< Κατα Λουκαν 4 >
1 Ἰησοῦς δὲ πλήρης Πνεύματος Ἁγίου ὑπέστρεψεν ἀπὸ τοῦ Ἰορδάνου, καὶ ἤγετο ἐν τῷ Πνεύματι ἐν τῇ ἐρήμῳ
Yesu, wodzazidwa ndi Mzimu Woyera, anachoka ku mtsinje wa Yorodani ndipo anatsogozedwa ndi Mzimu Woyerayo kupita ku chipululu,
2 ἡμέρας τεσσεράκοντα πειραζόμενος ὑπὸ τοῦ διαβόλου. Καὶ οὐκ ἔφαγεν οὐδὲν ἐν ταῖς ἡμέραις ἐκείναις, καὶ συντελεσθεισῶν αὐτῶν ἐπείνασεν.
kumene anayesedwa ndi mdierekezi masiku makumi anayi. Sanadye kena kalikonse pa masiku amenewo, ndipo pa mapeto pake anamva njala.
3 εἶπεν δὲ αὐτῷ ὁ διάβολος Εἰ Υἱὸς εἶ τοῦ Θεοῦ, εἰπὲ τῷ λίθῳ τούτῳ ἵνα γένηται ἄρτος.
Mdierekezi anati kwa Iye, “Ngati ndiwe Mwana wa Mulungu, uza mwala uwu kuti usanduke buledi.”
4 καὶ ἀπεκρίθη πρὸς αὐτὸν ὁ Ἰησοῦς Γέγραπται ὅτι Οὐκ ἐπ’ ἄρτῳ μόνῳ ζήσεται ὁ ἄνθρωπος.
Yesu anayankha kuti, “Zalembedwa: ‘Munthu sadzakhala ndi moyo ndi chakudya chokha.’”
5 Καὶ ἀναγαγὼν αὐτὸν ἔδειξεν αὐτῷ πάσας τὰς βασιλείας τῆς οἰκουμένης ἐν στιγμῇ χρόνου.
Mdierekezi anamutengera Iye pamalo aatali ndipo mʼkamphindi namuonetsa maufumu onse a dziko lapansi.
6 καὶ εἶπεν αὐτῷ ὁ διάβολος Σοὶ δώσω τὴν ἐξουσίαν ταύτην ἅπασαν καὶ τὴν δόξαν αὐτῶν, ὅτι ἐμοὶ παραδέδοται καὶ ᾧ ἐὰν θέλω δίδωμι αὐτήν·
Ndipo anati kwa Iye, “Ndidzakupatsani ulamuliro ndi ulemerero wawo; pakuti anandipatsa ine, ndipo ndingathe kupereka kwa aliyense amene ndikufuna.
7 σὺ οὖν ἐὰν προσκυνήσῃς ἐνώπιον ἐμοῦ, ἔσται σοῦ πᾶσα.
Ngati mutandilambira, zonsezi zidzakhala zanu.”
8 καὶ ἀποκριθεὶς ὁ Ἰησοῦς εἶπεν αὐτῷ Γέγραπται Προσκυνήσεις Κύριον τὸν Θεόν σου καὶ αὐτῷ μόνῳ λατρεύσεις.
Yesu anayankha kuti, “Zalembedwa: ‘Pembedza Yehova Mulungu wako ndi kumutumikira Iye yekha.’”
9 Ἤγαγεν δὲ αὐτὸν εἰς Ἱερουσαλὴμ καὶ ἔστησεν ἐπὶ τὸ πτερύγιον τοῦ ἱεροῦ, καὶ εἶπεν αὐτῷ Εἰ Υἱὸς εἶ τοῦ Θεοῦ, βάλε σεαυτὸν ἐντεῦθεν κάτω·
Mdierekezi anapita naye ku Yerusalemu namuyimiritsa pamwamba penipeni pa Nyumba ya Mulungu. Ndipo anati, “Ngati ndinu Mwana wa Mulungu dziponyeni nokha pansi kuchokera pano.
10 γέγραπται γὰρ ὅτι τοῖς ἀγγέλοις αὐτοῦ ἐντελεῖται περὶ σοῦ τοῦ διαφυλάξαι σε,
Pakuti kwalembedwa, “Adzalamulira angelo ake za iwe kuti akutchinjirize mosamala;
11 καὶ ὅτι ἐπὶ χειρῶν ἀροῦσίν σε μή ποτε προσκόψῃς πρὸς λίθον τὸν πόδα σου.
ndipo adzakunyamula ndi manja awo, kuti phazi lako lisagunde pa mwala.”
12 καὶ ἀποκριθεὶς εἶπεν αὐτῷ ὁ Ἰησοῦς ὅτι Εἴρηται Οὐκ ἐκπειράσεις Κύριον τὸν Θεόν σου.
Yesu anayankha kuti, “Mawu akuti, ‘Musamuyese Yehova Mulungu wanu.’”
13 Καὶ συντελέσας πάντα πειρασμὸν ὁ διάβολος ἀπέστη ἀπ’ αὐτοῦ ἄχρι καιροῦ.
Mdierekezi atamaliza mayesero awa onse, anamusiya Iye kufikira atapeza mpata wina.
14 Καὶ ὑπέστρεψεν ὁ Ἰησοῦς ἐν τῇ δυνάμει τοῦ Πνεύματος εἰς τὴν Γαλιλαίαν· καὶ φήμη ἐξῆλθεν καθ’ ὅλης τῆς περιχώρου περὶ αὐτοῦ.
Yesu anabwerera ku Galileya mu mphamvu ya Mzimu Woyera, ndipo mbiri yake inafalikira ku madera onse a ku midzi.
15 καὶ αὐτὸς ἐδίδασκεν ἐν ταῖς συναγωγαῖς αὐτῶν, δοξαζόμενος ὑπὸ πάντων.
Iye ankaphunzitsa mʼmasunagoge awo, ndipo aliyense ankamulemekeza.
16 Καὶ ἦλθεν εἰς Ναζαρά, οὗ ἦν τεθραμμένος, καὶ εἰσῆλθεν κατὰ τὸ εἰωθὸς αὐτῷ ἐν τῇ ἡμέρᾳ τῶν σαββάτων εἰς τὴν συναγωγήν, καὶ ἀνέστη ἀναγνῶναι.
Iye anapita ku Nazareti, kumene anakulira, ndipo pa tsiku la Sabata anakalowa mʼsunagoge, monga mwa chikhalidwe chake. Ndipo anayimirira kuti awerenge malemba.
17 καὶ ἐπεδόθη αὐτῷ βιβλίον τοῦ προφήτου Ἡσαΐου, καὶ ἀνοίξας τὸ βιβλίον εὗρεν τὸν τόπον οὗ ἦν γεγραμμένον
Anamupatsa buku la mneneri Yesaya. Atalitsekula, anapeza pamalo pamene panalembedwa kuti,
18 Πνεῦμα Κυρίου ἐπ’ ἐμέ, οὗ εἵνεκεν ἔχρισέν με εὐαγγελίσασθαι πτωχοῖς, ἀπέσταλκέν με κηρῦξαι αἰχμαλώτοις ἄφεσιν καὶ τυφλοῖς ἀνάβλεψιν, ἀποστεῖλαι τεθραυσμένους ἐν ἀφέσει,
“Mzimu wa Ambuye ali pa Ine; chifukwa wandidzoza kuti ndilalikire Uthenga Wabwino kwa osauka. Wandituma kuti ndilalikire kwa a mʼndende kuti amasulidwe ndi kwa osaona kuti apenyenso, kumasulidwa kwa osautsidwa,
19 κηρῦξαι ἐνιαυτὸν Κυρίου δεκτόν.
ndi kulalikira za nthawi imene Ambuye adzakomere mtima anthu awo.”
20 καὶ πτύξας τὸ βιβλίον ἀποδοὺς τῷ ὑπηρέτῃ ἐκάθισεν· καὶ πάντων οἱ ὀφθαλμοὶ ἐν τῇ συναγωγῇ ἦσαν ἀτενίζοντες αὐτῷ.
Kenaka Iye anatseka bukulo, nalibwezera kwa wotumikira ndipo anakakhala pansi. Maso a aliyense mʼsunagogemo anali pa Iye,
21 ἤρξατο δὲ λέγειν πρὸς αὐτοὺς ὅτι Σήμερον πεπλήρωται ἡ γραφὴ αὕτη ἐν τοῖς ὠσὶν ὑμῶν.
ndipo anawawuza kuti, “Lero malemba awa akwaniritsidwa mmene mwamveramu.”
22 καὶ πάντες ἐμαρτύρουν αὐτῷ καὶ ἐθαύμαζον ἐπὶ τοῖς λόγοις τῆς χάριτος τοῖς ἐκπορευομένοις ἐκ τοῦ στόματος αὐτοῦ, καὶ ἔλεγον Οὐχὶ υἱός ἐστιν Ἰωσὴφ οὗτος;
Onse anayankhula zabwino za Iye ndipo anadabwa ndi mawu ogwira moyo amene anatuluka mʼkamwa mwake. Iwo anafunsa kuti, “Kodi uyu si mwana wa Yosefe?”
23 καὶ εἶπεν πρὸς αὐτούς Πάντως ἐρεῖτέ μοι τὴν παραβολὴν ταύτην Ἰατρέ, θεράπευσον σεαυτόν· ὅσα ἠκούσαμεν γενόμενα εἰς τὴν Καφαρναοὺμ, ποίησον καὶ ὧδε ἐν τῇ πατρίδι σου.
Yesu anawawuza kuti, “Zoonadi, mudzandiwuza mwambi uwu: Singʼanga, dzichiritse wekha! Chitanso mʼmudzi wa kwanu kuno zimene ife tamva kuti Iwe unazichita ku Kaperenawo.”
24 εἶπεν δέ Ἀμὴν λέγω ὑμῖν ὅτι οὐδεὶς προφήτης δεκτός ἐστιν ἐν τῇ πατρίδι αὐτοῦ.
Iye anapitiriza kuti, “Zoonadi, ndikukuwuzani kuti palibe mneneri amene amavomerezedwa ku mudzi kwawo.
25 ἐπ’ ἀληθείας δὲ λέγω ὑμῖν, πολλαὶ χῆραι ἦσαν ἐν ταῖς ἡμέραις Ἡλείου ἐν τῷ Ἰσραήλ, ὅτε ἐκλείσθη ὁ οὐρανὸς ἐπὶ ἔτη τρία καὶ μῆνας ἕξ, ὡς ἐγένετο λιμὸς μέγας ἐπὶ πᾶσαν τὴν γῆν,
Ine ndikukutsimikizirani kunali amayi ambiri amasiye mu Israeli mʼnthawi ya Eliya, kumwamba kutatsekedwa kwa zaka zitatu ndi theka ndipo kunali njala yayikulu mʼdziko lonselo.
26 καὶ πρὸς οὐδεμίαν αὐτῶν ἐπέμφθη Ἡλείας εἰ μὴ εἰς Σάρεπτα τῆς Σιδωνίας πρὸς γυναῖκα χήραν.
Komabe Eliya sanatumidwe kwa mmodzi mwa iwo, koma kwa mkazi wamasiye wa ku Zerefati ku chigawo cha Sidoni.
27 καὶ πολλοὶ λεπροὶ ἦσαν ἐν τῷ Ἰσραὴλ ἐπὶ Ἑλισαίου τοῦ προφήτου, καὶ οὐδεὶς αὐτῶν ἐκαθαρίσθη εἰ μὴ Ναιμὰν ὁ Σύρος.
Ndipo kunali akhate ambiri ku Israeli mʼnthawi ya mneneri Elisa, koma panalibe mmodzi mwa iwo anachiritsidwa kupatula Naamani wa ku Siriya.”
28 καὶ ἐπλήσθησαν πάντες θυμοῦ ἐν τῇ συναγωγῇ ἀκούοντες ταῦτα,
Anthu onse mʼsunagogemo anapsa mtima atamva izi.
29 καὶ ἀναστάντες ἐξέβαλον αὐτὸν ἔξω τῆς πόλεως, καὶ ἤγαγον αὐτὸν ἕως ὀφρύος τοῦ ὄρους ἐφ’ οὗ ἡ πόλις ᾠκοδόμητο αὐτῶν, ὥστε κατακρημνίσαι αὐτόν·
Anayimirira namutulutsira kunja kwa mzindawo, ndipo anamutengera pamwamba pa phiri pamene mzindawo unamangidwapo, ndi cholinga chakuti amuponyere ku phompho.
30 αὐτὸς δὲ διελθὼν διὰ μέσου αὐτῶν ἐπορεύετο.
Koma Iye anangoyenda pakati pa gulu la anthulo nachokapo.
31 Καὶ κατῆλθεν εἰς Καφαρναοὺμ πόλιν τῆς Γαλιλαίας. καὶ ἦν διδάσκων αὐτοὺς ἐν τοῖς σάββασιν·
Kenaka Iye anapita ku Kaperenawo, mudzi wa ku Galileya, ndipo pa Sabata anayamba kuphunzitsa anthu.
32 καὶ ἐξεπλήσσοντο ἐπὶ τῇ διδαχῇ αὐτοῦ, ὅτι ἐν ἐξουσίᾳ ἦν ὁ λόγος αὐτοῦ.
Iwo anadabwa ndi chiphunzitso chake chifukwa uthenga wake unali ndi ulamuliro.
33 καὶ ἐν τῇ συναγωγῇ ἦν ἄνθρωπος ἔχων πνεῦμα δαιμονίου ἀκαθάρτου, καὶ ἀνέκραξεν φωνῇ μεγάλῃ
Mʼsunagogemo munali munthu wogwidwa ndi mzimu woyipa. Iye analira ndi mawu akulu, akuti
34 Ἔα, τί ἡμῖν καὶ σοί, Ἰησοῦ Ναζαρηνέ; ἦλθες ἀπολέσαι ἡμᾶς; οἶδά σε τίς εἶ, ὁ Ἅγιος τοῦ Θεοῦ.
“Aa! Kodi mukufuna chiyani kwa ife, Yesu wa ku Nazareti? Kodi mwabwera kudzatiwononga? Ndikudziwa kuti ndinu ndani, ndinu Woyerayo wa Mulungu!”
35 καὶ ἐπετίμησεν αὐτῷ ὁ Ἰησοῦς λέγων Φιμώθητι καὶ ἔξελθε ἀπ’ αὐτοῦ. καὶ ῥίψαν αὐτὸν τὸ δαιμόνιον εἰς τὸ μέσον ἐξῆλθεν ἀπ’ αὐτοῦ μηδὲν βλάψαν αὐτόν.
Yesu anachidzudzula kwambiri nati, “Khala chete! Tuluka mwa iye.” Chiwandacho chinamugwetsa munthuyo pansi pamaso pa onse ndipo chinatuluka wosamupweteka.
36 καὶ ἐγένετο θάμβος ἐπὶ πάντας, καὶ συνελάλουν πρὸς ἀλλήλους λέγοντες Τίς ὁ λόγος οὗτος, ὅτι ἐν ἐξουσίᾳ καὶ δυνάμει ἐπιτάσσει τοῖς ἀκαθάρτοις πνεύμασιν καὶ ἐξέρχονται;
Anthu onse anadabwa ndipo anati kwa wina ndi mnzake, “Kodi chiphunzitso ichi ndi chotani? Ndi ulamuliro ndi mphamvu Iye akulamulira mizimu yoyipa ndipo ikutuluka!”
37 καὶ ἐξεπορεύετο ἦχος περὶ αὐτοῦ εἰς πάντα τόπον τῆς περιχώρου.
Ndipo mbiri yake inafalikira madera onse ozungulira.
38 Ἀναστὰς δὲ ἀπὸ τῆς συναγωγῆς εἰσῆλθεν εἰς τὴν οἰκίαν Σίμωνος. πενθερὰ δὲ τοῦ Σίμωνος ἦν συνεχομένη πυρετῷ μεγάλῳ, καὶ ἠρώτησαν αὐτὸν περὶ αὐτῆς.
Yesu anatuluka mʼsunagoge ndipo anapita kwa Simoni. Tsopano mpongozi wake wa Simoni amadwala malungo akulu, ndipo anamupempha Yesu kuti amuthandize.
39 καὶ ἐπιστὰς ἐπάνω αὐτῆς ἐπετίμησεν τῷ πυρετῷ, καὶ ἀφῆκεν αὐτήν· παραχρῆμα δὲ ἀναστᾶσα διηκόνει αὐτοῖς.
Ndipo anawerama nadzudzula malungowo ndipo anamusiya. Anadzuka nthawi yomweyo nayamba kuwatumikira.
40 Δύνοντος δὲ τοῦ ἡλίου ἅπαντες ὅσοι εἶχον ἀσθενοῦντας νόσοις ποικίλαις ἤγαγον αὐτοὺς πρὸς αὐτόν· ὁ δὲ ἑνὶ ἑκάστῳ αὐτῶν τὰς χεῖρας ἐπιτιθεὶς ἐθεράπευεν αὐτούς.
Pamene dzuwa linkalowa, anthu anabweretsa kwa Yesu onse amene anali ndi matenda osiyanasiyana, ndipo atasanjika manja ake pa aliyense, anachiritsidwa.
41 ἐξήρχετο δὲ καὶ δαιμόνια ἀπὸ πολλῶν, κραυγάζοντα καὶ λέγοντα ὅτι Σὺ εἶ ὁ Υἱὸς τοῦ Θεοῦ. καὶ ἐπιτιμῶν οὐκ εἴα αὐτὰ λαλεῖν, ὅτι ᾔδεισαν τὸν Χριστὸν αὐτὸν εἶναι.
Komanso ziwanda zinkatuluka mwa anthu ambiri, zikufuwula kuti, “Inu ndinu Mwana wa Mulungu!” Koma Iye anazidzudzula ndipo sanazilole kuyankhula chifukwa zimadziwa kuti Iye ndi Khristu.
42 Γενομένης δὲ ἡμέρας ἐξελθὼν ἐπορεύθη εἰς ἔρημον τόπον· καὶ οἱ ὄχλοι ἐπεζήτουν αὐτόν, καὶ ἦλθον ἕως αὐτοῦ, καὶ κατεῖχον αὐτὸν τοῦ μὴ πορεύεσθαι ἀπ’ αὐτῶν.
Kutacha, Yesu anapita ku malo a yekha. Anthu ankamufunafuna Iye ndipo pamene anafika kumene anali, anthuwo anayesetsa kumuletsa kuti asawachokere.
43 ὁ δὲ εἶπεν πρὸς αὐτοὺς ὅτι Καὶ ταῖς ἑτέραις πόλεσιν εὐαγγελίσασθαί με δεῖ τὴν βασιλείαν τοῦ Θεοῦ, ὅτι ἐπὶ τοῦτο ἀπεστάλην.
Koma Iye anati, “Ine ndikuyenera kulalikira Uthenga Wabwino wa ufumu wa Mulungu ku mizinda inanso chifukwa ichi ndi chimene ananditumira.”
44 καὶ ἦν κηρύσσων εἰς τὰς συναγωγὰς τῆς Ἰουδαίας.
Ndipo Iye anapitirirabe kulalikira mʼmasunagoge a ku Yudeya.