< Néhémie 3 >

1 Or Eliasib, le grand prêtre, se leva, et ses frères, les prêtres, et ils bâtirent la porte du troupeau; eux-mêmes la sanctifièrent, en établirent les battants et la sanctifièrent jusqu’à la tour de cent coudées, jusqu’à la tour Hananéel.
Pambuyo pake Eliyasibu mkulu wa ansembe ndi ansembe anzake anayamba kugwira ntchito ndipo anamanganso Chipata cha Nkhosa. Iwo anachipatulira Mulungu ndipo anayika zitseko zake. Khoma limene analipatula linafika mpaka pa Nsanja ya Zana ndi Nsanja ya Hananeli.
2 Et près de lui bâtirent les hommes de Jéricho; près de lui aussi bâtit Zachur, fils d’Amri.
Anthu a ku Yeriko anamanga chigawo china pambali pake ndipo Zakuri mwana wa Imuri anamanga chigawo chinanso choyandikana nawo.
3 Quant à la porte des Poissons, ce sont les fils d’Asnaa qui la bâtirent; eux-mêmes la couvrirent, et en établirent les battants, les serrures et verrous, et près d’eux bâtirent Marimuth, fils d’Urie, et les fils de Accus.
Chipata cha Nsomba chinamangidwanso ndi ana a fuko la Hasena. Iwo anayika mitanda yake ndi zitseko, zotsekera zake, ndi mipiringidzo yake.
4 Près de lui bâtit Mosollam, fils de Barachias, fils de Mésézébel; et près d’eux bâtit Sadoc, fils de Baana.
Meremoti mwana wa Uriya, mwana wa Hakozi, anakonza chigawo choyandikana nacho. Motsatana naye, Mesulamu mwana wa Berekiya, mwana wa Mesezabeli anakonza chigawo china. Pambali pake, Zadoki mwana wa Baana anakonzanso chigawo china.
5 Et près d’eux bâtirent les Thécuens; mais les grands d’entre eux ne soumirent pas leurs cœurs dans l’ouvrage de leur Seigneur.
Pambali pa iwowa anthu a ku Tekowa anakonza chigawo china. Koma wolemekezeka awo anakana kugwira ntchito imene akuluakulu awo anawapatsa.
6 Mais la porte ancienne, ce sont Joïada, fils de Phaséa, et Mosollam, fils de Bésodia, qui la bâtirent; eux-mêmes la couvrirent, et en établirent les portes, les serrures et les verrous.
Chipata cha Yesana chinakonzedwa ndi Yoyada mwana wa Paseya ndi Mesulamu mwana wa Besodeya. Iwo anayika mitanda yake ndi kuyika zitseko, zotsekera zake ndi mipiringidzo yake.
7 Et près d’eux bâtirent Meltias le Gabaonite, et Jadon le Méronathite, hommes de Gabaon et de Maspha, pour le chef qui était dans la contrée au-delà du fleuve.
Pambali pawo Melatiya Mgibeyoni ndi Yadoni Mmerenoti ndiponso anthu a ku Gibiyoni ndi a ku Mizipa anakonza chigawo chawo mpaka ku nyumba ya bwanamkubwa wa chigawo cha Patsidya pa Yufurate.
8 Et près de lui bâtit Eziel, fils d’Araïa, orfèvre; et près de lui bâtit Ananias, fils du parfumeur; et ils laissèrent Jérusalem jusqu’au mur de la rue large.
Pambali pawo Uzieli mwana wa Harihaya wa mʼgulu amisiri osula golide anakonzanso chigawo china. Pambali pake Hananiya mmodzi mwa anthu oyenga mafuta onunkhira, anakonzanso chigawo china. Iwo anakonzanso Yerusalemu mpaka ku Khoma Lotambasuka.
9 Et près de lui bâtit Raphaïa, fils de Hur, prince d’un bourg de Jérusalem.
Refaya mwana wa Huri wolamulira theka la chigawo cha Yerusalemu anakonza chigawo china motsatana nawo.
10 Et près de lui bâtit Jédaïa, fils d’Haromaph, contre sa maison; et près de lui bâtit Hattus, fils d’Hasébonia.
Kulumikiza ichi, Yedaya mwana wa Harumafi anakonza chigawo choyangʼanana ndi nyumba yake, ndipo Hatusi mwana wa Hasabaneya anakonzanso motsatana naye.
11 Melchias, fils de Hérem, et Hasub, fils de Phahath-Moab, bâtirent la moitié de la rue et la tour des fours.
Malikiya mwana wa Harimu ndi Hasubu mwana wa Pahati-Mowabu anakonzanso chigawo china ndiponso Nsanja ya Ngʼanjo.
12 Et près de lui bâtit Sellum, fils d’Alohès, prince de la moitié d’un bourg de Jérusalem, lui et ses filles.
Salumu mwana wa Halohesi wolamulira theka la chigawo cha Yerusalemu, anakonzanso chigawo chotsatana nawo mothandizidwa ndi ana ake akazi.
13 Pour la porte de la vallée, Hanum la bâtit avec les habitants de Zanoé: eux-mêmes la bâtirent et en établirent les battants, les serrures, les verrous, et mille coudées dans le mur jusqu’à la porte du fumier.
Chipata cha ku chigwa chinakonzedwa ndi Hanuni ndi anthu okhala ku Zanowa. Iwo anachimanganso ndi kuyika zitseko zake ndi zotsekera ndi mipiringidzo yake. Iwo anakonzanso khoma lotalika mamita 450 mpaka ku Chipata cha Zinyalala.
14 Mais la porte du fumier, Melchias, fils de Réchab, prince du bourg de Bethacharam, la bâtit; lui-même la bâtit, et en établit les battants, les serrures et les verrous.
Chipata cha Zinyalala chinakonzedwa ndi Malikiya mwana wa Rekabu, wolamulira chigawo cha Beti-Hakeremu. Iye anachimanganso ndi kuyika zitseko zake, zotsekera zake ndi mipiringidzo.
15 Et la porte de la fontaine, Sellum, fils de Cholhoza, prince du village de Maspha, la bâtit; lui-même la bâtit, la couvrit et en établit les battants, les serrures et les verrous, ainsi que les murs de la piscine de Siloé, jusqu’au jardin du roi, et jusqu’aux degrés qui descendent de la cité de David.
Chipata cha Kasupe chinakonzedwa ndi Saluni mwana wa Koli-Hoze, wolamulira chigawo cha Mizipa. Iye anachimanganso ndi kuyikanso denga ndiponso zitseko, zotsekera ndi mipiringidzo yake. Iye anakonzanso khoma la Dziwe la Siloamu limene lili pafupi ndi munda wa mfumu mpaka ku makwerero otsikira potuluka mzinda wa Davide.
16 Après lui bâtit Néhémias, fils d’Azboc, prince de la moitié du bourg de Bethsur, jusqu’en face du sépulcre de David, jusqu’à la piscine qui a été construite avec un grand travail, et jusqu’à la maison des forts.
Pambali pa iyeyo, Nehemiya mwana wa Azibuki, wolamulira theka la chigawo cha Beti Zuri anakonza chigawo china mpaka kumalo oyangʼanana ndi manda a Davide, mpaka ku dziwe lokumba ndi ku nyumba ya anthu ankhondo.
17 Après lui bâtirent les Lévites, Réhem, fils de Benni; après lui bâtit Hasébias, prince de la moitié du bourg de Céila, dans son bourg.
Pambali pake Alevi anakonza chigawo china, ndipo mtsogoleri wawo anali Rehumi mwana wa Bani. Pambali pa iye Hasabiya wolamulira theka la chigawo cha Keyila anagwira ntchito ku chigawo chake.
18 Après lui bâtirent leurs frères, Bavaï, fils d’Enadad, prince de la moitié de Céila.
Pambuyo pa iyeyu abale awo anapitiriza kukonza, ndipo mtsogoleri wawo anali Bawai mwana wa Henadadi, wolamulira theka lina la chigawo cha Keyila.
19 Et près de lui Azer, fils de Josué, prince de Maspha, bâtit la seconde mesure contre la montée de l’angle le plus fort.
Motsatana naye Ezeri mwana wa Yesuwa, wolamulira Mizipa anakonza chigawo chinanso choyangʼanana ndi chikweza chofikira ku nyumba yosungira zida za nkhondo pa ngodya.
20 Après lui, Baruch, fils de Zachaï, bâtit la seconde mesure sur la montagne, depuis l’angle jusqu’à la porte de la maison d’Eliasib, le grand prêtre.
Motsatana naye, Baruki mwana wa Zakai anakonzanso chigawo china kuchokera pa ngodya mpaka pa chitseko cha nyumba ya Eliyasibu mkulu wa ansembe.
21 Après lui Mérimuth, fils d’Urie, fils de Haccus, bâtit la seconde mesure depuis la porte de la maison d’Eliasib, aussi loin que s’étendait la maison d’Eliasib.
Motsatana naye, Meremoti mwana wa Uriya, mwana wa Hakozi anakonzanso chigawo china kuchokera ku chitseko cha nyumba ya Eliyasibu mpaka kumapeto kwake.
22 Et après lui bâtirent les prêtres, hommes des plaines du Jourdain.
Pambuyo pake ansembe okhala ku chidikha anakonzanso chigawo china.
23 Après lui bâtit Benjamin, et Hasub contre sa maison; et près de lui bâtit Azarias, fils de Maasias, fils d’Ananias, contre sa maison.
Pambuyo pawo, Benjamini ndi Hasubu anakonza kutsogolo kwa nyumba zawo. Ndipo motsatana nawo, Azariya mwana wa Maaseya mwana wa Ananiya, anakonza chigawo choyangʼanana ndi nyumba zawo.
24 Après lui, Bennuï, fils de Hénadad, bâtit la seconde mesure, depuis la maison d’Azarias jusqu’au tournant et jusqu’à l’angle;
Motsatana naye, Binuyi mwana wa Henadadi anakonzanso chigawo china, kuchokera pa nyumba ya Azariya kukafika potsirizira pa ngodya.
25 Phalel, fils d’Ozi, contre le tournant et la tour qui, élevée, avance hors de la maison du roi, c’est-à-dire dans le parvis de la prison; après lui, Phadaïa, fils de Pharos.
Palali mwana Uzai anakonza chigawo china choyangʼanana ndi ngodya ndi nsanja yotuluka pa nyumba yapamwamba ya mfumu ku bwalo la alonda. Motsatana naye, Pedaya mwana wa Parosi,
26 Mais les Nathinéens habitaient à Ophel, jusqu’en face de la porte des eaux, vers l’orient, et de la tour qui avançait au dehors.
ndi otumikira mʼNyumba ya Mulungu amene amakhala pa khoma la Ofeli anakonza chigawo china mpaka pa malo oyangʼanana ndi Chipata cha Madzi kuloza kummawa ndiponso nsanja yayitali ija.
27 Après lui, les Thécuens bâtirent un second espace vis-à-vis, depuis la tour grande et haute, jusqu’au mur du temple.
Motsatana nawo, anthu a ku Tekowa anakonzanso chigawo china choyangʼanana ndi nsanja ija yayikulu ndi yayitali mpaka ku khoma la Ofeli.
28 Mais en haut, depuis la porte des chevaux, les prêtres bâtirent, chacun contre sa maison;
Kuyambira ku Chipata cha Akavalo anakonza ndi ansembe ena ndipo aliyense amakonza khoma loyangʼanana ndi nyumba yake.
29 Après eux, Sadoc, fils d’Emmer, bâtit contre sa maison. Et après lui bâtit Sémaïa, fils de Séchénia, garde de la porte orientale.
Motsatana nawo, Zadoki mwana wa Imeri anakonza chigawo china choyangʼanana ndi nyumba yake. Motsatana naye, Semeya mwana wa Sekaniya, mlonda wa Chipata cha Kummawa, anakonzanso khoma.
30 Après lui, Hanania, fils de Sélémia, et Hanun, sixième fils de Séleph, bâtirent un second espace; après lui, Mosollam, fils de Barachias, bâtit contre sa trésorerie. Après lui bâtit Melchias, fils de l’orfèvre, jusqu’à la maison des Nathinéens et de ceux qui vendaient des hardes, contre la porte des juges, et jusqu’à la chambre de l’angle.
Hananiya mwana wa Selemiya ndiponso Hanuni mwana wachisanu ndi chimodzi wa Zalafi anakonza chigawo china. Motsatana naye, Mesulamu mwana wa Berekiya anakonza chigawo choyangʼanana ndi chipinda chake.
31 Et entre la chambre de l’angle, à la porte du troupeau, bâtirent les orfèvres et les marchands.
Motsatana naye, Malikiya mmodzi mwa amisiri a golide anakonza chigawo china mpaka ku nyumba ya atumiki a ku Nyumba ya Mulungu ndiponso ku nyumba ya anthu amalonda moyangʼanana ndi chipata cha Mifikade ndiponso mpaka pa chipinda chapamwamba chapangodya.
Ndipo pakati pa chipinda chapamwamba chapangodya ndi Chipata cha Nkhosa anakonza ndi amisiri a golide ndi anthu amalonda.

< Néhémie 3 >