< Psalm 46 >

1 Dem Vorsänger. Von den Söhnen Korahs; auf Alamoth, ein Lied. Gott ist uns Zuflucht und Stärke, eine Hilfe, reichlich gefunden in Drangsalen.
Kwa mtsogoleri wa mayimbidwe. Ndakatulo ya ana a Kora. Nyimbo ya anamwali. Mulungu ndiye kothawira kwathu ndi mphamvu yathu, thandizo lopezekeratu pa nthawi ya mavuto.
2 Darum werden wir uns nicht fürchten, wenngleich gewandelt würde die Erde, und wenn die Berge wankten im Herzen des Meeres,
Nʼchifukwa chake sitidzaopa ngakhale dziko lapansi lisunthike, ngakhale mapiri agwe pakati pa nyanja,
3 wenn seine Wasser tobten und schäumten, die Berge erbebten durch sein Ungestüm. (Sela)
ngakhale madzi ake atakokoma ndi kuchita thovu, ngakhale mapiri agwedezeke ndi kukokoma kwake.
4 Ein Strom, seine Bäche erfreuen die Stadt Gottes, das Heiligtum der Wohnungen des Höchsten.
Kuli mtsinje umene njira zake za madzi zimasangalatsa mzinda wa Mulungu, malo oyera kumene Wammwambamwamba amakhalako.
5 Gott ist in ihrer Mitte, sie wird nicht wanken; Gott wird ihr helfen beim Anbruch des Morgens.
Mulungu ali mʼkati mwake, iwo sudzagwa; Mulungu adzawuthandiza mmawa.
6 Es toben die Nationen, die Königreiche wanken; er läßt seine Stimme erschallen: die Erde zerschmilzt.
Mitundu ikupokosera, mafumu akugwa; Iye wakweza mawu ake, dziko lapansi likusungunuka.
7 Jehova der Heerscharen ist mit uns, eine hohe Feste ist uns der Gott Jakobs. (Sela)
Yehova Wamphamvuzonse ali ndi ife, Mulungu wa Yakobo ndi linga lathu.
8 Kommet, schauet die Großtaten Jehovas, der Verheerungen angerichtet hat auf der Erde!
Bwerani kuti mudzaone ntchito za Yehova, chiwonongeko chimene wachibweretsa pa dziko lapansi.
9 Der die Kriege beschwichtigt bis an das Ende der Erde, den Bogen zerbricht und den Speer zerschlägt, die Wagen mit Feuer verbrennt.
Iye amathetsa nkhondo ku malekezero a dziko lapansi; Iye amathyola uta ndi kupindapinda mkondo; amatentha zishango ndi moto.
10 Lasset ab und erkennet, daß ich Gott bin! Ich werde erhöht werden unter den Nationen, ich werde erhöht werden auf Erden.
Iye akuti, “Khala chete, ndipo dziwa kuti ndine Mulungu; ndidzakwezedwa pakati pa mitundu ya anthu; ine ndidzakwezedwa mʼdziko lapansi.”
11 Jehova der Heerscharen ist mit uns, eine hohe Feste ist uns der Gott Jakobs. (Sela)
Yehova Wamphamvuzonse ali ndi ife, Mulungu wa Yakobo ndi linga lathu.

< Psalm 46 >