< Προς Κορινθιους Β΄ 11 >

1 οφελον ανειχεσθε μου μικρον τη αφροσυνη αλλα και ανεχεσθε μου
Ndikukhulupirira kuti mupirira nako pangʼono kupusa kwanga. Chonde tandipirirani!
2 ζηλω γαρ υμας θεου ζηλω ηρμοσαμην γαρ υμας ενι ανδρι παρθενον αγνην παραστησαι τω χριστω
Nsanje imene ndimakuchitirani ndi yofanana ndi ya Mulungu. Ndinakulonjezani mwamuna mmodzi yekha, mwamunayo ndiye Khristu, kuti ndidzakuperekeni inuyo kwa Iyeyo monga namwali wangwiro.
3 φοβουμαι δε μηπως ως ο οφις ευαν εξηπατησεν εν τη πανουργια αυτου ουτως φθαρη τα νοηματα υμων απο της απλοτητος της εις τον χριστον
Koma ndikuopa kuti monga Hava ananyengedwa ndi kuchenjera kwa njoka, mitima yanunso ingasocheretsedwe kuleka nʼkudzipereka moona mtima ndi modzipereka kwenikweni kwa Khristu.
4 ει μεν γαρ ο ερχομενος αλλον ιησουν κηρυσσει ον ουκ εκηρυξαμεν η πνευμα ετερον λαμβανετε ο ουκ ελαβετε η ευαγγελιον ετερον ο ουκ εδεξασθε καλως ανειχεσθε
Pakuti ngati wina abwera kwa inu nalalikira Yesu wina wosiyana ndi Yesu amene tinamulalikira, kapena ngati mulandira mzimu wina wosiyana ndi Mzimu amene munalandira, kapena uthenga wabwino wina wosiyana ndi umene munawuvomereza, inuyo mumangolandira mosavuta.
5 λογιζομαι γαρ μηδεν υστερηκεναι των υπερλιαν αποστολων
Komatu sindikuganiza kuti ndine wotsika kwambiri kwa “atumwi apamwamba.”
6 ει δε και ιδιωτης τω λογω αλλ ου τη γνωσει αλλ εν παντι φανερωθεντες εν πασιν εις υμας
Mwina ndikhoza kukhala wosaphunzitsidwa kayankhulidwe, koma ndili ndi chidziwitso. Izi tinakufotokozerani momveka bwinobwino.
7 η αμαρτιαν εποιησα εμαυτον ταπεινων ινα υμεις υψωθητε οτι δωρεαν το του θεου ευαγγελιον ευηγγελισαμην υμιν
Kodi linali tchimo kwa ine kudzichepetsa nʼcholinga chakuti ndikukwezeni pamene ndinkalalikira Uthenga Wabwino wa Mulungu kwa inu mwaulere?
8 αλλας εκκλησιας εσυλησα λαβων οψωνιον προς την υμων διακονιαν
Ndinkalanda mipingo ina pomalandira thandizo kwa iwo kuti ndikutumikireni.
9 και παρων προς υμας και υστερηθεις ου κατεναρκησα ουδενος το γαρ υστερημα μου προσανεπληρωσαν οι αδελφοι ελθοντες απο μακεδονιας και εν παντι αβαρη υμιν εμαυτον ετηρησα και τηρησω
Ndipo pamene ndinali pakati panu, nditasowa kanthu, sindinalemetse munthu aliyense, pakuti abale ena amene anachokera ku Makedoniya anandipatsa zonse zimene ndinkazisowa. Ndayesetsa kuti ndisakhale cholemetsa kwa inu mʼnjira ina iliyonse, ndipo ndidzapitiriza kutero.
10 εστιν αληθεια χριστου εν εμοι οτι η καυχησις αυτη ου φραγησεται εις εμε εν τοις κλιμασιν της αχαιας
Kunena moona mtima molingana ndi chilungamo cha Khristu chimene chili mwa ine, palibe amene angandiletse kudzitamandira mʼzigawo za ku Akaya.
11 διατι οτι ουκ αγαπω υμας ο θεος οιδεν
Nʼchifukwa chiyani ndikutero? Kodi nʼchifukwa choti sindikukondani? Mulungu akudziwa kuti ndimakukondani!
12 ο δε ποιω και ποιησω ινα εκκοψω την αφορμην των θελοντων αφορμην ινα εν ω καυχωνται ευρεθωσιν καθως και ημεις
Ndipo ndipitiriza kuchita zomwe ndikuchitazi nʼcholinga chakuti ndisapereke mpata kwa amene akufuna kupezera mwayi woti afanane nafe pa zinthu zimene iwowo amadzitamandira.
13 οι γαρ τοιουτοι ψευδαποστολοι εργαται δολιοι μετασχηματιζομενοι εις αποστολους χριστου
Pakuti anthu oterewa ndi atumwi onama, antchito achinyengo, odzizimbayitsa ngati atumwi a Khristu.
14 και ου θαυμαστον αυτος γαρ ο σατανας μετασχηματιζεται εις αγγελον φωτος
Sizododometsa zimenezi, pakuti Satana mwini amadzizimbayitsa kuoneka ngati mngelo wowunikira anthu.
15 ου μεγα ουν ει και οι διακονοι αυτου μετασχηματιζονται ως διακονοι δικαιοσυνης ων το τελος εσται κατα τα εργα αυτων
Nʼzosadabwitsa tsono ngati atumiki ake akudzizimbayitsa ngati otumikira chilungamo. Matsiriziro awo adzalandira zoyenerana ndi ntchito zawo.
16 παλιν λεγω μη τις με δοξη αφρονα ειναι ει δε μη γε καν ως αφρονα δεξασθε με ινα καγω μικρον τι καυχησωμαι
Ndibwereze kunena kuti, wina aliyense asandiyese chitsiru. Koma ngati mutero, mundilandire monga mmene mukhoza kulandirira chitsiru, kuti ndinyadirepo pangʼono.
17 ο λαλω ου λαλω κατα κυριον αλλ ως εν αφροσυνη εν ταυτη τη υποστασει της καυχησεως
Kudzinyadira kwangaku, sindikuyankhula monga mmene Ambuye akufunira koma ngati chitsiru.
18 επει πολλοι καυχωνται κατα την σαρκα καγω καυχησομαι
Popeza ambiri akudzitama monga dziko lapansi limachitira, inenso ndidzitamanso.
19 ηδεως γαρ ανεχεσθε των αφρονων φρονιμοι οντες
Inu mumalolera kukhala ndi zitsiru mokondwera chifukwa mumati ndinu anzeru!
20 ανεχεσθε γαρ ει τις υμας καταδουλοι ει τις κατεσθιει ει τις λαμβανει ει τις επαιρεται ει τις υμας εις προσωπον δερει
Kunena zoona mumangololera aliyense; amene amakusandutsani akapolo, kapena amene amakudyerani masuku pamutu, kapena amene amakupezererani, kapena amene amadzitukumula, kapena amene amakumenyani khofi.
21 κατα ατιμιαν λεγω ως οτι ημεις ησθενησαμεν εν ω δ αν τις τολμα εν αφροσυνη λεγω τολμω καγω
Ndikuvomera mwamanyazi kuti ife sitinali olimba mtima kuti nʼkuchita zinthu zimenezi. Ndikuyankhula ngati chitsiru kuti chimene wina aliyense akhoza kudzitama nacho, Inenso ndikhoza kudzitama nachonso.
22 εβραιοι εισιν καγω ισραηλιται εισιν καγω σπερμα αβρααμ εισιν καγω
Kodi iwo ndi Ahebri? Inenso ndine Mhebri. Kodi iwo ndi Aisraeli? Inenso ndine Mwisraeli. Kodi iwo ndi zidzukulu za Abrahamu? Inenso ndine mdzukulu wa Abrahamu.
23 διακονοι χριστου εισιν παραφρονων λαλω υπερ εγω εν κοποις περισσοτερως εν πληγαις υπερβαλλοντως εν φυλακαις περισσοτερως εν θανατοις πολλακις
Kodi iwo ndi atumiki a Khristu? Ndikuyankhula ngati wamisala. Ine ndine woposa iwowo. Ndagwira ntchito kwambiri kupambana iwo, ndakhala ndikuyikidwa mʼndende kawirikawiri, ndakwapulidwapo kwambiri, kawirikawiri ndinali pafupi kufa.
24 υπο ιουδαιων πεντακις τεσσαρακοντα παρα μιαν ελαβον
Andikwapulapo kasanu zikoti zija za Ayuda, makumi anayi kuchotsapo chimodzi.
25 τρις ερραβδισθην απαξ ελιθασθην τρις εναυαγησα νυχθημερον εν τω βυθω πεποιηκα
Katatu anandimenya ndi ndodo. Kamodzi anandigendapo miyala. Katatu sitima yathu ya panyanja inasweka, ndipo ndinakhala usiku ndi usana ndi kuyandama pa nyanja.
26 οδοιποριαις πολλακις κινδυνοις ποταμων κινδυνοις ληστων κινδυνοις εκ γενους κινδυνοις εξ εθνων κινδυνοις εν πολει κινδυνοις εν ερημια κινδυνοις εν θαλασση κινδυνοις εν ψευδαδελφοις
Ndakhala ndikuyenda maulendo ataliatali. Moyo wanga wakhala ukukumana ndi zoopsa pa mitsinje, zoopsa za achifwamba, zoopsa zochokera kwa abale anga Ayuda, zoopsa zochokera kwa anthu akunja. Ndinakumana ndi zoopsa mʼmizinda, mʼmidzi, pa nyanja, ndi pakati pa abale onyenga.
27 εν κοπω και μοχθω εν αγρυπνιαις πολλακις εν λιμω και διψει εν νηστειαις πολλακις εν ψυχει και γυμνοτητι
Ndakhala ndikugwira ntchito molimbika ndipo kawirikawiri ndakhala ndikuchezera usiku wonse osagona. Ndakhala ndikumva njala ndi ludzu ndipo kawirikawiri ndakhala wopanda chakudya. Ndakhala ndi kuzizidwa ndi wosowa zovala.
28 χωρις των παρεκτος η επισυστασις μου η καθ ημεραν η μεριμνα πασων των εκκλησιων
Kuwonjezera pa zonsezi, tsiku ndi tsiku ndimakhala pa chipsinjo cha nkhawa ya mipingo yonse.
29 τις ασθενει και ουκ ασθενω τις σκανδαλιζεται και ουκ εγω πυρουμαι
Ndani ali wofowoka, ine wosakhala naye mʼkufowoka kwakeko? Ndani amene mnzake amuchimwitsa, ine wosavutika mu mtima?
30 ει καυχασθαι δει τα της ασθενειας μου καυχησομαι
Ngati nʼkoyenera kudzitamandira, ndidzadzitamandira pa zinthu zimene zimaonetsa kufowoka kwanga.
31 ο θεος και πατηρ του κυριου ημων ιησου χριστου οιδεν ο ων ευλογητος εις τους αιωνας οτι ου ψευδομαι (aiōn g165)
Mulungu, Atate a Ambuye Yesu, amene tiyenera kumutamanda nthawi zonse, akudziwa kuti sindikunama. (aiōn g165)
32 εν δαμασκω ο εθναρχης αρετα του βασιλεως εφρουρει την δαμασκηνων πολιν πιασαι με θελων
Ku Damasiko, bwanamkubwa woyimira Mfumu Areta, anayika alonda kuzungulira mzinda wonse kuti andigwire.
33 και δια θυριδος εν σαργανη εχαλασθην δια του τειχους και εξεφυγον τας χειρας αυτου
Koma abale anandiyika mʼdengu nanditsitsira pa chipupa kudzera pa zenera la mpandawo, motero ndinapulumuka mʼmanja mwake.

< Προς Κορινθιους Β΄ 11 >