< 1 Pierre 5 >
1 Je m'adresse maintenant aux anciens qui sont parmi vous, moi qui suis ancien avec eux et témoin des souffrances de Christ, et qui ai part aussi à la gloire qui doit apparaître.
Ine ndikupempha akulu a mpingo amene ali pakati panu, monga inenso mkulu mnzawo, mboni ya zowawa za Khristu ndiponso amene ndidzalandira nawo ulemerero umene uti udzaonetsedwe.
2 Paissez le troupeau de Dieu, qui vous est confié, veillant sur lui, non par contrainte, mais de bon gré; non en vue d'un gain sordide, mais par dévouement;
Wetani gulu la Mulungu limene lili mʼmanja mwanu, muziliyangʼanira. Muzichita osati mowumirizidwa, koma mwakufuna kwanu, monga momwe Mulungu akufunira kuti mutero. Musachite chifukwa chadyera la ndalama, koma ndi mtima ofuna kutumikira.
3 non en maîtrisant ceux qui vous sont échus en partage, mais en vous rendant les modèles du troupeau;
Musakhale ngati mafumu pa amene mukuwayangʼanira, koma mukhale chitsanzo kwa gululo.
4 et, lorsque le souverain Pasteur paraîtra, vous remporterez la couronne immortelle de gloire.
Ndipo Mʼbusa wamkulu akadzaonekera, mudzalandira chipewa cha ulemerero chosafota.
5 De même, vous qui êtes jeunes, soyez soumis aux anciens, et tous revêtez les uns à l'égard des autres la livrée de l'humilité, car «Dieu résiste aux orgueilleux, mais il fait grâce aux humbles.»
Momwemonso, inu anyamata gonjerani amene ndi akulu. Inu nonse mukhale odzichepetsa kuti mutumikirane, chifukwa, “Mulungu amatsutsana nawo odzikuza, koma amapereka chisomo kwa odzichepetsa.”
6 Humiliez-vous sous la puissante main de Dieu, afin qu'il vous élève quand il en sera temps,
Choncho, mudzichepetse pamaso pa Mulungu wamphamvu, kuti pa nthawi yake adzakukwezeni.
7 vous déchargeant sur lui de tout ce qui vous inquiète, car lui-même prend soin de vous.
Tayani pa Iye nkhawa zanu zonse chifukwa ndiye amakusamalani.
8 Soyez sobres; veillez. Le diable, votre adversaire, rôde autour de vous, comme un lion rugissant, cherchant qui il pourra dévorer:
Khalani odziretsa ndi atcheru. Mdani wanu mdierekezi amayendayenda monga mkango wobangula kufunafuna wina kuti amumeze.
9 résistez-lui par votre fermeté dans la foi, sachant que vos frères dispersés dans le monde subissent les mêmes épreuves que nous; et, après quelque temps de souffrance,
Mukaneni iye, ndipo mukhazikike mʼchikhulupiriro, chifukwa mukudziwa kuti abale anzanu pa dziko lonse lapansi nawonso akumva zowawa zomwezi.
10 le Dieu de toute grâce, qui vous a appelés en Jésus-Christ à son éternelle gloire, vous rétablira, vous soutiendra, vous fortifiera et vous rendra inébranlables. (aiōnios )
Ndipo Mulungu wachisomo chonse, amene anakuyitanani ku ulemerero wake wamuyaya mwa Khristu, mutamva zowawa pa kanthawi, adzakukonzaninso ndi kukulimbitsani pa maziko olimba. (aiōnios )
11 A lui soient la gloire et la puissance aux siècles des siècles. Amen! (aiōn )
Kwa Iye kukhale mphamvu mpaka muyaya, Ameni. (aiōn )
12 Je vous écris ces quelques mots par Silvain, que j'estime être un fidèle frère, pour vous exhorter et pour vous assurer que c'est bien à la vraie grâce de Dieu que vous êtes attachés.
Mothandizidwa ndi Sila, amene ndi mʼbale wokhulupirika, ndakulemberani mwachidule kukulimbikitsani ndi kuchita umboni kuti ichi ndi chisomo choona cha Mulungu.
13 L’église élue qui est à Babylone, vous salue, ainsi que Marc mon fils.
Imani mwamphamvu mʼchisomochi. Mlongo wanu amene ali ku Babuloni, wosankhidwa pamodzi nanu akupereka moni, nayenso Marko, mwana wanga, akupereka moni.
14 Saluez-vous les uns les autres par un baiser affectueux. Que la paix soit avec vous tous qui êtes en Jésus-Christ!
Mupatsane moni ndi mpsopsono wachikondi. Mtendere ukhale ndi inu nonse amene muli mwa Khristu.