< Jérémie 37 >

1 Et Sédécias, fils de Josias, succéda comme roi à Chonia, fils de Jéhojakim: Nébucadnézar, roi de Babel, l'avait fait roi du pays de Juda.
Nebukadinezara mfumu ya Babuloni, inakhazika pa mpando waufumu Zedekiya mwana wa Yosiya kukhala mfumu ya Yuda. Iye analowa mʼmalo mwa Yehoyakini mwana wa Yehoyakimu.
2 Et il n'obéit, non plus que ses serviteurs, ni le peuple du pays, aux paroles que l'Éternel prononça par l'entremise de Jérémie, le prophète.
Koma Zedekiya kapena atumiki ake ngakhalenso anthu a mʼdzikomo sanasamalire mawu a Yehova amene anayankhula kudzera mwa mneneri Yeremiya.
3 Et le roi Sédécias envoya Jouchal, fils de Sélémia, et Sophonie, fils de Mahaséïa, le sacrificateur, à Jérémie, le prophète, pour lui dire: Prie pour nous l'Éternel, notre Dieu!
Tsono Zedekiya anatuma Yehukali mwana wa Selemiya ndi wansembe Zefaniya mwana wa Maseya kwa mneneri Yeremiya ndi uthenga uwu: “Chonde tipempherereni kwa Yehova Mulungu wathu.”
4 Or Jérémie entrait et sortait encore librement parmi le peuple, et on ne l'avait pas encore incarcéré.
Nthawi imeneyinso nʼkuti Yeremiya ali ndi ufulu woyenda pakati pa anthu chifukwa anali asanaponyedwe mʼndende.
5 Et l'armée de Pharaon était sortie de l'Egypte, et les Chaldéens qui assiégeaient Jérusalem, en ayant appris la nouvelle, s'étaient retirés de Jérusalem.
Nthawi imeneyinso nʼkuti gulu lankhondo la Farao litatuluka mʼdziko la Igupto. Ndipo Ababuloni amene anali atazinga Yerusalemu atamva zimenezi, anachoka ku Yerusalemuko.
6 Alors la parole de l'Éternel fut adressée à Jérémie, le prophète, en ces mots:
Tsono Yehova anawuza mneneri Yeremiya kuti,
7 Ainsi parle l'Éternel, Dieu d'Israël: Ainsi parlez au roi de Juda qui vous envoie vers moi pour me consulter: Voici, l'armée de Pharaon qui s'avance à votre secours, retournera dans son pays, en Egypte;
“Uyiwuze mfumu ya Yuda imene inakutuma kuti udzapemphe nzeru kwa ine kuti Ine Yehova, Mulungu wa Israeli ndikuti, gulu lankhondo la Farao limene linatuluka kuti lidzakuthandize lidzabwerera kwawo ku Igupto.
8 et les Chaldéens reviendront assiéger cette ville, et ils la prendront, et la brûleront par le feu.
Ndipo Ababuloni adzabwerera kudzathira nkhondo mzinda uno. Iwo adzawugonjetsa ndi kuwutentha.
9 Ainsi parle l'Éternel: Ne vous abusez pas vous-mêmes en disant: Les Chaldéens vont s'éloigner de nous! car ils ne s'en iront point.
“Yehova akuti: Musadzinyenge, nʼkumaganiza kuti, ‘Ndithu Ababuloni adzatisiya.’ Ndithudi sadzakusiyani!
10 Car eussiez-vous défait toute l'armée des Chaldéens qui vous assiègent, et ne restât-il d'eux que des hommes percés, ils se lèveront chacun de leur tente, et brûleront cette ville par le feu.
Ngakhale mutagonjetsa gulu lonse lankhondo la Ababuloni limene likukuthirani nkhondo ndipo mʼmatenti mwawo ndikutsala anthu ovulala okhaokha, amenewo adzabwera ndi kudzatentha mzinda uno.”
11 Et lorsque l'armée des Chaldéens se retirait de Jérusalem devant l'armée de Pharaon,
Gulu lankhondo la Ababuloni litaleka kuthira nkhondo mzinda wa Yerusalemu chifukwa choopa gulu lankhondo la Farao,
12 Jérémie sortit de Jérusalem, pour se rendre dans le pays de Benjamin, afin d'y recueillir un héritage, au milieu du peuple.
Yeremiya ananyamuka kuchoka ku Yerusalemu ndi kumapita ku dziko la Benjamini kuti akalandire gawo lake la minda ya makolo ake.
13 Et il se trouvait dans la porte de Benjamin, et là celui qui en avait l'inspection et dont le nom était Jérija, fils de Sélémia, fils d'Ananias, arrêta Jérémie, le prophète, en disant: Tu passes aux Chaldéens.
Koma atafika pa Chipata cha Benjamini, mkulu wa alonda amene dzina lake linali Iriya mwana wa Selemiya, mwana wa Hananiya, anagwira mneneri Yeremiyayo ndipo anati, “Iwe ukuthawira kwa Ababuloni!”
14 Et Jérémie dit: C'est une fausseté! je ne passe point aux Chaldéens. Mais Jérija, sans l'écouter, arrêta Jérémie et le conduisit aux princes.
Yeremiya anati, “Zimenezo si zoona! Ine sindikuthawira kwa Ababuloni.” Koma Iriya sanamumvere. Mʼmalo mwake anagwira Yeremiya nʼkupita naye kwa akuluakulu.
15 Et les princes s'irritèrent contre Jérémie, et le frappèrent, et le mirent en prison dans la maison de Jonathan, le scribe; car ils en avaient fait une prison.
Akuluakuluwo anamupsera mtima Yeremiya ndipo anamukwapula ndi kumuyika mʼnyumba ya mlembi Yonatani, imene anayisandutsa ndende.
16 Et lorsque Jérémie fut venu dans le cachot, et dans les cellules, et qu'il y fut resté longtemps,
Yeremiya anayikidwa mʼndende ya pansi pa nthaka, kumene anakhalako nthawi yayitali.
17 le roi Sédécias envoya et le fit chercher. Et le roi l'interrogea dans sa maison en secret et lui dit: Y a-t-il une parole de par l'Éternel? Et Jérémie dit: Il y en a une. Et il dit: Tu seras livré entre les mains du roi de Babel.
Kenaka Mfumu Zedekiya inatuma anthu kuti akayitane Yeremiya ndipo anabwera naye ku nyumba ya mfumu. Atafika mfumu inamufunsa mwamseri kuti, “Kodi pali mawu ena amene Yehova wakuwuza?” Yeremiya anayankha kuti, “Inde. Inu mfumu mudzaperekedwa kwa mfumu ya ku Babuloni.”
18 Et Jérémie dit au roi Sédécias: En quoi ai-je péché contre toi ou tes serviteurs ou ce peuple, que vous m'avez mis en prison?
Pamenepo Yeremiya anafunsa Mfumu Zedekiya kuti, “Kodi ndakulakwirani chiyani inuyo kapena akuluakulu anu kapenanso anthu awa, kuti mundiyike mʼndende?
19 Et où sont vos prophètes qui vous prophétisaient disant: Le roi de Babel ne marchera pas contre vous, ni contre ce pays?
Kodi ali kuti aneneri anu amene anakuloserani kuti, ‘Mfumu ya ku Babuloni sidzakuthirani nkhondo pamodzi ndi dziko lino’?
20 Et maintenant, écoute, ô roi, mon Seigneur, je t'en prie, reçois mon humble prière, et ne me fais pas rentrer dans la maison de Jonathan, le scribe, pour que je n'y meure pas!
Koma tsopano, mbuye wanga mfumu, chonde tamverani. Loleni ndinene pempho langa pamaso panu: Musandibwezere ku nyumba ya mlembi Yonatani, kuopa kuti ndingakafere kumeneko.”
21 Alors le roi Sédécias ordonna qu'on déposât Jérémie dans le vestibule de la prison, et qu'on lui donnât chaque jour un pain de la rue des boulangers, jusqu'à ce que tout le pain fût consommé dans la ville. Ainsi Jérémie demeura dans le vestibule de la prison.
Tsono Mfumu Zedekiya analamula kuti Yeremiya asungidwe mʼbwalo la alonda. Ankamupatsa buledi tsiku ndi tsiku amene ankamugula kwa ophika buledi. Anapitiriza kutero mpaka buledi yense anatha mu mzindamo. Choncho Yeremiya anapitirira kukhala mʼbwalo la alonda.

< Jérémie 37 >