< Romains 11 >
1 Je dis donc: Est-ce que Dieu a rejeté son peuple? Non, sans doute; car moi-même je suis Israélite, de la race d’Abraham, de la tribu du Benjamin;
Ine ndikufunsa kuti kodi Mulungu anakana anthu ake? Ayi. Ndi pangʼono pomwe! Inenso ndine Mwisraeli, mmodzi mwa zidzukulu za Abrahamu, ndiponso wa fuko la Benjamini.
2 Dieu n’a point rejeté son peuple qu’il a connu dans sa prescience. Ne savez-vous pas ce que l’Ecriture dit d’Elie, comment il interpelle Dieu contre Israël, disant:
Mulungu sanawakane anthu ake amene Iye anawadziwiratu. Kodi inu simukudziwa zimene Malemba akunena pa ndime imene Eliya akudandaula kwa Mulungu kuneneza Aisraeli? Iye anati,
3 Seigneur, ils ont tué vos prophètes, démoli vos autels; et moi, je suis resté seul, et ils recherchent mon âme?
“Ambuye, anthuwa apha aneneri anu ndi kugwetsa maguwa anu ansembe. Ndatsala ine ndekha wamoyo ndipo akufuna kundipha?”
4 Mais que lui dit la réponse divine? Je me suis réservé sept mille hommes qui n’ont point fléchi le genou devant Baal.
Ndipo yankho la Mulungu linali lotani? “Ine ndadzisungira ndekha anthu 7,000 amene sanapembedzepo Baala.”
5 De même donc, en ce temps aussi, un reste a été sauvé, selon l’élection de la grâce.
Chimodzimodzinso lero lino, alipo Aisraeli pangʼono osankhidwa mwachisomo.
6 Mais si c’est par la grâce, ce n’est donc point par les œuvres; autrement la grâce ne serait plus grâce.
Ndipo ngati ndi mwachisomo, sikungakhalenso mwa ntchito. Ngati zikanatero, chisomo sichikanakhalanso chisomo ayi.
7 Qu’est-il donc arrivé? Ce que cherchait Israël, il ne l’a pas trouvé; mais ceux qui ont été choisis l’ont trouvé; les autres ont été aveuglés,
Nʼchiyani tsopano? Chimene Aisraeli anachifuna ndi mtima wonse sanachipeze koma osankhidwawo anachipeza. Enawo anawumitsidwa mtima
8 Selon qu’il est écrit: Dieu leur a donné jusqu’à ce jour un esprit de torpeur; des yeux pour ne point voir, et des oreilles pour ne point entendre.
monga kwalembedwa kuti, “Mulungu anawapatsa mzimu wosatha kumvetsa zinthu, maso osatha kupenya; makutu osatha kumva mpaka lero lino.”
9 David dit encore: Que leur table devienne pour eux lacet, piège, scandale et rétribution.
Ndipo Davide akuti, “Maphwando awo asanduke msampha ndi diwa lowakola ndi chopunthwitsa kuti alandire chilango.
10 Que leurs yeux s’obscurcissent pour qu’ils ne voient point, et faites que leur dos soit toujours courbé.
Maso awo atsekedwe kuti asaone, ndi misana yawo ikhale yokhota nthawi zonse.”
11 Je dis donc: Ont-ils trébuché de telle sorte qu’ils soient tombés? Point du tout. Mais par leur péché, le salut est venu aux gentils qui devaient ainsi leur donner de l’émulation.
Ine ndikufunsanso kuti, kodi iwo anapunthwa ndi kugwa kotheratu? Ayi. Ndi pangʼono pomwe! Koma chifukwa cha kulakwa kwawo, chipulumutso chinafika kwa a mitundu ina kuti Aisraeli achite nsanje.
12 Que si leur péché est la richesse du monde, et leur diminution, la richesse des gentils; combien plus encore leur plénitude?
Koma ngati kulakwa kwawo kwapindulitsa dziko lapansi ndi kulephera kwawo kwapindulitsa a mitundu ina, nanga kudzakhala kupindula kwakukulu chotani iwo akadzabwera chonse!
13 Car je le dis à vous, gentils: Tant que je serai apôtre des gentils, j’honorerai mon ministère,
Ine ndikuyankhula kwa inu a mitundu ina monga ine ndili mtumwi wa kwa a mitundu ina ndipo ndimawunyadira utumiki wangawu.
14 M’efforçant d’exciter l’émulation de ceux de mon sang, et d’en sauver quelques-uns.
Ine cholinga changa nʼchakuti ndichititse nsanje anthu a mtundu wanga kuti ena mwa iwo apulumutsidwe.
15 Car si leur perte est la réconciliation du monde, que sera leur rappel, sinon une résurrection?
Pakuti ngati kukanidwa kwawo kunayanjanitsa anthu a dziko lapansi ndi Mulungu, nanga kudzatani, Iye akadzawalandiranso? Kudzakhala monga ngati anthu akufa akuuka.
16 Que si les prémices sont saintes, la masse l’est aussi; et si la racine est sainte, les rameaux aussi.
Ngati chigawo chimodzi cha buledi woperekedwa monga zipatso zoyamba ndi choyera, ndiye kuti zonsezo ndi zoyera. Ngati muzu ndi oyera, nʼchimodzimodzinso nthambi zake.
17 Si donc quelques-uns des rameaux ont été rompus, et si toi, qui n’étais qu’un olivier sauvage, tu as été enté en eux et fait participant de la racine et de la graisse de l’olivier,
Ngati nthambi zina zinakhadzulidwa ndipo inu, inu ndiye nthambi za olivi wakuthengo, nʼkulumikizidwa pamalo pa nthambi zimenezo, ndipo tsopano mukulandira nawo zakudya zochokera ku mizu ya olivi,
18 Ne te glorifie point aux dépens des rameaux. Que si tu te glorifies, sache que tu ne portes point la racine, mais que c’est la racine qui te porte.
musadzitame kunyoza nthambi zinazo. Ngati mutero, ganizirani ichi kuti Inu simugwiriziza mizu, koma muzu ukugwiriziza inu.
19 Tu diras, sans doute: Les rameaux ont été brisés pour que je fusse enté.
Tsono mudzati, “Nthambizo zinakhadzulidwa kuti ine ndilumikizidwepo.”
20 Fort bien. C’est à cause de leur incrédulité qu’ils ont été rompus. Pour toi, tu demeures ferme par ta foi, ne cherche pas à t’élever, mais crains.
Nʼzoona. Koma iwo anakhadzulidwa chifukwa chosakhulupirira ndipo inu mukuyima mwachikhulupiriro. Musadzitukumule, koma muchite mantha.
21 Car si Dieu n’a pas épargné les rameaux naturels, il pourra bien ne pas t’épargner toi-même.
Pakuti ngati Mulungu sanalekerere nthambi zachibadwidwe, Iye sadzakulekererani inunso.
22 Vois donc la bonté et la sévérité de Dieu: sa sévérité envers ceux qui sont tombés, et sa bonté envers toi, si toutefois tu demeures ferme dans cette bonté; autrement tu seras aussi retranché.
Nʼchifukwa chake ganizirani za kukoma mtima ndi za ukali wa Mulungu. Ukali uli kwa iwo amene anagwa koma kukoma mtima kwa inu, malinga ngati musamala kukoma mtima kwakeko kupanda kutero inunso mudzakhadzulidwanso.
23 Mais eux-mêmes, s’ils ne demeurent point dans l’incrédulité, seront entés; car Dieu est puissant pour les enter de nouveau.
Ngati iwo asiya kukhala osakhulupirira, adzalumikizidwanso pakuti Mulungu akhoza kuwalumikizanso.
24 En effet, si tu as été coupé de l’olivier sauvage, ta tige naturelle, et enté contre nature sur l’olivier franc, à combien plus forte raison, ceux qui sont les rameaux naturels seront-ils entés sur leur propre olivier?
Pakuti ngati inu, mwa chilengedwe munali mtengo wa olivi wa kuthengo, Mulungu anakukhadzulani nakulumikizani ku mtengo wa olivi wodzalidwa, zomwe ndi zotsutsana ndi chilengedwe, kodi sikudzakhala kwapafupi kwa Iye kuwalumikizanso mu mtengo wawowawo wa olivi?
25 Car je ne veux pas, mes frères, que vous ignoriez ce mystère ( afin que vous ne soyez pas sages à vos propres yeux), qu’une partie d’Israël est tombée dans l’aveuglement, jusqu’à ce que la plénitude des gentils soit entrée;
Abale, ine sindifuna kuti mukhale osadziwa za chinsinsi ichi, kuti mungadziyese nokha anzeru. Kuwuma mtima kumene Aisraeli akuchita ndi kwa kanthawi kufikira chiwerengero cha a mitundu chitalowa.
26 Et qu’ainsi tout Israël soit sauvé, selon qu’il est écrit: Il viendra de Sion celui qui doit délivrer, et qui doit bannir l’impiété de Jacob.
Kotero tsono Aisraeli onse adzapulumuka, monga kwalembedwa kuti, “Mpulumutsi adzachokera ku Ziyoni; Iye adzachotsa zoyipa zonse za Yakobo.
27 Et ce sera là mon alliance avec eux quand j’aurai effacé leurs péchés.
Ndipo ili lidzakhala pangano langa ndi iwo pamene Ine ndidzachotsa machimo awo.”
28 Il est vrai que, selon l’Evangile, ils sont ennemis à cause de vous; mais, selon l’élection, ils sont très aimés à cause de leurs pères.
Chifukwa cha Uthenga Wabwino, Aisraeli asanduka adani a Mulungu kuti inu mupindule. Koma kunena za kusankhidwa, iwo ndi okondedwa ndi Mulungu chifukwa cha makolo awo aja.
29 Parce que les dons et la vocation de Dieu sont sans repentir.
Pakuti Mulungu akayitana munthu ndi kumupatsa mphatso sangasinthenso.
30 Comme donc autrefois vous-mêmes n’avez pas cru à Dieu, et que maintenant vous avez obtenu miséricorde à cause de leur incrédulité
Monga mmene inu munalili, osamvera Mulungu pa nthawi ina, tsopano mwalandira chifundo chifukwa cha kusamvera kwawo.
31 Ainsi eux maintenant n’ont pas cru, pour que miséricorde vous fût faite, et qu’à leur tour ils obtiennent miséricorde.
Chonchonso iwo akhala osamvera tsopano kuti iwonso alandire chifundo chifukwa cha chifundo cha Mulungu kwa inu.
32 Car Dieu a renfermé tout dans l’incrédulité, pour faire miséricorde à tous. (eleēsē )
Pakuti Mulungu anasandutsa anthu onse a mʼndende ya kusamvera kuti Iye akaonetse chifundo kwa onse. (eleēsē )
33 Ô profondeur des trésors de la sagesse et de la science de Dieu! Que ses jugements sont incompréhensibles et ses voies impénétrables!
Aa! Nzeru za Mulungu ndi chidziwitso chake ndi zozama kwambiri! Ndani angazindikire maweruzidwe ake, ndipo njira zake angazitulukire ndani?
34 Car qui a connu la pensée du Seigneur? ou qui a été son conseiller?
“Kodi wadziwa ndani maganizo a Ambuye? Kapena ndani anakhalapo mlangizi wake?”
35 Ou qui, le premier, lui a donné, et sera rétribué?
“Kodi ndani anapereka mphatso kwa Mulungu, kuti Mulunguyo amubwezere iye?”
36 Puisque c’est de lui, et par lui, et en lui, que sont toutes choses; à lui la gloire dans les siècles. Amen. (aiōn )
Pakuti zinthu zonse nʼzochokera kwa Iye, nʼzolengedwa ndi Iye ndipo zimabweretsa ulemerero kwa Iye. Kwa Iye kukhale ulemerero mpaka muyaya! Ameni. (aiōn )