< Actes 24 >
1 Cinq jours après, le prince des prêtres, Ananie, descendit avec quelques anciens, et un certain Tertullus, orateur: lesquels comparurent contre Paul devant le gouverneur.
Patapita masiku asanu mkulu wa ansembe Hananiya, pamodzi ndi akuluakulu ena ndi katswiri woyankhulira anthu pa milandu wotchedwa Tertuliyo anapita ku Kaisareya ndipo anafotokoza mlandu wa Paulo kwa Bwanamkubwayo.
2 Or Paul ayant été appelé, Tertullus commença de l’accuser, disant: Jouissant par vous d’une profonde paix, et beaucoup de choses étant redressées par votre prévoyance,
Atamuyitana Paulo, ndipo Tertuliyo anafotokozera Felike nkhani yonse ya Paulo. Iye anati, “Wolemekezeka, ife takhala pamtendere nthawi yayitali chifukwa cha inu, ndipo utsogoleri wanu wanzeru wabweretsa kusintha mʼdziko lino.
3 Toujours et partout, excellent Félix, nous le reconnaissons, avec toute sorte d’actions de grâces.
Wolemekezeka Felike ife timazilandira zimenezi moyamika kwambiri ponseponse ndi mwa njira iliyonse.
4 Mais pour ne point vous retenir plus longtemps, je vous prie de nous écouter un moment avec toute votre bonté.
Koma kuti tisakuchedwetseni, ndikupempha kuti mwa kuleza mtima kwanu mutimvere ife.
5 Nous avons trouvé que cet homme, vraie peste, excite le trouble parmi les Juifs répandus dans le monde entier, et qu’il est chef de la secte séditieuse des Nazaréens;
“Ife tapeza kuti munthu uyu amayambitsa mavuto ndi kuwutsa mapokoso pakati pa Ayuda onse a dziko lonse lapansi. Iyeyu ndi mtsogoleri wa mpatuko wa Anazareti.
6 Il a même tenté de profaner le temple; et l’ayant saisi, nous avons voulu le juger suivant notre loi.
Anayesera ngakhale kudetsa Nyumba ya Mulungu wathu. Ndiye ife tinamugwira.
7 Mais le tribun Lysias survenant, l’a arraché avec une grande violence de nos mains,
Koma, mkulu wa asilikali Lusiya anafika mwamphamvu namuchotsa mʼmanja mwathu.
8 Ordonnant que ses accusateurs vinssent vers vous; c’est par lui que vous pourrez vous-même, l’interrogeant, vous assurer des choses dont nous l’accusons.
Ndipo Lusiya analamula kuti amene anali naye ndi mlandu abwere kwa inu. Mukamufunsa ameneyu kwa nokha mudzadziwa choonadi cha zimene ife tikumunenera.”
9 Et les Juifs ajoutèrent que cela était ainsi.
Ayuda anavomereza nanenetsa kuti zimenezi zinali zoona.
10 Mais Paul (le gouverneur lui ayant fait signe de parler) répondit: Sachant que depuis plusieurs années, vous êtes établi juge sur ce peuple, je me défendrai avec confiance.
Bwanamkubwayo atakodola Paulo ndi kulola kuti ayankhule, Pauloyo anati, “Ine ndikudziwa kuti inu mwakhala mukuweruza dziko lino zaka zambiri, kotero ndikukondwera kuti ndikudziteteza ndekha pamaso panu.
11 Car vous pouvez savoir qu’il n’y a pas plus de douze jours que je suis monté pour adorer à Jérusalem;
Inu mukhoza kupeza umboni wake. Sipanapite masiku khumi ndi awiri chipitireni changa ku Yerusalemu kukapembedza.
12 Et ils ne m’ont trouvé disputant avec quelqu’un ou ameutant la foule, ni dans le temple, ni dans la synagogue,
Amene akundiyimba mlanduwa sanandipeze mʼNyumba ya Mulungu ndi kutsutsana ndi wina aliyense kapena kuyambitsa chisokonezo mʼsunagoge kapena pena paliponse mu mzindamo.
13 Ni dans la ville; et ils ne sauraient vous prouver ce dont ils m’accusent maintenant.
Ndipo sangathe kupereka umboni wa mlandu umene akundiyimba inewu.
14 Mais ce que je confesse devant vous, c’est que, suivant la secte qu’ils appellent hérésie, je sers mon Père et mon Dieu, croyant à tout ce qui est écrit dans la loi et dans les prophètes;
Komatu ine ndikuvomera kuti ndimapembedza Mulungu wa makolo athu, monga wotsatira wa Njirayo, imene iwo akuyitchula mpatuko. Ine ndimakhulupirira chilichonse chimene chimagwirizana ndi malamulo ndiponso zimene zinalembedwa ndi Aneneri.
15 Ayant en Dieu l’espérance qu’il y aura une résurrection, qu’eux aussi attendent, de justes et de méchants.
Ine ndili nacho chiyembekezo chomwecho chimene iwo ali nacho mwa Mulungu, kuti kudzakhala kuuka kwa akufa kwa olungama ndiponso kwa ochimwa.
16 C’est pourquoi je m’efforce d’avoir toujours ma conscience sans reproche devant Dieu et devant les hommes.
Kotero ine ndimayesetsa kuti ndikhale ndi chikumbumtima chosanditsutsa pamaso pa Mulungu ndi anthu onse.
17 Mais après plusieurs années, je suis venu pour faire des aumônes à ma nation, et à Dieu des offrandes et des vœux.
“Patapita zaka zambiri, ndinabwera ku Yerusalemu kudzapereka mphatso kwa anthu osauka a mtundu wanga komanso kudzapereka nsembe.
18 C’est dans ces exercices qu’ils m’ont trouvé dans le temple, sans concours ni tumulte.
Pamene ndinkachita zimenezi, iwo anandipeza mʼbwalo la Nyumba ya Mulungu nditachita mwambo wodziyeretsa. Panalibe gulu la anthu kapena kuti ndimachita za chisokonezo chilichonse.
19 Et ce sont certains Juifs d’Asie, lesquels auraient dû se présenter devant vous et m’accuser, s’ils avaient quelque chose contre moi;
Koma pali Ayuda ena ochokera ku Asiya, amene amayenera kukhala pano pamaso panu, kundiyimba mlandu ngati ali ndi kalikonse konditsutsa ine.
20 Ou bien que ceux-ci disent s’ils ont trouvé en moi quelque iniquité, quand j’ai comparu devant le conseil;
Kapena awa amene ali panowa anene mlandu umene anapeza mwa ine, pamene ndinayima pamaso pa Bwalo lawo Lalikulu.
21 Si ce n’est à l’égard de cette seule parole que j’ai prononcée hautement étant au milieu d’eux: C’est à cause de la résurrection des morts, que suis aujourd’hui jugé par vous.
Koma cholakwa changa chingathe kukhala chokhachi chakuti, nditayima pamaso pawo ndinafuwula kuti, ‘Mukundiweruza ine lero chifukwa ndimakhulupirira kuti akufa adzauka.’”
22 Mais Félix qui connaissait très bien cette voie, les remit, disant: Quand le tribun Lysias sera venu, je vous écouterai.
Kenaka Felike, amene amadziwa bwino za Njirayo, anayamba wayimitsa mlanduwo, nati, “Ndidzagamula mlandu wako akabwera mkulu wa asilikali Lusiya.”
23 Et il commanda au centurion de garder Paul, mais de lui laisser du repos, et de n’empêcher aucun des siens de le servir.
Iye analamulira woyangʼanira asilikali 100 kuti alondere Paulo, koma azimupatsako ufulu ndiponso kulola abwenzi ake kuti adzimusamalira.
24 Or quelques jours après, Félix venant avec Drusille, sa femme, qui était Juive, appela Paul, et l’entendit sur ce qui touche la foi dans le Christ-Jésus.
Patapita masiku angapo Felike anabwera pamodzi ndi mkazi wake Drusila, amene anali Myuda. Anayitana Paulo ndipo anamvetsera zimene amayankhula za chikhulupiriro mwa Khristu Yesu.
25 Mais Paul discourant sur la justice, la chasteté, et le jugement futur, Félix effrayé, répondit: Quant à présent, retire-toi; je te manderai en temps opportun;
Paulo atayankhula za chilungamo, za kudziretsa ndiponso za chiweruzo chimene chikubwera, Felike anachita mantha ndipo anati, “Basi tsopano! Pita. Tidzakuyitanitsa tikadzapeza mpata.”
26 Il espérait en même temps que Paul lui donnerait de l’argent; c’est pourquoi, le faisant souvent venir, il s’entretenait avec lui.
Pa nthawi imeneyi amayembekeza kuti Paulo adzamupatsa ndalama, nʼchifukwa chake amamuyitanitsa kawirikawiri ndi kumayankhula naye.
27 Deux années s’étant écoulées, Félix eut pour successeur Portius Festus. Or Félix, voulant faire plaisir aux Juifs, laissa Paul en prison.
Patapita zaka ziwiri, Porkiyo Festo analowa mʼmalo mwa Felike, koma anamusiya Paulo mʼndende, chifukwa amafuna kuti Ayuda amukonde.