< 1 Chronik 25 >
1 Ferner bestellte David Dienstobere für die Dienstleistung der Söhne Asaphs, Hemans und Jedutuns, die mit Zithern, Harfen und Zimbeln vorspielen sollten. Es erfolgte aber eine Zählung der mit diesem Dienste Beschäftigten.
Davide ndi atsogoleri a asilikali anapatula ena mwa ana a Asafu, Hemani ndi Yedutuni ku utumiki wa uneneri pogwiritsa ntchito apangwe, azeze ndi ziwaya zamalipenga. Tsopano nawu mndandanda wa anthu amene ankagwira ntchito imeneyi:
2 Von Asaphs Söhnen standen Zakkur, Joseph, Netanja und Asarela, Asaphs Söhne, unter Asaph, der nach des Königs Geheiß vorspielte.
Kuchokera kwa ana a Asafu: Zakuri, Yosefe, Netaniya ndi Asareli. Ana a Asafu amalamulidwa ndi Asafu ndipo amanenera moyangʼaniridwa ndi mfumu.
3 Von Jedutun standen Jedutuns Söhne Gedalja, Suri, Jesaja, Chasabja und Mattitja, sechs, mit Zithern unter ihrem Vater Jedutun, der beim Danksagen und beim Lobpreise des Herrn vorspielte.
Kwa Yedutuni, kuchokera kwa ana ake: Gedaliya, Zeri, Yesaya, Simei, Hasabiya ndi Matitiya. Onse analipo 9 ndipo amayangʼaniridwa ndi Yedutuni abambo awo, amene amanenera pogwiritsa ntchito apangwe poyamika ndi kutamanda Yehova.
4 Von Heman waren es Hemans Söhne Bukkiahu, Mattanjahu, Uzziel, Sebuel, Jerimot, Chananja, Chanani, Eliata, Giddalti, Romamtiezer, Josbekasa, Malloti, Hotir und Machaziot.
Kwa Hemani, kuchokera kwa ana ake: Bukiya, Mataniya, Uzieli, Subaeli ndi Yerimoti; Hananiya, Hanani, Eliata, Gidaliti ndi Romamiti-Ezeri; Yosibakasa, Maloti, Hotiri ndi Mahazioti.
5 Dies alles sind Söhne Hemans, des königlichen Sehers in göttlichen Dingen und Zeichendeuters. Gott schenkte Heman vierzehn Söhne und drei Töchter.
Onsewa anali ana a Hemani mlosi wa mfumu. Iye anapatsidwa anawa potsata mawu a Mulungu akuti adzamukweza. Mulungu anapatsa Hemani ana aamuna 14 ndi ana aakazi atatu.
6 Diese alle standen unter ihrem Vater beim Gesang im Hause des Herrn, mit Zimbeln, Harfen und Zithern beim Dienst im Gotteshause unter dem König, Asaph, Jedutun und Heman.
Anthu onsewa ankayangʼaniridwa ndi makolo awo pa mayimbidwe a mʼNyumba ya Yehova. Iwowatu ankayimba ndi ziwaya zamalipenga, azeze ndi apangwe potumikira mʼNyumba ya Mulungu. Koma Asafu, Yedutuni ndi Hemani amayangʼaniridwa ndi mfumu.
7 Ihre Zahl nebst der ihrer Brüder, die in den Liedern des Herrn wohlerfahren waren, insgesamt Meister, betrug 288.
Iwo pamodzi ndi abale awo onse ophunzitsidwa ndi aluso loyimbira Yehova chiwerengero chawo chinali 288.
8 Sie warfen Lose für den Dienst, für den der jüngeren und für den der Älteren, für Meister und Schüler.
Angʼonoangʼono ndi akulu omwe, mphunzitsi ndi wophunzira yemwe anachita maere pa ntchito zawo.
9 Das erste Los Asaphs fiel auf Joseph, das zweite auf Gedalja; er, seine Brüder und Söhne waren zusammen zwölf,
Maere woyamba amene anali a Asafu, anagwera Yosefe, ana ndi abale ake. 12 Maere achiwiri anagwera Gedaliya, ndi abale ake ndi ana ake. 12
10 das dritte auf Zakkur; seine Söhne und Brüder: zwölf,
Maere achitatu anagwera Zakuri, ana ake ndi abale ake. 12
11 das vierte auf Isri; seine Söhne und Brüder: zwölf,
Maere achinayi anagwera Iziri, ana ake ndi abale ake. 12
12 das fünfte auf Netanjahu; seine Söhne und Brüder: zwölf,
Maere achisanu anagwera Netaniya, ana ake ndi abale ake. 12
13 das sechste auf Bukkiahu; seine Söhne und Brüder: zwölf,
Maere achisanu ndi chimodzi anagwera Bukiya, ana ake ndi abale ake. 12
14 das siebte auf Jesarela; seine Söhne und Brüder: zwölf,
Maere achisanu ndi chiwiri anagwera Yesarela, ana ake ndi abale ake. 12
15 das achte auf Jesajahu; seine Söhne und Brüder: zwölf,
Maere achisanu ndi chitatu anagwera Yeshaya, ana ake ndi abale ake. 12
16 das neunte auf Mattanjahu; seine Söhne und Brüder: zwölf,
Maere achisanu ndi chinayi anagwera Mataniya, ana ake ndi abale ake. 12
17 das zehnte auf Simei; seine Söhne und Brüder: zwölf,
Maere a khumi anagwera Simei, ana ake ndi abale ake. 12
18 das elfte auf Azarel; seine Söhne und Brüder: zwölf,
Maere a 11 anagwera Azareli, ana ake ndi abale ake. 12
19 das zwölfte auf Chasabja; seine Söhne und Brüder: zwölf,
Maere a 12 anagwera Hasabiya, ana ake ndi abale ake. 12
20 das dreizehnte auf Subael; seine Söhne und Brüder: zwölf,
Maere a 13 anagwera Subaeli, ana ake ndi abale ake. 12
21 das vierzehnte auf Mattijahu; seine Söhne und Brüder: zwölf,
Maere a 14 anagwera Matitiya, ana ake ndi abale ake. 12
22 das fünfzehnte auf Jeremot; seine Söhne und Brüder: zwölf,
Maere a 15 anagwera Yeremoti, ana ake ndi abale ake. 12
23 das sechzehnte auf Chananjabu; seine Söhne und Bruder: Zwölf,
Maere a 16 anagwera Hananiya, ana ake ndi abale ake. 12
24 das siebzehnte auf Josbekasa; seine Söhne und Brüder: zwölf,
Maere a 17 anagwera Yosibakasa, ana ake ndi abale ake. 12
25 das achtzehnte auf Chanani; seine Söhne und Brüder: zwölf,
Maere a 18 anagwera Hanani, ana ake ndi abale ake. 12
26 das neunzehnte auf Malloti; seine Söhne und Brüder: zwölf,
Maere a 19 anagwera Maloti, ana ake ndi abale ake. 12
27 das zwanzigste auf Eliata; seine Söhne und Brüder: zwölf,
Maere a 20 anagwera Eliyata, ana ake ndi abale ake. 12
28 das einundzwanzigste auf Hotir; seine Söhne und Brüder: zwölf,
Maere a 21 anagwera Hotiri, ana ake ndi abale ake. 12
29 das zweiundzwanzigste auf Giddalti; seine Söhne und Brüder: zwölf,
Maere a 22 anagwera Gidaliti, ana ake ndi abale ake. 12
30 das dreiundzwanzigste auf Machaziot; seine Söhne und Brüder: zwölf,
Maere a 23 anagwera Mahazioti, ana ake ndi abale ake. 12
31 das vierundzwanzigste auf Romamtiezer; seine Söhne und Brüder: zwölf.
Maere a 24 anagwera Romamiti-Ezeri, ana ake ndi abale ake 12.