< Galates 5 >
1 Tenez-vous donc fermes dans la liberté à l'égard de laquelle Christ nous a affranchis, et ne vous soumettez plus au joug de la servitude.
Khristu anatimasula kuti tikhale mfulu. Tsono chirimikani, ndipo musakodwenso mʼgoli la ukapolo.
2 Voici, je vous dis moi Paul, que si vous êtes circoncis, Christ ne vous profitera de rien.
Chonde mvetsetsani! Ine Paulo, ndikukuwuzani kuti mukalola kuchita mdulidwe, Khristu simupindula nayenso konse.
3 Et de plus je proteste à tout homme qui se circoncit, qu'il est obligé d'accomplir toute la Loi.
Ndikubwerezanso kuwuza munthu aliyense wovomereza kuchita mdulidwe kuti ayeneranso kutsata Malamulo onse.
4 Christ devient inutile à l'égard de vous tous qui [voulez] être justifiés par la Loi; et vous êtes déchus de la grâce.
Inu amene mukufuna kulungamitsidwa ndi lamulo mwachotsedwa mwa Khristu; munagwa kusiyana nacho chisomo.
5 Mais pour nous, nous espérons par l'esprit d'être justifiés par la foi.
Koma mwachikhulupiriro, ife tikudikira mwachidwi kudzera mwa Mzimu, chilungamo chimene tikuyembekeza.
6 Car en Jésus-Christ ni la Circoncision ni le prépuce n'ont aucune efficace, mais la foi opérante par la charité.
Pakuti mwa Khristu Yesu mdulidwe kapena kusachita mdulidwe zilibe phindu. Chinthu chokhacho chimene chimafunika ndi chikhulupiriro chogwira ntchito mwachikondi.
7 Vous couriez bien: qui est-ce [donc] qui vous a empêchés d'obéir à la vérité?
Inu munkathamanga mpikisano wanu wabwino. Anakuletsani ndani kuti musamverenso choonadi?
8 Cette persuasion ne vient pas de celui qui vous appelle.
Kukopeka kwanu kumeneku sikuchokera kwa Iye amene anakuyitanani.
9 Un peu de levain fait lever toute la pâte.
“Yisiti wapangʼono amagwira ntchito mu buledi yense.”
10 Je m'assure de vous en [notre] Seigneur, que vous n'aurez point d'autre sentiment; mais celui qui vous trouble en portera la condamnation, quel qu'il soit.
Ine ndikutsimikiza mwa Ambuye kuti inu simudzasiyana nane maganizo. Iye amene akukusokonezani adzalangidwa, kaya iyeyo ndiye ndani.
11 Et pour moi, mes frères, si je prêche encore la Circoncision, pourquoi est-ce que je souffre encore la persécution? le scandale de la croix est donc aboli.
Abale, ngati ine ndikulalikirabe za mdulidwe, nʼchifukwa chiyani ndikusautsidwabe? Ngati ndikanakhala kuti sindikulalikira chipulumutso cha mtanda, palibe amene akanakhumudwa.
12 Plût à Dieu que ceux qui vous troublent fussent retranchés!
Kunena za amene akukuvutani, ndikanakonda akanangodzithena okha!
13 Car, mes frères, vous avez été appelés à la liberté; seulement ne [prenez] pas une telle liberté pour une occasion de vivre selon la chair; mais servez-vous l'un l'autre avec charité.
Inu abale, Mulungu anakuyitanani kuti mukhale mfulu. Koma musagwiritse ntchito ufulu wanuwo kuchita zoyipa zachikhalidwe cha uchimo cha thupi lanu, koma mutumikirane wina ndi mnzake mwachikondi.
14 Car toute la Loi est accomplie dans cette seule parole: tu aimeras ton Prochain comme toi-même.
Pakuti malamulo onse akuphatikizidwa mu lamulo ili, “Konda mnansi wako monga iwe mwini.”
15 Mais si vous vous mordez et vous dévorez les uns les autres, prenez garde que vous ne soyez consumés l'un par l'autre.
Ngati mupitiriza kulumana ndi kukhadzulana, samalani kuti mungawonongane.
16 Je [vous] dis donc: marchez selon l'Esprit; et vous n'accomplirez point les convoitises de la chair.
Choncho ine ndikuti, mulole kuti Mzimu akutsogolereni ndipo simudzachita zofuna za thupi lanu la uchimo.
17 Car la chair convoite contre l'esprit, et l'esprit contre la chair; et ces choses sont opposées l'une à l'autre; tellement que vous ne faites point les choses que vous voudriez.
Pakuti thupi lanu la uchimo limalakalaka zimene ndi zotsutsana ndi Mzimu, ndi Mzimu zimene ndi zotsutsana ndi thupi lanu la uchimo. Ziwirizi zimadana, kotero kuti simungachite zimene mukufuna.
18 Or si vous êtes conduits par l'Esprit, vous n'êtes point sous la Loi.
Koma ngati Mzimu akutsogolerani, ndiye kuti simuli pansi pa lamulo.
19 Car les œuvres de la chair sont évidentes, lesquelles sont l'adultère, la fornication, la souillure, l'impudicité,
Ntchito za thupi lanu la uchimo zimaonekera poyera ndi izi: dama, zodetsa ndi kuchita zonyansa;
20 L'idolâtrie, l'empoisonnement, les inimitiés, les querelles, les jalousies, les colères, les disputes, les divisions, les sectes,
kupembedza mafano ndi ufiti; kudana, kukangana, kupsa mtima, kudzikonda, kugawikana, mipatuko
21 Les envies, les meurtres, les ivrogneries, les gourmandises, et les choses semblables à celles-là; au sujet desquelles je vous prédis, comme je vous l'ai déjà dit, que ceux qui commettent de telles choses n'hériteront point le Royaume de Dieu.
ndi nsanje, kuledzera, mchezo ndi zina zotere. Ine ndikukuchenjezani monga ndinachita poyamba paja kuti amene amachita zimenezi sadzalandira ufumu wa Mulungu.
22 Mais le fruit de l'Esprit est la charité, la joie, la paix, un esprit patient, la bonté, la bénéficence, la fidélité, la douceur, la tempérance.
Koma chipatso cha Mzimu Woyera ndi chikondi, chimwemwe, mtendere, kuleza mtima, chifundo, kukoma mtima, kukhulupirika,
23 Or la Loi ne condamne point de telles choses.
kufatsa ndi kudziretsa. Palibe lamulo loletsa zimenezi.
24 Or ceux qui sont de Christ, ont crucifié la chair avec ses affections et ses convoitises.
Amene ali ake a Khristu Yesu anapachika pa mtanda thupi lawo la uchimo pamodzi ndi zokhumba zawo ndi zolakalaka zawo.
25 Si nous vivons par l'Esprit, conduisons-nous aussi par l'Esprit.
Popeza timakhala ndi moyo mwa Mzimu Woyera, tiyeni tiyende pamodzi ndi Mzimu Woyera.
26 Ne désirons point la vaine gloire, en nous provoquant l'un l'autre, et en nous portant envie l'un à l'autre.
Tisakhale odzitukumula, oputana ndi ochitirana nsanje.