μὴ φοβεῖσθε.
Koma Yesu nthawi yomweyo anawawuza kuti, “Limbani mtima! Ndine, musaope.”
28 ἀποκριθεὶς δὲ αὐτῷ ὁ Πέτρος εἶπεν Κύριε, εἰ σὺ εἶ, κέλευσόν με ἐλθεῖν πρὸς σὲ ἐπὶ τὰ ὕδατα.
Petro anayankha nati, “Ambuye ngati ndinu, mundiwuze ndibwere kuli inuko pa madzipo.”
29 ὁ δὲ εἶπεν Ἐλθέ. καὶ καταβὰς ἀπὸ τοῦ πλοίου Πέτρος περιεπάτησεν ἐπὶ τὰ ὕδατα καὶ ἦλθεν πρὸς τὸν Ἰησοῦν.
Iye anati, “Bwera.” Pamenepo Petro anatuluka mʼbwato ndipo anayenda pa madzi kupita kwa Yesu.
30 βλέπων δὲ τὸν ἄνεμον ἐφοβήθη, καὶ ἀρξάμενος καταποντίζεσθαι ἔκραξεν λέγων Κύριε, σῶσόν με.
Koma ataona mphepo, iye anachita mantha ndipo anayamba kumira, nafuwula nati, “Ambuye ndipulumutseni!”
31 εὐθέως δὲ ὁ Ἰησοῦς ἐκτείνας τὴν χεῖρα ἐπελάβετο αὐτοῦ καὶ λέγει αὐτῷ Ὀλιγόπιστε, εἰς τί ἐδίστασας;
Ndipo mofulumira Yesu anatambasula dzanja lake namugwira iye, nati, “Iwe wachikhulupiriro chochepa, bwanji unakayika?”
32 καὶ ἀναβάντων αὐτῶν εἰς τὸ πλοῖον ἐκόπασεν ὁ ἄνεμος.
Ndipo atalowa mʼbwato mphepo inaleka.
33 οἱ δὲ ἐν τῷ πλοίῳ προσεκύνησαν αὐτῷ λέγοντες Ἀληθῶς Θεοῦ Υἱὸς εἶ.
Pamenepo amene anali mʼbwato anamulambira Iye, nati, “Zoonadi, Inu ndinu Mwana wa Mulungu.”
34 Καὶ διαπεράσαντες ἦλθον ἐπὶ τὴν γῆν εἰς Γεννησαρέτ.
Atawoloka, anafika ku Genesareti.
35 καὶ ἐπιγνόντες αὐτὸν οἱ ἄνδρες τοῦ τόπου ἐκείνου ἀπέστειλαν εἰς ὅλην τὴν περίχωρον ἐκείνην, καὶ προσήνεγκαν αὐτῷ πάντας τοὺς κακῶς ἔχοντας,
Anthu akumeneko atamuzindikira Yesu, iwo anatumiza mawu kwa onse ozungulira deralo. Anthu anabwera ndi odwala awo onse kwa Iye.
36 καὶ παρεκάλουν αὐτὸν ἵνα μόνον ἅψωνται τοῦ κρασπέδου τοῦ ἱματίου αὐτοῦ· καὶ ὅσοι ἥψαντο διεσώθησαν.
Ndipo anamupempha alole kuti akhudze mphonje ya mkanjo wake, ndipo onse amene anamukhudza anachiritsidwa.