< Romains 9 >
1 Je dis la vérité dans le Christ, je ne mens pas, ma conscience me rendant témoignage par l’Esprit-Saint,
Ine ndikunena zoona mwa Khristu. Sindikunama ndipo chikumbumtima changa kudzera mwa Mzimu Woyera chikundichitira umboni.
2 Qu’il y a une grande tristesse en moi, et une douleur continuelle dans mon cœur.
Ndili ndi chisoni chachikulu ndipo ndikumva kupwetekeka kosalekeza mu mtima mwanga.
3 Car je désirais ardemment d’être moi-même anathème à l’égard du Christ, pour mes frères, qui sont mes proches selon la chair,
Pakuti ndikanafuna ine mwini nditatembereredwa ndi kuchotsedwa mwa Khristu chifukwa cha abale anga, amene ndi a mtundu wanga,
4 Qui sont les Israélites, auxquels appartiennent l’adoption des enfants, la gloire, l’alliance, la loi, le culte et les promesses,
anthu Aisraeli. Iwo anasankhidwa kukhala ana. Mulungu anawapatsa ulemerero, anachita nawo mapangano, kuwapatsa Malamulo, Nyumba yopembedzeramo ndi malonjezano ake.
5 Dont les pères sont ceux de qui est sorti, selon la chair, le Christ même qui est au-dessus de toutes choses, Dieu béni dans tous les siècles. Amen. (aiōn )
Awo ndi makolo athu. Kuchokera kwa iwo mʼthupi ndi kumene kunachokera makolo a Khristu Yesu amene ndi Mulungu wolamulira zinthu zonse, alemekezeke mpaka muyaya! Ameni. (aiōn )
6 Non que la parole de Dieu soit restée sans effet; mais tous ceux qui descendent d’Israël ne sont pas Israélites;
Sikuti mawu a Mulungu analephera. Pakuti si onse obadwa mwa Israeli amene ndi Israeli.
7 Ni ceux qui appartiennent à la race d’Abraham ne sont pas tous ses enfants; mais c’est en Isaac que sera ta postérité;
Kapena kuti ana ake chifukwa anachokera mwa Abrahamu. Koma zidzukulu zako zidzachokera mwa Isake.
8 C’est-à-dire, ce ne sont pas les enfants selon la chair qui sont enfants de Dieu, mais ce sont les enfants de la promesse qui sont comptés dans la postérité.
Kutanthauza kuti, si ana obadwa mʼthupi amene ndi ana a Mulungu koma ndi ana a lonjezano amene amatengedwa kukhala zidzukulu za Abrahamu.
9 Car voici les termes de la promesse: En ce temps, je viendrai, et Sara aura un fils.
Pakuti Mulungu analonjeza ponena kuti, “Pa nthawi yake ngati yomwe ino chaka chamawa ndidzabweranso, ndipo Sara adzakhala ndi mwana wamwamuna.”
10 Et non-seulement elle, mais aussi Rebecca, qui eut deux fils à la fois d’Isaac notre père.
Ndipo si pokhapo ayi. Ana awiri a Rebeka aja abambo awo anali mmodzi, kholo lathu Isake.
11 Car avant qu’ils fussent nés ou qu’ils eussent fait ni aucun bien, ni aucun mal (afin que le décret de Dieu demeurât ferme selon son élection),
Komabe, ana amapasawa asanabadwe kapena asanachite chilichonse chabwino kapena choyipa, nʼcholinga choti chifuniro cha Mulungu chosankhiratu munthu aliyense chipitirire,
12 Non à cause de leurs œuvres, mais par la volonté de celui qui appelle, il lui fut dit:
osati chifukwa cha ntchito za munthu koma chifuniro cha Iye mwini, anawuza Rebeka kuti, “Wamkulu adzatumikira wamʼngʼono.”
13 L’aîné servira sous le plus jeune, selon qu’il est écrit: J’ai aimé Jacob, et j’ai haï Esaü.
Monga momwe kwalembedwa kuti, “Ine ndinakonda Yakobo, koma ndinamuda Esau.”
14 Que dirons-nous donc? Y a-t-il en Dieu de l’injustice? Nullement.
Nanga tsono tidzanena chiyani? Kodi Mulungu ndi osalungama? Ayi, ndi pangʼono pomwe!
15 Car il dit à Moïse: J’aurai pitié de qui j’ai pitié, et je ferai miséricorde à qui je ferai miséricorde.
Pakuti Mulungu anawuza Mose kuti, “Ine ndidzachitira chifundo amene ndikufuna kumuchitira chifundo, ndipo ndidzakomera mtima amene ndikufuna kumukomera mtima.”
16 Cela ne dépend donc ni de celui qui veut, ni de celui qui court, mais de Dieu, qui fait miséricorde.
Nʼchifukwa chake, izi sizitengera zokhumba za munthu kapena kuyesetsa koma chifundo cha Mulungu.
17 Car l’Ecriture dit à Pharaon: Voici pourquoi je t’ai suscité: c’est pour faire éclater en toi ma puissance, et pour que mon nom soit annoncé dans toute la terre.
Malemba akuti Mulungu anamuwuza Farao kuti, “Ine ndakuyika kukhala mfumu ndi cholinga choti ndionetse mphamvu zanga, kuti mwa iwe dzina langa litchuke pa dziko lonse lapansi.”
18 Donc il a pitié de qui il veut, et il endurcit qui il veut.
Choncho Mulungu amachitira chifundo munthu amene akufuna kumuchitira chifundo ndipo amawumitsa mtima munthu amene Iye akufuna kumuwumitsa mtima.
19 Certainement vous me direz: De quoi se plaint-il encore? car qui résiste à sa volonté?
Tsono mmodzi wa inu nʼkundifunsa kuti, “Nanga nʼchifukwa chiyani Mulungu amatipeza olakwa? Nanga ndani amene amakana chifuniro chake?”
20 Ô homme, qui es-tu, pour contester avec Dieu? Le vase dit-il au potier: Pourquoi m’as-tu fait ainsi?
Koma ndiwe yani, munthu wamba, woti nʼkutsutsana ndi Mulungu? “Kodi chimene chinawumbidwa nʼkufunsa amene anachiwumba kuti, ‘Kodi unandiwumbiranji motere?’”
21 N’a-t-il pas le pouvoir, le potier, de faire de la même masse d’argile un vase d’honneur et un autre d’ignominie?
Kodi wowumba alibe ufulu wowumba kuchokera ku dothi lomwelo mbiya yamtengowapatali ndi ina yamtengo wotsika?
22 Que si Dieu, voulant manifester sa colère et signaler sa puissance, a supporté avec une patience extrême les vases de colère propres à être détruits,
Koma Mulungu, anafuna kuonetsa mkwiyo wake ndi kuti mphamvu yake idziwike. Iye anapirira modekha mtima kwambiri zochita za anthu omwe anawakwiyirawo amene anayeneradi chiwonongeko.
23 Afin de manifester les richesses de sa gloire sur les vases de miséricorde qu’il a préparés pour la gloire,
Iye anachita izi kufuna kuonetsa kulemera kwa ulemerero wake ndi kuti udziwike kwa amene analandira chifundo chake. Iye anawakonzeratu kuti alandire ulemerero wake
24 En nous qu’il a de plus appelés, non-seulement d’entre les Juifs, mais aussi d’entre les gentils,
ngakhale ifenso amene anatiyitana osati kuchokera kwa Ayuda okha komanso kwa a mitundu ina.
25 Comme il dit dans Osée: J’appellerai celui qui n’est pas mon peuple, mon peuple; celle qui n’est pas bien-aimée, bien-aimée; celle qui n’a point obtenu miséricorde, objet de miséricorde:
Monga momwe Mulungu akunenera mʼbuku la Hoseya kuti, “Amene sanali anthu anga ndidzawatcha ‘anthu anga;’ ndipo Ine ndidzatcha ‘wokondedwa wanga’ amene sali wokondedwa wanga,”
26 Et il arrivera que dans le lieu même où il leur fut dit: Vous n’êtes point mon peuple, ils seront appelés enfants du Dieu vivant.
ndipo, “Pamalo omwewo pamene ananena kuti, ‘Sindinu anthu anga,’ pomweponso adzawatchula kuti, ‘Ana a Mulungu wamoyo.’”
27 Et Isaïe s’écrie à l’égard d’Israël: Le nombre des enfants d’Israël fût-il comme le sable de la mer, il n’y aura qu’un reste de sauvé.
Yesaya anafuwula za Aisraeli kuti, “Ngakhale chiwerengero cha Aisraeli chingakhale ngati mchenga wa ku nyanja, otsala okha ndiye adzapulumuke.
28 Or le Seigneur accomplira cette parole et l’abrégera avec équité; oui, le Seigneur abrégera cette parole sur la terre;
Pakuti Ambuye adzagamula milandu ya anthu pa dziko lapansi mofulumira ndi kumaliziratu.”
29 Et comme Isaïe avait dit auparavant: Si le Seigneur Sabaoth ne nous avait réservé un rejeton, nous serions devenus comme Sodome, et semblables à Gomorrhe.
Monga momwe Yesaya ananena malo ena kuti, “Ngati Yehova Wamphamvuzonse akanapanda kutisiyira zidzukulu, ife tikanawonongeka ngati anthu a ku Sodomu, tikanakhala ngati anthu a ku Gomora.”
30 Que dirons-nous donc? Que les gentils qui ne cherchaient point la justice ont embrassé la justice; mais la justice qui vient de la foi.
Kodi nanga tidzati chiyani? Tidzati a mitundu ina amene sanafune chilungamo analandira chilungamo chachikhulupiriro
31 Et qu’Israël, au contraire, en recherchant la loi de justice, n’est point parvenu à la loi de justice.
koma Aisraeli, amene anafuna chilungamo cha lamulo sanachilandire.
32 Et pourquoi? Parce que ce n’est point par la foi, mais comme par les œuvres qu’ils l’ont recherchée; car ils se sont heurtés contre la pierre de l’achoppement,
Chifukwa chiyani? Chifukwa iwo sanachifune ndi chikhulupiriro koma ngati mwa ntchito. Iwo anapunthwa pa “Mwala wopunthwitsa.”
33 Comme il est écrit: Voici que je mets en Sion une pierre d’achoppement et une pierre de scandale; et quiconque croit en lui ne sera point confondu.
Monga momwe kwalembedwa kuti, “Taonani, Ine ndikuyika mwala mu Ziyoni wopunthwitsa anthu, thanthwe limene limagwetsa anthu. Koma amene akhulupirira Iye sadzachititsidwa manyazi.”