< 1 Pierre 3 >
1 Pareillement, que les femmes aussi soient soumises à leurs maris; afin que si quelques-uns ne croient pas à la parole, ils soient gagnés sans la parole, par la conduite de leurs femmes,
Momwemonso, akazi inu gonjerani amuna anu kuti ngati ena a iwo sakhulupirira Mawu a Mulungu, akopeke ndi makhalidwe a akazi awo ndipo sipadzafunikanso mawu
2 En considérant votre conduite chaste, jointe à une crainte respectueuse.
pamene aona moyo wanu wachiyero ndi moyo woopa Mulungu.
3 Qu’elles n’aient pas au dehors une chevelure habilement arrangée, ou des ornements d’or, ou de riches vêtements pour parure,
Kudzikongoletsa kwanu kusakhale kwa maonekedwe akunja, monga kuluka tsitsi ndi kuvala zokometsera zagolide ndi zovala zamberewere.
4 Mais au dedans, l’homme caché dans l’incorruptibilité de l’esprit calme et modeste, qui est d’un grand prix aux yeux de Dieu.
Mʼmalo mwake kudzikongoletsa kwanu kukhale kwa munthu wa mʼkatimo, kukongola kosatha kwa mtima ofatsa ndi mzimu wachete, zimene ndi za mtengowapatali pamaso pa Mulungu.
5 Car c’est ainsi qu’autrefois les saintes femmes, espérant en Dieu, se paraient, étant soumises à leurs maris.
Pakuti umo ndi mmene akazi oyera mtima akale amene anali ndi chiyembekezo pa Mulungu anadzikongoletsera. Iwo ankagonjera amuna awo,
6 Telle était Sara, qui obéissait à Abraham, l’appelant son seigneur, et dont vous êtes les filles, en faisant le bien, et ne craignant aucun trouble.
monga Sara, amene anamvera Abrahamu namutcha iye mbuye wake. Akazi inu ndinu ana ake ngati muchita zoyenera, ndipo musaope choopsa chilichonse.
7 Vous aussi, maris, vivez sagement avec vos femmes, les honorant comme un vase plus faible, et comme cohéritières de la grâce de vie; afin que vos prières n’aient point d’empêchement.
Momwemonso amuna inu, khalani mwanzeru ndi akazi anu, ndipo muwachitire ulemu monga anzanu ofowoka ndiponso olandira nanu pamodzi mphatso ya moyo wosatha, kuti pasakhale kanthu kotsekereza mapemphero anu.
8 Enfin soyez tous unis d’un même cœur, compatissants, vous aimant en frères, miséricordieux, modestes, humbles,
Potsiriza, nonse khalani a mtima umodzi, omverana chisoni. Kondanani monga abale, muchitirane chifundo ndi kudzichepetsa.
9 Ne rendant point mal pour mal, ni malédiction pour malédiction; mais, au contraire, bénissant parce que c’est à cela que vous avez été appelés, afin de posséder la bénédiction en héritage.
Wina akakuchitirani choyipa musabwezere pochitanso choyipa, kapena kubwezera chipongwe akakuchitirani chipongwe, koma muwadalitse. Munayitanidwa kuti mulandire mdalitso.
10 Que celui donc qui veut aimer la vie, et voir des jours bons, défende sa langue du mal, et que ses lèvres ne profèrent point les paroles de tromperie;
Pakuti, “Iye amene angakonde moyo ndi kuona masiku abwino, aletse lilime lake kuyankhula zoyipa, ndiponso milomo yake kunena mabodza.
11 Qu’il se détourne du mal et fasse le bien; qu’il cherche la paix et la poursuive;
Apewe zoyipa, ndipo azichita zabwino. Afunefune mtendere ndi kuyesetsa kuwupeza.
12 Parce que les yeux du Seigneur sont sur les justes, et ses oreilles à leurs prières; mais la face du Seigneur est sur ceux qui font le mal.
Pakuti Ambuye amayangʼanira bwino anthu olungama ndipo amatchera khutu ku mapemphero awo. Koma Ambuye sawayangʼana bwino amene amachita zoyipa.”
13 Et qui est-ce qui vous nuira, si vous avez le zèle du bien?
Ndani angakuchitireni zoyipa ngati muchita changu kuchita zabwino?
14 Et si même vous souffrez pour la justice, vous serez bien heureux. N’ayez donc aucune crainte d’eux, et ne vous en troublez point.
Koma ngakhale mumve zowawa chifukwa cha chilungamo, ndinu odala. “Musaope anthu, musachite mantha.”
15 Mais glorifiez dans vos cœurs la sainteté du Seigneur Jésus-Christ, toujours prêts à satisfaire quiconque vous demandera la raison de l’espérance qui est en vous;
Koma lemekezani Khristu mʼmitima mwanu ngati Ambuye wanu. Khalani okonzeka nthawi zonse kuyankha aliyense amene akufunsani za chiyembekezo chimene muli nacho.
16 Toutefois, avec modestie et respect, conservant une bonne conscience, afin qu’ils soient confondus pour le mal qu’ils disent de vous, ceux qui calomnient votre bonne conduite dans le Christ.
Koma chitani zimenezi mofatsa ndi mwaulemu, mukhale ndi chikumbumtima chosakutsutsani, kuti anthu ena akanena zoyipa za makhalidwe anu abwino mwa Khristu, achite okha manyazi ndi chipongwe chawocho.
17 Car il vaut mieux souffrir (si Dieu le veut ainsi) en faisant le bien qu’en faisant le mal;
Nʼkwabwino ngati ndi chifuniro cha Mulungu kumva zowawa chifukwa chochita zabwino kusiyana ndi kumva zowawa chifukwa chochita zoyipa.
18 Puisque le Christ lui-même est mort une fois pour nos péchés, le juste pour les injustes, afin de nous offrir à Dieu, ayant été mis à mort selon la chair, mais étant ressuscité selon l’esprit,
Pakuti Khristu anafa chifukwa cha machimo kamodzi kokha kufera onse, wolungama kufera osalungama, kuti akufikitseni kwa Mulungu. Anaphedwa ku thupi koma anapatsidwa moyo mu mzimu.
19 En lequel il vint aussi prêcher les esprits retenus en prison,
Ndipo ali ngati mzimu chomwecho anapita ndi kukalalikira mizimu imene inali mʼndende,
20 Qui avaient été incrédules autrefois, lorsqu’aux jours de Noé ils se reposaient sur la patience de Dieu, pendant qu’on bâtissait l’arche dans laquelle peu de personnes, c’est-à-dire huit seulement, furent sauvées par l’eau.
ya anthu amene sanamvere Mulungu atadikira moleza mtima pa nthawi imene Nowa ankapanga chombo. Mʼchombo chija anthu owerengeka okha, asanu ndi atatu, ndiwo anapulumutsidwa ku madzi.
21 Ce qui vous sauve maintenant vous-mêmes, c’est un baptême semblable: non pas une purification des souillures de la chair, mais l’engagement d’une bonne conscience envers Dieu par la résurrection de Jésus-Christ,
Madziwo akufanizira ubatizo umene lero ukukupulumutsaninso, osati chifukwa chochotsa litsiro la mʼthupi koma chifukwa cha chikumbumtima choona pamaso pa Mulungu. Umakupulumutsani chifukwa cha kuuka kwa Yesu Khristu,
22 Qui est à la droite de Dieu, après avoir absorbé la mort, pour que nous devinssions héritiers de la vie éternelle; et qui est monté au ciel, les anges, les puissances et les vertus lui étant assujettis.
amene anapita kumwamba ndipo ali kudzanja lamanja la Mulungu komwe angelo ndi maulamuliro ndi amphamvu amamvera Iye.