< 2 Mose 5 >

1 Hernach kamen Moses und Aaron und sprachen zu Pharao: "So spricht der Herr, der Gott Israels: 'Entlaß mein Volk, daß sie mir ein Fest in der Wüste feiern!'"
Zitachitika izi, Mose ndi Aaroni anapita kwa Farao ndipo anati, “Yehova Mulungu wa Israeli akuti, ‘Aloleni anthu anga apite, kuti akachite chikondwerero cha Ine mʼchipululu.’”
2 Da sprach Pharao: "Wer ist der Herr, daß ich ihm gehorchen und Israel entlassen soll? Den Herrn kenne ich nicht, und Israel entlasse ich nicht."
Koma Farao anati, “Yehova ndani kuti ine ndimumvere ndi kulola Aisraeli kuti apite? Ine Yehova sindikumudziwa ndipo sindilola kuti Aisraeli apite.”
3 Sie sprachen.- "Der Gott der Hebräer ist uns begegnet. Wir möchten nur drei Tagereisen in die Wüste gehen und dem Herrn, unserem Gott, opfern, daß er uns nicht mit Pest oder Schwert überfalle!"
Ndipo iwo anati, “Mulungu wa Ahebri anakumana nafe. Chonde tiloleni tipite ulendo wa masiku atatu ku chipululu kuti tikapereke nsembe kwa Yehova Mulungu wathu, ngati sititero iye adzatipweteka ndi miliri kapena lupanga.”
4 Da sprach der König von Ägypten zu ihnen: "Warum wollt ihr, Moses und Aaron, das Volk an seiner Arbeit hindern? Kümmert euch doch um eure Sachen!"
Koma mfumu ya Igupto inati, “Mose ndi Aaroni, chifukwa chiyani mukuchititsa anthuwa kuti asagwire ntchito zawo? Bwererani ku ntchito zanu!”
5 Und Pharao sprach: "Fürwahr, allzuviel Leute sind schon im Land. Da lasset ihr diese von ihren Arbeiten ausruhen!"
Ndiponso Farao anati, “Taonani, anthuwa mʼdziko muno alipo ochuluka, ndipo inu mukuwaletsa kugwira ntchito.”
6 Und Pharao befahl am gleichen Tage des Volkes Fronvögten und seinen Aufsehern:
Pa tsiku lomwelo Farao analamulira akapitawo a thangata ndi anzawo a Chiisraeli amene ankayangʼanira anthu kuti
7 "Liefert kein Stroh mehr dem Volk zum Ziegelmachen wie bisher! Selber sollen sie gehen und Stroh auflesen!
“Inu musawapatsenso udzu wopangira njerwa monga mumachitira kale, iwo azipita ndi kukatenga udzu wawo.
8 Aber den Satz der Ziegel, die sie bisher hergestellt, belaßt für sie! Macht keinen Abzug daran! Faul sind sie, drum schreien sie: 'Laßt uns gehen, unserem Gott zu opfern!'
Koma musawachepetsere chiwerengero cha njerwa chomwe munawalamulira kale kuti aziwumba. Iwowa ndi aulesi. Nʼchifukwa chake akulira kuti, ‘Tiloleni tipite tikapereke nsembe kwa Mulungu wathu.’
9 Wuchtig laste die Arbeit auf diesen Leuten, und sie sollen daran zu tun haben, daß sie nicht auf Lügenreden achten!"
Muwakhawulitse ndi ntchito anthu amenewa kuti azitanganidwa, asakhale ndi mpata omvera zabodza.”
10 Da kamen des Volkes Fronvögte und seine Aufseher heraus und sagten zum Volke: "So spricht der Pharao: Ich liefere euch kein Stroh mehr.
Choncho akapitawo a thangata ndi anzawo a Chiisraeli amene ankayangʼanira anthu anapita kwa anthu aja nati, “‘Farao akuti sadzakupatsaninso udzu.
11 Geht selber! Holt euch Stroh, wo ihr es findet! Von eurem Frondienst aber wird nichts gekürzt"
Mʼmalo mwake mupite mukadzimwetere udzu kulikonse kumene mungawupeze. Komabe ntchito yanu sichepetsedwa.’”
12 Da zerstreute sich das Volk über ganz Ägypterland, Stoppeln für die Ziegel zu sammeln.
Kotero anthuwo anamwazikana mʼdziko lonse la Igupto kukamweta udzu.
13 Aber die Fronvögte drängten und sprachen: "Die volle Arbeit müßt ihr täglich liefern wie damals, als es Stroh gab."
Akapitawo a thangata aja anawafulumiza anthu aja nati, “Malizani kugwira ntchito yanu ya tsiku ndi tsiku monga mmene zinalili pamene munkapatsidwa udzu.”
14 Da wurden die israelitischen Aufseher gezüchtigt. Ihnen hatten Pharaos Fronvögte die Schuld gegeben, indem sie sprachen: "Warum habt ihr nicht euer Maß an Ziegeln wie bisher, so auch heute fertig gebracht?"
Akapitawo a thangata a Farao ankawamenya oyangʼanira anzawo a Chiisraeli aja nawapanikiza kuti, “Chifukwa chiyani lero simunawumbe chiwerengero chovomerezeka cha njerwa monga chakale chija?”
15 So kamen die israelitischen Aufseher, schrien zu Pharao und sprachen: "Warum tust du so mit deinen Sklaven?
Pamenepo oyangʼanira anzawo a Chiisraeli aja anapita kukadandaula kwa Farao kuti, “Chifukwa chiyani mwachitira antchito anu zotere?
16 Stroh wird deinen Sklaven nicht mehr geliefert; doch 'Ziegel', sagt man uns, 'liefert ab!' Nun werden deine Sklaven schwer gezüchtigt, indes an dir die Schuld liegt."
Antchito anu sakupatsidwa udzu, komabe akutiwuza kuti, ‘Umbani njerwa!’ Antchito anu akumenyedwa, koma cholakwa sichili ndi anthu anu.”
17 Er sprach: "Faul seid ihr, faul. Deshalb sagt ihr: 'Wir wollen gehen, dem Herrn zu opfern.'
Farao anati, “Ulesi, inu ndinu alesi! Nʼchifukwa chake mukumanena kuti, ‘Mutilole tipite kukapereka nsembe kwa Yehova.’
18 Jetzt marsch! Fort an die Arbeit! Stroh wird euch nicht geliefert; doch den Satz an Ziegeln habt ihr zu liefern."
Pitani tsopano kuntchito. Simudzapatsidwanso udzu komabe muyenera kuwumba muyeso wanu wovomerezeka wa njerwa.”
19 Da sahen die Aufseher der Israeliten sie traurig an und sprachen: "Ihr dürft das Tagwerk an Ziegeln nicht kürzen."
Oyangʼanira anzawo a Chiisraeli anazindikira kuti ali pa mavuto pamene anawuzidwa kuti, “Musachepetse chiwerengero cha njerwa chimene muyenera kuwumba tsiku lililonse.”
20 Als sie von Pharao weggingen, trafen sie auf Moses und Aaron, die sie erwarteten.
Atachoka pamaso pa Farao, anakumana ndi Mose ndi Aaroni akuwadikira,
21 Sie sprachen zu ihnen: "Der Herr blicke auf euch und richte, daß ihr uns bei Pharao und seinen Dienern in übelsten Geruch gebracht, ja ihnen das Schwert in die Hand gedrückt habt, uns zu morden!"
ndipo iwo anati, “Yehova akupenyeni ndi kukuweruzani popeza mwachititsa Farao ndi nduna zake kuti anyansidwe nafe ndipo mwayika lupanga mʼmanja mwawo kuti atiphe.”
22 Da wandte sich Moses an den Herrn und sprach: "Herr! Warum tust du diesem Volk so übel? Wozu hast du mich hergesandt?
Mose anabwerera kwa Yehova ndipo anati, “Chonde Ambuye, chifukwa chiyani mukuzunza anthu anu? Kodi munanditumira zimenezi?
23 Seit ich zu Pharao gekommen bin, in deinem Namen zu reden, hat er diesem Volke übel getan, und du hast dein Volk nicht davor geschützt."
Chipitireni changa kwa Farao kukamuyankhula mʼdzina lanu, iye wakhala akuzunza anthuwa, ndipo inu simunawapulumutse konse anthu anu.”

< 2 Mose 5 >