< 1 Corinthiens 15 >
1 Mais je vous rappelle, mes frères, l’Evangile que je vous ai prêché, que vous avez reçu, dans lequel vous demeurez fermes,
Tsono abale, ndikufuna ndikukumbutseni za Uthenga Wabwino umene ndinakulalikirani. Munawulandira ndipo munawukhulupirira kolimba.
2 Et par lequel vous êtes sauvés, si vous le gardez comme je vous l’ai annoncé; à moins que vous n’ayez cru en vain.
Inu munapulumutsidwa ndi Uthenga Wabwinowu, ngati mwasunga mawu amene ndinakulalikirani. Kupanda kutero, mwangokhulupirira pachabe.
3 Car je vous ai transmis en premier lieu, ce que j’ai reçu moi-même: que le Christ est mort pour nos péchés, selon les Ecritures;
Pakuti chimene ndinalandira ndinapereka kwa inu monga chofunika kuposa zonse, kuti Khristu anafera zoyipa zathu monga mwa Malemba,
4 Qu’il a été enseveli, et qu’il est ressuscité le troisième jour, selon les Ecritures;
kuti anayikidwa mʼmanda, kuti anaukitsidwa tsiku lachitatu monga mwa Malemba;
5 Qu’il a été vu de Céphas, puis des onze;
ndipo kuti anaonekera kwa Petro, ndipo kenaka kwa Atumwi khumi ndi awiriwo.
6 Qu’ensuite il a été vu par plus de cinq cents frères ensemble, dont beaucoup vivent encore aujourd’hui, et quelques-uns se sont endormis;
Pambuyo pake, Iye anaonekera kwa anthu oposa 500 mwa abale pa nthawi imodzi, ndipo ambiri mwa iwo akanali ndi moyo ngakhale kuti ena anagona tulo.
7 Qu’après il a été vu de Jacques, puis de tous les apôtres;
Kenaka anaonekeranso kwa Yakobo, kenaka kwa atumwi onse.
8 Et qu’enfin, après tous les autres, il s’est fait voir aussi à moi, comme à l’avorton.
Potsiriza pa onse anaonekeranso kwa ine, monga mwana wobadwa nthawi isanakwane.
9 Car je suis le moindre des apôtres, et je ne suis pas digne d’être appelé apôtre, parce que j’ai persécuté l’Eglise de Dieu.
Pakuti ine ndine wamngʼono kwa atumwi ndipo sindiyenera nʼkomwe kutchedwa mtumwi chifukwa ndinazunza mpingo wa Mulungu.
10 Mais c’est par la grâce de Dieu que je suis ce que je suis, et sa grâce n’a pas été stérile en moi, mais plus qu’eux tous, j’ai travaillé, non pas moi toutefois, mais la grâce de Dieu avec moi;
Koma mwachisomo cha Mulungu, ndili mmene ndililimu, ndipo chisomo chake kwa ine sichinali chopanda ntchito. Ndinagwira ntchito kuposa ena onse a iwo. Choncho sindine koma chisomo cha Mulungu chimene chinali ndi ine.
11 Ainsi, soit moi, soit eux, voilà ce que nous prêchons et voilà ce que vous avez cru.
Tsono kaya ndi ineyo kapena iwowo, izi ndi zomwe timalalikira, ndipo izi ndi zimene munakhulupirira.
12 Mais si on prêche que le Christ est ressuscité d’entre les morts, comment quelques-uns disent-ils parmi vous qu’il n’y a point de résurrection des morts?
Koma ngati timalalikira kuti Khristu anaukitsidwa kwa akufa, zikutheka bwanji kuti ena mwa inu azinena kuti kulibe kuuka kwa akufa?
13 Or s’il n’y a point de résurrection des morts, le Christ n’est point ressuscité.
Ngati kulibe kuuka kwa akufa, ndiye kuti ngakhale Khristu sanaukenso.
14 Et si le Christ n’est point ressuscité, notre prédication est donc vaine, et vaine est aussi votre foi;
Ndipo ngati Khristu sanaukitsidwe, ndiye kuti kulalikira kwathu nʼkopanda ntchito, ndipo chikhulupiriro chanu nʼchopandanso ntchito.
15 Nous nous trouvons même être de faux témoins à l’égard de Dieu, puisque nous rendons ce témoignage contre Dieu, qu’il a ressuscité le Christ, qu’il n’a pourtant pas ressuscité, si les morts ne ressuscitent point.
Kuwonjezera pamenepa, ndiye kuti ndife mboni zabodza pa za Mulungu, pakuti tikuchita umboni kuti Mulungu anaukitsa Khristu kwa akufa. Ngati nʼzoona kuti akufa saukitsidwa, ndiye kuti Mulungu sanaukitsenso Khristu.
16 Car si les morts ne ressuscitent point, le Christ non plus n’est pas ressuscité.
Pakuti ngati akufa saukitsidwa, ndiye kuti nayenso Khristu sanaukitsidwe.
17 Que si le Christ n’est pas ressuscité, votre foi est vaine; vous êtes encore dans vos péchés.
Ndipo ngati Khristu sanaukitsidwe, chikhulupiriro chanu nʼchopanda ntchito; mukanali mu machimo anu.
18 Donc ceux aussi qui se sont endormis dans le Christ ont péri.
Ndiye kuti nawonso amene agona tulo mwa Ambuye ndi otayika.
19 Si c’est pour cette vie seulement que nous espérons dans le Christ, nous sommes les plus malheureux de tous les hommes.
Ngati kukanakhala kuti tili ndi chiyembekezo mwa Khristu mʼmoyo uno wokha, tikanakhala omvetsa chisoni kuposa anthu ena onse.
20 Mais très certainement le Christ est ressuscité d’entre les morts, comme prémices de ceux qui dorment;
Koma nʼzoonadi kuti Khristu anaukitsidwa kwa kufa, chipatso choyamba cha onse ogona tulo.
21 Car par un homme est venue la mort, et par un homme la résurrection des morts.
Pakuti monga imfa inadza kudzera mwa munthu, kuuka kwa akufa kwabweranso kudzera mwa munthu.
22 Et comme tous meurent en Adam, tous revivront aussi dans le Christ;
Pakuti monga mwa Adamu onse amafa, chomwechonso mwa Khristu onse adzakhala ndi amoyo.
23 Mais chacun en son rang; le Christ comme prémices, puis ceux qui sont au Christ, qui ont cru en son avènement.
Koma aliyense adzauka pa nthawi yake. Khristu ndiye woyambirira, pambuyo pake, pamene Khristu adzabwera, iwo amene ali ake adzauka.
24 La fin suivra, lorsqu’il aura remis le royaume à Dieu et au Père; qu’il aura anéanti toute principauté, toute domination et toute puissance.
Pamenepo chimaliziro chidzafika, pamene Iye adzapereka ufumu kwa Mulungu Atate, atathetsa ufumu wonse, ulamuliro wonse ndi mphamvu zonse.
25 Car il faut qu’il règne jusqu’à ce que le Père ait mis tous ses ennemis sous ses pieds.
Pakuti Iye ayenera kulamulira mpaka Mulungu atayika pansi pa mapazi ake adani ake onse.
26 Or le dernier ennemi détruit sera la mort; car il lui a mis tout sous les pieds. Quand donc l’Ecriture dit:
Mdani wotsiriza kuwonongedwa ndi imfa.
27 Tout lui a été soumis, elle excepte, sans doute, celui qui lui a tout soumis.
Pakuti Mulungu “wayika zinthu zonse pansi pa mapazi ake.” Ponena kuti wayika “zinthu zonse pansi pa mapazi ake,” nʼchodziwikiratu kuti sakuphatikizapo ndi Mulungu yemwe, amene anayika zinthu zonse pansi pa Khristu.
28 Et lorsque tout lui aura été soumis, alors le Fils lui-même sera soumis à celui qui lui a soumis toutes choses, afin que Dieu soit tout en tous.
Pamene adzatsiriza kuchita zimenezi, Mwana weniweniyo adzakhala pansi pa ulamuliro wa Iye amene anayika zinthu zonse pansi pake, kuti Mulungu akhale zonse mu zonse.
29 Autrement, que feront ceux qui sont baptisés pour les morts, si réellement les morts ne ressuscitent point? Pourquoi sont-ils baptisés pour les morts?
Tsono ngati kulibe kuuka kwa akufa, kodi iwo amene akubatizidwa chifukwa cha akufa, adzatani? Ngati akufa saukitsidwa nʼkomwe, bwanji nanga anthu akubatizidwa mʼmalo mwawo?
30 Et nous, pourquoi à toute heure, nous exposons-nous au danger?
Ndipo kwa ife, tikuyikiranji moyo wathu pachiswe nthawi ndi nthawi?
31 Chaque jour, mes frères, je meurs, je le jure, par la gloire que je reçois de vous en Jésus-Christ Notre Seigneur.
Abale, ndimafa tsiku ndi tsiku, ndikunenetsa zimenezi, mongotsimikizira monga ndimakunyadirani mwa Khristu Yesu Ambuye athu.
32 Que me sert (humainement parlant) d’avoir combattu contre les bêtes à Ephèse, si les morts ne ressuscitent point? Mangeons et buvons, car nous mourrons demain.
Ngati ndinalimbana ndi zirombo za kuthengo ku Efeso pa zifukwa za umunthu chabe, ndapindulanji? Ngati akufa sadzaukitsidwa, “Tiyeni tidye ndi kumwa, pakuti mawa tifa.”
33 Ne vous laissez point séduire, les mauvais entretiens corrompent les bonnes mœurs.
Musasocheretsedwe, “Kukhala mʼmagulu oyipa kumawononga makhalidwe abwino.”
34 Justes, veillez, et ne péchez point, car quelques-uns sont dans l’ignorance de Dieu; je vous le dis pour votre honte.
Ganizani bwino monga kuyenerera, ndiye lekani kuchimwa; pakuti pali ena amene sadziwa Mulungu. Ndikunena izi kuti muchite manyazi.
35 Mais, dira quelqu’un: Comment les morts ressuscitent-ils? ou avec quel corps reviendront-ils?
Koma wina akhoza kufunsa kuti, “Kodi akufa amaukitsidwa motani? Adzauka ndi thupi la mtundu wanji?”
36 Insensé, ce que tu sèmes n’est point vivifié, si auparavant il ne meurt.
Wopusa iwe! Chimene mudzala sichikhala ndi moyo pokhapokha chitayamba chafa.
37 Et ce que tu sèmes n’est pas le corps même qui doit venir, mais une simple graine, comme de blé, ou de quelque autre chose.
Mukadzala, simudzala thupi limene lidzamere, koma mbewu chabe, mwina ya tirigu kapena ya china chake.
38 Mais Dieu lui donne un corps, comme il veut, de même qu’il donne à chaque semence son corps propre.
Koma Mulungu amayipatsa thupi monga Iye wafunira, ku mbewu ya mtundu uliwonse amapereka thupi lakelake.
39 Toute chair n’est pas la même chair; mais autre est celle des hommes, autre celle des brebis, autre celle des oiseaux, autre celle des poissons.
Mnofu siwofanana. Anthu ali ndi mnofu wa mtundu wina, nyama zili ndi wina, mbalame zili ndi wina, nsomba zili ndi winanso.
40 Il y a aussi des corps célestes et des corps terrestres•• mais autre est la gloire des célestes, autre celle des terrestres.
Palinso matupi akumwamba ndipo palinso matupi a dziko lapansi; koma ulemerero wa matupi akumwamba ndi wina, ndi wa matupi a dziko lapansi ndi winanso.
41 Autre est la clarté du soleil, autre la clarté de la lune, autre la clarté des étoiles. Une étoile même diffère d’une autre étoile en clarté.
Dzuwa lili ndi ulemerero wake, ndipo pali ulemerero wina wa mwezi, palinso ulemerero winanso wa nyenyezi. Ulemerero wa nyenyezi ndi wosiyanasiyana.
42 Ainsi est la résurrection des morts. Le corps est semé dans la corruption, il ressuscitera dans l’incorruptibilité.
Zidzaterenso pamene akufa adzauka. Thupi loyikidwa mʼnthaka ngati mbewu limavunda, koma likadzauka lidzakhala losavunda.
43 Il est semé dans l’abjection, il ressuscitera dans la gloire; il est semé dans la faiblesse, il ressuscitera dans la force.
Limayikidwa mʼmanda mopanda ulemu, koma likadzaukitsidwa lidzakhala ndi ulemerero. Limayikidwa mʼmanda lili lofowoka, koma likadzaukitsidwa lidzakhala ndi mphamvu.
44 Il est semé corps animal, il ressuscitera corps spirituel, comme il est écrit:
Limayikidwa mʼmanda thupi la mnofu chabe, koma likadzaukitsidwa lidzakhala lauzimu. Ngati pali thupi la mnofu, palinso thupi lauzimu.
45 Le premier homme, Adam, a été fait âme vivante; le dernier Adam, esprit vivifiant.
Kwalembedwa kuti, “Munthu woyamba Adamu anakhala wamoyo,” Adamu wotsiriza anakhala wopatsa moyo.
46 Non d’abord ce qui est spirituel, mais ce qui est animal.
Zauzimu sizinabwere koyambirira, koma zachilengedwe, pambuyo pake zauzimu.
47 Le premier homme tiré de la terre est terrestre; le second, venu du ciel, est céleste.
Munthu woyamba anali wa dziko lapansi, wochokera mʼnthaka koma munthu wachiwiri anali wochokera kumwamba.
48 Tel qu’est le terrestre, tels sont les terrestres; tel qu’est le céleste, tels sont les célestes.
Monga analili munthu wa dziko lapansi, momwemonso anthu onse amene ndi a dziko lapansi. Ndipo monga alili munthu wakumwamba, momwemonso anthu onse amene ndi akumwamba.
49 Comme donc, nous avons porté l’image du terrestre, portons aussi l’image du céleste.
Ndipo monga momwe tinabadwa ofanana ndi munthu wa dziko lapansi uja, momwemonso tidzakhala ofanana ndi munthu wakumwamba.
50 Or je dis cela, mes frères, parce que ni la chair ni le sang ne peuvent posséder le royaume de Dieu, et la corruption ne possédera point l’incorruptibilité,
Ndikunenetsa, abale, kuti thupi ndi magazi sizingathe kulowa mu ufumu wa Mulungu, ndipo zimene zimavunda sizingathe kulowa kumene zinthu sizivunda.
51 Voici que je vais vous dire un mystère. Nous ressusciterons bien tous, mais nous ne serons pas tous changés.
Tamverani, ndikuwuzeni chinsinsi. Tonse sitidzagona tulo, koma tonse tidzasandulika.
52 En un moment, en un clin d’oeil, au son de la dernière trompette; car la trompette sonnera, et les morts ressusciteront incorruptibles, et nous, nous serons changés.
Zidzachitika mwadzidzidzi, mʼkamphindi kochepa, monga ngati kuphethira kwa diso, pa lipenga lotsiriza. Pakuti lipenga lidzalira, akufa adzaukitsidwa opanda chovunda, ndipo ife tidzasandulika.
53 Puisqu’il faut que ce corps corruptible revête l’incorruptibilité, et que ce corps mortel revête l’immortalité.
Pakuti chovunda chiyenera kuvala chosavunda, ndi thupi ili lakufa liyenera kuvala losafa.
54 Et quand ce corps mortel aura revêtu l’immortalité, alors sera accomplie cette parole qui est écrite: La mort a été absorbée dans sa victoire.
Pamene thupi lovundali likadzasanduka losavunda, ndipo thupi lotha kufali likadzasanduka losatha kufa, pamenepo zidzakwaniritsidwa zimene zinalembedwa zakuti, “Imfa yogonjetsedwa kwathunthu.”
55 Ô mort, où est ta victoire? où est, ô mort, ton aiguillon? (Hadēs )
“Iwe imfa, kupambana kwako kuli kuti? Iwe imfa, ululu wako uli kuti?” (Hadēs )
56 Or l’aiguillon de la mort, c’est le péché; et la force du péché, la loi.
Ululu wa imfa ndi tchimo, ndipo mphamvu ya tchimo ndi lamulo.
57 Ainsi, grâces à Dieu, qui nous a donné la victoire par Notre Seigneur Jésus-Christ!
Koma tiyamike Mulungu amene amatipambanitsa mwa Ambuye athu Yesu Khristu.
58 C’est pourquoi, mes frères bien-aimés, soyez fermes et inébranlables, vous appliquant toujours de plus en plus à l’œuvre du Seigneur, sachant que votre travail n’est pas vain dans le
Choncho, abale anga okondedwa imani njii. Musasunthike ndi chilichonse. Nthawi zonse mudzipereke kwathunthu ku ntchito ya Ambuye, chifukwa mukudziwa kuti ntchito zanu mwa Ambuye sizili zopanda phindu.