< Nehemia 11 >

1 Und die Obersten des Volks wohneten zu Jerusalem. Das andere Volk aber warfen das Los darum, daß unter zehn ein Teil gen Jerusalem in die heilige Stadt zögen, zu wohnen, und neun Teile in den Städten.
Nthawi imeneyo atsogoleri a anthu ankakhala ku Yerusalemu. Tsono anthu ena onse anachita maere kuti apeze munthu mmodzi pa anthu khumi aliwonse kuti azikhala ku Yerusalemu, mzinda wopatulika. Anthu asanu ndi anayi otsalawo ankakhala mʼmidzi yawo.
2 Und das Volk segnete alle die Männer, die freiwillig waren, zu Jerusalem zu wohnen.
Anthu anayamikira onse amene anadzipereka kuti azikhala mu Yerusalemu.
3 Dies sind die Häupter in der Landschaft, die zu Jerusalem wohneten. In den Städten Judas aber wohnete ein jeglicher in seinem Gut, das in ihren Städten war, nämlich Israel, Priester, Leviten, Nethinim und die Kinder der Knechte Salomos.
Aisraeli wamba, ansembe, Alevi, ogwira ntchito ku Nyumba ya Mulungu ndiponso zidzukulu za antchito a Solomoni ankakhala mʼmidzi yawo, aliyense mu dera lake. Koma atsogoleri a chigawo cha Yuda anali atakhazikika mu Yerusalemu.
4 Und zu Jerusalem wohneten etliche der Kinder Juda und Benjamin. Von den Kindern Juda: Athaja, der Sohn Usias, des Sohns Sacharjas, des Sohns Amarjas, des Sohns Sephatjas, des Sohns Mahelaleels, aus den Kindern Parez;
Ku Yerusalemu kunkakhalanso anthu ena a mafuko a Yuda ndi Benjamini. Ena mwa zidzukulu za Yuda ndi awa: Ataya, mwana wa Uziya, mwana wa Zekariya, mwana wa Amariya mwana wa Sefatiya, mwana wa Mahalaleli. Onsewa anali ana a Perezi.
5 und Maeseja, der Sohn Baruchs, des Sohns Chal-Hoses, des Sohns Hasajas, des Sohns Adajas, des Sohns Jojaribs, des Sohns Sacharjas, des Sohns Silonis.
Ena ndi awa: Maaseya mwana wa Baruki, mwana wa Koli-Hoze mwana wa Hazaya, mwana wa Adaya, mwana wa Yowaribu, Zekariya mwana wa Msiloni.
6 Aller Kinder Parez, die zu Jerusalem wohneten, waren vierhundertundachtundsechzig, redliche Leute.
Zidzukulu zonse za Perezi, anthu amphamvu zawo amene ankakhala ku Yerusalemu analipo anthu okwanira 468.
7 Dies sind die Kinder Benjamin: Sallu, der Sohn Mesullams, des Sohns Joeds, des Sohns Pedajas, des Sohns Kolajahs, des Sohns Maesejas, des Sohns Ithiels, des Sohns Jesaias;
Nazi zidzukulu za Benjamini: Salu mwana wa Mesulamu, mwana wa Yowedi, mwana wa Pedaya, mwana wa Kolaya, mwana wa Maaseiya, mwana wa Itieli, mwana wa Yesaiya.
8 und nach ihm Gabai, Sallai, neunhundertundachtundzwanzig.
Abale ake anali Gabayi ndi Salaya. Onse pamodzi anali 928.
9 Und Joel, der Sohn Sichris, war ihr Vorsteher, und Juda, der Sohn Hasnuas, über das andere Teil der Stadt.
Yoweli mwana wa Zikiri ndiye anali mtsogoleri wawo, ndipo Yuda mwana wa Hasenuya ndiye amayangʼanira chigawo cha chiwiri cha mzinda.
10 Von den Priestern wohneten Jedaja, der Sohn Jojaribs, Jachin,
Ansembe anali awa: Yedaya mwana wa Yowaribu; Yakini;
11 Seraja, der Sohn Hilkias, des Sohns Mesullams, des Sohns Zadoks, des Sohns Merajoth, des Sohns Ahitobs, war Fürst im Hause Gottes.
Seraya mwana wa Hilikiya mwana wa Mesulamu, mwana wa Zadoki, mwana wa Merayoti, mwana wa Ahitubi amene anali woyangʼanira Nyumba ya Mulungu,
12 Und seine Brüder, die im Hause schafften, der waren achthundertundzweiundzwanzig. Und Adaja, der Sohn Jerohams, des Sohns Plaljas, des Sohns Amzis, des Sohns Sacharjas, des Sohns Pashurs, des Sohns Malchias,
ndi abale awo, amene ankagwira ntchito ku Nyumba ya Mulungu. Onse pamodzi anali 822. Panalinso Adaya mwana wa Yerohamu, mwana wa Pelaliya, mwana wa Amizi, mwana wa Zekariya, mwana wa Pasi-Huri, mwana wa Malikiya,
13 und seine Brüder, Obersten unter den Vätern, waren zweihundertundzweiundvierzig. Und Amassai, der Sohn Asareels, des Sohns Ahusais, des Sohns Mesillemoths, des Sohns Immers,
ndi abale ake, amene anali atsogoleri a mabanja. Onse pamodzi anali 242. Kuphatikiza apo panalinso Amasisai mwana wa Azaireli, mwana wa Ahazayi, mwana wa Mesilemoti, mwana wa Imeri
14 und seine Brüder, gewaltige Leute, waren hundertundachtundzwanzig. Und ihr Vorsteher war Sabdiel, der Sohn Gedolims.
ndi abale ake. Onse pamodzi anali 128 ndipo anali anthu olimba mtima kwambiri. Mtsogoleri wawo wamkulu anali Zabidieli mwana wa Hagedolimu.
15 Von den Leviten: Semaja, der Sohn Hasubs, des Sohns Asrikams, des Sohns Hasabjas, des Sohns Bunnis,
Alevi anali awa: Semaya mwana wa Hasubu, mwana wa Azirikamu, mwana wa Hasabiya, mwana wa Buni.
16 und Sabthai und Josabad aus der Leviten Obersten an den äußerlichen Geschäften im Hause Gottes,
Sabetayi ndi Yozabadi anali atsogoleri amene ankayangʼanira ntchito ya kunja kwa Nyumba ya Mulungu.
17 und Mathanja, der Sohn Michas, des Sohns Sabdis, des Sohns Assaphs, der das Haupt war, Dank anzuheben zum Gebet, und Bakbukja, der andere unter seinen Brüdern, und Abda, der Sohn Sammuas, des Sohns Galals, des Sohns Jedithuns.
Mataniya mwana wa Mika, mwana wa Zabidi, mwana wa Asafu ndiye anali wotsogolera pa mapemphero achiyamiko. Panalinso Bakibukiya amene anali wachiwiri pakati pa abale ake. Kuwonjezera apo panalinso Abida mwana wa Samuwa, mwana wa Galali, mwana wa Yedutuni.
18 Aller Leviten in der heiligen Stadt waren zweihundertundvierundachtzig.
Alevi onse amene anali mu mzinda woyera analipo 284.
19 Und die Torhüter, Akub und Talmon und ihre Brüder, die in den Toren hüteten, waren hundertundzweiundsiebenzig.
Alonda a ku Nyumba ya Mulungu anali awa: Akubu, Talimoni ndi abale awo. Onse pamodzi anali 172.
20 Das andere Israel aber, Priester und Leviten, waren in allen Städten Judas, ein jeglicher in seinem Erbteil.
Aisraeli ena onse pamodzi ndi ansembe ndi Alevi ankakhala mʼmizinda ya Yuda, ndipo aliyense ankakhala mʼdera la makolo ake.
21 Und die Nethinim wohneten an Ophel. Und Ziha und Gispa gehörten zu den Nethinim.
Koma antchito a ku Nyumba ya Mulungu ankakhala pa phiri la Ofeli, ndipo Ziha ndi Gisipa ndiwo anali kuwayangʼanira.
22 Der Vorsteher aber über die Leviten zu Jerusalem war Usi, der Sohn Banis, des Sohns Hasabjas, des Sohns Mathanjas, des Sohns Michas. Aus den Kindern Assaphs waren Sänger um das Geschäft im Hause Gottes.
Wamkulu wa Alevi mu Yerusalemu anali Uzi mwana wa Bani, mwana wa Hasabiya, mwana wa Mataniya, mwana wa Mika. Uzi anali mmodzi wa zidzukulu za Asafu, amene anali oyimba nyimbo pa nthawi zachipembedzo mʼNyumba ya Mulungu.
23 Denn es war des Königs Gebot über sie, daß die Sänger treulich handelten, einen jeglichen Tag seine Gebühr.
Pakuti mfumu inalamula kuti tsiku ndi tsiku pa nthawi zachipembedzo oyimba nyimbowo azikhalapo.
24 Und Pethahja, der Sohn Mesesabeels, aus den Kindern Serahs, des Sohns Judas, war Befehlshaber des Königs zu allen Geschäften an das Volk.
Petahiya mwana wa Mesezabeli, mmodzi mwa zidzukulu za Zera mwana wa Yuda ndiye ankayimirira Aisraeli pa bwalo la mfumu ya Perisiya.
25 Und der Kinder Juda, die außen auf den Dörfern auf ihrem Lande waren, wohneten etliche zu Kiriath-Arba und in ihren Töchtern und zu Dibon und in ihren Töchtern und zu Kabzeel und in ihren Dörfern
Anthu ena a fuko la Yuda ankakhala ku Kiriyati-Ariba ndi midzi yake, ku Diboni ndi midzi yake, ku Yekabizeeli ndi midzi yake,
26 und zu Jesua, Molada, Beth-Palet,
ku Yesuwa, Molada, Beti-Peleti,
27 Hazar-Sual, Berseba und ihren Töchtern
Hazari-Suwali, Beeriseba ndi midzi yawo.
28 und zu Ziklag und Mochona und ihren Töchtern
Ku Zikilagi, Mekona ndi midzi yawo,
29 und zu En-Rimmon, Zarega, Jeremuth,
ku Eni-Rimoni, Zora, Yarimuti,
30 Sanoah, Adullam und ihren Dörfern, zu Lachis und auf ihrem Felde, zu Aseka und in ihren Töchtern. Und lagerten sich von Berseba an bis ans Tal Hinnom.
Zanowa, Adulamu ndi midzi yake, ku Lakisi ndi minda yake, ku Beeriseba mpaka ku chigwa cha Hinomu.
31 Die Kinder Benjamin aber von Gaba wohneten zu Michmas, Aja, Bethel und ihren Töchtern
Nazonso zidzukulu za Benjamini zinkakhala mʼdera lawo kuyambira ku Geba mpaka ku Mikimasi, Ayiya, Beteli ndi midzi yake,
32 und zu Anathoth, Nob, Ananja,
ku Anatoti, Nobu ndi Ananiya,
33 Hazor, Rama, Githaim,
ku Hazori, Rama ndi Gitaimu,
34 Hadid, Ziboim, Neballat,
ku Hadidi, Zeboimu ndi Nebalati,
35 Lod, Ono und im Zimmertal.
ku Lodi, Ono ndi ku chigwa cha Amisiri.
36 Und etliche Leviten, die Teil in Juda hatten, wohneten unter Benjamin.
Magulu ena a Alevi a ku Yuda ankakhala ku Benjamini.

< Nehemia 11 >