< Job 42 >
1 Job répondit à l’Éternel et dit:
Pamenepo Yobu anayankha Yehova kuti,
2 Je reconnais que tu peux tout, Et que rien ne s’oppose à tes pensées.
“Ndikudziwa kuti Inu mungathe kuchita zinthu zonse; chimene mufuna kuchita wina sangaletse konse.
3 Quel est celui qui a la folie d’obscurcir mes desseins? Oui, j’ai parlé, sans les comprendre, De merveilles qui me dépassent et que je ne conçois pas.
Munandifunsa kuti, ‘Kodi ndiwe yani amene ukufuna kusokoneza uphungu wanga ndi mawu opanda nzeru? Zoonadi ndinayankhula zimene sindinazimvetse, zinthu zodabwitsa kwambiri kwa ine zimene sindinazidziwe.
4 Écoute-moi, et je parlerai; Je t’interrogerai, et tu m’instruiras.
“Inu munandiwuza kuti, ‘Mvetsetsa tsopano ndipo ndidzayankhula; ndidzakufunsa ndipo iwe udzandiyankhe.’
5 Mon oreille avait entendu parler de toi; Mais maintenant mon œil t’a vu.
Ndinkangomva za Inu ndi makutu anga, koma tsopanonso ndakuonani ndi maso anga.
6 C’est pourquoi je me condamne et je me repens Sur la poussière et sur la cendre.
Nʼchifukwa chake ndi kuchita manyazi, ndikulapa podzithira fumbi ndi phulusa.”
7 Après que l’Éternel eut adressé ces paroles à Job, il dit à Éliphaz de Théman: Ma colère est enflammée contre toi et contre tes deux amis, parce que vous n’avez pas parlé de moi avec droiture comme l’a fait mon serviteur Job.
Yehova atayankhula ndi Yobu mawu amenewa anawuza Elifazi wa ku Temani kuti, “Ine ndakukwiyira pamodzi ndi abwenzi ako awiri, chifukwa simunayankhule zabwino za Ine, monga mmene wayankhulira mtumiki wanga Yobu.
8 Prenez maintenant sept taureaux et sept béliers, allez auprès de mon serviteur Job, et offrez pour vous un holocauste. Job, mon serviteur, priera pour vous, et c’est par égard pour lui seul que je ne vous traiterai pas selon votre folie; car vous n’avez pas parlé de moi avec droiture, comme l’a fait mon serviteur Job.
Kotero tsopano mutenge ngʼombe zazimuna zisanu ndi ziwiri ndi nkhosa zazimuna zisanu ndi ziwiri ndi kupita nazo kwa mtumiki wanga Yobu kuti mukapereke nsembe zopsereza. Mtumiki wanga Yobu adzakupemphererani, ndipo Ine ndidzalandira pemphero lake. Sindidzakuchitirani kanthu molingana ndi uchitsiru wanu. Inu simunayankhule zabwino za Ine, monga anayankhulira Yobu mtumiki wanga.”
9 Éliphaz de Théman, Bildad de Schuach, et Tsophar de Naama allèrent et firent comme l’Éternel leur avait dit: et l’Éternel eut égard à la prière de Job.
Motero Elifazi wa ku Temani, Bilidadi wa ku Suki ndi Zofari wa ku Naama anachita zimene Yehova anawawuza ndipo Yehova anamvera pemphero la Yobu.
10 L’Éternel rétablit Job dans son premier état, quand Job eut prié pour ses amis; et l’Éternel lui accorda le double de tout ce qu’il avait possédé.
Yobu atawapempherera abwenzi ake aja, Yehova anamubwezera chuma chake ndipo anamupatsa mowirikiza kuposa zomwe anali nazo kale.
11 Les frères, les sœurs, et les anciens amis de Job vinrent tous le visiter, et ils mangèrent avec lui dans sa maison. Ils le plaignirent et le consolèrent de tous les malheurs que l’Éternel avait fait venir sur lui, et chacun lui donna un kesita et un anneau d’or.
Abale ake ndi alongo ake onse, kuphatikizapo onse amene ankamudziwa kale, amabwera kwa iye nʼkudzadya naye chakudya mʼnyumba mwake. Iwo anamutonthoza ndi kumupepesa chifukwa cha mavuto onse amene Yehova analola kuti amugwere. Aliyense wa iwowa anamupatsa ndalama ndi mphete yagolide.
12 Pendant ses dernières années, Job reçut de l’Éternel plus de bénédictions qu’il n’en avait reçu dans les premières. Il posséda quatorze mille brebis, six mille chameaux, mille paires de bœufs, et mille ânesses.
Yehova anadalitsa Yobu pa masiku ake otsirizawa kupambana poyamba paja. Iye anali ndi nkhosa 14,000, ngamira 6,000, ngʼombe zantchito 2,000 ndi abulu aakazi 1,000.
13 Il eut sept fils et trois filles:
Anaberekanso ana aamuna asanu ndi awiri ndi ana aakazi atatu.
14 il donna à la première le nom de Jemima, à la seconde celui de Ketsia, et à la troisième celui de Kéren-Happuc.
Mwana wake wamkazi woyamba anamutcha Yemima, wachiwiri anamutcha Keziya, wachitatu anamutcha Kereni Hapuki.
15 Il n’y avait pas dans tout le pays d’aussi belles femmes que les filles de Job. Leur père leur accorda une part d’héritage parmi leurs frères.
Mʼdziko monsemo munalibe akazi okongola ngati ana a Yobu, ndipo abambo awo anawapatsa cholowa pamodzi ndi alongo awo.
16 Job vécut après cela cent quarante ans, et il vit ses fils et les fils de ses fils jusqu’à la quatrième génération.
Zitachitika zimenezi, Yobu anakhala ndi moyo zaka 140. Iye anaona zidzukulu zake mpaka mʼbado wachinayi.
17 Et Job mourut âgé et rassasié de jours.
Potsiriza, Yobu anamwalira ali nkhalamba ya zaka zochuluka kwambiri.