< 2 Samuel 2 >
1 Et après cela David consulta le Seigneur, disant: Est-ce que je monterai dans une des villes de Juda? Et le Seigneur lui dit: Monte. Alors David demanda: Où monterai-je? Et le Seigneur lui répondit: À Hébron.
Patapita nthawi, Davide anafunsa Yehova kuti, “Kodi ndipite ku umodzi mwa mizinda ya Yuda?” Yehova anayankha kuti, “Pita.” Davide anafunsanso kuti, “Kodi ndipite kuti?” Yehova anayankha kuti, “Ku Hebroni.”
2 David donc monta, et ses deux femmes Achinoam, Jezraélite, et Abigaïl, femme de Nabal du Carmel.
Choncho Davide anapita kumeneko ndi akazi ake awiri, Ahinoamu wa ku Yezireeli ndi Abigayeli mkazi wamasiye uja wa Nabala wa ku Karimeli.
3 Mais David mena aussi les hommes qui étaient avec lui, chacun avec sa maison; et ils demeurèrent dans les villes d’Hébron.
Davide anatenganso anthu amene anali nawo aliyense ndi banja lake, ndipo anakakhala ku midzi ya ku Hebroni.
4 Alors vinrent les hommes de Juda, et ils oignirent là David, afin qu’il régnât sur la maison de Juda. Et on annonça à David que les hommes de Jabès-Galaad avaient enseveli Saül.
Kenaka amuna a ku Yuda anabwera ku Hebroni ndipo kumeneko anadzoza Davide kukhala mfumu ya fuko la Yuda. Davide atawuzidwa kuti anthu a ku Yabesi Giliyadi ndi amene anayika mʼmanda Sauli,
5 David donc envoya des messagers aux hommes de Jabès-Galaad, et leur dit: Bénis soyez du Seigneur, vous qui avez fait cette miséricorde à votre seigneur Saül, et l’avez enseveli!
iye anatuma amithenga kwa anthu a ku Yabesi Giliyadi kuti akayankhule nawo kuti, “Yehova akudalitseni poonetsa kukoma mtima kwanu kwa Sauli mbuye wanu pomuyika mʼmanda.
6 Et maintenant le Seigneur vous rendra miséricorde et fidélité; mais moi aussi je vous rendrai grâces de ce que vous avez fait cette action.
Tsopano Yehova akuonetseni kukoma mtima ndi kukhulupirika kwake ndipo inenso ndidzakukomerani mtima chifukwa munachita zimenezi.
7 Que vos mains se fortifient, et soyez des fils de courage; car, quoique votre seigneur Saül soit mort, néanmoins la maison de Juda m’a oint pour son roi.
Tsopano khalani amphamvu ndi olimba mtima, pakuti Sauli mbuye wanu wafa, ndipo fuko la Yuda landidzoza kukhala mfumu yawo.”
8 Mais Abner, fils de Ner, prince de l’armée de Saül, prit Isboseth, fils de Saül, et lui fit parcourir le camp.
Pa nthawi imeneyi Abineri mwana wa Neri, wolamulira ankhondo a Sauli, anatenga Isi-Boseti mwana wa Sauli ndi kubwera naye ku Mahanaimu.
9 Et il l’établit roi sur Galaad, sur Gessuri, sur Jezraël, sur Ephraïm, sur Benjamin et sur tout Israël.
Iye anamuyika kuti akhale mfumu yoyangʼanira Giliyadi, Asuri ndi Yezireeli, pamodzi ndi Efereimu, Benjamini ndi Israeli yense.
10 Isboseth, fils de Saül, avait quarante ans, lorsqu’il commença à régner sur Israël, et il régna deux ans; mais la seule maison de Juda suivait David.
Isi-Boseti mwana wa Sauli anali wa zaka makumi anayi pamene anakhala mfumu ya Israeli ndipo analamulira zaka ziwiri. Koma fuko la Yuda linatsatira Davide.
11 Et le nombre des jours que David demeura, régnant à Hébron sur la maison de Juda, fut de sept ans et six mois.
Davide anakhala mfumu ku Hebroni akulamulira fuko la Yuda, kwa zaka zisanu ndi chimodzi ndi miyezi isanu ndi umodzi.
12 Et Abner, fils de Ner, sortit du camp, et les serviteurs d’Isboseth, fils de Saül, pour venir à Gabaon.
Abineri mwana wa Neri, pamodzi ndi ankhondo a Isi-Boseti mwana wa Sauli, anachoka ku Mahanaimu ndi kupita ku Gibiyoni.
13 Mais Joab, fils de Sarvia, et les serviteurs de David sortirent, et les rencontrèrent près de la piscine de Gabaon. Et lorsqu’ils se furent assemblés, ils se postèrent en droite ligne, ceux-ci d’un côté de la piscine, et ceux-là de l’autre.
Yowabu mwana wa Zeruya pamodzi ndi ankhondo a Davide anapita ndi kukakumana nawo ku dziwe la ku Gibiyoni. Gulu lina linakhala mbali ina ya dziwelo pamene gulu lina linakhala mbali inayo.
14 Alors Abner dit à Joab: Que les jeunes hommes se lèvent, et qu’ils escarmouchent devant nous. Et Joab répondit: Qu’ils se lèvent.
Kenaka Abineri anati kwa Yowabu, “Tiye tibweretse ena mwa anyamata athu kuti amenyane patsogolo pathupa.” Yowabu anayankha, “Chabwino, amenyane.”
15 Ils se levèrent donc, et ils passèrent au nombre de douze de Benjamin, du côté d’Isboseth, fils de Saül, et de douze d’entre les serviteurs de David.
Kotero anayimirira ndipo anawawerenga: anyamata khumi ndi awiri a fuko la Benjamini ndi Isi-Boseti mwana wa Sauli ndiponso anyamata khumi ndi awiri a Davide.
16 Et chacun, ayant pris par la tête son concurrent, enfonça son glaive dans le côté de son adversaire, et ils tombèrent ensemble; et on appela ce lieu du nom de Champ des forts à Gabaon.
Tsono aliyense anagwira mutu wa mnzake namubaya mnzakeyo mʼnthiti ndi mpeni ndipo onse anagwera pansi limodzi. Kotero malo amenewo ku Gibiyoni amatchedwa Helikati Hazurimu.
17 Et il s’éleva une guerre très violente en ce jour-là; et Abner fut mis en fuite et les hommes d’Israël par les serviteurs de David.
Tsiku limeneli nkhondo yake inali yoopsa kwambiri, ndipo Abineri ndi ankhondo a Israeli anagonjetsedwa ndi ankhondo a Davide.
18 Or étaient là les trois fils de Sarvia, Joab, Abisaï et Asaël; et Asaël fut un coureur très agile, comme un des chevreuils qui demeurent dans les forêts.
Ana atatu aamuna a Zeruya, Yowabu, Abisai ndi Asaheli anali komweko. Koma Asaheli anali waliwiro ngati insa.
19 Aussi Asaël poursuivait Abner, et il ne se détourna ni à droite ni à gauche, ne cessant de poursuivre Abner.
Iye anathamangitsa Abineri ndipo sanakhotere kumanja kapena kumanzere pamene amamutsatira.
20 C’est pourquoi Abner regarda derrière lui, et dit: Es-tu Asaël, toi? Et il répondit: Oui, je le suis.
Abineri anayangʼana mʼmbuyo ndipo anafunsa, “Kodi ndiwe Asaheli?” Iye anayankha kuti, “Ndine.”
21 Et Abner lui dit: Va à droite ou à gauche, et saisis un de ces jeunes hommes et prends pour toi ses dépouilles. Mais Asaël ne voulut pas cesser de le poursuivre.
Ndipo Abineri anati kwa iye, “Khotera kumanja kapena kumanzere: tsatira mmodzi mwa anyamatawa ndipo umulande zida zake.” Koma Asaheli sanasiye kumuthamangitsa.
22 Et Abner parla de nouveau à Asaël: Retire-toi, ne me suis point, pour ne pas que je sois forcé de te percer contre la terre; car je ne pourrai lever ma face du côté de Joab ton frère.
Abineri anamuchenjezanso Asaheli, “Siya kuthamangitsa ine! Kodi ndikukanthe chifukwa chiyani? Kodi ndikaonana naye bwanji mʼbale wako Yowabu?”
23 Asaël dédaigna de l’entendre, et ne voulut pas se détourner. Abner donc, retournant sa lance, le frappa dans l’aîne, le transperça, et il mourut dans le même lieu; et tous ceux qui passaient par ce lieu dans lequel Asaël était tombé et était mort, s’arrêtaient.
Koma iye anakana kuleka kumuthamangitsa. Choncho Abineri anabaya Asaheli mʼmimba ndi msonga ya mkondo wake ndipo mkondowo unatulukira mbali ina. Iye anagwa ndi kufera pamalo pomwepo. Ndipo munthu aliyense amayima akafika pamalo pamene anagwera ndi kufa.
24 Or, Joab et Abisaï poursuivant Abner qui s’enfuyait, le soleil se coucha; et ils vinrent jusqu’à la colline de l’aqueduc, qui est vis-à-vis de la vallée, sur le chemin du désert de Gabaon.
Koma Yowabu ndi Abisai anathamangitsa Abineri, ndipo dzuwa likulowa, anafika ku phiri la Ama, pafupi ndi Giya pa njira yopita ku chipululu cha ku Gibiyoni.
25 Et les enfants de Benjamin s’assemblèrent auprès d’Abner; et réunis en un seul bataillon, ils s’arrêtèrent sur le haut d’un tertre.
Pamenepo anthu a fuko la Benjamini anasonkhana kudzathandiza Abineri. Iwo anapanga gulu ndipo anayima pamwamba pa phiri.
26 Alors Abner cria à Joab, et dit: Est-ce jusqu’à la dernière extermination que ton glaive tranchant sévira? Ignores-tu que le désespoir est dangereux? Jusqu’à quand ne diras-tu pas au peuple, qu’il cesse de poursuivre ses frères?
Abineri anayitana Yowabu, “Kodi tipitirize kumenyana mpaka kalekale? Kodi sukuzindikira kuti mathero ake kudzakhala kuwawidwa mitima? Kodi udzawaletsa liti ankhondo ako kuthamangitsa abale awo?”
27 Et Joab lui répondit: Le Seigneur vit! si tu avais parlé, ce matin se serait retiré le peuple qui poursuit son frère.
Yowabu anayankha kuti, “Pali Yehova wamoyo, ukanapanda kuyankhula, ankhondo anga akanapitiriza kuthamangitsa abale awo mpaka mmawa.”
28 Joab donc sonna de la trompette, et toute l’armée s’arrêta; et ils ne poursuivirent plus Israël, et ils n’engagèrent pas le combat.
Chomwecho Yowabu analiza lipenga, ndipo ankhondo onse anayima. Iwo analeka kuthamangitsa Aisraeli kapena kumenyana nawo.
29 Or, Abner et ses hommes s’en allèrent à travers les plaines, pendant toute cette nuit-là, et ils passèrent le Jourdain, et, tout Béthoron traversé, ils vinrent au camp.
Usiku wonsewo Abineri ndi ankhondo ake anayenda kudutsa Araba. Iwo anawoloka Yorodani, napitirira mpaka kudutsa dera lonse la Bitironi ndipo anafika ku Mahanaimu.
30 Quant à Joab, étant revenu, après avoir laissé Abner de côté, il assembla tout le peuple; et il manqua des serviteurs de David dix-neuf hommes, sans compter Asaël.
Choncho Yowabu anabwerera kuchokera kothamangitsa Abineri ndipo anasonkhanitsa ankhondo ake onse. Kupatula Asaheli, panali ankhondo khumi ndi anayi a Davide amene anasowa.
31 Mais les serviteurs de David frappèrent de Benjamin et des hommes qui étaient avec Abner trois cent soixante, qui même moururent.
Koma ankhondo a Davide anapha ankhondo a fuko la Benjamini 360 amene anali ndi Abineri.
32 Et ils emportèrent Asaël, et l’ensevelirent dans le sépulcre de son père à Bethléhem; et Joab et les hommes qui étaient avec lui marchèrent pendant toute la nuit, et au point du jour ils parvinrent à Hébron.
Iwo anatenga Asaheli ndi kukamuyika mʼmanda a abambo ake ku Betelehemu. Ndipo Yowabu ndi ankhondo ake anayenda usiku wonse ndi kufika ku Hebroni kukucha.