< Jean 12 >
1 Jésus donc, six jours avant la pâque, vint à Béthanie, où était mort Lazare qu’avait ressuscité Jésus.
Masiku asanu ndi limodzi Paska asanafike, Yesu anafika ku Betaniya, kumene kumakhala Lazaro, amene Yesu anamuukitsa kwa akufa.
2 On lui prépara là un souper; Marthe servait, et Lazare était un de ceux qui étaient à table avec lui.
Kumeneko anamukonzera Yesu chakudya cha madzulo. Marita anatumikira pamene Lazaro anali mmodzi wa iwo amene anakhala nawo pa chakudyacho.
3 Or Marie prit une livre de parfum d’un nard pur de grand prix; elle en oignit les pieds de Jésus, et les essuya avec ses cheveux, et la maison fut remplie de l’odeur du parfum.
Kenaka Mariya anatenga botolo la mafuta a nadi, onunkhira bwino kwambiri, amtengowapatali; Iye anadzoza mapazi a Yesu napukuta ndi tsitsi lake. Ndipo nyumba yonse inadzaza ndi fungo lonunkhira bwino la mafutawo.
4 Alors un de ses disciples, Judas Iscariote, qui devait le trahir, dit:
Koma mmodzi wa ophunzira ake, Yudasi Isikarioti, amene pambuyo pake adzamupereka anati,
5 Pourquoi ce parfum n’a-t-il pas été vendu trois cents deniers, et n’a-t-il pas été donné aux pauvres?
“Nʼchifukwa chiyani mafuta awa sanagulitsidwe ndipo ndalama zake nʼkuzipereka kwa osauka?” Mafutawo anali a mtengo wa malipiro a chaka chimodzi.
6 Or il dit cela, non qu’il se souciât des pauvres, mais parce qu’il était voleur, et qu’ayant la bourse, il portait ce qu’on y mettait.
Iye sananene izi chifukwa cha kuganizira osauka koma chifukwa anali mbava; ngati wosunga thumba la ndalama, amabamo zomwe ankayikamo.
7 Jésus dit donc: Laissez-la réserver ce parfum pour le jour de ma sépulture.
Yesu anayankha kuti, “Mulekeni. Mafutawa anayenera kusungidwa mpaka tsiku loyika maliro anga.
8 Car, les pauvres, vous les avez toujours avec vous, mais moi, vous ne m’avez pas toujours.
Inu mudzakhala ndi osauka nthawi zonse, koma simudzakhala nane nthawi zonse.”
9 Une grande multitude de Juifs sut qu’il était là; et ils y vinrent, non à cause de Jésus seulement, mais pour voir Lazare, qu’il avait ressuscité d’entre les morts.
Pa nthawi imeneyi gulu lalikulu la Ayuda linadziwa kuti Yesu anali kumeneko, ndipo linabwera, sichifukwa cha Iye yekha koma kudzaonanso Lazaro, amene anamuukitsa kwa akufa.
10 Les princes des prêtres songèrent donc à faire mourir Lazare lui-même,
Choncho akulu a ansembe anakonza njira yoti aphenso Lazaro,
11 Parce que beaucoup d’entre les Juifs se retiraient d’eux à cause de lui, et croyaient en Jésus.
pakuti chifukwa cha iye Ayuda ambiri amapita kwa Yesu ndi kumukhulupirira.
12 Le lendemain, une foule nombreuse qui était venue pour la fête, ayant appris que Jésus venait à Jérusalem,
Tsiku lotsatira, gulu lalikulu la anthu lomwe linabwera kuphwando linamva kuti Yesu anali mʼnjira kupita ku Yerusalemu.
13 Prit des rameaux de palmiers, et alla au-devant de lui, criant: Hosanna, béni celui qui vient au nom du Seigneur, comme roi d’Israël!
Iwo anatenga nthambi za kanjedza ndi kupita kukakumana naye, akufuwula kuti, “Hosana! “Wodala Iye amene akubwera mʼdzina la Ambuye! “Yodala Mfumu ya Israeli!”
14 Et Jésus trouva un ânon, et s’assit dessus, comme il est écrit:
Yesu anapeza bulu wamngʼono ndi kukwerapo, monga kunalembedwa kuti:
15 Ne craignez point, filles de Sion, voici votre roi qui vient, assis sur le petit d’une ânesse.
“Usachite mantha mwana wamkazi wa Ziyoni; taona mfumu yako ikubwera, itakhala pa mwana wabulu.”
16 Ses disciples ne comprirent point ceci d’abord; mais quand Jésus fut entré dans sa gloire, alors ils se souvinrent que ces choses étaient écrites de lui, et qu’ils les lui avaient appliquées.
Poyamba ophunzira ake sanamvetsetse zonsezi. Koma pomwe Yesu analemekezedwa ndi pamene anazindikira kuti zinthu izi zinalembedwa ndipo kuti anamuchitira Iye.
17 Or c’est ainsi que rendait témoignage la multitude qui était avec lui lorsqu’il appela Lazare du tombeau et le ressuscita d’entre les morts.
Tsopano gulu la anthu lomwe linali naye pa nthawi imene amaukitsidwa Lazaro ku manda linapitiriza kuchitira umboni.
18 C’est pour cela aussi que la foule vint au-devant de lui, parce qu’ils avaient appris qu’il avait fait ce miracle.
Anthu ambiri, anapita kukakumana naye, chifukwa iwo anamva kuti Iye anachita chizindikiro chodabwitsachi.
19 Les pharisiens se dirent donc entre eux: Voyez-vous que nous ne gagnons rien? voilà que tout le monde court après lui.
Choncho Afarisi anati kwa wina ndi mnzake, “Taonani, palibe chimene mwachitapo. Anthu onse akumutsatira Iye!”
20 Or il y avait quelques gentils, de ceux qui étaient venus adorer à la fête.
Tsopano panali Agriki ena pakati pa amene anapita kukapembedza ku phwando.
21 Ceux-ci s’approchèrent de Philippe, qui était de Bethsaïde en Galilée, et ils le priaient disant: Seigneur, nous voudrions voir Jésus.
Iwo anabwera kwa Filipo, wochokera ku Betisaida wa ku Galileya, ndi pempho, nati, “Akulu, ife tikufuna kuona Yesu.”
22 Philippe vint et le dit à André; puis André et Philippe le dirent à Jésus.
Filipo anapita kukawuza Andreya; Andreya ndi Filipo pamodzi anakawuza Yesu.
23 Et Jésus leur répondit, disant: L’heure est venue que le Fils de l’homme doit être glorifié.
Yesu anayankha kuti, “Nthawi yafika yakuti Mwana wa Munthu alemekezedwe.
24 En vérité, en vérité, je vous le dis, si le grain de froment, tombant sur la terre, ne meurt pas,
Zoonadi, Ine ndikukuwuzani kuti, ‘Mbewu ya tirigu imakhala imodzi yokha ngati sikugwa mʼnthaka ndi kufa. Koma ngati imfa, imabereka mbewu zambiri.’
25 Il reste seul; mais s’il meurt, il porte beaucoup de fruits. Celui qui aime son âme la perdra; et celui qui hait son âme en ce monde, la conserve pour la vie éternelle. (aiōnios )
Munthu amene amakonda moyo wake adzawutaya, pamene munthu amene amadana ndi moyo wake mʼdziko lino lapansi adzawusungira ku moyo wosatha. (aiōnios )
26 Si quelqu’un me sert, qu’il me suive, et où je suis, là sera aussi mon serviteur. Si quelqu’un me sert, mon Père l’honorera.
Aliyense amene atumikira Ine ayenera kunditsata; ndipo kumene Ine ndili, wotumikira wanga adzakhalanso komweko. Atate anga adzalemekeza amene atumikira Ine.
27 Maintenant mon âme est troublée. Et que dirai-je? Mon Père, délivrez-moi de cette heure. Mais c’est pour cela que je suis venu en cette heure.
“Moyo wanga ukuvutika tsopano, kodi ndidzanena chiyani? Ndinene kuti Atate pulumutseni ku nthawi ino? Ayi. Chifukwa chimene Ine ndinabwera pa nthawi iyi ndi chimenechi.
28 Mon Père, glorifiez votre nom. Vint donc une voix du ciel: Je l’ai glorifié et je le glorifierai encore.
Atate, lemekezani dzina lanu!” Kenaka mawu anabwera kuchokera kumwamba, “Ine ndalilemekeza, ndipo ndidzalilemekezanso.”
29 Or la foule qui était là et qui avait entendu disait: C’est le tonnerre. D’autres disaient: Un ange lui a parlé.
Gulu la anthu lomwe linali pamenepo litamva linati, “Kwagunda bingu,” ena anati, “Mngelo wayankhula kwa Iye.”
30 Jésus répondit et dit: Ce n’est pas pour moi que cette voix est venue, mais pour vous.
Yesu anati, “Mawu awa abwera chifukwa cha inu osati chifukwa cha Ine.
31 C’est maintenant le jugement du monde, maintenant le prince de ce monde sera jeté dehors.
Ino tsopano ndi nthawi yachiweruzo pa dziko lapansi; tsopano olamulira wa dziko lapansi adzathamangitsidwa.
32 Et moi, quand j’aurai été élevé de la terre, j’attirerai tout à moi;
Koma Ine, akadzandipachika pa dziko lapansi, ndidzakokera anthu onse kwa Ine.”
33 (Or il disait cela, pour marquer de quelle mort il devait mourir.)
Iye ananena izi kuti aonetse mmene adzafere.
34 Le peuple lui répondit: Nous avons appris par la loi que le Christ demeure éternellement; et comment dis-tu, toi: Il faut que le Fils de l’homme soit élevé? Qui est-ce Fils de l’homme? (aiōn )
Gulu la anthu linayankha kuti, “Ife tinamva kuchokera mʼmalamulo kuti Khristu adzakhala kwamuyaya, nanga bwanji Inu mukunena kuti, ‘Mwana wa Munthu ayenera kukwezedwa?’ Kodi Mwana wa Munthuyu ndani?” (aiōn )
35 Jésus leur dit donc: C’est pour un peu de temps encore que la lumière est au milieu de vous. Marchez pendant que vous avez la lumière, de peur que les ténèbres ne vous surprennent; celui qui marche dans les ténèbres ne sait où il va.
Kenaka Yesu anawawuza kuti, “Inu mukhala ndi kuwunika kwa nthawi pangʼono. Yendani pamene mukanali ndi kuwunika, kuti mdima usakupitirireni. Munthu amene amayenda mu mdima sadziwa kumene akupita.
36 Pendant que vous avez la lumière, croyez en la lumière, afin que vous soyez des enfants de lumière. Jésus dit ces choses, puis il s’en alla, et se cacha d’eux.
Khulupirirani kuwunika, pamene mukanali ndi kuwunika, kuti mukhale ana a kuwunika.” Yesu atamaliza kuyankhula izi, Iye anachoka nabisala kuti asamuone.
37 Mais quoiqu’il eût fait de si grands miracles devant eux, ils ne croyaient pas en lui;
Ngakhale Yesu anachita zizindikiro zodabwitsa zonsezi pamaso pawo, sanamukhulupirirebe.
38 Afin que fût accomplie la parole que le prophète Isaïe a dite: Seigneur, qui a cru à ce qu’il a entendu de nous? Et le bras du Seigneur, à qui a-t-il été révélé?
Izi zinakwaniritsa mawu a mneneri Yesaya kuti: “Ambuye, wakhulupirira uthenga wathu ndani, ndipo ndi kwa yani komwe mkono wa Ambuye wavumbulutsidwa?”
39 C’est pourquoi ils ne pouvaient croire; et parce que Isaïe a dit encore:
Pa chifukwa cha ichi iwo sanakhulupirire, chifukwa Yesaya ananenanso kuti:
40 Il a aveuglé leurs yeux et endurci leurs cœurs, pour qu’ils ne voient des yeux, et ne comprennent du cœur, et qu’ils ne se convertissent, et que je ne les guérisse.
“Iye wachititsa khungu maso awo ndi kuwumitsa mitima yawo, kotero kuti iwo sangathe kuona ndi maso awo, kapena kuzindikira ndi mitima yawo, kapena kutembenuka kuti Ine ndikanawachiza.”
41 Isaïe a dit ces choses quand il a vu sa gloire et qu’il a parlé de lui.
Yesaya ananena izi chifukwa anaona ulemerero wa Yesu ndi kuyankhula za Iye.
42 Cependant, même parmi les chefs du peuple, beaucoup crurent en lui; mais à cause des pharisiens, ils ne le confessaient point, de peur d’être rejetés de la synagogue;
Komabe pa nthawi yomweyi ambiri ngakhale atsogoleri anakhulupirira Iye. Koma chifukwa cha Afarisi iwo sanavomereze chikhulupiriro chawo chifukwa amaopa kuti angawatulutse mʼsunagoge;
43 Car ils aimèrent la gloire des hommes plus que la gloire de Dieu.
pakuti iwo amakonda kuyamikiridwa ndi anthu kuposa kuyamikiridwa ndi Mulungu.
44 Mais Jésus s’écria et dit: Qui croit en moi ne croit pas en moi, mais en celui qui m’a envoyé.
Kenaka Yesu anafuwula nati, “Munthu aliyense amene akhulupirira Ine, sakhulupirira Ine ndekha, komanso Iye amene anandituma Ine.
45 Et qui me voit, voit celui qui m’a envoyé.
Iye amene waona Ine, waonanso Iye amene anandituma Ine.
46 Moi, la lumière, je suis venu dans le monde, afin que quiconque croit en moi ne demeure point dans les ténèbres.
Ine ndabwera mʼdziko lapansi monga kuwunika, kotero palibe amene amakhulupirira Ine nʼkumakhalabe mu mdima.
47 Et si quelqu’un entend mes paroles et ne les garde point, je ne le juge pas, moi, car je ne suis pas venu pour juger le monde, mais pour sauver le monde.
“Ndipo munthu amene amva mawu anga koma osawasunga, Ine sindimuweruza. Pakuti Ine sindinabwere kudzaweruza dziko lapansi, koma kudzapulumutsa.
48 Celui qui me méprise et ne reçoit pas mes paroles, a qui le juge: la parole que j’ai annoncée sera elle-même son juge au dernier jour.
Iye amene akana Ine ndipo salandira mawu anga ali ndi womuweruza. Tsiku lomaliza mawu amene ndiyankhulawa adzamutsutsa.
49 Parce que je n’ai point parlé de moi-même, mais mon Père qui m’a envoyé lui-même m’a prescrit ce que je dois dire et ce dont je dois parler.
Pakuti Ine sindiyankhula mwa Ine ndekha, koma Atate amene anandituma amandilamulira choti ndinene ndi momwe ndinenere.
50 Et je sais que son commandement est la vie éternelle. Ainsi ce que je dis, je le dis comme mon Père me l’a ordonné. (aiōnios )
Ine ndikudziwa kuti lamulo lake ndi moyo wosatha. Choncho chilichonse chimene Ine ndinena ndi chimene Atate andiwuza.” (aiōnios )