< Actes 10 >

1 Il y avait à Césarée un certain homme, du nom de Corneille, centurion de la cohorte qui est appelée Italique,
Ku Kaisareya kunali munthu wina dzina lake Korneliyo, mkulu wa asilikali 100 wa gulu la Italiya.
2 Religieux et craignant Dieu, avec toute sa maison, faisant beaucoup d’aumônes au peuple, et priant Dieu sans cesse;
Iye ndi banja lake lonse amapembedza ndi kuopa Mulungu. Iye amathandiza osowa mowolowamanja ndipo amapemphera kwa Mulungu nthawi zonse.
3 Cet homme vit manifestement en vision, vers la neuvième heure, un ange de Dieu venant à lui, et lui disant: Corneille.
Tsiku lina, nthawi ili ngati 3 koloko masana, anaona masomphenya. Anaona bwino ndithu mngelo wa Mulungu, amene anabwera kwa iye ndi kuti, “Korneliyo.”
4 Et lui, le regardant, tout saisi de crainte, dit: Qu’est-ce, Seigneur? Et l’ange lui répondit: Tes prières et tes aumônes sont montées en souvenir devant Dieu.
Korneliyo anamuyangʼanitsitsa mngeloyo mwa mantha. Iye anafunsa kuti, “Nʼchiyani kodi Ambuye?” Mngelo anayankha kuti, “Mapemphero ako ndi zachifundo zako zafika pamaso pa Mulungu ngati chikumbutso.
5 Et maintenant envoie des hommes à Joppé, et fais venir Simon, qui est surnommé Pierre;
Tsopano tuma anthu apite ku Yopa kuti akayitane munthu dzina lake Simoni Petro.
6 Il loge chez un certain Simon, corroyeur, dont la maison est près de la mer; c’est lui qui te dira ce qu’il faut faire.
Iye akukhala ndi Simoni mmisiri wa zikopa, amene nyumba yake ili mʼmbali mwa nyanja.”
7 Lorsque l’ange qui lui parlait se fut retiré, il appela deux de ses serviteurs, et un soldat craignant Dieu, de ceux qui lui étaient subordonnés.
Mngeloyo anayankhula naye anachoka, Korneliyo anayitana antchito ake awiri ndiponso msilikali mmodzi wa iwo amene ankamutumikira yemwe ankapembedza Mulungu.
8 Quand il leur eut tout raconté, il les envoya à Joppé.
Iye anawafotokozera zonse zimene zinachitika ndipo anawatuma kuti apite ku Yopa.
9 Or, le jour suivant, eux étant en chemin et approchant de la ville, Pierre monta sur le haut de la maison, vers la sixième heure, pour prier.
Mmawa mwake, nthawi ili ngati 12 koloko anthuwo atayandikira mzindawo, Petro anakwera pa denga kukapemphera.
10 Et comme il eut faim, il voulut prendre quelque nourriture. Pendant qu’on lui en apprêtait, il lui survint un ravissement d’esprit:
Iye anamva njala ndipo anafuna chakudya, ndipo akukonza chakudyacho, iye anachita ngati wakomoka.
11 Il vit le ciel ouvert, et comme une grande nappe suspendue par les quatre coins, et qu’on abaissait du ciel sur la terre,
Iye anaona kuthambo kutatsekuka, ndi chinthu china chikutsitsidwa pansi chooneka ngati chinsalu chachikulu chomangidwa pa msonga zake zinayi.
12 Et dans laquelle étaient toutes sortes de quadrupèdes, de reptiles de la terre, et d’oiseaux du ciel.
Mʼmenemo munali nyama zonse zamiyendo inayi pamodzinso ndi zokwawa za dziko lapansi ndiponso mbalame zamlengalenga.
13 Et une voix vint à lui: Lève-toi, Pierre, tue et mange.
Petro anamva mawu akuti, “Petro, dzuka, ipha nudye.”
14 Mais Pierre dit: À Dieu ne plaise. Seigneur, car je n’ai jamais mangé rien d’impur et de souillé.
Petro anayankha kuti, “Ayi, Ambuye! Ine sindinadyepo kanthu kosayeretsedwa kapena konyansa.”
15 Et la voix lui dit encore une seconde fois: Ce que Dieu a purifié, ne l’appelle pas impur.
Petro anamvanso kachiwiri mawu akuti, “Usachiyese chonyansa chimene Mulungu wachiyeretsa.”
16 Or cela fut fait par trois fois, et aussitôt la nappe fut retirée dans le ciel.
Zimenezi zinachitika katatu ndipo nthawi yomweyo chinsalu chija chinatengedwanso kupita kumwamba.
17 Pendant que Pierre hésitait en lui-même sur ce que signifiait la vision qu’il avait eue, voilà que les hommes qui avaient été envoyés par Corneille, s’enquérant de la maison de Simon, arrivèrent à la porte.
Petro akuganizira za tanthauzo la masomphenyawo, anthu amene Korneliyo anawatuma anapeza kumene kunali nyumba ya Simoni ndipo anayima pa chipata.
18 Et ayant appelé, ils demandaient si ce n’était point là que logeait Simon, surnommé Pierre.
Iwo anayitana nafunsa ngati Simoni amene amadziwika ndi dzina loti Petro amakhala kumeneko.
19 Cependant, comme Pierre songeait à la vision, l’Esprit lui dit: Voilà trois hommes qui te cherchent.
Petro akuganizirabe za masomphenyawo, Mzimu Woyera anati kwa iye, “Simoni, anthu atatu akukufunafuna.
20 Lève-toi donc, descends, et va avec eux sans hésitation aucune, parce que c’est moi qui les ai envoyés.
Dzuka, tsika. Usakayike upite nawo pakuti ndawatuma ndine.”
21 Or Pierre étant descendu vers les hommes dit: Je suis celui que vous cherchez; quelle est la cause pour laquelle vous êtes venus?
Petro anatsika ndipo anati kwa anthuwo, “Amene mukufunayo ndine. Mwabwera kuno chifukwa chiyani?”
22 Ils répondirent: Corneille, centurion, homme juste et craignant Dieu, et ayant pour lui le témoignage de toute la nation juive a reçu d’un ange saint l’ordre de vous appeler dans sa maison, et d’écouter vos paroles.
Anthuwo anayankha kuti, “Ife tachokera kwa Korneliyo, mkulu woyangʼanira asilikali 100. Iye ndi munthu wolungama ndiponso woopa Mulungu, amene amalemekezedwa ndi Ayuda onse. Mngelo woyera anamuwuza kuti mupite ku nyumba yake kuti akamve mawu amene inu mukanene.”
23 Les faisant donc entrer, il les logea. Mais le jour suivant, il partit avec eux; et quelques-uns des frères de Joppé l’accompagnèrent.
Pamenepo Petro anawalowetsa mʼnyumba ndipo anawasamala ngati alendo ake. Mmawa mwake Petro ananyamuka napita nawo ndipo abale ena a ku Yopa anapita naye pamodzi.
24 Et le jour d’après il entra dans Césarée. Or Corneille les attendait, ses parents et ses amis les plus intimes étant assemblés.
Tsiku linalo Petro anafika ku Kaisareya. Korneliyo anawadikirira ndipo anali atawasonkhanitsa pamodzi abale ake ndi abwenzi ake a pamtima.
25 Et il arriva que lorsque Pierre entrait, il vint au devant de lui, et, tombant à ses pieds, il l’adora.
Petro akulowa mʼnyumba, Korneliyo anakumana naye ndipo anadzigwetsa pa mapazi ake namulambira.
26 Mais Pierre le releva, disant: Levez-vous; et moi aussi je ne suis qu’un homme.
Koma Petro anamuyimiritsa nati, “Imirira, inenso ndine munthu ngati iwe.”
27 Et s’entretenant avec lui, il entra, et trouva un grand nombre de personnes qui étaient assemblées;
Akuyankhula naye, Petro analowa mʼnyumba ndipo anapeza gulu lalikulu la anthu litasonkhana.
28 Et il leur dit: Vous savez, vous, quelle abomination c’est pour un homme juif, que de fréquenter ou même d’approcher un étranger; mais Dieu m’a montré à ne traiter aucun homme d’impur ou de souillé.
Iye anawawuza kuti, “Inu mukudziwa bwino kuti ndi kutsutsana ndi lamulo ngati Myuda ayanjana ndi Mkunja kapena kuyendera wina aliyense wa mtundu wina. Koma Mulungu wandionetsa ine kuti ndisatchule munthu aliyense kuti ndi wosayenera kapena wonyansa.
29 C’est pourquoi, ayant été appelé, je suis venu sans hésitation. Je vous demande donc pour quel sujet vous m’avez appelé?
Nʼchifukwa chake ndabwera mosawiringula pamene munandiyitana. Tsopano ndikufunseni,” Mwandiyitanira chiyani?
30 Et Corneille lui dit: Il y a en ce moment quatre jours, j’étais priant dans ma maison, à la neuvième heure; et voilà qu’un homme vêtu de blanc se présenta devant moi, et dit:
Komeliyo anayankha kuti, “Masiku anayi apitawo, nthawi yonga yomwe ino, 3 koloko masana ndimapemphera mʼnyumba mwanga. Mwadzidzidzi patsogolo panga panayimirira munthu wovala zovala zonyezimira.
31 Corneille, ta prière a été exaucée, et tes aumônes ont été en souvenir devant Dieu.
Ndipo anati, ‘Korneliyo, Mulungu wamva mapemphero ako ndipo wakumbukira mphatso zako kwa osauka.
32 Ainsi envoie à Joppé et fais venir Simon, qui est surnommé Pierre; il est logé dans la maison de Simon, corroyeur, près de la mer.
Tuma anthu ku Yopa akayitane Simoni wotchedwa Petro. Iye akukhala mʼnyumba ya Simoni mmisiri wazikopa amene amakhala mʼmbali mwa nyanja.’
33 Aussitôt donc, j’ai envoyé vers vous, et vous m’avez fait la grâce de venir. Maintenant donc, nous sommes tous devant vous pour entendre tout ce que le Seigneur vous a commandé.
Nʼchifukwa chake ndinatumiza anthu nthawi yomweyo ndipo mwachita bwino kuti mwabwera. Tsopano ife tonse tili pano pamaso pa Mulungu kuti timve zonse zimene Ambuye akukulamulani kuti mutiwuze ife.”
34 Alors, ouvrant la bouche, Pierre dit: En vérité, je vois que Dieu ne fait point acception des personnes;
Ndipo Petro anayamba kuyankhula nati, “Zoonadi, tsopano ndazindikira kuti Mulungu sakondera.
35 Mais qu’en toute nation celui qui le craint et pratique la justice, lui est agréable.
Koma amalandira anthu a mtundu uli wonse amene amaopa Iye ndiponso kuchita chilungamo.
36 Dieu a envoyé la parole aux enfants d’Israël, annonçant la paix par Jésus-Christ (qui est le Seigneur de tous);
Uwu ndi uthenga umene Mulungu anatumiza kwa Aisraeli, kulalikira Uthenga Wabwino wamtendere mwa Yesu Khristu amene ndi Ambuye wa onse.
37 Vous savez, vous, ce qui est arrivé dans toute la Judée, en commençant par la Galilée, après le baptême que Jean a prêché;
Inu mukudziwa zimene zinachitika ku Yudeya konse, kuyambira ku Galileya pambuyo pa ubatizo umene Yohane analalikira,
38 Comment Dieu a oint de l’Esprit-Saint et de sa vertu, Jésus de Nazareth, qui a passé en faisant le bien et guérissant tous ceux qui étaient opprimés par le diable, parce que Dieu était avec lui.
kuti Mulungu, anamudzoza Yesu, wa ku Nazareti ndi Mzimu Woyera ndi mphamvu ndiponso mmene Iye anapita nachita zabwino ndi kuchiritsa onse amene anali pansi pa mphamvu ya mdierekezi, popeza kuti Mulungu anali naye.
39 Et nous, nous sommes témoins de tout ce qu’il a fait dans le pays des Juifs et à Jérusalem, ce Jésus qu’ils ont tué, le suspendant à un bois.
“Ife ndife mboni za zonse zimene anachita mʼdziko la Ayuda ndiponso ku Yerusalemu. Anamupha Iye pakumupachika pa mtengo,
40 Dieu l’a ressuscité le troisième jour, et lui a donné de se manifester,
koma Mulungu anamuukitsa kwa akufa pa tsiku lachitatu, ndipo analola kuti aonekere poyera.
41 Non à tout le peuple, mais aux témoins préordonnés de Dieu, à nous, qui avons mangé et bu avec lui, après qu’il fut ressuscité des morts.
Iye sanaonekere kwa anthu onse koma kwa mboni zimene Mulungu anazisankhiratu, kwa ife amene timadya ndi kumwa naye atauka kwa akufa.
42 Et il nous a commandé de prêcher au peuple et d’attester que c’est celui que Dieu a établi juge des vivants et des morts.
Iye anatilamulira ife kuti tilalikire kwa anthu ndi kuchitira umboni kuti Iye ndiye amene Mulungu anamusankha kukhala woweruza wa amoyo ndi akufa.
43 C’est à lui que tous les prophètes rendent ce témoignage que tous ceux qui croient en lui reçoivent, par son nom, la rémission des péchés.
Aneneri onse achitira Iye umboni kuti aliyense amene akhulupirira Iye amakhululukidwa machimo chifukwa cha dzina lake.”
44 Pierre parlant encore, l’Esprit-Saint descendit sur tous ceux qui écoutaient la parole.
Petro akuyankhulabe mawu amenewa, Mzimu Woyera unatsikira pa onse amene amamva uthengawo.
45 Et les fidèles circoncis, qui étaient venus avec Pierre, s’étonnèrent grandement de ce que la grâce de l’Esprit-Saint était aussi répandue sur les gentils.
Abale a mdulidwe omwe anabwera ndi Petro anadabwa kuona kuti mphatso ya Mzimu Woyera yapatsidwanso kwa anthu a mitundu ina.
46 Car ils les entendaient parlant diverses langues et glorifiant Dieu.
Pakuti anamva iwo akuyankhula mʼmalilime ndi kuyamika Mulungu. Ndipo Petro anati,
47 Alors Pierre dit: Peut-on refuser l’eau du baptême à ceux qui ont reçu l’Esprit-Saint comme nous?
“Kodi alipo amene angawaletse anthu awa kubatizidwa mʼmadzi? Iwotu alandira Mzimu Woyera monga ifenso.”
48 Et il ordonna qu’ils fussent baptisés au nom du Seigneur Jésus-Christ. Alors ils le prièrent de demeurer avec eux quelques jours.
Tsono iye analamula kuti abatizidwe mʼdzina la Yesu Khristu. Ndipo anthu aja anamupempha Petro kuti akhale nawo masiku angapo.

< Actes 10 >