< Isaïe 46 >

1 Bel est culbuté, Nebo précipité; on met leurs images sur des animaux et des bêtes; ceux que vous portiez chargent de leur poids des bestiaux fatigués!
Beli wagwada pansi, Nebo wawerama; nyama zonyamula katundu za nyamula milungu yawo. Mafano awo asanduka katundu wolemera pa msana pa ngʼombe. Asandukadi ngati katundu pa msana pa nyama zotopa.
2 Ils sont culbutés, précipités ensemble, et ne peuvent sauver le fardeau, et eux-mêmes ils s'en vont captifs. –
Nyamazo zikuwerama ndi kufuna kugwa ndi milunguyo; sizikutha kupulumutsa katunduyo, izo zomwe zikupita ku ukapolo.
3 Écoutez-moi, maison de Jacob, et vous, tous les restes de la maison d'Israël! je me suis chargé de vous dès votre origine, je vous ai portés dès votre naissance, et jusqu'à vos vieux jours je serai le même,
Mverani Ine, Inu nyumba ya Yakobo, inu nonse otsala a mʼnyumba ya Israeli, Ine ndakhala ndi kukusamalirani kuyambira mʼmimba ya amayi anu, ndakhala ndikukunyamulani chibadwire chanu.
4 et jusqu'à la blanche vieillesse je vous soutiendrai; je l'ai fait et je vous porterai encore, je veux soutenir et sauver.
Mpaka pamene mudzakalambe ndi kumera imvi ndidzakusamalirani ndithu. Ndinakulengani ndipo ndidzakunyamulani, ndidzakusamalirani ndi kukulanditsani.
5 A qui pourriez-vous m'assimiler? de qui me faire l'égal? à qui me comparer, pour que nous nous ressemblions?
“Kodi inu mudzandifanizira ndi yani, kapena mufananitsa ndi yani? Kodi mudzandiyerekeza kapena kundifanizitsa ndi yani?
6 Ceux qui laissent couler l'or de leur bourse et pèsent l'argent à la balance, prennent à gages un orfèvre pour qu'il leur fasse un Dieu: ils se prosternent et l'adorent.
Anthu ena amakhuthula golide mʼzikwama zawo ndipo amayeza siliva pa masikelo; amalemba ntchito mʼmisiri wosula kuti awapangire mulungu, kenaka iwo amagwada pansi ndikupembedza kamulunguko.
7 Ils le lèvent, en chargent leur épaule, et le mettent sur pied pour qu'il se tienne; et de sa place il ne bouge; on a beau lui crier, il ne répond pas; de leur détresse il ne les sauve pas.
Amanyamula nʼkumayenda nayo milunguyo pa mapewa awo; amayikhazika pa malo pake ndipo imakhala pomwepo. Singathe kusuntha pamalo pakepo. Ngakhale wina apemphere kwa milunguyo singathe kuyankha; kapena kumupulumutsa ku mavuto ake.
8 Souvenez-vous-en et pensez en hommes! rebelles, réfléchissez-y!
“Kumbukirani zimenezi ndipo muchite manyazi, Muzilingalire mu mtima, inu anthu owukira.
9 Rappelez-vous les premiers événements de jadis; car je suis Dieu, et il n'en est point d'autre; je suis Seigneur, et n'ai pas mon pareil;
Kumbukirani zinthu zakale zinthu zamakedzana; chifukwa Ine ndine Mulungu ndipo palibe wina ofanana nane.
10 c'est moi qui dès l'origine annonce l'avenir, et dans le passé ce qui n'était pas encore; qui dis: « Ce que j'arrête, se fera, et j'accomplirai toute ma volonté! »
Ndinaneneratu zakumathero kuchokera pachiyambi pomwe. Kuyambira nthawi yamakedzana ndinaloseratu zoti zidzachitike. Ndikanena zimene ndifuna kuchita ndipo zimachitikadi. Chilichonse chimene ndafuna ndimachichita.
11 qui du Levant ai appelé un aigle, et d'une terre lointaine l'exécuteur de mon décret. Je l'ai dit, et je le réalise; je l'ai projeté, et je l'exécuterai.
Ndikuyitana chiwombankhanga kuchokera kummawa. Ndikuyitana kuchokera ku dziko lakutali munthu amene adzakwaniritsa cholinga changa. Zimene ndanena ndidzazikwaniritsadi; zimene ndafuna ndidzazichitadi.
12 Écoutez-moi, vous qui êtes endurcis de cœur et loin de la justice!
Ndimvereni, inu anthu owuma mtima, inu amene muli kutali ndi chipulumutso.
13 Je fais approcher ma justice; elle n'est pas loin, et mon salut ne tardera pas. Je mettrai mon salut en Sion, et sur Israël ma gloire.
Ndikubweretsa pafupi tsiku la chipulumutso changa; sichili kutali. Tsikulo layandikira ndipo sindidzachedwa kukupulumutsani ndi kupereka ulemerero wanga kwa Israeli.

< Isaïe 46 >