< Luc 18 >
1 Or, pour leur montrer qu'il fallait toujours prier et ne pas perdre courage, il leur adressait une parabole
Kenaka Yesu anawuza ophunzira ake fanizo kuwaonetsa kuti iwo ayenera kumapemphera nthawi zonse ndikuti asafowoke.
2 en ces termes: « Il y avait dans une ville un certain juge qui ne craignait point Dieu et n'avait d'égards pour personne;
Iye anati, “Mʼmudzi wina munali woweruza wosaopa Mulungu ngakhalenso kulabadira za anthu.
3 or dans cette ville-là était une veuve, et elle venait lui dire: « Fais-moi justice de mon adversaire. »
Ndipo panali mkazi wamasiye mʼmudzimo amene ankabwerabwera kwa iye ndi dandawulo lake kuti, ‘Mundiweruze mlandu mwachilungamo pakati pa ine ndi otsutsana nane.’
4 Et pendant longtemps il ne le voulait pas; mais ensuite il se dit en lui-même: Quoique je ne craigne point Dieu et que je n'aie non plus d'égards pour personne,
“Kwa nthawi yayitali woweruzayo ankakana. Koma pa mapeto analingalira nati, ‘Ngakhale kuti sindiopa Mulungu kapena kulabadira za anthu,
5 cependant comme cette veuve me cause du tracas, je lui ferai justice, de peur qu'elle ne finisse par venir me donner des coups. »
koma chifukwa chakuti mkazi wamasiyeyu akundivutitsa, ine ndimuweruzira mlandu wake mwachilungamo kuti asanditopetse ndi kubwerabwera kwakeko!’”
6 Or le seigneur dit: « Écoutez ce que dit le juge inique;
Ndipo Ambuye anati, “Tamvani zimene woweruza wopanda chilungamoyu wanena.
7 mais Dieu ne fera-t-Il pas justice à Ses élus qui crient à Lui jour et nuit, et tarde-t-Il à leur égard?
Tsono chingamuletse nʼchiyani Mulungu kubweretsa chilungamo kwa osankhika ake, amene amalira kwa Iye usana ndi usiku? Kodi adzapitirirabe osawalabadira?
8 Je vous déclare qu'il leur fera justice au plus tôt. Toutefois le fils de l'homme, quand il viendra, trouvera-t-il la foi sur la terre? »
Ine ndikukuwuzani inu, adzaonetsetsa kuti alandire chilungamo, ndiponso mofulumira. Komabe, pamene Mwana wa Munthu akubwera, kodi adzapeza chikhulupiriro pa dziko lapansi?”
9 Or il dit aussi à quelques personnes qui possédaient pour elles-mêmes l'assurance d'être justes et qui méprisaient les autres, la parabole suivante:
Yesu ananena fanizoli kwa amene amadzikhulupirira mwa iwo okha kuti anali wolungama nanyoza ena onse.
10 « Deux hommes montèrent au temple pour prier, l'un était pharisien, et l'autre publicain.
“Anthu awiri anapita ku Nyumba ya Mulungu kukapemphera, wina Mfarisi ndi winayo wolandira msonkho.
11 Le pharisien, se tenant debout, faisait en lui-même cette prière: « O Dieu! Je Te rends grâce de ce que je ne suis pas comme les autres hommes qui sont spoliateurs, injustes, adultères, ou même comme ce publicain:
Mfarisiyo anayimirira ndipo anapemphera za iye mwini kuti, ‘Mulungu, ine ndikuyamika kuti sindili ngati anthu ena onse, achifwamba, ochita zoyipa, achigololo, sindilinso ngati wolandira msonkhoyu.
12 je jeûne deux fois la semaine, je donne la dîme de tout ce que j'acquiers. »
Ine ndimasala kudya kawiri pa Sabata ndipo ndimapereka chakhumi pa zonse ndimapeza.’
13 Mais le publicain se tenant à distance ne se permettait pas même de lever les yeux vers le ciel, mais il se frappait la poitrine en disant: « O Dieu, aie compassion de moi qui suis pécheur! »
“Koma wolandira msonkhoyo ali chiyimire potero, sanathe nʼkomwe kuyangʼana kumwamba; koma anadziguguda pachifuwa ndipo anati, ‘Mulungu, chitireni chifundo, ine wochimwa.’
14 Je vous le déclare, celui-ci redescendit justifié dans sa maison à l'inverse de l'autre, car quiconque s'élève lui-même sera abaissé, tandis que celui qui s'abaisse lui-même sera élevé. »
“Ine ndikukuwuzani kuti munthu wolandira msonkhoyu, osati Mfarisiyu, anapita kwawo atalungamitsidwa pamaso pa Mulungu. Chifukwa chake, aliyense wodzikweza adzachepetsedwa, ndipo wodzichepetsa adzakwezedwa.”
15 Or on lui apportait aussi les petits enfants, afin qu'il les touchât; ce que les disciples ayant vu ils les réprimandaient.
Anthu amabweretsanso ana aangʼono kwa Yesu kuti awadalitse. Ophunzira ataona izi, anawadzudzula.
16 Mais Jésus les appela à lui, en disant: « Laissez les petits enfants venir à moi, et ne les en empêchez pas, car c'est à ceux qui leur ressemblent qu'appartient le royaume de Dieu.
Koma Yesu anayitana anawo kuti abwere kwa Iye nati, “Lolani ana abwere kwa Ine ndipo musawatsekereze, pakuti ufumu wa Mulungu uli wa anthu otere.
17 En vérité je vous le déclare, celui qui n'aura pas reçu le royaume de Dieu comme un petit enfant n'y entrera certainement point. »
Zoonadi, Ine ndikukuwuzani kuti aliyense amene salandira ufumu wa Mulungu ngati mwana wamngʼono, sadzalowamo.”
18 Et un chef l'interrogea en disant: « Bon Maître, par quelle conduite hériterai-je la vie éternelle? » (aiōnios )
Oweruza wina wake anamufunsa Iye kuti, “Aphunzitsi abwino, ndichite chiyani kuti ndilandire moyo wosatha?” (aiōnios )
19 Mais Jésus lui dit: « Pourquoi m'appelles-tu bon? Nul n'est bon, si ce n'est un seul, Dieu.
Yesu anamuyankha kuti, “Chifukwa chiyani ukunditcha wabwino, palibe wabwino kupatula Mulungu yekha.
20 Tu connais les commandements: « Ne commets point d'adultère; ne tue point; ne dérobe point; ne fais point de faux témoignage; honore ton père et ta mère. »
Iwe umadziwa malamulo: ‘Usachite chigololo, usaphe, usabe, usapereke umboni wonama, lemekeza abambo ndi amayi ako.’”
21 L'autre dit: « J'ai observé toutes ces choses dès ma jeunesse. »
Iye anati, “Zonsezi ndinasunga kuyambira ndili mnyamata.”
22 Ce que Jésus ayant ouï, il lui dit: « Il te manque encore une chose: vends tout ce que tu possèdes, et distribue-le aux pauvres, et tu auras un trésor dans les cieux; puis viens, suis-moi. »
Yesu atamva izi, anati kwa iye, “Ukusowabe chinthu chimodzi: Gulitsa zonse zimene uli nazo ndipo uzipereke kwa osauka, ndipo udzakhala ndi chuma kumwamba. Kenaka ubwere, nunditsate ine.”
23 Mais l'autre en entendant cela devint tout triste, car il était très riche.
Atamva zimenezi, anakhumudwa kwambiri chifukwa anali munthu wachuma chambiri.
24 Or Jésus l'ayant regardé dit: « Avec quelle difficulté ceux qui possèdent les richesses entrent-ils dans le royaume de Dieu!
Yesu anamuyangʼana nati, “Nʼkwapatali kwambiri kuti anthu achuma akalowe mu ufumu wa Mulungu!
25 Il est en effet plus facile qu'un chameau entre par un trou d'aiguille, qu'un riche n'entre dans le royaume de Dieu. »
Ndithudi, nʼkwapafupi kuti ngamira idutse pa kabowo ka zingano kusiyana ndi munthu wachuma kulowa mu ufumu wa Mulungu.”
26 Mais les auditeurs dirent: « Et qui peut être sauvé? »
Amene anamva izi anafunsa kuti, “Nanga ndani amene angapulumuke?”
27 Or il dit: « Ce qui est impossible quant aux hommes est possible quant à Dieu. »
Yesu anayankha kuti, “Zinthu zosatheka ndi anthu zimatheka ndi Mulungu.”
28 Or Pierre lui dit: « Voici, pour nous, après avoir abandonné nos propres biens, nous t'avons suivi. »
Petro anati kwa Iye, “Ife tinasiya zonse tinali nazo kutsatira Inu!”
29 Et il leur dit: « En vérité je vous déclare qu'il n'est personne qui, ayant abandonné maison, ou femme, ou frères, ou parents, ou enfants, à cause du royaume de Dieu,
Yesu anawawuza kuti, “Zoonadi, Ine ndikukuwuzani kuti palibe amene anasiya nyumba kapena mkazi kapena abale kapena makolo kapena ana chifukwa cha ufumu wa Mulungu
30 ne reçoive infiniment davantage dans ce temps-ci, et dans le siècle à venir la vie éternelle. » (aiōn , aiōnios )
adzalephera kulandira mowirikiza mʼmoyo uno, ndi mʼmoyo ukubwerawo, moyo wosatha.” (aiōn , aiōnios )
31 Et ayant pris les douze à part, il leur dit: « Voici, nous montons à Jérusalem, et tout ce qui a été écrit par les prophètes relativement au fils de l'homme s'accomplira;
Yesu anatengera khumi ndi awiriwo pambali ndi kuwawuza kuti, “Taonani ife tikupita ku Yerusalemu, ndipo zonse zimene zalembedwa ndi Aneneri za Mwana wa Munthu zidzakwaniritsidwa.
32 car il sera livré aux Gentils, et il sera bafoué et injurié, et on crachera sur lui,
Iye adzaperekedwa kwa anthu a mitundu ina. Ndipo adzamuchita chipongwe, adzamunyoza, adzamulavulira,
33 et après l'avoir fouetté ils le mettront à mort, et le troisième jour il ressuscitera. »
adzamukwapula ndi kumupha. Tsiku lachitatu Iye adzaukanso.”
34 Et pour eux ils ne comprenaient rien à cela, et cette parole leur était cachée, et ils ne saisissaient pas ce qui avait été dit.
Ophunzira sanazindikire china chilichonse cha izi. Tanthauzo lake linabisika kwa iwo, ndipo sanadziwe chimene Iye amayankhula.
35 Or il advint, au moment où il approchait de Jéricho, qu'un aveugle se trouvait assis près du chemin pour mendier.
Yesu atayandikira ku Yeriko, munthu wina wosaona amene amakhala pambali pa msewu namapempha,
36 Mais ayant entendu la foule qui passait devant lui, il s'informait de ce que c'était.
anamva gulu la anthu likudutsa. Iye anafunsa chomwe chimachitika.
37 On lui dit: « C'est Jésus le Nazaréen qui passe. »
Iwo anamuwuza kuti “Yesu wa ku Nazareti akudutsa.”
38 Et il s'écria: « Jésus, fils de David, aie pitié de moi. »
Iye anayitana mofuwula, “Yesu Mwana wa Davide, mundichitire chifundo!”
39 Et ceux qui marchaient les premiers le réprimandaient pour le faire taire; mais lui criait de plus belle: « Fils de David, aie pitié de moi. »
Iwo amene amamutsogolera njira anamudzudzula ndi kumuwuza kuti akhale chete, koma iye anafuwulabe, “Mwana wa Davide, chitireni chifundo!”
40 Et Jésus s'étant arrêté ordonna qu'on le lui amenât; et quand il se fut approché, il lui demanda: « Que veux-tu que je fasse pour toi? »
Yesu anayima nalamula kuti abwere naye kwa Iye. Atabwera pafupi, Yesu anamufunsa kuti,
41 Et l'autre dit: « Seigneur, que je recouvre la vue.
“Kodi ukufuna kuti ndikuchitire chiyani?” Iye anayankha kuti, “Ambuye, ine ndifuna ndionenso.”
42 Et Jésus lui dit: « Recouvre la vue; ta foi t'a guéri. »
Yesu anati kwa iye, “Onanso; chikhulupiriro chako chakupulumutsa.”
43 Et immédiatement il recouvra la vue, et il le suivait en glorifiant Dieu. Et tout le peuple voyant cela rendit louange à Dieu.
Nthawi yomweyo anaonanso ndipo anayamba kumutsatira Yesu, akulemekeza Mulungu. Anthu onse ataona izi, iwonso analemekeza Mulungu.