< Prediger 7 >
1 Ein guter Ruf ist besser denn gute Salbe, und der Tag des Todes denn der Tag der Geburt.
Mbiri yabwino ndi yopambana mafuta onunkhira bwino, ndipo tsiku lomwalira ndi lopambana tsiku lobadwa.
2 Es ist besser in das Klagehaus gehen, denn in ein Trinkhaus; in jenem ist das Ende aller Menschen, und der Lebendige nimmt's zu Herzen.
Kuli bwino kupita ku nyumba yamaliro kusiyana ndi kupita ku nyumba yamadyerero: Pakuti imfa ndiye mathero a munthu aliyense; anthu amoyo azichisunga chimenechi mʼmitima mwawo.
3 Es ist Trauern besser als Lachen; denn durch Trauern wird das Herz gebessert.
Chisoni nʼchabwino kusiyana ndi kuseka, pakuti nkhope yakugwa ndi yabwino chifukwa imakonza mtima.
4 Das Herz der Weisen ist im Klagehause, und das Herz der Narren im Hause der Freude.
Mtima wa munthu wanzeru nthawi zonse umalingalira za imfa, koma mitima ya zitsiru imalingalira za chisangalalo.
5 Es ist besser hören das Schelten der Weisen, denn hören den Gesang der Narren.
Kuli bwino kumva kudzudzula kwa munthu wanzeru kusiyana ndi kumvera mayamiko a zitsiru.
6 Denn das Lachen der Narren ist wie das Krachen der Dornen unter den Töpfen; und das ist auch eitel.
Kuseka kwa zitsiru kuli ngati kuthetheka kwa moto kunsi kwa mʼphika, izinso ndi zopandapake.
7 Ein Widerspenstiger macht einen Weisen unwillig und verderbt ein mildtätiges Herz.
Kuzunza ena kumasandutsa munthu wanzeru kukhala chitsiru, ndipo chiphuphu chimawononga mtima.
8 Das Ende eines Dinges ist besser denn sein Anfang. Ein geduldiger Geist ist besser denn ein hoher Geist.
Mathero ake a chinthu ndi abwino kupambana chiyambi chake, ndipo kufatsa nʼkwabwino kupambana kudzikuza.
9 Sei nicht schnellen Gemütes zu zürnen; denn Zorn ruht im Herzen eines Narren.
Usamafulumire kukwiya mu mtima mwako, pakuti mkwiyo ndi bwenzi la zitsiru.
10 Sprich nicht: Was ist's, daß die vorigen Tage besser waren als diese? denn du fragst solches nicht weislich.
Usamafunse kuti, “Nʼchifukwa chiyani masiku amakedzana anali abwino kupambana masiku ano?” pakuti si chinthu chanzeru kufunsa mafunso oterewa.
11 Weisheit ist gut mit einem Erbgut und hilft, daß sich einer der Sonne freuen kann.
Nzeru ngati cholowa, ndi chinthu chabwino ndipo imapindulitsa wamoyo aliyense pansi pano.
12 Denn die Weisheit beschirmt, so beschirmt Geld auch; aber die Weisheit gibt das Leben dem, der sie hat.
Nzeru ndi chitetezo, monganso ndalama zili chitetezo, koma phindu la chidziwitso ndi ili: kuti nzeru zimasunga moyo wa munthu amene ali nazo nzeruzo.
13 Siehe an die Werke Gottes; denn wer kann das schlicht machen, was er krümmt?
Taganizirani zimene Mulungu wazichita: ndani angathe kuwongola chinthu chimene Iye anachipanga chokhota?
14 Am guten Tage sei guter Dinge, und den bösen Tag nimm auch für gut; denn diesen schafft Gott neben jenem, daß der Mensch nicht wissen soll, was künftig ist.
Pamene zinthu zili bwino, sangalala; koma pamene zinthu sizili bwino, ganizira bwino: Mulungu ndiye anapanga nthawi yabwinoyo, ndiponso nthawi imene si yabwinoyo. Choncho munthu sangathe kuzindikira chilichonse cha mʼtsogolo mwake.
15 Allerlei habe ich gesehen in den Tagen meiner Eitelkeit. Da ist ein Gerechter, und geht unter mit seiner Gerechtigkeit; und ein Gottloser, der lange lebt in seiner Bosheit.
Pa moyo wanga wopanda phinduwu ndaona zinthu ziwiri izi: munthu wolungama akuwonongeka mʼchilungamo chake, ndipo munthu woyipa akukhala moyo wautali mʼzoyipa zake.
16 Sei nicht allzu gerecht und nicht allzu weise, daß du dich nicht verderbest.
Usakhale wolungama kwambiri kapena wanzeru kwambiri, udziwonongerenji wekha?
17 Sei nicht allzu gottlos und narre nicht, daß du nicht sterbest zur Unzeit.
Usakhale woyipa kwambiri, ndipo usakhale chitsiru, uferenji nthawi yako isanakwane?
18 Es ist gut, daß du dies fassest und jenes auch nicht aus deiner Hand lässest; denn wer Gott fürchtet, der entgeht dem allem.
Nʼkwabwino kuti utsate njira imodzi, ndipo usataye njira inayo. Munthu amene amaopa Mulungu adzapewa zinthu ziwiri zonsezi.
19 Die Weisheit stärkt den Weisen mehr denn zehn Gewaltige, die in der Stadt sind.
Nzeru zimapereka mphamvu zambiri kwa munthu wanzeru kupambana olamulira khumi a mu mzinda.
20 Denn es ist kein Mensch so gerecht auf Erden, daß er Gutes tue und nicht sündige.
Palibe munthu wolungama pa dziko lapansi amene amachita zabwino zokhazokha ndipo sachimwa.
21 Gib auch nicht acht auf alles, was man sagt, daß du nicht hören müssest deinen Knecht dir fluchen.
Usamamvetsere mawu onse amene anthu amayankhula, mwina udzamva wantchito wako akukutukwana,
22 Denn dein Herz weiß, daß du andern oftmals geflucht hast.
pakuti iwe ukudziwa mu mtima mwako kuti nthawi zambiri iwenso unatukwanapo ena.
23 Solches alles habe ich versucht mit Weisheit. Ich gedachte, ich will weise sein; sie blieb aber ferne von mir.
Zonsezi ndinaziyesa ndi nzeru zanga ndipo ndinati, “Ine ndatsimikiza mu mtima mwanga kuti ndikhale wanzeru,” koma nzeruyo inanditalikira.
24 Alles, was da ist, das ist ferne und sehr tief; wer will's finden?
Nzeru zimene zilipo, zili kutali ndipo ndi zozama kwambiri, ndani angathe kuzidziwa?
25 Ich kehrte mein Herz, zu erfahren und erforschen und zu suchen Weisheit und Kunst, zu erfahren der Gottlosen Torheit und Irrtum der Tollen,
Kotero ndinayikapo mtima wanga kuti ndidziwe, ndifufuze ndi kumafunafuna nzeru ndi mmene zinthu zimakhalira ndipo ndinafunanso kudziwa kuyipa kwa uchitsiru ndiponso kupusa kwake kwa misala.
26 und fand, daß bitterer sei denn der Tod ein solches Weib, dessen Herz Netz und Strick ist und deren Hände Bande sind. Wer Gott gefällt, der wird ihr entrinnen; aber der Sünder wird durch sie gefangen.
Ndinapeza kanthu kowawa kupambana imfa, mkazi amene ali ngati khoka, amene mtima wake uli ngati khwekhwe, ndipo manja ake ali ngati maunyolo. Munthu amene amakondweretsa Mulungu adzathawa mkaziyo, koma mkaziyo adzakola munthu wochimwa.
27 Schau, das habe ich gefunden, spricht der Prediger, eins nach dem andern, daß ich Erkenntnis fände.
Mlaliki akunena kuti, “Taonani, chimene ndinachipeza ndi ichi: “Kuwonjezera chinthu china pa china kuti ndidziwe mmene zinthu zimachitikira,
28 Und meine Seele sucht noch und hat's nicht gefunden: unter tausend habe ich einen Mann gefunden; aber ein Weib habe ich unter den allen nicht gefunden.
pamene ine ndinali kufufuzabe koma osapeza kanthu, ndinapeza munthu mmodzi wolungama pakati pa anthu 1,000, koma pakati pawo panalibepo mkazi mmodzi wolungama.
29 Allein schaue das: ich habe gefunden, daß Gott den Menschen hat aufrichtig gemacht; aber sie suchen viele Künste.
Chokhacho chimene ndinachipeza ndi ichi: Mulungu analenga munthu, anamupatsa mtima wolungama, koma anthu anatsatira njira zawozawo zambirimbiri.”