< 2 Corinthiens 7 >
1 Ayant donc ces promesses, purifions-nous, mes bien-aimés, de toute souillure de la chair et de l’esprit, et achevons notre sanctification dans la crainte de Dieu.
Abwenzi okondedwa, popeza tili ndi malonjezo amenewa, tiyeni tidziyeretse, kusiyana nazo zilizonse zimene zikhoza kudetsa thupi ndi mzimu, ndipo tiyesetse kukhala oyera mtima poopa Mulungu.
2 Donnez-nous place. Nous n’avons lésé personne, corrompu personne, fraudé personne.
Mutipatse malo mʼmitima mwanu. Ife sitinalakwire munthu aliyense, kapena kuyipitsa munthu aliyense, kapena kumuchenjerera munthu aliyense.
3 Ce n’est pas pour vous condamner que je vous parle ainsi; car je vous ai déjà dit que vous êtes dans nos cœurs à la mort et à la vie.
Sindikunena izi kuti mupezeke olakwa. Ndinanena kale kuti ife timakuganizirani kwambiri kotero kuti tili pamodzi, ngakhale tikhale moyo kapena timwalire.
4 J’use d’une grande liberté envers vous; je me glorifie beaucoup de vous; Je suis rempli de consolation, je surabonde de joie dans toutes nos tribulations.
Ndimakukhulupirirani kwambiri ndipo ndimakunyadirani kwambiri. Ndikulimbikitsidwa kwambiri; mʼmasautso athu onse, chimwemwe changa chilibe malire.
5 Car, lorsque nous sommes venus en Macédoine, notre chair n’a eu aucun repos, mais nous avons souffert toute sorte d’afflictions: au dehors, combats; au dedans, frayeurs.
Pakuti titafika ku Makedoniya, sitinapume nʼkomwe, koma tinavutitsidwa mbali zonse. Kunja kunali mikangano, ndipo mʼmitima mwathu munali mantha.
6 Mais celui qui console les humbles, Dieu, nous a consolés par l’arrivée de Tite;
Koma Mulungu, amene amatonthoza mtima wopsinjika, anatitonthoza mtima ndi kufika kwa Tito,
7 Non-seulement par son arrivée, mais encore par la consolation qu’il a reçue de vous; nous ayant raconté votre désir, vos pleurs, votre zèle pour moi, de sorte que ma joie en a été plus grande.
sikubwera kwake kokhako, komanso mawu achilimbikitso amene analandira kuchokera kwa inu. Iye anatiwuza kuti mukufuna kundiona, zachisoni chanu chachikulu, ndi kudzipereka kwanu kwa ine, motero chimwemwe changa chinachuluka kuposa kale.
8 Car quoique je vous aie contristés par ma lettre, je ne m’en repens point; et si je m’en suis repenti, en voyant que cette lettre vous avait (bien que pour peu de temps) causé de la tristesse,
Ngakhale kalata yanga ija inakupwetekani mtima, sindikudandaula kuti ndinalemberanji. Ngakhale zinandikhudza, ndikudziwa kuti kalata yanga inakupwetekani, koma kwa kanthawi kochepa.
9 Maintenant je me réjouis, non de ce que vous avez été contristés, mais de ce que vous avez été contristés de manière à faire pénitence; car vous avez été contristés selon Dieu, de sorte que vous n’avez reçu de nous aucun dommage.
Koma tsopano ndine wokondwa, osati chifukwa chakuti kalatayo inakupwetekani, koma chifukwa chakuti chisoni chanu chinakuthandizani kutembenuka mtima. Pakuti munamva chisoni monga mmene Mulungu amafunira, choncho simunapwetekedwe mwanjira iliyonse.
10 Car la tristesse qui est selon Dieu produit pour le salut une pénitence stable; mais la tristesse du siècle produit la mort.
Chisoni chimene Mulungu amafuna chimabweretsa kutembenuka mtima komwe kumabweretsa chipulumutso, ndipo sichikhumudwitsa. Koma chisoni cha dziko lapansi chimabweretsa imfa.
11 Voyez, en effet, combien cette tristesse selon Dieu que vous avez ressentie a produit en vous non-seulement de vigilance, mais de soin de vous justifier, mais d’indignation, mais de crainte, mais de désir, mais de zèle, mais de vengeance; de toute manière, vous avez montré que vous étiez purs dans cette affaire.
Taonani zimene chisoni chimene Mulungu amafuna chatulutsa mwa inu. Chatulutsa khama lalikulu, chakuthandizani kuti mudzikonze nokha, chakukwiyitsani kwambiri, komanso chakupatsani mantha aakulu. Chakuchititsani kuti mufune kundiona ine, mwakhudzidwa kwambiri ndipo mukufuna kuonetsetsa kuti chilungamo chachitikadi. Pa nkhani yonseyi, mwaonetsadi kuti ndinu osalakwa.
12 Si donc je vous ai écrit, ce n’était, ni à cause de celui qui a commis l’injure, ni à cause de celui qui l’a soufferte, mais pour vous faire connaître la sollicitude que nous avons pour vous
Choncho ngakhale ndinakulemberani kalata ija, sindinayilembe ndi chifukwa cha amene analakwayo kapena wolakwiridwa, koma ndinayilemba kuti inuyo muone kudzipereka kwanu kwa ife pamaso a Mulungu.
13 Devant Dieu; c’est pourquoi nous avons été consolés. Or dans notre consolation, notre joie s’est accrue de celle de Tite, parce que vous avez tous contribué au repos de son esprit.
Zimenezi zatilimbikitsa kwambiri. Kuwonjezera pa zotilimbikitsazo, tinakondwa kwambiri poona chisangalalo cha Tito, chifukwa nonsenu munamuthandiza kukhazikitsa mtima wake pansi.
14 Et si je me suis glorifié de vous auprès de lui, je n’ai pas eu à en rougir; mais comme nous vous avions dit toutes choses selon la vérité, aussi le témoignage glorieux que nous avions rendu à Tite a été justifié.
Ndinamuwuza kuti ndimakunyadirani, ndipo simunandichititse manyazi. Koma monga zonse zimene tinakuwuzani zinali zoona, tsono zomwe ndinawuza Tito zokunyadirani zinali zoona.
15 C’est pourquoi, dans le fond de ses entrailles, il redouble d’affection pour vous, lorsqu’il se ressouvient de l’obéissance de vous tous, et avec quelle crainte et quel tremblement vous l’avez reçu.
Ndipo chikondi chake pa inu nʼchachikulu kwambiri akakumbukira kuti nonse munali omvera, munamulandira ndi mantha ndi kunjenjemera.
16 Je me réjouis donc de ce qu’en toutes choses je puis me lier à vous.
Ndine wokondwa kuti ndingathe kukukhulupirirani pa zonse.